Lachitatu, October 15
Ine ndine Alefa ndi Omega.—Chiv. 1:8.
Mawu akuti alefa amapezeka kumayambiriro kwa afabeti ya Chigiriki ndipo mawu akuti omega amapezeka kumapeto. Pogwiritsa ntchito mawu akuti “Alefa ndi Omega,” Yehova anasonyeza kuti akayamba kuchita chinthu sasiya mpaka chitatheka. Atangolenga Adamu ndi Hava, Yehova anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi ndipo muziliyang’anira.” (Gen. 1:28) Pa nthawi imeneyi zinali ngati Yehova akunena kuti “Alefa.” Apa iye anafotokoza momveka bwino cholinga chake. Cholingacho chinali choti pakapita nthawi, ana a Adamu ndi Hava omwe akanakhala angwiro komanso omvera adzaze dzikoli n’kulikonza kukhala Paradaiso. Pa nthawi imeneyi m’pamene zikanakhala ngati wanena kuti “Omega.” Atamaliza kulenga “kumwamba ndi dziko lapansi komanso zonse zimene zili mmenemo,” ananena mawu otsimikizira kuti cholinga chake chidzatheka. Yehova ankatsimikizira kuti cholinga chake chokhudza dziko komanso anthu sichidzalephereka. Cholingachi chikanakwaniritsidwa kumapeto kwa tsiku la 7.—Gen. 2:1-3. w23.11 5 ¶13-14
Lachinayi, October 16
Konzani njira ya Yehova! Mulungu wathu mukonzereni msewu wowongoka wodutsa m’chipululu.—Yes. 40:3.
Ulendo wovuta wochokera ku Babulo kupita ku Isiraeli ukanawatengera Ayuda miyezi pafupifupi 4. Koma Yehova anali atalonjeza kuti adzachotsa chilichonse chomwe chinkaoneka kuti chingawalepheretse kubwerera. Kwa Ayuda okhulupirika, kubwerera ku Isiraeli kunali kofunika kwambiri kuposa chilichonse chomwe akanasiya. Chofunika kwambiri chinali chakuti zinthu zikanayambiranso kuwayendera bwino pa nkhani ya kulambira. Ku Babulo kunalibeko kachisi wa Yehova. Kunalibe guwa limene Aisiraeli akanamaperekapo nsembe zomwe zinkafunika malinga ndi Chilamulo cha Mose. Komanso kunalibe ansembe omwe akanamapereka nsembezo. Kuwonjezera pamenepo, anthu a Yehova anali ochepa kwambiri poyerekeza ndi amuna ndi akazi achikunja omwe sankalemekeza Yehova kapenanso mfundo zake. Choncho Ayuda ambiri okhulupirika ankafunitsitsa atabwerera kwawo kuti akabwezeretse kulambira koona. w23.05 14-15 ¶3-4
Lachisanu, October 17
Pitirizani kuyenda ngati ana a kuwala.—Aef. 5:8.
Timafunika mzimu woyera wa Mulungu kuti tipitirize kuchita zinthu ngati “ana a kuwala.” Chifukwa chiyani? Chifukwa si zophweka kupitiriza kukhala oyera m’dziko la makhalidwe oipali. (1 Ates. 4:3-5, 7, 8) Mzimu woyera ungatithandize kupewa maganizo a m’dzikoli kuphatikizapo nzeru za anthu komanso mfundo zimene zimasemphana ndi maganizo a Mulungu. Ungatithandizenso kuti tizichita ‘chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama.’ (Aef. 5:9) Njira imodzi imene tingalandirire mzimu woyera ndi kuupempha. Yesu ananena kuti Yehova “adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akumupempha.” (Luka 11:13) Komanso tikamatamanda Yehova pamisonkhano ndi Akhristu anzathu timalandira mzimu woyera. (Aef. 5:19, 20) Mzimu woyera umatithandiza kuti tizichita zinthu zimene zimasangalatsa Mulungu. w24.03 23-24 ¶13-15