MUTU 1
Mulungu Analenga Kumwamba ndi Dziko Lapansi
Yehova Mulungu ndi amene anatilenga. Iye analenganso zinthu zonse zimene timaonazi komanso zimene sitingathe kuziona. Koma asanalenge zinthu zimene timaonazi, analenga angelo ambirimbiri. Kodi angelo umawadziwa? Angelo ndi osiyana ndi anthu, ndipo mofanana ndi Yehova amene sitingathe kumuona, nawonso angelo sitingathe kuwaona. Mngelo woyamba kulengedwa anathandiza Yehova kulenga zinthu zina zonse. Anamuthandiza kulenga nyenyezi ndi mapulaneti komanso zinthu zina zonse. Limodzi mwa mapulaneti amenewo ndi dziko lathu lapansi lokongolali.
Kenako Yehova anakonza dziko lapansili kuti pazikhala nyama ndi anthu. Anapangitsanso kuti kuwala kwa dzuwa kuzifika padzikoli. Komanso analenga mapiri, nyanja ndi mitsinje.
Kodi ukudziwa zimene anachita kenako? Yehova anati: ‘Ndipanga udzu, mitengo ndi zomera zina.’ Choncho padzikoli panayamba kumera mitengo ya zipatso, maluwa komanso zinthu zina. Kenako Yehova analenga nyama zosiyanasiyana, zina zouluka, zina zam’madzi ndipo zina zinali zokwawa. Nyama zina zinali zing’onozing’ono monga akalulu ndipo zina zinali zikuluzikulu monga njovu. Kodi iweyo nyama imene imakusangalatsa ndi iti?
Kenako Yehova anauza mngelo woyamba uja kuti: “Tiyeni tipange munthu.” Anthu analengedwa mosiyana ndi nyama chifukwa amatha kupanga zinthu, amalankhula, kuseka komanso kupemphera. Yehova anauza anthuwo kuti aziyang’anira dziko lapansi ndi nyama. Kodi ukudziwa kuti munthu woyamba kulengedwa anali ndani? Tiona m’mutu wotsatira.
“Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1