Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
    Yandikirani Yehova
    • Yosefe wamangidwa ndipo ali m’ndende ndi akaidi ena.

      MUTU 11

      “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”

      1, 2. (a) Kodi ndi zinthu zopanda chilungamo ziti zimene zinachitikira Yosefe? (b) Kodi Yehova anachita chiyani pothetsa zinthu zopanda chilungamozo?

      MNYAMATA wina anachitiridwa zinthu zomwe sizinali zachilungamo ngakhale pang’ono. Mnyamata ameneyu anali wooneka bwino kwambiri ndipo sanalakwe chilichonse, koma anali m’ndende chifukwa chomunamizira kuti ankafuna kugwiririra mkazi. Komatu aka sikanali koyamba kuti achitiridwe zinthu zopanda chilungamo. M’mbuyomo ali ndi zaka 17, mnyamatayu yemwe dzina lake ndi Yosefe, azichimwene ake enieni ankafuna kumupha ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo kudziko lina. Kumeneko mkazi wa abwana ake ankamunyengerera kuti agone naye koma iye anakana. Mkaziyo ataona kuti Yosefe wamukana, anamunamizira kuti amafuna kumugwiririra ndipo zimenezi ndi zimene zinachititsa kuti atsekeredwe m’ndende. Zinali zomvetsa chisoni chifukwa zinkaoneka ngati palibe aliyense amene akanamuthandiza.

      2 Komabe, Mulungu yemwe “amakonda chilungamo ndipo amaweruza mosakondera” ankaona zonsezo. (Salimo 33:5) Yehova anachitapo kanthu kuti athetse zinthu zopanda chilungamozo ndipo Yosefe anamasulidwa. Kuwonjezera pamenepo, Yosefe yemwe anali mkaidi, anapatsidwa udindo waukulu kwambiri ndiponso ulemu wapadera. (Genesis 40:15; 41:41-43; Salimo 105:17, 18) Pamapeto pake anthu anadziwa kuti Yosefe analibe mlandu ndipo iye anagwiritsa ntchito udindo wake wapamwambawu pothandiza kuti zofuna za Mulungu zichitike.​—Genesis 45:5-8.

      Yosefe anakumana ndi zinthu zopanda chilungamo m’ndende

      3. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti tonsefe timafuna kuti tizichitiridwa zinthu mwachilungamo?

      3 Nkhani ya Yosefe imatilimbikitsa kwambiri chifukwa tonsefe ena anatichitirapo zinthu zopanda chilungamo kapena tinaonapo ena zikuwachitikira. Zoonadi, aliyense amafuna azichitiridwa zinthu moyenera komanso mosakondera. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Yehova anatilenga m’njira yoti tizisonyeza makhalidwe ake, ndipo chilungamo ndi limodzi mwa makhalidwe ake akuluakulu. (Genesis 1:27) Kuti timudziwe bwino Yehova, tifunika kumvetsa mmene amaonera chilungamo. Zimenezi zingatithandize kuti tiyambe kusangalala ndi mmene amachitira zinthu komanso kuti akhale mnzathu wapamtima.

      Kodi Chilungamo N’chiyani?

      4. Kodi nthawi zambiri anthu amaona kuti chilungamo n’chiyani?

      4 Nthawi zambiri anthu amaona kuti chilungamo ndi kugwiritsa ntchito malamulo mosakondera. Buku lina limanena kuti “chilungamo chimakhudza malamulo, zimene munthu amaloledwa kuchita, zimene ayenera kuchita ndiponso mfundo yoti munthu ayenera kupatsidwa mphoto kapena kulangidwa pa zimene wachita.” (Right and Reason​—Ethics in Theory and Practice) Koma chilungamo cha Yehova sichimangotanthauza kugwiritsa ntchito malamulo chifukwa choti akufunika kugwira ntchito kapenanso chifukwa choti iye ali ndi udindo wogwiritsa ntchito malamulowo.

      5, 6. (a) Kodi mawu a zilankhulo zoyambirira omwe anawamasulira kuti “chilungamo” amatanthauza chiyani? (b) Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamati Mulungu ndi wachilungamo?

      5 Tingamvetse bwino chilungamo cha Yehova tikaganizira mawu a zilankhulo zoyambirira omwe anawagwiritsa ntchito m’Baibulo pofotokoza mawu akuti chilungamo. Mawu amene anawagwiritsa ntchitowa angatanthauze “zoyenera” kapena “kuchita zabwino.”​—Genesis 18:25; Amosi 5:24.

      6 Choncho Baibulo likamanena kuti Mulungu ndi wachilungamo, limasonyeza kuti iye amachita zinthu zoyenera ndipo nthawi zonse amazichita mopanda tsankho. (Aroma 2:11) Sitingayembekezere kuti iye angachite zosiyana ndi zimenezi. Elihu, yemwe anali wokhulupirika, anati: “N’zosatheka kuti Mulungu woona achite zoipa, kapena kuti Wamphamvuyonse achite zinthu zolakwika.” (Yobu 34:10) N’zosathekadi kuti Yehova achite zinthu zopanda chilungamo. Chifukwa chiyani? Pali zifukwa ziwiri zikuluzikulu.

      7, 8. (a) N’chifukwa chiyani Yehova sangachite zinthu zopanda chilungamo? (b) Kodi n’chiyani chimachititsa kuti Yehova azichitira anthu zinthu zachilungamo?

      7 Choyamba, iye ndi woyera. Monga tinaonera m’Mutu 3, Yehova ndi woyera kwambiri ndiponso wolungama. Choncho sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Popeza Yehova yemwe ndi Bambo athu ndi woyera, tingakhulupirire ndi mtima wonse kuti sangatichitire zoipa. Yesu ankakhulupirira kwambiri zimenezi. Pa usiku wake womaliza padzikoli, anapemphera kuti: “Atate Woyera, ayang’anireni (kutanthauza ophunzira ake) chifukwa cha dzina lanu.” (Yohane 17:11) M’Malemba, ndi Yehova yekha amene amatchulidwa kuti “Atate Woyera.” Zimenezi n’zoyenera, chifukwa palibe bambo aliyense amene angafanane ndi Yehova pa nkhani yokhala woyera. Yesu ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova, yemwe ndi woyera pa chilichonse ndipo alibiretu uchimo, adzateteza ophunzira ake.​—Mateyu 23:9.

      8 Chachiwiri, Mulungu ndi wosadzikonda ndipo nthawi zonse amasonyeza chikondi. Chikondi chimenechi chimamupangitsa kuti azichitira ena zinthu mwachilungamo. Koma anthu opanda chilungamo amachitira ena zoipa chifukwa cha dyera komanso kudzikonda, zomwe ndi zosiyana ndi chikondi. Ponena za Mulungu wachikondi, Baibulo limatitsimikizira kuti: “Yehova ndi wolungama. Iye amakonda ntchito zolungama.” (Salimo 11:7) Ponena za iyeyo, Yehova anati: “Ine Yehova ndimakonda chilungamo.” (Yesaya 61:8) Kodi si zolimbikitsa kudziwa kuti Mulungu wathu amasangalala kuchita zoyenera, kapena kuti zachilungamo?​—Yeremiya 9:24.

      Chifundo Ndiponso Chilungamo cha Yehova

      9-11. (a) Kodi chilungamo cha Yehova chimagwirizana bwanji ndi chifundo chake? (b) Kodi mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ochimwa zimasonyeza bwanji kuti ndi wachilungamo ndiponso wachifundo?

      9 Mofanana ndi ena mwa makhalidwe, Yehova amasonyeza chilungamo m’njira yabwino kwambiri. Mose anatamanda Yehova kuti: “Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita zinthu zopanda chilungamo. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.” (Deuteronomo 32:3, 4) Nthawi zonse Yehova akamasonyeza chilungamo, salakwitsa zinazake. Iye si wolekerera komanso sachita zinthu mwankhanza.

      10 Chilungamo cha Yehova n’chogwirizana kwambiri ndi chifundo chake. Lemba la Salimo 116:5 limati: “Yehova ndi wokoma mtima komanso wolungama. Mulungu wathu ndi wachifundo.” Zoonadi, Yehova ndi wachifundo ndiponso wachilungamo. Makhalidwe awiriwa si otsutsana. Yehova akasonyeza chifundo, sizitanthauza kuti akanapanda kuchita zimenezi chilungamo chake chikanachititsa kuti apereke chiweruzo chokhwima. M’malomwake, iye amasonyeza makhalidwe awiri onsewa pa nthawi imodzi. Taganizirani chitsanzo ichi.

      11 Tonsefe tinatengera uchimo kwa Adamu, choncho timayenera kulandira chilango cha uchimowo chomwe ndi imfa. (Aroma 5:12) Koma Yehova sasangalala ndi imfa ya anthu ochimwa. Iye ndi ‘Mulungu wokonzeka kukhululuka, wachisomo ndiponso wachifundo.’ (Nehemiya 9:17) Komabe popeza ndi woyera, sangalekerere zinthu zosalungama. Ndiye kodi angasonyeze bwanji chifundo kwa anthu omwe anatengera uchimo? Mfundo ina yofunika kwambiri ya choonadi yopezeka m’Mawu a Mulungu imatithandiza kupeza yankho. Mfundoyi ndi yakuti Yehova anapereka dipo kuti apulumutse anthu. Tidzaphunzira zambiri pa nkhaniyi m’Mutu 14. Zimene Yehova anachitazi zimasonyeza kuti ndi wachilungamo komanso wachifundo kwambiri. Pogwiritsa ntchito dipoli iye angachitire chifundo anthu ochimwa omwe alapa, kwinaku akutsatirabe mfundo zake zokhudza chilungamo.​—Aroma 3:21-26.

      Chilungamo cha Yehova Chimatichititsa Kuti Tizimukonda

      12, 13. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti chilungamo cha Yehova chimatichititsa kuti tizifuna kuti akhale mnzathu? (b) Kodi Davide ananena chiyani zokhudza chilungamo cha Yehova, nanga zimenezi zingatilimbikitse bwanji?

      12 Chilungamo cha Yehova sichichititsa kuti tizichita naye mantha, koma ndi khalidwe labwino limene limatichititsa kufuna kuti akhale mnzathu. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Yehova amasonyeza chilungamo chake mwachifundo. Tiyeni tikambirane zitsanzo zina zolimbikitsa pa nkhaniyi.

      13 Chilungamo cha Yehova, chomwe amachisonyeza mosalakwitsa chilichonse, chimamuchititsa kukhala wokhulupirika kwa atumiki ake. Wolemba masalimo Davide anaona umboni wa zimenezi. Kuchokera pa zimene zinamuchitikira ndiponso zimene anaphunzira zokhudza Yehova, iye anati: “Yehova amakonda chilungamo, ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.” (Salimo 37:28) Amenewatu ndi mawu olimbikitsa kwambiri. Mulungu wathu sadzasiya ngakhale pang’ono atumiki ake okhulupirika. Choncho tingamukhulupirire kuti amakhala nafe pafupi komanso amatikonda. Izi zili choncho chifukwa choti iye ndi wachilungamo.​—Miyambo 2:7, 8.

      14. Kodi Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisiraeli chimasonyeza bwanji kuti iye amadera nkhawa anthu ovutika?

      14 Chilungamo cha Mulungu chimamuchititsa kuti azichita zinthu moganizira anthu ovutika. Mfundo yoti Yehova amadera nkhawa anthu ovutika imaoneka bwino m’Chilamulo chimene anapatsa Aisiraeli. Mwachitsanzo, m’Chilamulochi munali malamulo apadera omwe ankathandiza kuti akazi amasiye ndi ana amasiye azisamaliridwa. (Deuteronomo 24:17-21) Podziwa kuti moyo wa mabanja amenewa umakhala wovuta, Yehova, yemwe “amachitira chilungamo ana amasiye ndi akazi amasiye,”a anakhala Woweruza wawo ndiponso Bambo wowateteza. (Deuteronomo 10:18; Salimo 68:5) Yehova anachenjeza Aisiraeli kuti ngati angazunze akazi ndi ana opanda owateteza, adzamva kulira kwawo. Iye anati: “Mkwiyo wanga udzakuyakirani.” (Ekisodo 22:22-24) Ngakhale kuti kukwiya si limodzi mwa makhalidwe akuluakulu a Yehova, chilungamo chake chimamuchititsa kukwiya ngati mwadala anthu akuchitira ena zinthu zopanda chilungamo, makamaka otsika ndiponso osowa owathandiza.​—Salimo 103:6.

      15, 16. Fotokozani mfundo yochititsa chidwi yosonyeza kuti Yehova alibe tsankho.

      15 Yehova amatitsimikiziranso kuti “sakondera munthu aliyense ndipo salandira chiphuphu.” (Deuteronomo 10:17) Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amene ali ndi udindo kapena mphamvu amachita, Yehova sakopeka ndi chuma kapena mmene munthu akuonekera. Iye sakondera komanso alibe tsankho ngakhale pang’ono. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo yochititsa chidwi iyi yosonyeza kuti zimenezi ndi zoona. Mwayi wokhala atumiki ake, omwe akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha, sunaperekedwe kwa anthu apadera ochepa okha. M’malomwake, “iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Munthu aliyense angakhale ndi chiyembekezo chimenechi mosatengera kuti ndi wotani, ali ndi khungu lamtundu wanji komanso amachokera dziko liti. Kodi chilungamo chingapose pamenepa?

      16 Palinso njira ina imene Yehova amasonyezera chilungamo chake yomwenso tiyenera kuiganizira. Njirayi ndi yokhudza mmene amachitira zinthu ndi anthu amene aphwanya mfundo zake zachilungamo.

      Amapereka Chilango

      17. Fotokozani chifukwa chake zoipa zomwe zikuchitika m’dzikoli si umboni wakuti Yehova si wachilungamo.

      17 Ena angafunse kuti: ‘Popeza Yehova sasangalala ndi zinthu zopanda chilungamo, nanga n’chifukwa chiyani masiku ano anthu osalakwa akuvutika komanso makhalidwe oipa ali paliponse m’dzikoli?’ Komatu zoipa zimenezi si umboni wakuti Yehova si wachilungamo. Zinthu zambiri zopanda chilungamo zomwe zimachitika m’dziko loipali ndi zotsatirapo za uchimo womwe anthu anatengera kwa Adamu. M’dzikoli mumachitika zinthu zopanda chilungamo chifukwa choti anthu ambiri asankha kumachita zoipa, komabe zimenezi zitha posachedwapa.​—Deuteronomo 32:5.

      18, 19. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova sadzalekerera mpaka kalekale anthu amene amaphwanya mwadala malamulo ake olungama?

      18 Ngakhale kuti Yehova amasonyeza chifundo chachikulu kwa anthu amtima wabwino omwe akufuna kukhala anzake, sadzalola kuti dzina lake lizinyozedwa mpaka kalekale. (Salimo 74:10, 22, 23) Mulungu wachilungamo sapusitsika ndipo sadzalola kuti anthu omwe samumvera mwadala asalandire chilango chomwe akuyenera kulandira. Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka komanso choonadi, . . . koma sadzalekerera wolakwa osam’patsa chilango.” (Ekisodo 34:6, 7) Mogwirizana ndi mawu amenewa, nthawi zina Yehova amaona kuti m’pofunika kulanga anthu amene amaphwanya mwadala malamulo ake olungama.

      19 Mwachitsanzo, taganizirani za Aisiraeli. Nthawi zambiri ankachita zinthu zosakhulupirika ngakhale pamene anakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa. Zochita zawo zoipa ‘zinkakhumudwitsa’ Yehova, komabe iye sanawasiye nthawi yomweyo. (Salimo 78:38-41) M’malomwake, ankawachitira chifundo ndipo ankawapatsa mwayi woti asinthe zochita zawo. Anawachonderera kuti: “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa, koma ndimafuna kuti munthu woipa asinthe zochita zake n’kupitiriza kukhala ndi moyo. Bwererani! Bwererani n’kusiya zinthu zoipa zimene mukuchita. Muferenji inu a nyumba ya Isiraeli?” (Ezekieli 33:11) Poona kuti moyo ndi wamtengo wapatali, Yehova anatumiza aneneri ake mobwerezabwereza kuti mwina Aisiraeli angasiye makhalidwe awo oipa. Koma ambiri anaumitsa mitima yawo ndipo sanalape. Pamapeto pake Yehova anawapereka m’manja mwa adani awo pofuna kuteteza dzina lake loyera komanso zonse zimene dzinalo limaimira.​—Nehemiya 9:26-30.

      20. (a) Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli? (b) N’chifukwa chiyani n’zoyenera kuti mkango ndi chizindikiro cha chilungamo cha Yehova?

      20 Kodi tingaphunzire chiyani tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli? Tikuphunzira kuti maso ake omwe amaona chilichonse, amaonanso zinthu zosalungama ndipo zimene amaonazo zimamukhudza kwambiri. (Miyambo 15:3) N’zolimbikitsanso kudziwa kuti amasonyeza chifundo ngati pali chifukwa chochitira zimenezi. Komanso tikuphunzirapo kuti amaleza mtima ndipo amapereka mwayi kwa anthu kuti asinthe. Chifukwa choti Yehova ndi woleza mtima, anthu ambiri amaganiza molakwika kuti sadzaweruza anthu oipa. Koma zimenezi si zoona, chifukwa mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi Aisiraeli zimatiphunzitsanso kuti kuleza mtima kwake kuli ndi malire. Nthawi zonse Yehova amaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Mosiyana ndi anthu, omwe nthawi zambiri amalephera kuchita chilungamo, Yehova amalimba mtima n’kuchita zinthu mwachilungamo. Mpake kuti Baibulo limagwiritsa ntchito mkango, womwe ndi nyama yolimba mtima, ngati chizindikiro cha chilungamo cha Yehova.b (Ezekieli 1:10; Chivumbulutso 4:7) Choncho tisamakayikire kuti adzakwaniritsa lonjezo lake loti adzachotsa zinthu zopanda chilungamo padzikoli. Mwachidule tinganene kuti iye amaweruza chonchi: amachita zinthu molimba mtima pamene pakufunika kutero, ndipo amasonyeza chifundo ngati zingatheke.​—2 Petulo 3:9.

      Yesetsani Kuti Mulungu Wachilungamo Akhale Mnzanu

      21. Tikamaganizira mmene Yehova amasonyezera chilungamo, kodi tizimuona kuti ndi wotani, nanga n’chifukwa chiyani?

      21 Tikamaganizira mmene Yehova amasonyezera chilungamo, tisamaone kuti iye ali ngati woweruza wosaganizira ena yemwe amangofuna kupereka chilango kwa olakwa. M’malomwake, tizimuona ngati bambo wachikondi koma wolimba mtima, amene nthawi zonse amachita zinthu ndi ana ake m’njira yabwino kwambiri. Popeza Yehova ndi Bambo wachilungamo, sasunthika pa nkhani yochita chilungamo koma pa nthawi imodzimodziyo amasonyezanso chifundo kwa ana ake apadziko lapansi, omwe amafunika kuwathandiza ndiponso kuwakhululukira.​—Salimo 103:10, 13.

      22. Chifukwa cha chilungamo chake, kodi Yehova anakonza zoti tikhale ndi chiyembekezo chotani, nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?

      22 Tikuthokoza chifukwa sikuti Mulungu amasonyeza chilungamo chake polanga anthu olakwa basi. Chifukwa cha chilungamo chake, Yehova anakonza zoti tiziyembekezera kudzakhala ndi moyo wangwiro komanso wosatha m’dziko limene ‘mudzakhale chilungamo.’ (2 Petulo 3:13) Zimenezi zikusonyeza kuti chifukwa choti Yehova ndi wachilungamo, amafuna kupulumutsa anthu, osati kuwalanga. Zoonadi, tikamvetsa bwino zokhudza chilungamo cha Yehova, timafunitsitsa kuti akhale mnzathu. M’mitu yotsatirayi, tiphunzira mmene Yehova amasonyezera khalidwe labwino kwambiri limeneli.

      a Mawu akuti “mwana wamasiye” akusonyeza kuti Yehova amadera nkhawa kwambiri ana onse amasiye, kaya aamuna kapena aakazi. Yehova anaonetsetsa kuti m’Chilamulo mwalembedwa zokhudza chigamulo chomwe chinaperekedwa pa nkhani ya ana aakazi a Tselofekadi omwe anali amasiye. Chigamulo chimenechi chinakhala lamulo ndipo chinkateteza ufulu wa ana aakazi amasiye.​—Numeri 27:1-8.

      b N’zochititsa chidwi kuti Yehova anadziyerekezera ndi mkango pamene ankapereka chiweruzo kwa Aisiraeli osakhulupirika.​—Yeremiya 25:38; Hoseya 5:14.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Yeremiya 18:1-11 Kodi Yehova anaphunzitsa bwanji Yeremiya kuti safulumira kulanga munthu?

      • Habakuku 1:1-4, 13; 2:2-4 Kodi Yehova anatsimikizira bwanji Habakuku kuti sadzalola kuti zinthu zopanda chilungamo zikhalepo mpaka kalekale?

      • Zekariya 7:8-14 Kodi Yehova amamva bwanji anthu ena akamapondereza ufulu wa anzawo?

      • Aroma 2:3-11 Kodi Yehova amaweruza munthu aliyense ndiponso mitundu ya anthu potengera chiyani?

  • “Kodi Mulungu Alibe Chilungamo?”
    Yandikirani Yehova
    • Loti ndi ana ake aakazi awiri afika bwinobwino mumzinda wa Zowari pamene sulufule ndi moto zikugwera mumzinda wa Sodomu ndi Gomora.

      MUTU 12

      “Kodi Mulungu Alibe Chilungamo?”

      1. Kodi timamva bwanji tikaona zinthu zopanda chilungamo?

      MAYI wamasiye yemwenso ndi wachikulire amubera ndalama zimene ankasunga. Kholo louma mtima lasiya mwana wake wakhanda. Bambo wina waikidwa m’ndende pa mlandu woti sanapalamule. Kodi mumamva bwanji mukaganizira zinthu ngati zimenezi? Ziyenera kuti zimakukhumudwitsani ndipo m’pake kumva choncho. Mwachibadwa, anthufe timasangalala ndi zinthu zabwino ndipo timakhumudwa ndi zinthu zoipa. Zinthu zopanda chilungamo zikachitika, zimatikwiyitsa. Timafuna kuti amene walakwiridwayo apatsidwe chipukuta misozi ndipo wolakwayo alangidwe. Ngati zimenezi sizikuchitika, timadzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu akuona zimenezi? N’chifukwa chiyani sakuchitapo kanthu?’

      2. Kodi Habakuku anatani ataona zinthu zopanda chilungamo zomwe zinkachitika, nanga n’chifukwa chiyani Yehova sanamudzudzule?

      2 Kuyambira kale, atumiki okhulupirika a Yehova akhala akufunsa mafunso ngati amenewa. Mwachitsanzo, mneneri Habakuku anapemphera kwa Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zopanda chilungamo zoopsa chonchi? N’chifukwa chiyani mukulola kuti chiwawa, kusamvera malamulo, uchigawenga ndiponso nkhanza zifalikire paliponse?” (Habakuku 1:3, Contemporary English Version) Yehova sanadzudzule Habakuku chifukwa chofunsa mafunso moona mtima, chifukwa iye ndi amene anatilenga m’njira yoti tizikonda chilungamo. Pang’ono pokha, timasonyeza mmene Yehova amamvera pa nkhani ya chilungamo.

      Yehova Amadana ndi Zinthu Zopanda Chilungamo

      3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amadziwa bwino kwambiri zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitika kuposa ifeyo?

      3 Yehova amadziwa zinthu zopanda chilungamo zonse zomwe anthu amachita. Ponena za m’nthawi ya Nowa, Baibulo limati: “Yehova anaona kuti anthu aipa kwambiri padziko lapansi. Anaona kuti maganizo a anthu komanso zofuna za mtima wawo zinali zoipa zokhazokha nthawi zonse.” (Genesis 6:5) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Nthawi zambiri anthufe timangodziwa zinthu zopanda chilungamo zimene zachitikira ifeyo kapena zimene tamva kuti zachitikira ena. Koma Yehova amadziwa zinthu zopanda chilungamo zomwe zikuchitika padziko lonse. Iye amaona chilichonse. Kuwonjezera pamenepo, amadziwanso maganizo olakwika amene munthu ali nawo, omwe amam’pangitsa kuti achite zinthu zopanda chilungamo.​—Yeremiya 17:10.

      4, 5. (a) Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amadera nkhawa anthu amene achitiridwa zinthu zopanda chilungamo? (b) Kodi Yehova wakumanapo ndi zinthu zopanda chilungamo ziti?

      4 Koma sikuti Yehova amangodziwa zinthu zopanda chilungamo zimene anthu amachita. Amaderanso nkhawa anthu amene achitiridwa zinthu zopanda chilungamowo. Pamene anthu amitundu ina ankachitira nkhanza anthu ake, Yehova ankawamvera chisoni chifukwa ankamva “kulira kwawo chifukwa cha anthu omwe ankawapondereza komanso kuwachitira nkhanza.” (Oweruza 2:18) Mwina munaonapo kuti anthu ena akaona mobwerezabwereza zinthu zopanda chilungamo, amangofika pozizolowera ndipo samvanso chisoni. Koma Yehova sachita zimenezo. Ngakhale kuti waona zinthu zopanda chilungamo kwa zaka pafupipafupi 6,000, iye amadana nazobe. Ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova amanyansidwa ndi zinthu monga “lilime lonama,” “manja amene amakhetsa magazi a anthu osalakwa” komanso “mboni yachinyengo imene nthawi zonse imanena mabodza.”​—Miyambo 6:16-19.

      5 Taganiziraninso mmene Yehova anadzudzulira mwamphamvu atsogoleri opanda chilungamo a ku Isiraeli. Iye anauza mneneri wake kuti awafunse kuti: “Kodi simukuyenera kudziwa chilungamo?” Yehova atafotokoza momveka bwino mmene anthu achinyengowa ankagwiritsira ntchito mphamvu zawo molakwika, ananeneratu zimene zidzawachitikire kuti: “Adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha. Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo, chifukwa cha zochita zawo zoipa.” (Mika 3:1-4) Izitu zikusonyeza kuti Yehova amanyansidwa ndi zinthu zopanda chilungamo. Kumbukirani kuti iyenso zakhala zikumuchitikira. Kwa zaka zambirimbiri, Satana wakhala akumunyoza popanda chifukwa. (Miyambo 27:11) Ndiponso anthu anachitira Mwana wake zinthu zopanda chilungamo zoipa kwambiri. Ngakhale kuti Mwanayo “sanachite tchimo,” anaphedwa ngati chigawenga. (1 Petulo 2:22; Yesaya 53:9) N’zoonekeratu kuti Yehova amadziwa zinthu zopanda chilungamo zimene anthu akukumana nazo ndipo amawadera nkhawa.

      6. Kodi timamva bwanji zinthu zopanda chilungamo zikatichitikira, nanga n’chifukwa chiyani?

      6 Komabe, zinthu zopanda chilungamo zikatichitikira kapena zikachitikira ena, mwachibadwa timakhumudwa kwambiri. Tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu ndipo kupanda chilungamo n’kosiyana kwambiri ndi makhalidwe a Yehova. (Genesis 1:27) Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti zinthu zopanda chilungamo zizichitika?

      Nkhani Yofunika Kwambiri

      7. Kodi Satana ananena chiyani zokhudza Yehova m’munda wa Edeni?

      7 Yankho la funsoli ndi logwirizana ndi nkhani ina yofunika kwambiri. Monga taonera, Mlengi ali ndi ufulu wolamulira dziko lapansi ndiponso anthu onse. (Salimo 24:1; Chivumbulutso 4:11) Komabe anthu atangolengedwa chakumene, mngelo wina ananena bodza lokhudza Yehova komanso kuti salamulira bwino. Kodi zimenezi zinachitika bwanji? Yehova analamula Adamu, yemwe anali munthu woyamba, kuti asadye zipatso za mtengo winawake wa m’munda wa Edeni. Mulungu anamuuza kuti akapanda kumvera lamuloli ‘adzafa.’ (Genesis 2:17) Lamulo la Mulunguli linali losavuta kuti Adamu komanso mkazi wake Hava alitsatire. Komabe Satana anachititsa Hava kukhulupirira kuti Mulungu sanachite bwino kuwapatsa lamulo limeneli. Kodi Satana ananena kuti chingachitike n’chiyani Hava akadya zipatso za mtengowo? Iye anauza Hava mosapita m’mbali kuti: “Si zoona zimenezo, simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”​—Genesis 3:1-5.

      8. (a) Kodi Satana ankatanthauza chiyani pa zomwe anauza Hava? (b) Kodi Satana anatsutsa chiyani pa nkhani yokhudza ulamuliro wa Mulungu?

      8 Ponena mawu amenewa, Satana sankangotanthauza kuti Yehova anabisira Hava zinthu zimene ankafunika kuzidziwa, koma ankatanthauzanso kuti Yehova ananamiza Havayo. Satana anachititsa kuti Hava ayambe kukayikira Mulungu. Pamenepa ananyoza kwambiri dzina la Yehova. Iye anasonyezanso kuti Mulungu salamulira bwino. Satana anasamala kwambiri kuti asatsutse mfundo yoti Mulungu ndi wolamulira wa zinthu zonse. Koma ananena kuti si woyenera kulamulira, alibe ufulu wolamulira komanso salamulira mwachilungamo ndiponso m’njira yothandiza amene amawalamulirawo.

      9. (a) Kodi zotsatirapo za kusamvera kwa Adamu ndi Hava zinali zotani, nanga kunayambitsa mafunso ofunika ati? (b) N’chifukwa chiyani Yehova sanangopha oukirawo?

      9 Zotsatira zake zinali zakuti onse awiri, Adamu ndi Hava, sanamvere Yehova ndipo anadya zipatso za mtengo woletsedwawo. Chifukwa cha kusamverako, anafunika kulandira chilango cha imfa ngati mmene Mulungu ananenera. Koma bodza limene Satana ananena linayambitsa mafunso ofunika kwambiri. Kodi Yehova alidi ndi ufulu wolamulira anthu, kapena anthu ayenera kumadzilamulira okha? Kodi Yehova amalamuliradi bwino kwambiri? Popeza Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire, akanatha kuwononga oukirawo nthawi yomweyo. Komabe mafunsowa sankakhudza mphamvu za Mulungu koma dzina lake, zomwe zikuphatikizapo mmene amalamulirira. Choncho kupha Adamu, Hava ndiponso Satana sikukanathandiza kuti zitsimikizirike kuti Mulungu amalamulira mwachilungamo. M’malomwake, zikanangowonjezera vutolo. Njira yokha yotsimikizira kuti anthu sangathe kudzilamulira bwinobwino popanda Mulungu, inali kulola kuti papite nthawi anthuwo akudzilamulira.

      10. Kodi zimene zakhala zikuchitika zasonyeza chiyani pa nkhani ya ulamuliro wa anthu?

      10 Kwa zaka masauzande ambiri, anthu ayesapo maboma osiyanasiyana monga boma lolamulidwa ndi munthu mmodzi, boma la demokalase ndiponso mitundu ina ya maboma. Ndiye kodi zotsatira zake zimakhala zotani? Ndi zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) M’pake kuti mneneri Yeremiya ananena kuti: “Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu alibe ulamuliro wosankha yekha njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”​—Yeremiya 10:23.

      11. N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti anthu akumane ndi mavuto?

      11 Yehova anadziwa kuti anthu adzakumana ndi mavuto ambiri akamadzilamulira. Ndiye kodi iye anachita zinthu mopanda chilungamo polola kuti zimenezi zichitike? Ayi. Tiyerekeze kuti muli ndi mwana amene akufunika opaleshoni chifukwa ali ndi matenda oti akhoza kufa nawo. Mukudziwa kuti mwana wanuyo adzamva ululu chifukwa cha opaleshoniyo, ndipo zimenezi zikukumvetsani chisoni kwambiri. Koma mukudziwanso kuti opaleshoniyo imuthandiza kuti achire n’kumasangalala. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu ankadziwa ndipo ananeneratu kuti anthu adzakumana ndi mavuto chifukwa chowalola kuti azidzilamulira. (Genesis 3:16-19) Koma anadziwanso kuti angathe kudzachotsa mavuto onse ngati atalola kuti onse aone mavuto omwe amakhalapo anthu akamayesa kudzilamulira okha. Kuchita zimenezi kungathandize kuti nkhani ya ulamuliro wa Mulungu ithetsedwe mpaka kalekale.

      Nkhani Yokhudza Kukhulupirika kwa Anthu

      12. Mogwirizana ndi zimene nkhani ya Yobu ikusonyeza, kodi Satana anawanenera bodza lotani anthu?

      12 Pali mbali inanso yokhudza nkhaniyi. Ponena kuti Mulungu si woyenera kulamulira komanso salamulira mwachilungamo, sikuti Satana anangonena bodza lokhudza ulamuliro wa Yehova komanso dzina lake. Iye ananenanso bodza lokhudza kukhulupirika kwa atumiki a Mulungu. Mwachitsanzo, taonani zimene Satana anauza Yehova zokhudza munthu wolungama, Yobu. Iye anati: “Kodi inuyo simwamuteteza pomuikira mpanda? Mwatetezanso nyumba yake ndi zinthu zonse zimene ali nazo. Mwadalitsa ntchito ya manja ake ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri m’dzikoli. Koma panopa mutambasule dzanja lanu n’kuwononga zinthu zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”​—Yobu 1:10, 11.

      13. Kodi Satana ankatanthauza chiyani pa zomwe ananena zokhudza Yobu, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti zimenezi zikukhudza anthu onse?

      13 Satana ananena kuti Yehova ankagwiritsa ntchito mphamvu zake zoteteza pogula kukhulupirika kwa Yobu. Ponena zimenezi, Satana ankatanthauzanso kuti Yobu anali wokhulupirika mwachiphamaso ndipo ankalambira Mulungu chifukwa cha zimene ankamupatsa. Iye anati Yobu akanatha kutukwana Mlengi wake ngati akanapanda kumudalitsa. Satana ankadziwa kuti Yobu anali chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhala “munthu wokhulupirika amene amachita zoyenera, amaopa Mulungu ndiponso amapewa zoipa.”a Ankaganiza kuti ngati akanachititsa kuti Yobu asiye kukhala wokhulupirika, ndiye kuti akanathanso kuchita zimenezi kwa anthu onse. Choncho kwenikweni Satana ankanena kuti anthu amatumikira Mulungu pofuna kupezapo kenakake. Ndipotu posonyeza kuti nkhaniyo ikukhudza anthu onse, Satana anauza Yehova kuti: “Munthu angapereke chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.”​—Yobu 1:8; 2:4.

      14. Kodi zomwe zakhala zikuchitika zasonyeza chiyani pa zimene Satana ananena zokhudza anthu?

      14 Zimene zakhala zikuchitika zasonyeza kuti mofanana ndi Yobu, anthu ambiri akakumana ndi mayesero amakhalabe okhulupirika kwa Yehova. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi zimene Satana ananena. Anthuwa amasangalatsa mtima wa Yehova ndipo zimenezi zimachititsa kuti Yehovayo aziyankha Satana, yemwe amamutonza n’kumanena kuti anthu akhoza kusiya kutumikira Mulungu akakumana ndi mavuto. (Aheberi 11:4-38) Anthu a mitima yabwino samasiya kutumikira Mulungu. Amakhalabe okhulupirika ngakhale pamene akumana ndi mavuto aakulu ndipo amadalira kwambiri Yehova kuti awapatse mphamvu kuti athe kupirira.​—2 Akorinto 4:7-10.

      15. Kodi pangakhale funso liti lokhudza mmene Yehova anaweruzira anthu m’mbuyomu komanso mmene adzaweruzire m’tsogolomu?

      15 Koma sikuti chilungamo cha Yehova chimangokhudza nkhani ya ulamuliro wake, chimakhudzanso kukhulupirika kwa anthu. Baibulo limafotokoza mmene Yehova anaweruzira anthu ena paokha ndiponso mitundu ya anthu. Lilinso ndi maulosi onena kuti adzaweruza anthu m’tsogolomu. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhulupirira kuti Yehova anaweruza mwachilungamo ndipo m’tsogolomu adzaweruzanso mwachilungamo?

      Chilungamo cha Mulungu Chimaposa cha Aliyense

      Loti ndi ana ake aakazi awiri afika bwinobwino mumzinda wa Zowari pamene sulufule ndi moto zikugwera mumzinda wa Sodomu ndi Gomora. Kumbuyo kwawo kuli mkazi wake yemwe wasanduka chipilala chamchere.

      Yehova ‘sadzawononga olungama pamodzi ndi oipa’

      16, 17. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti nthawi zina anthu amalephera kuweruza mwachilungamo.

      16 Ponena za Yehova, Baibulo limanena zoona kuti: “Njira zake zonse ndi zolungama.” (Deuteronomo 32:4) Palibe munthu amene anganene kuti mmenemu ndi mmenenso iyeyo alili, chifukwa nthawi zambiri anthufe sitidziwa zonse ndipo zimenezi zimatilepheretsa kuzindikira kuti zoyenera ndi ziti. Mwachitsanzo taganizirani za Abulahamu. Anachonderera Yehova kuti asawononge mzinda wa Sodomu ngakhale kuti anthu amumzindawo anali oipa kwambiri. Iye anafunsa Yehova kuti: “Kodi zoona muwonongadi olungama pamodzi ndi oipa?” (Genesis 18:23-33) N’zodziwikiratu kuti yankho linali lakuti ayi. Yehova “anagwetsa sulufule ndi moto ngati mvula ku Sodomu” Loti ndi ana ake akazi atafika kale mumzinda wa Zowari. (Genesis 19:22-24) Mosiyana ndi zimenezi, Yona “anakwiya koopsa” pamene Mulungu anachitira chifundo anthu a ku Nineve. Popeza Yona anali atalengeza kale kuti iwo awonongedwa, akanasangalala kuwaona akuphedwa ngakhale kuti anthuwo anali atalapa mochokera pansi pa mtima.​—Yona 3:10 mpaka 4:1.

      17 Yehova anatsimikizira Abulahamu kuti sikuti amasonyeza chilungamo chake pongowononga oipa, koma populumutsanso anthu olungama. Pomwe Yona ankafunika kuphunzira mfundo yoti Yehova ndi wachifundo. Anthu akasiya kuchita zoipa, iye amakhala ‘wokonzeka kuwakhululukira.’ (Salimo 86:5) Mosiyana ndi anthu, Yehova sapereka chiweruzo chokhwima pongofuna kuti adziwike kuti ndi wamphamvu. Ndiponso salephera kuchitira anthu chifundo poopa kuti ena amuona ngati wofooka. Nthawi zonse amasonyeza chifundo pakakhala chifukwa chochitira zimenezo.​—Yesaya 55:7; Ezekieli 18:23.

      18. Perekani umboni wa m’Baibulo wosonyeza kuti Yehova salekerera zinthu zoipa chifukwa choti ndi wachifundo.

      18 Komabe, Yehova salekerera zoipa chifukwa choti ndi wachifundo. Pamene anthu ake ankapitirizabe kulambira mafano, iye analankhula mwamphamvu kuti: “Ndidzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndiponso kukulanga chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene umachita. Diso langa silidzakumvera chisoni ndipo sindidzakuchitira chifundo. Ndidzakulanga mogwirizana ndi njira zako.” (Ezekieli 7:3, 4) Choncho ngati anthu sakufuna kusintha, Yehova amawapatsa chilango. Koma sawaweruza pongotengera mphekesera. Moti atamva madandaulo ambiri okhudza Sodomu ndi Gomora, iye anati: “Ndipitako kuti ndikaone ngati akuchitadi zimene ndamvazo.” (Genesis 18:20, 21) Tikuthokoza kuti Yehova ndi wosiyana ndi anthu ambiri amene amangofulumira kuweruza asanamve mfundo zonse. M’pake kuti Baibulo limanena kuti Yehova ndi “Mulungu wokhulupirika, amene sachita zinthu zopanda chilungamo.”​—Deuteronomo 32:4.

      Musamakayikire Kuti Yehova Ndi Wachilungamo

      19. Kodi tingatani ngati sitikumvetsa zimene Yehova anachita pa nkhani inayake?

      19 Baibulo siliyankha mafunso onse okhudza zimene Yehova anachita m’mbuyomo. Silifotokozanso mwatsatanetsatane zinthu zonse zimene adzachite poweruza anthu ndi magulu a anthu m’tsogolomu. Choncho ngati sitikumvetsa nkhani zina kapena maulosi ena a m’Baibulo chifukwa choti sanafotokoze zinthu mwatsatanetsatane, tingasonyeze kukhulupirika ngati mneneri Mika, yemwe analemba kuti: “Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.”​—Mika 7:7.

      20, 21. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti nthawi zonse Yehova adzachita zinthu mwachilungamo?

      20 Tisamakayikire kuti Yehova adzachita zinthu mwachilungamo pa chilichonse. Ngakhale zitaoneka kuti anthu akulekerera zinthu zopanda chilungamo, Yehova amalonjeza kuti: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine.” (Aroma 12:19) Tikamayembekezera moleza mtima kuti Yehova achitepo kanthu, nafenso tinganene mawu ofanana ndi amene mtumwi Paulo ananena kuti: “Kodi Mulungu alibe chilungamo? Ayi ndithu.”​—Aroma 9:14.

      21 Panopa tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Kupanda chilungamo ndiponso ‘kuponderezana’ kwachititsa kuti anthu azichitidwa nkhanza kwambiri. (Mlaliki 4:1) Komabe Yehova sanasinthe. Iye amadanabe ndi kupanda chilungamo ndipo amadera nkhawa anthu amene amachitiridwa zopanda chilungamozo. Tikakhalabe okhulupirika kwa Yehova ndi ulamuliro wake, iye adzatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira mpaka nthawi imene adzachotse zinthu zonse zopanda chilungamo mu Ufumu wake.​—1 Petulo 5:6, 7.

      a Ponena za Yobu, Yehova anati: “Padziko lapansi palibe wina wofanana naye.” (Yobu 1:8) Ndiye kuti Yobu anakhalako Yosefe atamwalira kale komanso Mose asanasankhidwe kukhala mtsogoleri wa Aisiraeli. Choncho zinali zolondola pa nthawiyo kunena kuti panalibe yemwe anali wokhulupirika ngati Yobu.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Deuteronomo 10:17-19 N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova alibe tsankho?

      • Yobu 34:1-12 Anthu ena akakuchitirani zopanda chilungamo, kodi mawu a Elihu angakuthandizeni bwanji kuti muzikhulupirira kwambiri zoti Mulungu ndi wachilungamo?

      • Salimo 1:1-6 N’chifukwa chiyani n’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amaganizira mofatsa zochita za anthu olungama ndiponso oipa?

      • Malaki 2:13-16 Kodi Yehova ankamva bwanji chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene amuna ankachitira akazi awo pothetsa banja popanda zifukwa zomveka?

  • ‘Malamulo a Yehova Ndi Angwiro’
    Yandikirani Yehova
    • Mose akutsika m’phiri atanyamula miyala iwiri ndipo pamiyalayo palembedwa Malamulo Khumi.

      MUTU 13

      ‘Malamulo a Yehova Ndi Angwiro’

      1, 2. N’chifukwa chiyani anthu ambiri salemekeza malamulo, nanga n’chiyani chingatithandize kuti tizikonda malamulo a Mulungu?

      M’MAYIKO ambiri anthu sakulemekezanso malamulo. N’chifukwa chiyani zili choncho? Nthawi zambiri malamulowo amakhala ovuta kuwamvetsa. Komanso nthawi zina olamulira amachita zinthu mokondera. Anthu akapita kukhoti ndi mlandu, pamatenga nthawi yaitali kuti mlandu wawo uweruzidwe komanso amawononga ndalama zambiri.

      2 Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi mawu awa amene analembedwa zaka pafupifupi 2,700 zapitazo, akuti: “Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!” (Salimo 119:97) N’chifukwa chiyani wolemba masalimoyu ankakonda malamulo kwambiri chonchi? Chifukwa malamulowo anali ochokera kwa Yehova Mulungu osati opangidwa ndi maboma am’dzikoli. Mukamapitiriza kuphunzira malamulo a Yehova, nanunso mudzayamba kuwakonda kwambiri ngati mmene anachitira wamasalimoyu. Kuphunziraku kudzakuthandizani kuti mumvetse mmene Yehova, yemwe ndi Woweruza komanso Wopereka Malamulo Wamkulu, amaganizira.

      Wopereka Malamulo Wamkulu

      3, 4. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi Wopereka Malamulo?

      3 Baibulo limatiuza kuti: “Wopereka Malamulo komanso Woweruza alipo mmodzi yekha.” (Yakobo 4:12) Yehova ndi amene ali woyenera kukhazikitsa malamulo oti zinthu zonse zomwe analenga zizitsatira. Iye anapereka “malamulo amene zinthu zakuthambo zimatsatira.” (Yobu 38:33) Angelo oyera mamiliyoni ambirimbiri nawonso amatsatira malamulo a Mulungu, ndipo amamutumikira mwadongosolo komanso anawapatsa maudindo osiyanasiyana.​—Salimo 104:4; Aheberi 1:7, 14.

      4 Yehova anaperekanso malamulo kwa anthu. Munthu aliyense ali ndi chikumbumtima, chomwe chimasonyeza mmene Yehova amaonera chilungamo. Chikumbumtimachi chili ngati malamulo amene ali mumtima mwathu omwe amatithandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera. (Aroma 2:14) Makolo athu oyambirira anali ndi chikumbumtima changwiro, choncho sankafunika malamulo ambirimbiri. (Genesis 2:15-17) Koma anthu omwe si angwiro amafunika malamulo ambiri kuti aziwathandiza kuchita zofuna za Mulungu. Makolo akale monga Nowa, Abulahamu ndi Yakobo ankalandira malamulo kuchokera kwa Yehova ndipo ankauza anthu a m’banja lawo malamulowo. (Genesis 6:22; 9:3-6; 18:19; 26:4, 5) Koma Yehova anakhala Wopereka Malamulo m’njira ina yatsopano pamene anapereka Chilamulo kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose. Chilamulo chomwe anaperekachi chimatithandiza kudziwa mmene iye amaonera chilungamo.

      Zimene Zinali M’Chilamulo cha Mose

      5. Kodi Chilamulo cha Mose chinali ndi malamulo ambiri komanso ovuta kumvetsa? N’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?

      5 Anthu ambiri amaganiza kuti m’Chilamulo cha Mose munali malamulo ambiri komanso ovuta kuwamvetsa. Komatu maganizo amenewa si oona. M’Chilamulo munali malamulo oposa 600. Angaoneke ngati ambiri, koma taganizirani izi: Pofika kumapeto kwa zaka za m’ma 1900, malamulo a dziko la United States analembedwa m’mabuku ambiri moti kuphatikiza onse, masamba ake ankaposa 150,000. Pa zaka ziwiri zilizonse amawonjezera malamulo ena pafupifupi 600. Choncho Chilamulo cha Mose chinali ndi malamulo ochepa kwambiri tikayerekezera ndi malamulo a anthu. Komatu Chilamulo cha Mulungu chinkauza Aisiraeli zochita pa nkhani zina zimene malamulo a anthu masiku ano sakhudzako n’komwe. Tiyeni tione zitsanzo zina.

      6, 7. (a) Kodi n’chiyani chimasiyanitsa Chilamulo cha Mose ndi malamulo a anthu, nanga lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti? (b) Kodi Aisiraeli ankasonyeza bwanji kuti akulemekeza ulamuliro wa Yehova?

      6 Chilamulo chinkauza Aisiraeli kuti azimvera Yehova monga wolamulira. Zimenezi zimachititsa Chilamulo cha Mose kukhala chosiyana kwambiri ndi malamulo alionse amene anthu anapangako. Lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulochi linali lakuti: “Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi. Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse.” Kodi anthu a Mulungu akanasonyeza bwanji kuti amamukonda? Ankafunika kumamutumikira, kapena kuti kumumvera monga wolamulira wawo.​—Deuteronomo 6:4, 5; 11:13.

      7 Munthu aliyense wa ku Isiraeli ankasonyeza kuti amavomereza ulamuliro wa Yehova pogonjera anthu amene anali ndi udindo. Makolo, akalonga, oweruza, ansembe ndipo kenako mfumu, onsewa ankaimira ulamuliro wa Mulungu. Yehova ankaona kuti ngati munthu sakumvera anthu audindowa ndiye kuti sakumvera iyeyo. Komanso anthu audindo akamagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika ankakwiyitsa Yehova. (Ekisodo 20:12; 22:28; Deuteronomo 1:16, 17; 17:8-20; 19:16, 17) Choncho olamulira ndiponso olamulidwa ankafunika kulemekeza ulamuliro wa Mulungu.

      8. Kodi Chilamulo chinkathandiza bwanji Aisiraeli kuti azikhala oyera?

      8 Chilamulo chinkathandiza Aisiraeli kuti azikhala oyera. Mawu a Chiheberi omwe nthawi zambiri amawamasulira kuti “woyera” ndiponso “kuyera” amapezeka maulendo oposa 280 m’Chilamulo cha Mose. Chilamulo chinkathandiza anthu a Mulungu kusiyanitsa pakati pa chinthu choyera ndi chodetsedwa ndipo chinatchula zinthu pafupifupi 70 zimene mwamwambo zikanachititsa kuti Aisiraeli akhale odetsedwa. Malamulo amenewa anali okhudza ukhondo, zakudya komanso njira yoyenera yotayira zinthu zosafunika. Malamulowa ankathandiza kwambiri Aisiraeli kuti akhale ndi moyo wathanzi.a Koma panali chifukwa china chachikulu chomwe Yehova anawapatsira malamulowa. Iye ankafuna kuti anthuwa akhalebe naye pa ubwenzi popewa makhalidwe oipa amene anthu a mitundu ina ankachita. Taonani chitsanzo ichi.

      9, 10. Kodi malamulo a m’pangano la Chilamulo ankanena zotani pa nkhani yokhudza kugonana ndi kubereka ana, nanga ankathandiza bwanji Aisiraeli?

      9 Malamulo a m’pangano la Chilamulo ankanena kuti kugonana, ngakhale kwa anthu okwatirana, ndiponso kubereka mwana kunkachititsa anthuwo kukhala odetsedwa kwa kanthawi. (Levitiko 12:2-4; 15:16-18) Malamulowa sankasonyeza kuti kugonana kwa anthu okwatirana ndiponso kubereka ana si mphatso zoyera zochokera kwa Mulungu. (Genesis 1:28; 2:18-25) M’malomwake, Yehova anapereka malamulo amenewa kuti anthu ake akhale oyera n’kumapewa kulambira kwabodza. Anthu amitundu ina omwe ankakhala pafupi ndi Aisiraeli ankasakaniza kulambira ndi miyambo yokhudza kugonana komanso kubereka. Mwachitsanzo, Akanani ankakhala ndi mahule aamuna ndiponso aakazi ngati mbali ya chipembedzo chawo. Zimenezi zinachititsa kuti akhale ndi makhalidwe oipa kwambiri omwenso anafalikira. Mosiyana ndi zimenezi, Chilamulo chinachititsa kuti kulambira Yehova kusamakhudzane m’pang’ono pomwe ndi nkhani za kugonana.b Koma Chilamulo chinkathandizanso Aisiraeli m’njira zina.

      10 Malamulowo ankawaphunzitsa mfundo ya choonadi yofunika kwambiri.c Kodi anthu amapatsirana bwanji uchimo womwe tinatengera kwa Adamu, kuchoka ku m’badwo wina kupita m’badwo wina? Amachita zimenezi kudzera mu kugonana ndi kubereka ana. (Aroma 5:12) Choncho Chilamulo cha Mulungu chinkakumbutsa anthu ake kuti anali ochimwa. Ndipotu tonsefe timabadwa ochimwa. (Salimo 51:5) Timafunika kukhululukidwa machimo komanso kuwomboledwa kuti tiyandikire Mulungu wathu woyera.

      11, 12. (a) Kodi Chilamulo chinkalimbikitsa mfundo yofunika kwambiri iti ya chilungamo? (b) Kodi m’Chilamulo munali mfundo ziti zothandiza kuti anthu osalakwa asamapatsidwe chilango?

      11 Chilamulo chinkasonyeza kuti Yehova ndi wachilungamo. Chilamulo cha Mose chinkalimbikitsa mfundo yoti milandu iziweruzidwa mwachilungamo. Choncho m’Chilamulochi munali lamulo lakuti: “Moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.” (Deuteronomo 19:21) Ngati munthu waphwanya malamulo, chilango chake chinkayenera kukhala chofanana ndi mlandu umene wapalamulawo. Mbali imeneyi ya chilungamo cha Mulungu inkakhudza mfundo zonse za m’Chilamulocho ndipo monga mmene tionere m’Mutu 14, mpaka pano mbaliyi imatithandiza kwambiri kuti timvetse zokhudza nsembe ya dipo ya Khristu Yesu.​—1 Timoteyo 2:5, 6.

      12 M’Chilamulo munalinso mfundo zothandiza kuti anthu osalakwa asamapatsidwe chilango. Mwachitsanzo, pankafunika mboni zosachepera ziwiri kuti munthu amene amusumira mlandu apatsidwe chilango. Mboni yabodza inkapatsidwa chilango chokhwima. (Deuteronomo 19:15, 18, 19) Katangale ndi ziphuphu zinali zosaloleka ngakhale pang’ono. (Ekisodo 23:8; Deuteronomo 27:25) Ngakhalenso pochita zamalonda, anthu a Mulungu ankafunika kutsatira mfundo za Yehova zokhudza chilungamo. (Levitiko 19:35, 36; Deuteronomo 23:19, 20) Kunena zoona, Chilamulo chinali chabwino komanso chothandiza kwambiri kwa Aisiraeli.

      Malamulo Othandiza Kuweruza Mwachifundo Komanso Mwachilungamo

      13, 14. Kodi Chilamulo chinkathandiza bwanji kuti wakuba ndi oberedwa azichitiridwa zinthu mwachilungamo?

      13 Kodi Chilamulo cha Mose chinali ndi malamulo okhwima omwe ankachititsa anthu kuti asamasonyeze chifundo? Ayi. Mfumu Davide anauziridwa kulemba kuti: “Chilamulo cha Yehova ndi changwiro.” (Salimo 19:7) Iye ankadziwa bwino kuti Chilamulo chinkalimbikitsa anthu kukhala achifundo komanso achilungamo. N’chifukwa chiyani tikutero?

      14 Malamulo a m’mayiko ena masiku ano amakomera kwambiri anthu olakwa kusiyana ndi amene alakwiridwa. Mwachitsanzo, akuba angakhale kundende kwa nthawi ndithu. Anthu amene anaberedwawo angakhale kuti sanabwezeredwe katundu wawo, komabe amayenera kupereka ndalama zamsonkho zimene boma limagwiritsa ntchito kupeza malo okhala komanso chakudya cha akubawo. Ku Isiraeli kunalibe ndende ngati mmene zilili masiku ano. Ndiponso akamapereka chilango sankafunika kupitirira malire. (Deuteronomo 25:1-3) Mbava inkafunika kubweza kwa mwiniwake katundu amene inaba. Ndiponso mbavayo inkapereka katundu wina kuwonjezera pa zimene inabazo. Kodi ankakhala wochuluka bwanji? Zinkangotengera mlandu wake. Zikuoneka kuti oweruza ankaganizira mfundo zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, ankaganizira ngati wolakwayo walapa. N’chifukwa chake zinthu zimene mbava inkafunika kubweza mogwirizana ndi lemba la Levitiko 6:1-7 n’zochepa kwambiri kusiyana ndi zimene zinatchulidwa pa Ekisodo 22:7.

      15. Kodi m’Chilamulo munali malamulo ati omwe ankathandiza kuti munthu wopha mnzake mwangozi achitiridwe chifundo komanso chilungamo?

      15 Chilamulo chinkasonyeza kuti si machimo onse amene amachitidwa mwadala ndipo umenewu ndi umboni wakuti Yehova ndi wachifundo. Mwachitsanzo, munthu akapha mnzake mwangozi n’kuthawira ku umodzi wa mizinda yothawirako imene inali ku Isiraeli, sankafunika kupatsidwa chilango cha moyo kulipira moyo. Oweruza oyenerera akaweruza nkhani yake, iye ankakhalabe mumzindawo mpaka mkulu wa ansembe atamwalira. Zikatero ankatha kukakhala kulikonse kumene akufuna. Apatu chifundo cha Mulungu chinkamuthandiza kwambiri. Koma lamuloli linkasonyezanso kuti moyo wa munthu ndi wamtengo wapatali.​—Numeri 15:30, 31; 35:12-25.

      16. Kodi Chilamulo chinkateteza bwanji ufulu wa anthu?

      16 Chilamulo chinkateteza ufulu wa munthu. Taonani mmene chinkatetezera anthu amene anali ndi ngongole. Chilamulo chinkaletsa wokongoza kulowa m’nyumba ya wangongole n’kukatenga katundu monga chikole. M’malomwake, wokongozayo ankafunika kuima panja n’kuyembekezera wokongolayo kuti abweretsa chikolecho. Choncho munthu sankakhala ndi ufulu wolowa m’nyumba mwa mnzake n’kukasokoneza. Ngati wokongoza watenga chovala chakunja cha wangongole ngati chikole, ankafunika kubweza chovalacho dzuwa likamalowa chifukwa mwiniwakeyo ankachifuna kuti afunde usiku.​—Deuteronomo 24:10-14.

      17, 18. Pa nkhani zokhudza nkhondo, kodi Aisiraeli ankasiyana bwanji ndi anthu amitundu ina, nanga n’chifukwa chiyani?

      17 M’Chilamulo munalinso malamulo okhudza nkhondo. Anthu a Mulungu sankafunika kumenya nkhondo pofuna kungopeza mphamvu zolamulira kapena kugonjetsa ena, koma ankamenya “Nkhondo za Yehova.” (Numeri 21:14) Nthawi zambiri, Aisiraeli ankapatsa kaye mwayi anthuwo kuti angovomereza kugonja. Anthuwo akakana zimenezi m’pamene Aisiraeli ankamanga msasa kuzungulira mzinda wa anthuwo, koma mogwirizana ndi malamulo a Mulungu. Komanso mosiyana ndi zimene asilikali ambiri amachita, Aisiraeli sankaloledwa kuti azigwiririra akazi kapena kupha anthu mwachisawawa. Ankafunikanso kumasamala zachilengedwe moti sankayenera kugwetsa mitengo ya zipatso ya adani awo.d Asilikali amitundu ina sankaletsedwa kuchita zinthu ngati zimenezi.​—Deuteronomo 20:10-15, 19, 20; 21:10-13.

      18 Kodi mumakhumudwa mukamva kuti m’mayiko ena ana aang’ono amawaphunzitsa usilikali? Ku Isiraeli, munthu wosakwanitsa zaka 20 sankaloledwa kukhala msilikali. (Numeri 1:2, 3) Komanso ngati munthu akuchita mantha kwambiri, sankafunika kupita kunkhondo ngakhale kuti ali ndi zaka zoposa 20. Mwamuna yemwe wangokwatira kumene ankatha chaka asanapite kunkhondo kuti aone mwana wake woyamba akubadwa, asanayambe ntchito yoika moyo pachisweyi. Chilamulo chinafotokoza kuti zimenezi zinkachititsa kuti mwamuna wachinyamatayo “asangalatse mkazi wake.”​—Deuteronomo 20:5, 6, 8; 24:5.

      19. Kodi Chilamulo chinkateteza bwanji akazi, ana, mabanja, akazi amasiye komanso ana amasiye?

      19 Chilamulo chinkatetezanso akazi, ana ndi mabanja ndipo Aisiraeli ankafunika kuonetsetsa kuti anthuwa ali ndi zofunikira. Chinkalamula makolo kuti nthawi zonse azisamalira ana awo ndiponso kuwaphunzitsa zokhudza Yehova. (Deuteronomo 6:6, 7) Chinkaletsa kugonana ndi wachibale aliyense ndipo wochita zimenezi ankayenera kuphedwa. (Levitiko, chaputala 18) Chinkaletsanso kuchita chigololo, chomwe nthawi zambiri chimawononga mabanja komanso kubweretsa mavuto ambiri. M’Chilamulo munalinso malamulo othandiza kuti akazi amasiye ndi ana amasiye azipeza zofunikira, ndipo chinkaletsa mwamphamvu kuwachitira nkhanza.​—Ekisodo 20:14; 22:22-24.

      20, 21. (a) N’chifukwa chiyani Chilamulo cha Mose chinkalola Aisiraeli kukwatira mitala? (b) N’chifukwa chiyani pa nthawi ina Yehova ankalola kuti anthu azithetsa banja?

      20 Komabe ena angadabwe kuti, ‘N’chifukwa chiyani Chilamulo chinkaloleza mitala?’ (Deuteronomo 21:15-17) Tingamvetse zimenezi ngati titakumbukira mfundo yoti chikhalidwe cha Aisiraeli komanso zimene ankachita ndi zosiyana kwambiri ndi ife masiku ano. (Miyambo 18:13) Pamene Yehova analenga Adamu ndi Hava, anasonyeza momveka bwino kuti mwamuna ayenera kukhala ndi mkazi mmodzi ndipo awiriwo ayenera kukhala limodzi mpaka kalekale. (Genesis 2:18, 20-24) Koma pa nthawi imene Yehova ankapereka Chilamulo kwa Aisiraeli, zinthu ngati mitala zinali zitakhazikika kwa zaka zambiri. Yehova anadziwa kuti nthawi zambiri anthu ake omwe anali “okanika” azidzalephera kumvera ngakhale malamulo ofunika kwambiri, ngati oletsa kulambira mafano. (Ekisodo 32:9) Choncho anaona kuti imeneyi sinali nthawi yabwino yoti akonze zinthu zolakwika pa nkhani ya banja. Musaiwale kuti Yehova si amene anayambitsa mitala. Koma anapereka malamulo omwe ankateteza akazi kuti asamachitiridwe nkhanza m’mabanja amitala.

      21 Mofanana ndi zimenezi, Chilamulo cha Mose chinkalola mwamuna kuthetsa banja lake pa zifukwa zina zikuluzikulu. (Deuteronomo 24:1-4) Yesu anati Mulungu analola Ayuda kumachita zimenezi ‘chifukwa cha kuuma mtima kwawo.’ Komabe analola zimenezo kwa nthawi yochepa yokha. Patapita nthawi, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azitsatira zimene Yehova anakonza poyamba zokhudza banja.​—Mateyu 19:8.

      Chilamulo Chinkaphunzitsa Aisiraeli Kuti Azisonyeza Chikondi

      22. Kodi Chilamulo cha Mose chinkaphunzitsa Aisiraeli kuti azisonyeza chikondi m’njira ziti ndiponso kwa ndani?

      22 Masiku ano palibe dziko limene lingapange malamulo othandiza nzika zake kuti zizikondana. Chilamulo cha Mose chinkaphunzitsa anthu kuti azikondana. Moti m’buku la Deuteronomo lokha, mawu amene amanena za “chikondi” amapezeka maulendo oposa 20. Lamulo lachiwiri pa malamulo akuluakulu m’Chilamulo linali lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Levitiko 19:18; Mateyu 22:37-40) Anthu a Mulungu ankafunika kusonyeza chikondi choterechi kwa Aisiraeli anzawo komanso alendo amene ankakhala nawo, pokumbukira kuti nawonso pa nthawi ina anali alendo m’dziko lina. Ankafunika kumakonda anthu osauka ndiponso ovutika powathandiza kupeza zofunika komanso osamawachitira nkhanza. Anauzidwanso kuti azikomera mtima ndiponso kuganizira nyama zimene ankazigwiritsa ntchito.​—Ekisodo 23:6; Levitiko 19:14, 33, 34; Deuteronomo 22:4, 10; 24:17, 18.

      23. Kodi amene analemba Salimo 119 ananena kuti chiyani, nanga ifeyo tingatsimikize mtima kuchita chiyani?

      23 Palibenso mtundu wina wa anthu umene unakhalapo ndi malamulo oterewa. M’pake kuti wolemba masalimo wina anati: “Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!” Komatu sikuti ankangoona kuti amakonda malamulo a Mulungu. Chifukwa chokonda malamulowo, ankayesetsa kuwatsatira. Iye ananenanso kuti: “Ndimaganizira mozama chilamulocho tsiku lonse.” (Salimo 119:11, 97) Nthawi zonse wolemba masalimoyu ankaphunzira malamulo a Yehova. N’zosachita kufunsa kuti akamachita zimenezi ankawakondanso kwambiri. Zimenezi zinkachititsanso kuti azikonda kwambiri Yehova, yemwe anapereka malamulowo. Inunso mukamapitiriza kuphunzira malamulo a Mulungu, Yehova yemwe ndi wachilungamo komanso Wopereka Malamulo Wamkulu, adzakhala mnzanu wapamtima.

      a Mwachitsanzo, panali malamulo akuti munthu akamaliza kuchita chimbudzi azikwirira zonyansazo, wodwala azimuika kwayekha ndiponso aliyense wogwira mtembo azisamba. Pa nthawiyo mitundu ina sinkadziwa malamulo amenewa ndipo panapita zaka zambiri kuti iwadziwe.​—Levitiko 13:4-8; Numeri 19:11-13, 17-19; Deuteronomo 23:13, 14.

      b Mu akachisi a Akanani munkakhala zipinda zapadera zoti azichitiramo zachiwerewere koma Chilamulo cha Mose chinkanena kuti anthu odetsedwa asamalowe n’komwe m’kachisi. Choncho popeza kugonana kunkachititsa munthu kukhala wodetsedwa kwa kanthawi, palibe amene mwalamulo akanachititsa kuti kugonana kukhale mbali ya kulambira panyumba ya Yehova.

      c Cholinga chachikulu cha Chilamulo chinali kuphunzitsa. Ndipotu buku lina limanena kuti mawu a Chiheberi akuti toh·rahʹ omwe anawamasulira kuti “Chilamulo,” amatanthauza “malangizo.”​—Encyclopaedia Judaica

      d M’Chilamulo munali funso lakuti: “Kodi mtengo wam’munda ndi munthu kuti muwuukire?” (Deuteronomo 20:19) Katswiri wina wamaphunziro wa Chiyuda wa m’nthawi ya atumwi dzina lake Philo, anatchula lamulo limeneli ndipo anafotokoza kuti Mulungu amaona kuti “si chilungamo kuti munthu amene wakwiyira anthu athetsere mkwiyo wakewo pa zinthu zosalakwa.”

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Levitiko 19:9, 10; Deuteronomo 24:19 Kodi mukumva bwanji mukaganizira za Mulungu amene amapanga malamulo oterewa?

      • Salimo 19:7-14 Kodi Davide ankamva bwanji akaganizira za ‘malamulo a Yehova,’ nanga ifeyo tiyenera kumawaona bwanji?

      • Mika 6:6-8 Kodi mavesi amenewa akutithandiza bwanji kuona kuti malamulo a Yehova si olemetsa?

      • Mateyu 23:23-39 Kodi Afarisi anasonyeza bwanji kuti sankamvetsa mfundo yaikulu ya Chilamulo, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti zimenezi ndi chitsanzo chotichenjeza?

  • Yehova Anapereka “Dipo Kuti Awombole Anthu Ambiri”
    Yandikirani Yehova
    • Yesu waima kutsogolo kwa sikelo.

      MUTU 14

      Yehova Anapereka “Dipo Kuti Awombole Anthu Ambiri”

      1, 2. Kodi Baibulo limafotokoza kuti anthu akukumana ndi mavuto ati, nanga njira yokhayo yothetsera mavutowa ndi iti?

      “CHILENGEDWE chonse chikubuula pamodzi komanso kumva kuwawa pamodzi.” (Aroma 8:22) Ndi mawu amenewa, mtumwi Paulo anafotokoza mavuto amene anthufe tikukumana nawo. Anthufe timangoona kuti palibe njira iliyonse yothetsera kuvutika, uchimo ndi imfa. Koma mosiyana ndi anthu, palibe zinthu zimene Yehova angalephere kuchita. (Numeri 23:19) Iye ndi Mulungu wachilungamo ndipo anakonza njira yodzathetsera mavuto athu. Njirayi imatchedwa kuti dipo.

      2 Dipo ndi mphatso yoposa zonse imene Yehova anapatsa anthu. Limachititsa kuti tipulumutsidwe ku uchimo ndi imfa. (Aefeso 1:7) Chifukwa cha dipoli, tili ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha, kaya kumwamba kapena m’Paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43; Yohane 3:16; 1 Petulo 1:4) Koma kodi dipo n’chiyani? Nanga limatiphunzitsa chiyani zokhudza chilungamo chapadera cha Yehova?

      N’chifukwa Chiyani Panafunika Dipo?

      3. (a) N’chifukwa chiyani panafunika dipo? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu sanangosintha chilango cha imfa chomwe ana a Adamu ankayenera kulandira?

      3 Panafunika kuperekedwa dipo chifukwa cha tchimo la Adamu. Chifukwa choti sanamvere Mulungu, Adamu anachititsa kuti ana ake azidwala, azikhala ndi chisoni, azimva kupweteka ndiponso azimwalira. (Genesis 2:17; Aroma 8:20) Sizikanatheka kuti Mulungu angowamvera chisoni n’kusintha chilango cha imfa chomwe ankayenera kulandira. Ngati akanachita zimenezi, akanakhala kuti sakutsatira lamulo lake lakuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Ndiponso ngati Yehova akanathetsa mfundo zake za chilungamo, m’chilengedwe chonse mukanakhala chipwirikiti chokhachokha komanso kusamvera malamulo.

      4, 5. (a) Kodi Satana ananena mabodza ati okhudza Mulungu, nanga n’chifukwa chiyani Yehova anaona kuti n’zofunika kuti ayankhe mabodzawa? (b) Kodi Satana ananena zotani zokhudza atumiki okhulupirika a Yehova?

      4 Monga tinaonera m’Mutu 12, zimene Satana, Adamu ndi Hava anachita poukira ulamuliro wa Mulungu, zinayambitsa nkhani zofunika kwambiri. Satana anadetsa dzina la Mulungu lomwe ndi loyera. Iye ananena kuti Yehova ndi wabodza, ndi wolamulira wopondereza komanso sapereka ufulu kwa amene amawalamulira. (Genesis 3:1-5) Zimene Satana anachitazi zinaoneka ngati walepheretsa cholinga cha Mulungu chodzaza dziko lapansi ndi anthu olungama. Choncho anachititsa kuti Mulungu aoneke ngati wolephera. (Genesis 1:28; Yesaya 55:10, 11) Yehova akanapanda kuchitapo kanthu, anthu ndi angelo ambiri akanayamba kukayikira ngati iye amalamuliradi bwino.

      5 Satana ananamiziranso atumiki okhulupirika a Yehova kuti amatumikira Yehovayo chifukwa chofuna kupezapo kenakake ndipo ngati atakumana ndi mavuto aakulu sangakhalebe okhulupirika. (Yobu 1:9-11) Nkhani zimenezi zinali zofunika kwambiri kuposa kupulumutsa anthu ku mavuto awo. Choncho Yehova anaona kuti ankafunika kupeza njira yoyankhira zimene Satana ananena. Koma kodi Mulungu akanathetsa bwanji nkhani zimenezi n’kupulumutsanso anthu?

      Dipo Ndi Malipiro Ofanana Ndi Zimene Zinatayika

      6. Tchulani mawu ena omwe anagwiritsidwa ntchito m’Baibulo pofotokoza njira ya Mulungu yopulumutsira anthu.

      6 Yehova anasankha kuthetsa nkhanizi m’njira yachilungamo komanso yosonyeza chifundo kwambiri yomwe palibe munthu aliyense amene akanaiganizira. Njirayi inali yosavuta koma inasonyeza kuti iye ndi wanzeru kwambiri. Njirayi imatchulidwa ndi mawu osiyanasiyana monga kugula, kugwirizanitsanso, kuwombola ndiponso kuphimba machimo. (Salimo 49:8; Danieli 9:24; Agalatiya 3:13; Akolose 1:20; Aheberi 2:17) Koma mwina mawu abwino kwambiri ndi amene Yesu mwiniwakeyo anagwiritsa ntchito. Iye anati: “Mwana wa munthu . . . sanabwere kudzatumikiridwa koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo [m’Chigiriki, lyʹtron] kuti awombole anthu ambiri.”​—Mateyu 20:28.

      7, 8. (a) Kodi m’Baibulo mawu akuti “dipo” amatanthauza chiyani? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti mawu akuti “dipo” amanena za chinthu chofanana ndendende ndi chinthu china?

      7 Kodi dipo n’chiyani? Mawu a Chigiriki amene anawagwiritsa ntchito palembali akuchokera ku mawu otanthauza “kumasula.” Mawuwa ankawagwiritsa ntchito ponena za ndalama zomwe ankapereka kuti amasule akaidi ogwidwa pankhondo. Choncho tingati dipo ndi ndalama kapena chinthu chimene munthu amapereka powombola zinazake. M’Malemba a Chiheberi, mawu amene anawamasulira kuti “dipo” (koʹpher) amachokera ku mawu otanthauza “kuphimba.” Mwachitsanzo, Mulungu anauza Nowa kuti ‘amate’ (Chiheberi, ‘aphimbe’) chingalawa ndi phula. (Genesis 6:14) Zimenezi zikutithandiza kumvetsa mfundo yakuti kupereka dipo kumatanthauzanso kuphimba machimo.

      8 N’zochititsanso chidwi kuti buku lina linanena kuti mawuwa (koʹpher) “nthawi zonse amanena za kufanana ndendende.” (Theological Dictionary of the New Testament) Choncho kuti apereke dipo, kapena kuti kuphimba machimo, panafunika kupereka mtengo wofanana ndendende ndi zimene zinawonongeka chifukwa cha uchimo. N’chifukwa chake Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli chinkanena kuti: “Pazikhala moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.”​—Deuteronomo 19:21.

      9. N’chifukwa chiyani anthu okhulupirika ankapereka nsembe za nyama, nanga Yehova ankaziona bwanji nsembezo?

      9 Kungoyambira pa Abele, anthu okhulupirika ankapereka nsembe za nyama kwa Mulungu. Pochita zimenezi ankasonyeza kuti ankazindikira kuti anali ochimwa ndipo ankafunika kuwomboledwa. Anasonyezanso kuti ankakhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti adzawombola anthu pogwiritsa ntchito “mbadwa” yake. (Genesis 3:15; 4:1-4; Levitiko 17:11; Aheberi 11:4) Yehova ankasangalala ndi nsembezo ndipo ankaona kuti anthuwa anali atumiki ake okhulupirika. Komabe, nsembe za nyama zinali chizindikiro chabe. Nyama sizikanaphimbiratu machimo a anthu, chifukwa anthu ndi amtengo wapatali kuposa nyama. (Salimo 8:4-8) N’chifukwa chake Baibulo limati: “N’zosatheka kuti magazi a ng’ombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.” (Aheberi 10:1-4) Nsembe zimenezi zinkangoimira nsembe yeniyeni ya dipo imene inadzaperekedwa.

      ‘Dipo Lokwanira Ndendende’

      10. (a) Kodi wopereka dipo ankafunika kukhala wofanana ndi ndani, nanga n’chifukwa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani pankangofunika munthu mmodzi yekha woti apereke nsembe?

      10 Mtumwi Paulo ananena kuti: “Anthu onse amafa chifukwa cha Adamu.” (1 Akorinto 15:22) Choncho pankafunika munthu wangwiro ngati mmene Adamu analili kuti apereke moyo wake dipo. (Aroma 5:14) Palibe cholengedwa chilichonse chimene chikanaperekedwa n’kukwaniritsa mfundo za chilungamo pa nkhaniyi. Ndi munthu wangwiro yekha, yemwe si woyenera kufa chifukwa cha tchimo la Adamu, amene akanapereka “dipo la anthu onse lokwanira ndendende.” (1 Timoteyo 2:6) Sikuti pankafunika kuti anthu mamiliyoni ambirimbiri aperekedwe nsembe kuti munthu aliyense yemwe ndi mbadwa ya Adamu awomboledwe. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu] ndipo uchimowo unabweretsa imfa.” (Aroma 5:12) “Popeza imfa inabwera kudzera mwa munthu mmodzi,” Mulungu anakonza zoti anthu awomboledwenso “kudzera “mwa munthu mmodzi.” (1 Akorinto 15:21) Kodi anachita bwanji zimenezi?

      “Dipo la anthu onse lokwanira ndendende”

      11. (a) Kodi wopereka dipo anali woti adzalawa bwanji imfa m’malo mwa munthu aliyense? (b) N’chifukwa chiyani dipo silingathandize Adamu ndi Hava? (Onani mawu a m’munsi.)

      11 Yehova anakonza zoti munthu wangwiro apereke nsembe moyo wake mosachita kumukakamiza. Mogwirizana ndi Aroma 6:23, “malipiro a uchimo ndi imfa.” Popereka moyo wake nsembe, wopereka dipoyo anali woti ‘adzalawa imfa m’malo mwa munthu aliyense.’ M’mawu ena tinganene kuti anapereka malipiro a uchimo wa Adamu. (Aheberi 2:9; 2 Akorinto 5:21; 1 Petulo 2:24) Zotsatira zake ndi zothandiza kwambiri kwa anthu. Dipo lidzachititsa kuti ana omvera a Adamu asadzalandire chilango cha imfa. Choncho uchimo ndi imfa sizidzakhalanso ndi mphamvu pa anthu amenewa.a​—Aroma 5:16.

      12. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kubweza ngongole imodzi kukhoza kuthandiza anthu ambiri.

      12 Tiyerekeze kuti mukukhala m’tauni inayake imene anthu ambiri amagwira ntchito pafakitale ina yaikulu. Inuyo ndi maneba anu mumalandira ndalama zambiri ndipo mumakhala moyo wabwino. Koma tsiku lina fakitaleyo ikutsekedwa chifukwa bwana anayamba zakatangale ndipo wawononga ndalama moti fakitaleyo singathenso kubweza ngongole. Mwadzidzidzi inu ndi anzanu ntchito yakutherani moti mukuvutika kupeza zinthu zofunika pa moyo. Mabanja anu ndiponso anthu amene fakitaleyo ikufunika kuwapatsa ndalama akuvutika chifukwa cha katangale wa munthu mmodzi. Koma mwamwayi munthu wina wolemera kwambiri waganiza zothandizapo. Iye akuchita zimenezi chifukwa akudziwa kuti kampaniyo imathandiza anthu ambiri. Komanso akumvera chisoni anthu ambirimbiri ogwira ntchito pakampaniyo limodzi ndi mabanja awo. Choncho waganiza zobweza ngongole ya fakitaleyo n’kuitsegulanso. Kulipira ngongoleyo kukuthandiza antchito ambirimbiri, mabanja awo ndiponso anthu amene fakitaleyo imafunika kuwapatsa ndalama. Mofanana ndi zimenezi, kulipira ngongole ya Adamu kukuthandiza anthu mamiliyoni ambiri.

      Kodi Ndi Ndani Anapereka Dipo?

      13, 14. (a) Kodi Yehova anachita chiyani kuti apereke dipo lowombola anthu? (b) Kodi dipo linaperekedwa kwa ndani, nanga zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za Yehova?

      13 Ndi Yehova yekha yemwe akanapereka “Mwanawankhosa . . . amene akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yohane 1:29) Koma sikuti Mulungu anangotumiza mngelo wina aliyense kuti adzapulumutse anthu. Iye anatumiza mngelo amene akanapereka yankho labwino kwambiri pa zabodza zomwe Satana ananena zokhudza atumiki a Yehova. Yehova anadzimana kwambiri pololera kutumiza Mwana wake wobadwa yekha, yemwe ‘ankasangalala naye kwambiri.’ (Miyambo 8:30) Mofunitsitsa, Mwana wa Mulungu “anasiya zonse zimene anali nazo” kumwamba. (Afilipi 2:7) Yehova anasamutsa modabwitsa moyo wa Mwana wake woyamba kubadwa n’kuuika m’mimba mwa namwali wa Chiyuda dzina lake Mariya. (Luka 1:27, 35) Atabadwa monga munthu, ankatchedwa Yesu. Koma mwalamulo ankatchedwa kuti Adamu wachiwiri chifukwa anali wofanana ndendende ndi Adamu. (1 Akorinto 15:45, 47) Choncho Yesu anatha kupereka nsembe kuti akhale dipo la anthu ochimwa.

      14 Kodi dipolo linkayenera kuperekedwa kwa ndani? Lemba la Salimo 49:7 limanena mosapita m’mbali kuti dipo limayenera kuperekedwa “kwa Mulungu.” Koma kodi si Mulungu yemweyo amene anakonza zoti pakhale dipo? Inde. Komabe, zimenezi sizichititsa kuti kupereka dipo kukhale kosafunika kwenikweni, ngati kuti munthu wangochotsa ndalama m’thumba ili n’kuziika m’thumba linali. Tiyenera kumvetsa kuti dipo si kungosinthanitsa zinthu chabe, koma ndi nkhani yokhudza zamalamulo. Pokonza zoti dipo liperekedwe ngakhale kuti analuzapo zinthu zambiri, Yehova anasonyeza kuti nthawi zonse amatsatira mfundo zake zokhudza chilungamo.​—Genesis 22:7, 8, 11-13; Aheberi 11:17; Yakobo 1:17.

      15. N’chifukwa chiyani kunali kofunika kuti Yesu avutike ndiponso kufa?

      15 Chakumayambiriro kwa chaka cha 33 C.E., mofunitsitsa Yesu Khristu analola kuti azunzike kwambiri n’cholinga choti dipo liperekedwe. Analolera kumangidwa pamilandu yabodza, kuweruzidwa kuti anali wolakwa ndiponso kukhomeredwa pamtengo wozunzikirapo. Koma kodi Yesu ankafunikadi kuvutika chonchi? Inde, chifukwa nkhani yokhudza kukhulupirika kwa atumiki a Mulungu inkafunika kuthetsedwa. N’zochititsa chidwi kuti Mulungu sanalole kuti Herode aphe Yesu ali wakhanda. (Mateyu 2:13-18) Koma pamene Yesu anali munthu wamkulu, anatha kupirira mayesero onse a Satana ndipo ankadziwa bwino nkhani zimene Satana anayambitsa.b Pamene ankazunzidwa mwankhanza, Yesu anakhalabe “wokhulupirika, wosalakwa, wosaipitsidwa, wosiyana ndi anthu ochimwa.” Zimenezi zinapereka umboni wosatsutsika wakuti Yehova ali ndi atumiki ake amene amakhalabe okhulupirika akamayesedwa. (Aheberi 7:26) N’chifukwa chake atatsala pang’ono kufa, Yesu ananena mawu osonyeza kuti wapambana akuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!”​—Yohane 19:30.

      Kumaliza Ntchito Yake Yowombola Anthu

      16, 17. (a) Kodi Yesu anachita chiyani pomalizitsa ntchito yake yowombola anthu? (b) N’chifukwa chiyani kunali kofunika kuti Yesu akaonekere “pamaso pa Mulungu m’malo mwa ifeyo”?

      16 Komabe Yesu ankafunika kumaliza ntchito yake yowombola anthu. Pa tsiku lachitatu kuchokera pamene anafa, Yehova anamuukitsa. (Machitidwe 3:15; 10:40) Pochita zinthu zosaiwalika zimenezi, sikuti Yehova anangopatsa mphoto Mwana wake chifukwa chomutumikira mokhulupirika, koma anamupatsanso mwayi woti amalizitse ntchito yowombola anthu monga Mkulu wa Ansembe wa Mulungu. (Aroma 1:4; 1 Akorinto 15:3-8) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Pamene Khristu anabwera monga mkulu wa ansembe, . . .  analowa m’malo oyera ndi magazi ake, osati ndi magazi a mbuzi kapena a ng’ombe zazing’ono zamphongo. Analowa kamodzi kokha m’malo oyerawo ndipo anatipulumutsa kwamuyaya. Khristu sanalowe m’malo oyera opangidwa ndi manja a anthu, amene ndi chithunzi cha malo enieniwo, koma analowa kumwamba kwenikweniko. Panopa iye ali kumwamba kuti azionekera pamaso pa Mulungu m’malo mwa ifeyo.”​—Aheberi 9:11, 12, 24.

      17 Khristu sakanatenga magazi ake enieni n’kupita nawo kumwamba. (1 Akorinto 15:50) Koma anatenga chimene magaziwo amaimira. Magaziwo amaimira ufulu wokhala ndi moyo padziko lapansi monga munthu wangwiro ndipo Yesu analolera kudzimana ufulu umenewu. Kenako anapita kwa Mulungu n’kukapereka mtengo wa moyowo ngati dipo powombola anthu ochimwa. Kodi Yehova analandira nsembeyo? Inde, ndipo umboni wa zimenezi ndi zimene zinachitika ku Yerusalemu pa Pentekosite wa mu 33 C.E. pamene ophunzira pafupifupi 120 analandira mzimu woyera. (Machitidwe 2:1-4) Ngakhale kuti zimenezi zinali zosangalatsa kwambiri, zinali chiyambi chabe cha madalitso obwera chifukwa cha dipo.

      Mmene Dipo Limathandizira Anthu

      18, 19. (a) Kodi ndi magulu awiri ati a anthu amene apindula ndi kugwirizanitsidwa kumene kumatheka chifukwa cha magazi a Khristu? (b) Kodi dipo likuthandiza bwanji a “khamu lalikulu” panopa, nanga lidzawathandiza bwanji m’tsogolo?

      18 M’kalata yomwe analembera Akhristu a ku Kolose, Paulo anafotokoza kuti Mulungu anaona kuti ndi bwino kuti kudzera mwa Khristu, agwirizanitse zinthu zina zonse ndi iyeyo pokhazikitsa mtendere. Kuti achite zimenezi, anagwiritsa ntchito magazi amene Yesu anakhetsa pamtengo wozunzikirapo. Paulo anafotokozanso kuti kugwirizanitsa kumeneku kukukhudza magulu awiri a anthu, omwe ndi “zakumwamba” ndi “zapadziko lapansi.” (Akolose 1:19, 20; Aefeso 1:10) Gulu loyamba lili ndi Akhristu okwanira 144,000 amene apatsidwa chiyembekezo choti akakhale ansembe kumwamba komanso mafumu n’kumalamulira padziko lapansi limodzi ndi Khristu Yesu. (Chivumbulutso 5:9, 10; 7:4; 14:1-3) Kudzera mwa iwowa, anthu omvera adzapindula ndi dipo kwa zaka 1,000.​—1 Akorinto 15:24-26; Chivumbulutso 20:6; 21:3, 4.

      19 Zinthu “zapadziko lapansi” ndi anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wangwiro m’Paradaiso padzikoli. Lemba la Chivumbulutso 7:9-17 limanena kuti anthuwa ndi “khamu lalikulu” lomwe lidzapulumuke “chisautso chachikulu” chimene chikubwera. Komatu dipo limawathandiza ngakhale panopa. Iwo ‘achapa kale mikanjo yawo n’kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.’ Popeza amakhulupirira dipo, anayamba kale kupeza madalitso ambiri. Mwachitsanzo, Yehova amawaona kuti ndi olungama komanso anzake. (Yakobo 2:23) Chifukwa cha nsembe ya Yesu, anthuwa amatha ‘kufika kumpando wachifumu wa Mulungu ndipo amapemphera ndi ufulu wa kulankhula.’ (Aheberi 4:14-16) Akachita tchimo, Mulungu amawakhululukira. (Aefeso 1:7) Ngakhale kuti si angwiro, amakhala ndi chikumbumtima chabwino. (Aheberi 9:9; 10:22; 1 Petulo 3:21) Choncho anthu sakuchita kufunika kudikira kuti adzagwirizanitsidwe ndi Mulungu m’tsogolo, akugwirizanitsidwa naye panopa. (2 Akorinto 5:19, 20) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, pang’ono ndi pang’ono ‘azidzamasulidwa ku ukapolo wa thupi limene limawonongeka’ ndipo kenako ‘adzakhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’​—Aroma 8:21.

      20. Kodi inuyo mumamva bwanji mukamaganizira mozama zokhudza dipo?

      20 Tikuthokoza Mulungu “kudzera mwa Yesu Khristu” potipatsa dipo. (Aroma 7:25) Timagoma tikaganizira kuti linaperekedwa m’njira yosavuta koma yosonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru kwambiri. (Aroma 11:33) Tikamaganizira mozama za dipo, zimatikhudza mtima kwambiri moti ubwenzi wathu ndi Mulungu umalimba. Mofanana ndi wolemba masalimo wina, tili ndi zifukwa zomveka zotamandira Yehova, yemwe “amakonda chilungamo ndipo amaweruza mosakondera.”​—Salimo 33:5.

      a Dipo silingathandize kuti Adamu ndi Hava amasulidwe ku uchimo. M’Chilamulo cha Mose munali mfundo iyi yokhudza wopha munthu mwadala: “Musamalandire dipo lowombolera moyo wa munthu amene wapha mnzake, chifukwa ndi woyenera kuphedwa.” (Numeri 35:31) Choncho n’zoonekeratu kuti Adamu ndi Hava ankafunika kufa chifukwa sanamvere Mulungu mwa kufuna kwawo ndipo ankadziwa zomwe ankachita. Pamenepa anataya chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha.

      b Kuti apereke moyo wake ngati dipo lofanana ndendende ndi moyo umene Adamu anataya, Yesu ankafunika kufa ali munthu wamkulu wangwiro osati mwana wangwiro. Kumbukirani kuti Adamu anachimwa mwadala ndipo ankadziwa kuopsa kwa zimene ankachitazo komanso zotsatira zake. Choncho kuti Yesu akhale “Adamu womalizira” n’kuphimba tchimolo, ankafunika kukhala munthu wamkulu woti angathe kusankha kukhala wokhulupirika kwa Yehova akudziwa zimene akuchita. (1 Akorinto 15:45, 47) N’chifukwa chake zinthu zonse zokhulupirika zimene Yesu anachita kuphatikizapo kupereka moyo wake, zinali ngati “kuchita chinthu chimodzi cholungama.”​—Aroma 5:18, 19.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Numeri 3:39-51 N’chifukwa chiyani dipo limafunika kukhala lofanana ndendende ndi zimene zikulipiridwazo?

      • Salimo 49:7, 8 N’chifukwa chiyani tiyenera kuthokoza Mulungu potipatsa dipo?

      • Yesaya 43:25 Kodi lembali likutithandiza bwanji kuona kuti kupulumutsidwa kwa anthu si chifukwa chachikulu chimene Yehova anaperekera dipo?

      • 1 Akorinto 6:20 Kodi tiyenera kumachita chiyani chifukwa choyamikira dipo?

  • Yesu ‘Akukhazikitsa Chilungamo Padziko Lapansi’
    Yandikirani Yehova
    • Yesu akugubuduza tebulo ya osintha ndalama ndipo akuwalamula kuti atuluke m’kachisi.

      MUTU 15

      Yesu ‘Akukhazikitsa Chilungamo Padziko Lapansi’

      1, 2. Kodi ndi nthawi iti pamene Yesu anakwiya, nanga n’chifukwa chiyani?

      YESU ankaoneka kuti wakwiya ndipo zinali zomveka kutero. Mwina zimenezi zingakuvuteni kumvetsa chifukwa Yesu anali munthu wofatsa kwambiri. (Mateyu 21:5) Iye sanali munthu wosachedwa kukwiya ndipo akakwiya zinkakhala kuti waona kuti sipanachitike zachilungamo.a Ndiye kodi pa nthawiyi n’chiyani chinakwiyitsa munthu wokonda mtendereyu? Panali zinthu zinazake zoipa kwambiri zimene zinkachitika.

      2 Yesu ankakonda kwambiri kachisi wa ku Yerusalemu. Padziko lonse lapansi, malo okhawa ndi amene anali opatulika omwe anaperekedwa kuti azilambirirapo Atate ake akumwamba. Ayuda ochokera m’madera akutali ankapita kumeneko kukalambira. Nawonso anthu amitundu ina oopa Mulungu ankabwera kukachisiyu ndipo ankalowa m’bwalo limene analikonza kuti anthu oterewa azilambiriramo. Koma chakumayambiriro kwa utumiki wake, Yesu anafika pakachisi n’kupeza kuti pakuchitika zinthu zoipa kwambiri. Malowa ankangokhala ngati msika osati kachisi. Panali anthu ambiri ogulitsa malonda komanso osintha ndalama. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kunali kupanda chilungamo? Chifukwa choti anthuwa ankagwiritsa ntchito kachisi wa Mulungu kuti azichita zachinyengo ngakhalenso kubera anthu. Kodi ankachita bwanji zimenezi?​—Yohane 2:14.

      3, 4. Kodi ndi zinthu zolakwika ziti zomwe zinkachitika panyumba ya Yehova, ndipo Yesu anachita chiyani kuti akonze zolakwikazo?

      3 Atsogoleri achipembedzo analamula kuti mtundu umodzi wokha wa ndalama ndi umene uzigwiritsidwa ntchito pokhoma msonkho wapakachisi. Anthu omwe abwera pakachisipo ankafunika kusinthitsa ndalama zawo kuti apeze ndalama za mtundu umenewo. Choncho osinthitsa ndalama ankaika matebulo awo m’kati mwa kachisimo, ndipo kuti munthu asinthe ndalama zake ankamulipiritsa. Anthu ankagulitsanso ziweto ndipo ankapeza phindu lalikulu. Anthu omwe ankafuna kupereka nsembe akanatha kugula nyama yoti apereke nsembeyo kwa wogulitsa wina aliyense mumzindawo. Koma akuluakulu apakachisi ankatha kukana nyama zoterozo kuti n’zosayenera. Nyama zogulidwa pakachisi pomwepo ndi zimene sankazikana. Ndiye poti anthuwo sakanachitira mwina koma kugula pakachisipo, nthawi zina amalondawo ankawadulitsira kwambiri.b Komatu kumeneku sikunali kungodulitsa malonda chabe. Kunali kuba.

      4 Yesu sakanalekerera zinthu zopanda chilungamozi. Imeneyi inali nyumba ya Bambo ake. Choncho anapanga chikwapu cha zingwe n’kutulutsa ng’ombe ndi nkhosa m’kachisimo. Kenako anapita pomwe panali osinthitsa ndalama n’kugubuduza matebulo awo. Ndalama zambirimbiri zinangoti mbwee pansi pomwe anapakonza ndi miyala ya mabo. Ndiyeno Yesu analamula mokalipa anthu amene ankagulitsa nkhundawo kuti: “Chotsani izi muno!” (Yohane 2:15, 16) Zikuoneka kuti panalibe aliyense amene anayerekeza kutsutsa munthu wolimba mtimayu.

      “Chotsani izi muno!”

      Ankachita Zinthu Ngati Atate Ake

      5-7. (a) Asanabwere padzikoli, kodi Yesu anaphunzira bwanji mmene Yehova amaonera nkhani ya chilungamo, ndipo tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chake? (b) Kodi Yesu anatani pa zinthu zopanda chilungamo zimene Satana ananena, nanga adzachita chiyani m’tsogolomu?

      5 Patapita nthawi amalondawo anabweranso. Moti patatha zaka pafupifupi zitatu, Yesu anawathamangitsanso m’kachisi ndipo pa nthawiyi ananena mawu omwenso Yehova ananena potsutsa anthu omwe anasandutsa nyumba yake kukhala “phanga la achifwamba.” (Yeremiya 7:11; Mateyu 21:13) Yesu ataona kuti anthu akuberedwa ndiponso kachisi wa Mulungu akudetsedwa, anakhumudwa ngati mmene Atate ake anachitira ndipo n’zosadabwitsa. Yesu anaphunzitsidwa ndi Atate ake akumwamba kwa zaka mamiliyoni osawerengeka. Chifukwa cha zimenezi, iye ankakonda chilungamo ngati Yehova. Yesu ndi chitsanzo chenicheni cha mawu akuti, “Make mbuu, mwana mbuu.” Choncho ngati tikufuna kudziwa bwino mmene Yehova alili wachilungamo, njira yabwino n’kuganizira chitsanzo cha Yesu Khristu.​—Yohane 14:9, 10.

      6 Mwana wobadwa yekha wa Yehovayu analipo pamene Satana mopanda chilungamo ananena kuti Yehova Mulungu ndi wabodza ndiponso salamulira mwachilungamo. Limenelitu linali bodza lalikulu kwambiri. Kenako Mwanayu anamvanso Satana akunena kuti palibe munthu angatumikire Yehova chifukwa chomukonda. Mabodza amenewa anakhumudwitsa kwambiri Mwanayu chifukwa amakonda chilungamo. Choncho ayenera kuti anasangalala kwambiri atamva kuti adzathandiza nawo m’njira yapadera posonyeza kuti Satana ndi wabodza. (2 Akorinto 1:20) Kodi akanachita bwanji zimenezi?

      7 Monga taphunzirira m’Mutu 14, Yesu Khristu anapereka yankho losatsutsika pa zimene Satana ananena zokhudza kukhulupirika kwa atumiki a Yehova. Pochita zimenezi, Yesu anachita zinthu zomwe zidzathandize aliyense kudziwa kuti ulamuliro wa Yehova ndi wolungama ndiponso kuti dzina la Yehovayo lidzayeretsedwe. Monga Mtumiki Wamkulu wa Mulungu, Yesu adzaonetsetsa kuti aliyense akuchita zimene Yehova amaona kuti n’zolungama. (Machitidwe 5:31) Zimene ankachita komanso kuphunzitsa ali padzikoli, zinkasonyezanso kuti amatsanzira Mulungu pa nkhani ya chilungamo. Ponena za iye, Yehova anati: “Ndidzaika mzimu wanga pa iye ndipo anthu a mitundu ina adzawasonyeza bwinobwino chilungamo chenicheni.” (Mateyu 12:18) Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji mawu amenewa?

      Yesu Anathandiza Anthu Kudziwa “Chilungamo Chenicheni”

      8-10. (a) Kodi malamulo amene atsogoleri achipembedzo a Chiyuda anapanga ankalimbikitsa bwanji anthu kuti azinyansidwa ndi anthu a mitundu ina ndiponso kunyoza akazi? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti malamulo amene anthu anapanga anachititsa kuti kutsatira lamulo la Yehova lokhudza Sabata kukhale kovuta?

      8 Yesu ankakonda Chilamulo cha Yehova ndipo ankachita zimene chimanena. Koma atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake ankapotoza Chilamulocho. Yesu anawauza kuti: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! . . . Mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, zomwe ndi chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.” (Mateyu 23:23) Mwadala, aphunzitsi a Chilamulo cha Mulungu amenewo sankathandiza anthu kudziwa “chilungamo chenicheni,” kapena kuti zimene Mulungu amafuna pa nkhani ya chilungamo. Kodi ankachita bwanji zimenezi? Taonani zitsanzo izi.

      9 Yehova anauza anthu ake kuti asamagwirizane ndi anthu a mitundu ina omwe ankalambira mafano. (1 Mafumu 11:1, 2) Komabe, atsogoleri ena achipembedzo ankakokomeza n’kumalimbikitsa anthu kuti azinyansidwa ndi aliyense yemwe sanali Myuda. Moti m’buku la Mishnah munali lamulo lakuti: “Osasiya ng’ombe kunyumba kwa munthu yemwe si Myuda chifukwa akhoza kugona nayo.” Maganizo amenewa anali olakwika komanso osagwirizana ndi mfundo za m’Chilamulo cha Mose. (Levitiko 19:34) Panalinso malamulo ena amene anthu anapanga omwe ankanyoza akazi. Mwachitsanzo, lamulo lina linkati mkazi aziyenda kumbuyo kwa mwamuna wake, osati pambali pake. Mwamuna ankachenjezedwa kuti asamacheze ndi mkazi pagulu, ngakhale mkazi wake. Mofanana ndi akapolo, akazi sankaloledwa kupereka umboni m’khoti. Panalinso pemphero limene amuna ankanena n’kumathokoza Mulungu chifukwa chakuti anabadwa amuna osati akazi.

      10 Atsogoleri achipembedzo anapanga malamulo ambirimbiri omwe ankachititsa kuti zikhale zovuta kumvetsa Chilamulo cha Mulungu. Mwachitsanzo, lamulo lonena za Sabata linkangoletsa kugwira ntchito tsiku la Sabata kuti anthu pa tsikulo azichita zinthu zokhudza kulambira, azilimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova ndiponso azipuma. Koma Afarisi anachititsa kuti lamuloli likhale lovuta kulitsatira. Anangodzisankhira okha tanthauzo la mawu akuti “ntchito.” Anatchula zinthu 39 kuti ngati munthu atazichita, ndiye kuti wagwira ntchito. Zina mwa zinthuzi zinali kukolola ndiponso kusaka nyama. Koma zimenezi zinangobweretsa mafunso ambirimbiri. Munthu akapha nthata pa Sabata, kodi ndiye kuti wasaka? Ngati akudutsa m’munda wa tirigu n’kupulula tirigu wokwana m’manja mwake kuti adye, kodi akukolola? Ngati wachiritsa munthu wodwala, kodi ndiye kuti wagwira ntchito? Pofuna kuyankha mafunso ngati amenewa, atsogoleri achipembedzo anapanga malamulo okhwima kwambiri komanso ovuta kuwamvetsa.

      11, 12. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankatsutsa miyambo ya Afarisi yosagwirizana ndi Malemba?

      11 Popeza zinthu zinali choncho, kodi Yesu akanathandiza bwanji anthu kudziwa chilungamo chenicheni? Zimene Yesu ankaphunzitsa komanso kuchita pa moyo wake, zinasonyeza kuti ankatsutsa molimba mtima zochita za atsogoleri achipembedzowo. Mwachitsanzo, taonani zina mwa zimene anaphunzitsa. Anatsutsa mosapita m’mbali malamulo ambirimbiri amene atsogoleri achipembedzo anapanga ndipo anati: “Mumapangitsa kuti mawu a Mulungu akhale opanda pake chifukwa cha miyambo yanu imene munaipereka kwa anthu.”​—Maliko 7:13.

      12 Molimba mtima Yesu anaphunzitsa kuti zimene Afarisi ankanena zokhudza lamulo la Sabata zinali zolakwika ndipo iwo sanamvetse cholinga cha lamuloli. Anafotokoza kuti Mesiya ndi “Mbuye wa Sabata” choncho anali ndi ufulu wochiritsa anthu pa tsikuli. (Mateyu 12:8) Pofuna kutsindika mfundoyi, iye ankachiritsa anthu pa Sabata onse akuona. (Luka 6:7-10) Zimenezi zinkasonyeza kuti adzachiritsa anthu padziko lonse mu Ulamuliro wa Zaka 1,000. Zaka 1,000 zimenezo zidzakhaladi Sabata lalikulu, pamene anthu onse okhulupirika adzapume ku mavuto amene amakumana nawo chifukwa cha uchimo ndi imfa.

      13. Kodi Yesu anapatsa otsatira ake chilamulo chiti, ndipo chimasiyana bwanji ndi Chilamulo cha Mose?

      13 Yesu anasonyezanso tanthauzo la chilungamo chenicheni pamene anapatsa otsatira ake chilamulo chatsopano chomwe ndi “chilamulo cha Khristu.” Chilamulochi chinayamba kugwira ntchito iye atamaliza utumiki wake wapadziko lapansi. (Agalatiya 6:2) Chilamulo chatsopanochi ndi chosiyana ndi Chilamulo cha Mose, chifukwa chili ndi mfundo za choonadi osati malamulo ambirimbiri olembedwa. Komabe chili ndi malamulo ena achindunji. Limodzi la malamulo amenewa Yesu analitchula kuti “lamulo latsopano.” Iye anaphunzitsa otsatira ake onse kuti azikondana ngati mmene iyeyo anawakondera. (Yohane 13:34, 35) Zoonadi, chikondi chololera kuvutikira ena chinadzakhala chizindikiro cha anthu onse amene amatsatira “chilamulo cha Khristu.”

      Chitsanzo pa Nkhani ya Chilungamo

      14, 15. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amadziwa malire a udindo wake, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi n’zolimbikitsa?

      14 Sikuti Yesu anangophunzitsa zokhudza chikondi, koma nthawi zonse ankachitanso zinthu zogwirizana ndi “chilamulo cha Khristu.” Tiyeni tione zinthu zitatu zimene Yesu anachita zomwe zinasonyeza tanthauzo la chilungamo chenicheni.

      15 Choyamba, Yesu ankasamala kwambiri kuti asachite chilichonse chosemphana ndi chilungamo. Mwina munaona kuti zinthu zambiri zopanda chilungamo zimachitika munthu akadzikuza n’kuchita zinthu zomwe si udindo wake kuzichita. Koma Yesu sankachita zimenezo. Tsiku lina munthu wina anafika kwa Yesu n’kumuuza kuti: “Mphunzitsi, mumuuze mchimwene wanga kuti andigawireko cholowa.” Kodi Yesu anayankha bwanji? Anamuuza kuti: “Munthu iwe, ndi ndani amene anandisankha kuti ndikhale woweruza wanu kapena wogawa chuma chanu?” (Luka 12:13, 14) Kodi zimenezi si zochititsa chidwi? Ngakhale kuti Yesu ndi wanzeru kwambiri, wozindikira komanso Mulungu anamupatsa udindo waukulu kuposa aliyense padzikoli, anakana kulowerera nkhaniyi chifukwa sanapatsidwe udindo wochita zimenezo. Nthawi zonse Yesu amachita zinthu mosapitirira malire ndipo ndi zimene ankachitanso kwa zaka zambirimbiri asanabwere padzikoli. (Yuda 9) Zimenezi zikusonyeza kuti amadzichepetsa n’kumadalira Yehova kuti Yehovayo anene zimene zili zoyenera.

      16, 17. (a) Pa nkhani yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, kodi Yesu anasonyeza bwanji chilungamo? (b) Kodi Yesu anasonyeza chilungamo m’njira inanso iti?

      16 Chachiwiri, Yesu anasonyeza chilungamo pa zimene ankachita pa nkhani yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Iye sankachita zinthu mokondera. M’malomwake ankayesetsa kulalikira kwa anthu onse, kaya olemera kapena osauka. Koma Afarisi ankanyoza anthu wamba powatchula kuti ʽam-ha·ʼaʹrets, kapena kuti “eni dziko.” Molimba mtima Yesu anasonyeza kuti kumeneku kunali kupanda chilungamo. Iye ankaphunzitsa anthu uthenga wabwino, kudya nawo, kuwapatsa zakudya, kuwachiritsa ndiponso kuwaukitsa. Apatu ankatsanzira Mulungu wachilungamo amene amafuna kuti “anthu osiyanasiyana” apulumuke. c​—1 Timoteyo 2:4.

      17 Chachitatu, Yesu anasonyeza chilungamo pokhala wachifundo. Ankathandiza anthu ochimwa. (Mateyu 9:11-13) Komanso ankathandiza mofunitsitsa anthu omwe analibe owateteza. Mwachitsanzo, Yesu sankagwirizana ndi zimene atsogoleri achipembedzo ankauza anthu zoti asamakhulupirire anthu onse amene sanali Ayuda. Mwachifundo anathandiza komanso kuphunzitsa ena mwa anthuwa, ngakhale kuti anatumidwa kwa Ayuda okha. Anavomera kuchiritsa modabwitsa wantchito wa mtsogoleri wa asilikali a Roma ndipo anati: “Mu Isiraeli sindinapezemo aliyense wachikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.”​—Mateyu 8:5-13.

      18, 19. (a) Kodi Yesu anasonyeza kuti ankalemekeza akazi m’njira ziti? (b) Kodi chitsanzo cha Yesu chikutithandiza bwanji kuona kugwirizana pakati pa kulimba mtima ndi kuchita chilungamo?

      18 Komanso Yesu sankagwirizana ndi maganizo omwe anali ofala pa nthawiyo onyoza akazi. M’malomwake, iye molimba mtima ankachita zoyenera pa nkhaniyi. Ayuda ankakhulupirira kuti akazi a Chisamariya ndi odetsedwa ngati mmene ankaoneranso anthu onse omwe sanali Ayuda. Koma Yesu analalikira mayi wa Chisamariya pachitsime cha ku Sukari. Ndipotu kwa nthawi yoyamba, Yesu anauza mayi ameneyu kuti ndi Mesiya wolonjezedwa. (Yohane 4:6, 25, 26) Afarisi ankanena kuti akazi sayenera kuphunzitsidwa Chilamulo cha Mulungu, koma Yesu ankagwiritsa ntchito mphamvu komanso nthawi yake yambiri kuphunzitsa akazi. (Luka 10:38-42) Pa chikhalidwe chawo, Ayuda ankakhulupirira kuti akazi sangapereke umboni wodalirika. Koma Yesu analemekeza akazi angapo powapatsa mwayi wapadera woti akhale oyamba kumuona ataukitsidwa. Moti mpaka anawauza kuti apite kukauza ophunzira ake aamuna za nkhani yofunika kwambiri imeneyi.​—Mateyu 28:1-10.

      19 Zoonadi, Yesu anathandiza anthu kudziwa zimene chilungamo chenicheni chimatanthauza. Ndipo nthawi zambiri ankaika moyo wake pangozi kuti achite zimenezi. Chitsanzo cha Yesu chikusonyeza kuti pamafunika kulimba mtima kuti munthu achite chilungamo. M’pake kuti amatchedwa “Mkango wa fuko la Yuda.” (Chivumbulutso 5:5) Kumbukirani kuti mkango ndi chizindikiro cha kulimba mtima posonyeza chilungamo. Posachedwapa Yesu achita zambiri kuposa zomwe anachita ali padziko lapansi. Iye adzaonetsetsa kuti chilichonse padzikoli chikuchitika mwachilungamo.​—Yesaya 42:4.

      Mesiya Yemwenso Ndi Mfumu ‘Akukhazikitsa Chilungamo Padziko Lapansi’

      20, 21. Masiku ano kodi Yesu, yemwe ndi Mfumu komanso Mesiya, akulimbikitsa bwanji chilungamo padziko lonse komanso mumpingo wa Chikhristu?

      20 Kungoyambira pamene anakhala Mfumu mu 1914, Yesu akulimbikitsa chilungamo padzikoli. Kodi akuchita bwanji zimenezi? Akuonetsetsa kuti ulosi wake wopezeka pa Mateyu 24:14 ukukwaniritsidwa. Otsatira ake akuphunzitsa anthu m’mayiko onse choonadi cha Ufumu wa Yehova. Mofanana ndi Yesu, iwo amalalikira mosakondera ndiponso mwachilungamo. Amayesetsa kuti munthu aliyense kaya wamng’ono kapena wamkulu, wolemera kapena wosauka komanso mwamuna kapena mkazi apeze mwayi wodziwa Yehova, Mulungu wachilungamo.

      21 Yesu akulimbikitsanso chilungamo mumpingo wa Chikhristu, womwe iye ndi Mutu wake. Mogwirizana ndi ulosi, Yesu amapereka “amuna kuti akhale mphatso.” Amuna amenewa ndi akulu a Chikhristu okhulupirika amene amatsogolera mumpingo. (Aefeso 4:8-12) Akamaweta nkhosa zamtengo wapatali za Mulungu, akulu amatsanzira Yesu Khristu pa nkhani yolimbikitsa chilungamo. Nthawi zonse amakumbukira zoti Yesu amafuna kuti nkhosa zake zizichitiridwa zinthu mwachilungamo, posatengera udindo, kutchuka ngakhalenso chuma cha munthu.

      22. Kodi Yehova amamva bwanji akaona zinthu zopanda chilungamo zomwe zafala m’dzikoli, nanga anasankha Mwana wake kuti adzachite chiyani?

      22 Posachedwapa Yesu akhazikitsa chilungamo padziko lonse m’njira yoti sinachitikepo. M’dziko lachinyengoli, zinthu zopanda chilungamo zili paliponse. Si chilungamo kuti ana amamwalira chifukwa chosowa chakudya, chonsecho mayiko amawononga ndalama zambirimbiri popanga zida zankhondo. Komanso anthu amawononga ndalama zambiri pa zinthu zongosangalatsa iwowo. Chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambirimbiri amafa chifukwa cha mavuto oti akanatha kupewedwa. Zinthu zopanda chilungamo zimenezi komanso zina zambiri zimakwiyitsa kwambiri Yehova. Choncho iye anasankha Mwana wake kuti adzamenye nkhondo yolungama kuti awononge dziko loipali komanso kuthetseratu zinthu zopanda chilungamo.​—Chivumbulutso 16:14, 16; 19:11-15.

      23. Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, kodi Khristu adzalimbikitsa bwanji chilungamo mpaka kalekale?

      23 Komabe sikuti chilungamo cha Yehova chidzachititsa kuti angowononga anthu oipa. Iye anasankhanso Mwana wake kuti alamulire monga “Kalonga Wamtendere.” Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, ulamuliro wa Yesu udzabweretsa mtendere padziko lonse, ndipo iye azidzalamulira ‘mwachilungamo.’ (Yesaya 9:6, 7) Kenako, Yesu adzagwira mosangalala ntchito yothetsa zinthu zonse zopanda chilungamo zimene zikuchititsa kuti anthu ambiri azivutika. Ndiyeno mokhulupirika komanso mpaka kalekale adzaonetsetsa kuti zinthu zonse zikuchitika mogwirizana ndi chilungamo cha Yehova. Choncho n’zofunika kwambiri kuti panopa tiziyesetsa kutsanzira Yehova pa nkhani yochita chilungamo. M’mutu wotsatira tiona kuti tingachite bwanji zimenezi.

      a Posonyeza mkwiyo chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo, Yesu ankatsanzira Yehova, amene ndi “wokonzeka kusonyeza mkwiyo wake” pa zoipa zilizonse. (Nahumu 1:2) Mwachitsanzo, Yehova atauza anthu ake osamvera kuti anasandutsa nyumba yake kukhala “phanga la achifwamba,” anati: “Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zidzatsanulidwa pamalo awa.”​—Yeremiya 7:11, 20.

      b Mogwirizana ndi zomwe buku lotchedwa Mishnah linanena, patapita zaka zingapo kunachitika chionetsero chotsutsa kudula kwa nkhunda zogulitsidwa pakachisi. Nthawi yomweyo mtengowo unatsitsidwa kwambiri. Kodi ndi ndani amene ankapindula kwambiri ndi malonda apakachisi amenewa? Akatswiri ena a mbiri yakale amati misika yapakachisi inali ya banja la Mkulu wa Ansembe Anasi, ndipo n’kumene kunkachokera chuma chochuluka cha banjali.​—Yohane 18:13.

      c Afarisi ankanena kuti anthu wamba osadziwa Chilamulo anali ‘otembereredwa.’ (Yohane 7:49) Ankati munthu sayenera kuphunzitsa anthu amenewo, kuchita nawo malonda, kudya nawo ngakhalenso kupemphera nawo. Ankanenanso kuti kulola mwana wako kuti akwatiwe ndi mwamuna woteroyo chinali chinthu choipa kuposa kumulekerera kuti agwidwe ndi nyama yakutchire. Ankakhulupiriranso kuti anthu wambawa sali m’gulu la anthu odzaukitsidwa.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Salimo 45:1-7 N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yesu, yemwe ndi Mfumu komanso Mesiya, adzalimbikitsa chilungamo chenicheni?

      • Mateyu 12:19-21 Kodi ulosi unanena kuti Mesiya azidzachita bwanji zinthu ndi anthu otsika?

      • Mateyu 18:21-35 Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti munthu wachilungamo chenicheni amakhalanso wachifundo?

      • Maliko 5:25-34 Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti Yehova akamasonyeza chilungamo amaganiziranso mmene zinthu zilili pa moyo wa munthuyo?

  • ‘Muzichita Chilungamo’ Poyenda ndi Mulungu
    Yandikirani Yehova
    • Akulu awiri apita kukaona mlongo ndi ana ake kunyumba kwawo. Akumumvetsera mwatcheru pamene akulankhula.

      MUTU 16

      ‘Muzichita Chilungamo’ Poyenda ndi Mulungu

      1-3. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kumuchitira chinachake Yehova? (b) Kodi Yehova, yemwe anatipulumutsa, amafuna kuti tizichita chiyani?

      TAYEREKEZANI kuti muli musitima yapamadzi yomwe ikumira. Pamene mukuona kuti palibenso zopulumuka, pakufika munthu kudzakupulumutsani. Ndiye kodi mungamve bwanji munthu wokupulumutsaniyo atakufikitsani kumtunda n’kukuuzani kuti: “Musadandaule mwapulumuka”? N’zosachita kufunsa kuti mungafune kumuchitira chinachake posonyeza kumuthokoza chifukwa choti wapulumutsa moyo wanu.

      2 Zimenezi zikufanana ndi zimene Yehova anatichitira. Kunena zoona, timafunika kuchita zinazake pomuthokoza. Iye anapereka dipo lomwe limathandiza kuti tipulumutsidwe ku uchimo ndi imfa. Timaona kuti ndife otetezeka podziwa kuti tikamakhulupirira nsembe yamtengo wapataliyi, machimo athu amakhululukidwa komanso tidzakhala ndi moyo wosatha. (1 Yohane 1:7; 4:9) Monga tinaonera m’Mutu 14, dipo ndi umboni wamphamvu wakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo ndiponso wachikondi. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira?

      3 Njira yabwino ndi kuganizira zimene Yehovayo amafuna kuti tichite. Kudzera mwa mneneri Mika, Yehova akutiuza kuti: “Iye anakuuza munthu iwe zimene zili zabwino. Kodi Yehova akufuna kuti uzichita chiyani? Iye akungofuna kuti uzichita chilungamo, uziona kuti kukhulupirika n’kofunika, ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (Mika 6:8) Onani kuti chimodzi mwa zinthu zimene Yehova amafuna ndi chakuti ‘tizichita chilungamo.’ Kodi tingachite bwanji zimenezi?

      Muziyesetsa “Kuchita Zimene Zilidi Zolungama”

      4. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amayembekezera kuti tizitsatira mfundo zake zolungama?

      4 Yehova ndi amene amatiuza kuti ichi n’chabwino, ichi ndi choipa ndipo amayembekezera kuti tizitsatira mfundo zake. Popeza mfundo zakezo ndi zolungama, tikamazitsatira timakhala kuti tikuchita chilungamo. Lemba la Yesaya 1:17 limati: “Phunzirani kuchita zabwino, muzichita chilungamo.” Mawu a Mulungu amatilimbikitsanso kuti: “Yesetsani kukhala olungama.” (Zefaniya 2:3) Amatiuzanso kuti: “Muvale umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Mukachita zimenezi mudzatha kuchita zimene zilidi zolungama.” (Aefeso 4:24) Munthu amene amachita zimene zilidi zolungama amapewa zachiwawa, zachiwerewere komanso zinthu zodetsa chifukwa zimenezi zimaipitsa zinthu zoyera.​—Salimo 11:5; Aefeso 5:3-5.

      5, 6. (a) N’chifukwa chiyani kutsatira mfundo za Yehova si mtolo wolemetsa kwa ife? (b) Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti kuchita chilungamo ndi ntchito yopitirira?

      5 Kodi kuchita zimene Yehova amafuna ndi chimtolo cholemetsa? Ayi. Munthu amene amakonda Yehova saona kuti zimene Yehovayo amafuna n’zovuta kuzichita. Chifukwa choti timakonda Mulungu wathu ndiponso makhalidwe ake, timafuna kuti tizichita zinthu zomusangalatsa. (1 Yohane 5:3) Kumbukirani kuti Yehova “amakonda ntchito zolungama.”’ (Salimo 11:7) Ngati tikufunadi kumatsanzira Mulungu pa nkhani yochita chilungamo, tiyenera kuphunzira kukonda zimene Mulungu amakonda n’kumadana ndi zimene iye amadana nazo.​—Salimo 97:10.

      6 Anthu omwe si angwirofe zimativuta kuchita zinthu mwachilungamo. Tiyenera kuvula umunthu wakale ndi ntchito zake zauchimo n’kuvala umunthu watsopano. Baibulo limanena kuti umunthu watsopano ‘umapangidwa’ chifukwa chodziwa Mulungu molondola. (Akolose 3:9, 10) Mawu akuti ‘umapangidwa’ akusonyeza kuti kuvala umunthu watsopano ndi ntchito yopitirira yomwe imafuna khama. Komabe ngakhale titayesetsa kwambiri kuchita zoyenera, nthawi zina timaganiza, kulankhula komanso kuchita zinthu zolakwika chifukwa choti si ife angwiro.​—Aroma 7:14-20; Yakobo 3:2.

      7. Kodi tiyenera kumaona bwanji zimene timalakwitsa pamene tikuyesetsa kuchita chilungamo?

      7 Kodi tiyenera kumaona bwanji zimene timalakwitsa pamene tikuyesetsa kuchita chilungamo? N’zoona kuti sitiyenera kuchepetsa kuopsa kochita machimo. Komabe sitiyenera kugwa ulesi n’kumaona kuti si ife oyenera kutumikira Yehova chifukwa choti timalakwitsa zinthu zina. Mulungu wathu wokoma mtima anakonza zoti anthu omwe alapa mochokera pansi pa mtima azitha kukhala nayenso pa ubwenzi. Taganizirani mawu olimbikitsa amene mtumwi Yohane ananena. Iye anati: “Ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo.” Koma kenako ananenanso kuti: “Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.” (1 Yohane 2:1) Yehova anapereka nsembe ya dipo ya Yesu kuti tizitha kumutumikira movomerezeka ngakhale kuti ndife ochimwa. Zimenezitu zikuyenera kutilimbikitsa kuti tizifunitsitsa kusangalatsa Yehova.

      Uthenga Wabwino Ndi Wogwirizana Ndi Chilungamo cha Mulungu

      8, 9. Kodi ntchito yolalikira uthenga wabwino imasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wachilungamo?

      8 Njira ina yomwe tingasonyezere kuti timachita chilungamo komanso kutsanzira Yehova pa nkhaniyi, ndi kuchita zonse zimene tingathe pa ntchito yolalikira. Kodi ntchito yolalikira uthenga wabwino imasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wachilungamo?

      9 Yehova sadzawononga dziko loipali asanachenjeze anthu. Pamene Yesu ankanena ulosi wofotokoza zimene zidzachitike munthawi ya mapeto, ananena kuti: “Choyamba uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.” (Maliko 13:10; Mateyu 24:3) Mawu akuti “choyamba,” akusonyeza kuti zinthu zina zidzachitika pambuyo poti ntchito yolalikira yagwiridwa padziko lonse. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo chisautso chachikulu chimene chidzawononge oipa n’kubweretsa dziko latsopano. (Mateyu 24:14, 21, 22) Sizidzakhala zoona kunena kuti Yehova sanachitire chilungamo anthu oipa. Pochenjeza anthuwa, iye akuwapatsa mpata wokwanira woti asinthe zochita zawo kuti asadzawonongedwe.​—Yona 3:1-10.

      10, 11. Kodi timasonyeza bwanji kuti Mulungu ndi wachilungamo tikamagwira nawo ntchito yolalikira?

      10 Tikamalalikira uthenga wabwino, kodi timasonyeza bwanji kuti Mulungu ndi wachilungamo? Choyamba, n’zoyenera kuti tizichita zonse zomwe tingathe pothandiza ena kuti adzapulumuke. Taganiziranso chitsanzo chopulumutsidwa musitima yomwe ikumira ija. Pamene mwapulumutsidwa ndipo muli m’boti, n’zosachita kufunsa kuti mungakhale ofunitsitsa kuthandiza ena omwe adakali m’madzi. Mofanana ndi zimenezi, tili ndi udindo wothandiza anthu omwe tingati ali m’madzi m’dziko loipali. N’zoona kuti ambiri safuna kumvetsera uthenga wathu. Koma popeza Yehova akulezabe mtima, tili ndi udindo wowapatsa mwayi woti “alape” n’kudzapulumuka.​—2 Petulo 3:9.

      11 Tikamalalikira uthenga wabwino kwa anthu onse amene timakumana nawo, timasonyeza chilungamo m’njira inanso yofunika kwambiri. Timasonyeza kuti tilibe tsankho. Kumbukirani kuti “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Kuti timutsanzire pa nkhani yosonyeza chilungamo, sitiyenera kuweruziratu anthu. Koma tiyenera kuuza anthu onse uthenga wabwino posatengera mtundu wawo, mmene anthu amawaonera komanso kaya ndi olemera kapena osauka. Tikamachita zimenezi, timapatsa anthu mwayi woti amve uthenga wabwino komanso kuchita zomwe akuphunzira.​—Aroma 10:11-13.

      Zimene Timachitira Ena

      12, 13. (a) N’chifukwa chiyani sitifunika kufulumira kuweruza ena? (b) Kodi malangizo a Yesu akuti “siyani kuweruza ena” ndiponso akuti “siyani kutsutsa ena” amatanthauza chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi.)

      12 Tingasonyezenso chilungamo pochitira ena zinthu mofanana ndi zimene Yehova amatichitira. N’zosavuta kuweruza ena, kumangoganizira zolakwa zawo ndiponso kukayikira zolinga zawo. Koma ndi ndani angafune kuti Yehova azingokayikira zolinga zake komanso kumangomuimba mlandu pa zimene walakwitsa? Yehova satichitira zimenezi. Wolemba masalimo wina ananena kuti: “Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndi ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?” (Salimo 130:3) Kodi sitikuyamikira kuti Mulungu wathu wolungama ndiponso wachifundo anasankha kuti asamangoganizira zolakwa zathu? (Salimo 103:8-10) Ndiye kodi tizichita bwanji zinthu ndi anthu ena?

      13 Anthu ena akalakwitsa zinazake, tingatsanzire chilungamo komanso chifundo cha Yehova posafulumira kuwaweruza makamaka pa nkhani zazing’ono komanso zomwe sizikutikhudza. Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anachenjeza kuti: “Siyani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.” (Mateyu 7:1) Mogwirizana ndi zimene Luka analemba pa nkhaniyi, Yesu anawonjezera kuti: “Siyani kutsutsa ena ndipo inunso simudzatsutsidwa.”a (Luka 6:37) Yesu anasonyeza kuti amadziwa zoti anthu omwe si angwirofe tili ndi chizolowezi choweruza ena. Aliyense wa anthu omwe ankamumvetserawo, yemwe anali ndi chizolowezi choweruza ena, ankafunika kusiya.

      Mlongo akulalikira mtsikana komanso bambo wachikulire yemwe ndi wolumala.

      Timatsanzira chilungamo cha Yehova tikamalalikira uthenga wabwino mosakondera

      14. Kodi tiyenera ‘kusiya kuweruza ena’ pa zifukwa ziti?

      14 N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kusiya kuweruza ena’? Chifukwa chimodzi n’chakuti si udindo wathu kuchita zimenezi. Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anatikumbutsa kuti: “Wopereka Malamulo komanso Woweruza alipo mmodzi yekha” amene ndi Yehova. Choncho Yakobo anafunsa mosapita m’mbali kuti: “Iwe ndiwe ndani kuti uziweruza mnzako?” (Yakobo 4:12; Aroma 14:1-4) Kuwonjezera pamenepa, n’zosavuta kuweruza mopanda chilungamo chifukwa ndife ochimwa. Makhalidwe monga tsankho, kunyada, nsanje ndiponso kudzilungamitsa angachititse kuti tiziona ena molakwika. Komanso anthufe sitidziwa zonse ndipo kuganizira mfundo imeneyi kuyenera kutithandiza kuti tisamafulumire kupezera ena zifukwa. Sitingadziwe za mumtima mwa munthu ndiponso sitingadziwe zonse zokhudza mmene zinthu zilili pa moyo wake. Tikaganizira mfundo zimenezi, ndife ndani kuti tizinena Akhristu anzathu kuti sakuchita zokwanira potumikira Mulungu kapena alibe zolinga zabwino? Ndi bwino kuti tizitsanzira Yehova n’kumaona zabwino zimene abale ndi alongo athu amachita m’malo moganizira kwambiri zimene amalakwitsa.

      15. Kodi Akhristu sayenera kulankhula komanso kuchita zinthu ziti?

      15 Nanga kodi tiyenera kuchita bwanji zinthu ndi anthu a m’banja lathu? Anthu ayenera kumakhala mwamtendere komanso motetezeka m’banja. Koma n’zomvetsa chisoni kuti masiku ano nthawi zambiri anthu amachitiridwa nkhanza ndi anthu a m’banja lawo. Si zachilendo kumva zokhudza amuna, akazi ndiponso makolo amene amalalatira komanso kuchitira nkhanza anthu a m’banja lawo. Komatu Akhristu sayenera kuchitira ena nkhanza komanso kulankhula mawu okhadzula kapena onyoza. (Aefeso 4:29, 31; 5:33; 6:4) Malangizo a Yesu akuti ‘tisiye kuweruza ena’ komanso ‘tisiye kutsutsa ena’ amagwiranso ntchito panyumba. Kumbukirani kuti tingasonyeze chilungamo pochitira ena zinthu mofanana ndi zimene Yehova amatichitira. Ndipo Mulungu wathu satichitira zinthu mouma mtima kapena mwankhanza. Koma amakonda kwambiri anthu amene amamukonda. (Yakobo 5:11) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife.

      Akulu Amagwira Ntchito Yawo “Mwachilungamo”

      16, 17. (a) Kodi Yehova amayembekezera kuti akulu azichita chiyani? (b) Kodi akulu amayenera kuchita chiyani ngati wochimwa sakusonyeza kuti walapa kuchokera pansi pa mtima, ndipo n’chifukwa chiyani?

      16 N’zoona kuti tonsefe tili ndi udindo wochita zinthu mwachilungamo. Komabe akulu mumpingo wa Chikhristu ali ndi udindo waukulu pa nkhaniyi. Taonani zimene Yesaya analosera zokhudza “akalonga,” kapena kuti akulu. Iye anati: “Taonani! Mfumu idzalamulira mwachilungamo, ndipo akalonga adzalamuliranso mwachilungamo.” (Yesaya 32:1) Zoonadi, Yehova amayembekezera kuti akulu azigwira ntchito yawo mwachilungamo. Kodi akuluwo angachite bwanji zimenezi?

      17 Amuna oyenerera amenewa amadziwa mfundo yakuti, kuti achite chilungamo cha Yehova, ayenera kuthandiza mpingo kukhala woyera. Nthawi zina akulu amafunika kuweruza nkhani zokhudza tchimo lalikulu. Poweruzapo, iwo amakumbukira kuti Yehova amafuna kuti achitire munthuyo chifundo ngati zingatheke kutero. Choncho amayesetsa kuthandiza wochimwayo kuti alape. Koma bwanji ngati munthuyo sakusonyeza kuti walapadi ngakhale kuti ayesetsa kumuthandiza? Zikatere, akulu amayenera kuchita zinthu molimba mtima ndipo amatsatira malangizo a Yehova osonyeza chilungamo chenicheni akuti: “M’chotseni munthu woipayo pakati panu.” Zimenezi zikutanthauza kumuchotsa mumpingo. (1 Akorinto 5:11-13; 2 Yohane 9-11) Akulu amamva chisoni kuti akufunika kuchita zimenezi, koma amazindikira kuti n’zofunika poteteza mpingo kuti ukhalebe woyera. Koma iwo amakhulupirirabe kuti nthawi ina wochimwayo nzeru zidzamubwerera ndipo adzabwereranso mumpingo.​—Luka 15:17, 18.

      18. Kodi akulu amakumbukira chiyani akamapereka malangizo ochokera m’Baibulo?

      18 Kuti akulu achite zinthu mwachilungamo, nthawi zina amafunika kupereka malangizo a m’Baibulo. N’zoona kuti akulu sakhalira kufufuza zimene ena akulakwitsa. Komanso samangothamangira kupereka malangizo wina akalakwitsa. Koma nthawi zina Mkhristu ‘angayambe kulowera njira yolakwika mosazindikira.’ Zikatere, akulu amakumbukira kuti munthu amene amatsanzira chilungamo cha Yehova sachita zinthu mwankhaza komanso mopanda chifundo. Choncho amayesetsa “kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.” (Agalatiya 6:1) Ndipo akulu sangakalipire munthu wolakwa kapenanso kumulankhula mawu opweteka. M’malomwake, iwo amapereka malangizo mwachikondi ndipo zimenezi zimalimbikitsa munthuyo. Nthawi zina akulu amafunika kupereka malangizo osapita m’mbali ofotokoza mavuto amene angabwere ngati munthu atapitiriza kuchita zoipa. Komabe akamachita zimenezi amakumbukira kuti munthuyo ndi nkhosa ya Yehova.b (Luka 15:7) Ngati munthu wolakwa akuchita kuoneratu kuti akulu akumupatsa malangizo kapena uphungu mwachikondi komanso chifukwa chomufunira zabwino, zimakhala zosavuta kuti asinthe.

      19. Kodi akulu amafunika kusankha zinthu ziti, ndipo ayenera kudalira chiyani?

      19 Nthawi zambiri akulu amafunika kusankha zinthu zomwe zimakhudza Akhristu anzawo. Mwachitsanzo, amakumana kuti akambirane ngati abale ena mumpingo akuyenerera kukhala akulu kapena atumiki othandiza. Akulu amadziwa kuti sayenera kuchita zinthu mwatsankho. Posankha zochita, amatsatira mfundo za m’Baibulo zofotokoza zimene m’bale ayenera kuchita kuti akhale woyenera kuikidwa pa udindo, osangoti mmene iwowo akumuonera. Choncho amachita zinthu ‘mopanda tsankho kapena kukondera.’​—1 Timoteyo 5:21.

      20, 21. (a) Kodi akulu amayesetsa kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi akulu angatani kuti athandize “anthu amene ali ndi nkhawa”?

      20 Akulu amasonyeza chilungamo m’njira zinanso. Atanena kuti akulu azidzachita zinthu “mwachilungamo,” Yesaya ananenanso kuti: “Aliyense adzakhala ngati malo obisalirapo mphepo, malo obisalirapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.” (Yesaya 32:2) Choncho akulu amayesetsa kuti azilimbikitsa Akhristu anzawo.

      21 Popeza tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana omwe angatifooketse, anthu ambiri amafunika kulimbikitsidwa. Akulu, kodi mungatani kuti muthandize “anthu amene ali ndi nkhawa”? (1 Atesalonika 5:14) Muziwamvetsera mwachifundo. (Yakobo 1:19) Iwo angafune kufotokozera nkhawa zawo munthu amene amamudalira. (Miyambo 12:25) Muziwatsimikizira kuti Yehova komanso abale ndi alongo awo amawakonda kwambiri ndiponso amawaona kuti ndi ofunika. (1 Petulo 1:22; 5:6, 7) Mukhozanso kuwapempherera ndiponso kupemphera nawo limodzi. Zingawalimbikitse kwambiri kumva mkulu akuwapempherera mochokera pansi pamtima. (Yakobo 5:14, 15) Mulungu wathu wachilungamo amaona zonse zimene mumayesetsa kuchita pothandiza anthu amenewa.

      Akulu amatsanzira chilungamo cha Yehova akamalimbikitsa anthu omwe ali ndi nkhawa

      22. Kodi tingatsanzire Yehova pa nkhani yochita chilungamo m’njira ziti, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?

      22 Kunena zoona, tikamatsanzira Yehova pa nkhani yochita zinthu mwachilungamo, timakhala naye pa ubwenzi wolimba. Tikamatsatira mfundo zake zolungama, tikamauza ena uthenga wabwino wothandiza kuti adzapulumuke ndiponso tikamaganizira kwambiri zabwino zimene ena amachita osati zimene amalakwitsa, timakhala kuti tikutsanzira Yehova pa nkhani yochita chilungamo. Akulu, mukamateteza mpingo kuti ukhalebe woyera, mukamapereka malangizo ochokera m’Baibulo, mukamasankha zinthu mosakondera komanso mukamalimbikitsa anthu omwe ali ndi nkhawa, mumakhala mukusonyeza kuti Mulungu ndi wachilungamo. Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri kumwambako akamaona kuti anthu ake akuyesetsa ‘kuchita chilungamo’ pamene akumutumikira.

      a Mabaibulo ena amati, “musamaweruze ena” ndiponso “musamatsutse ena.” Koma mawu amenewa akhoza kungotanthauza kuti “musayambe kuweruza” ndiponso “musayambe kutsutsa.” Komabe m’mavesiwa, olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu omuuza munthu kuti asiye zimene akuchita. Choncho zimene Yesu ananenazi anthu ankazichita pa nthawiyo ndipo ankafunika kuzisiya.

      b Pa 2 Timoteyo 4:2, Baibulo limanena kuti nthawi zina akulu amayenera ‘kudzudzula, kutsutsa ndiponso kudandaulira.’ Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “dandaulira” (pa·ra·ka·leʹo) angatanthauzenso “kulimbikitsa.” Mawu enanso a Chigiriki ofanana nawo akuti pa·raʹkle·tos, amanena za loya amene amathandiza munthu wina m’khoti. Choncho ngakhale pamene akulu akupereka malangizo amphamvu, afunikanso kuthandiza munthu amene wafooka mwauzimuyo.

      Mafunso Ofunika Kuwaganizira

      • Deuteronomo 1:16, 17 Kodi Yehova ankafuna kuti oweruza a ku Isiraeli azichita chiyani, nanga akulu angaphunzirepo chiyani?

      • Yeremiya 22:13-17 Kodi Yehova akuchenjeza kuti tisamachite zinthu zopanda chilungamo ziti, nanga tingatani kuti tizitsanzira chilungamo chake?

      • Mateyu 7:2-5 N’chifukwa chiyani sitiyenera kufulumira kuona zimene Akhristu anzathu amalakwitsa?

      • Yakobo 2:1-9 Kodi Yehova amaona bwanji khalidwe lokondera, nanga malangizowa tingawagwiritse ntchito bwanji tikamachita zinthu ndi ena?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena