Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 103 tsamba 238-tsamba 239 ndime 2
  • “Ufumu Wanu Ubwere”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ufumu Wanu Ubwere”
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Kodi Mulungu Analenga Anthu Chifukwa Chiyani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Moyo Wobvuta Uyamba
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Cholinga cha Mulungu cha Dziko Lapansili Chikwaniritsidwa Posachedwapa
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 103 tsamba 238-tsamba 239 ndime 2
Ana ndi akuluakulu akusangalala m’Paradaiso

MUTU 103

“Ufumu Wanu Ubwere”

Yehova analonjeza kuti: ‘Ndidzapukuta misozi yonse m’maso mwa anthu ndipo sipadzakhalanso kulira, kumva kupweteka, matenda kapena imfa. Zoipa zonse zidzaiwalika.’

Yehova anaika Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni kuti azikhala mwamtendere komanso mosangalala. Iwo ankafunika kumalambira Atate wawo wakumwamba komanso kubereka ana mpaka anthu kudzaza dziko lonse. Adamu ndi Hava sanamvere Yehova koma cholinga chake sichinasinthe. Paja Baibulo limanena kuti Mulungu akalonjeza chinthu sichilephereka. Yehova analonjeza Abulahamu kuti adzabweretsa madalitso osaneneka padzikoli ndipo Ufumu wa Mulungu ndi umene udzabweretse madalitsowo.

Ana ndi akulu akusangalala ndi nyama zakutchire m’dziko lokongola

Posachedwapa Satana ndi ziwanda zake komanso anthu onse oipa adzawonongedwa. Anthu amene adzapulumuke azidzalambira Yehova. Sipadzakhalanso kudwala kapena kufa. Tsiku lililonse tizidzadzuka amphamvu komanso osangalala. Dziko lonse lidzakhala Paradaiso. Aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira komanso nyumba yabwino. Munthu aliyense adzakhala wachifundo osati wankhanza kapena wachiwawa. Anthu azidzakhala bwinobwino ndi nyama popanda kuopana.

Tidzasangalalanso kwambiri kuona Yehova akuukitsa anthu amene anamwalira. Tidzakumana ndi anthu monga Abele, Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Esitere ndiponso Davide. Tidzathandizana nawo kusintha dzikoli kuti likhale lokongola kwambiri. Padzakhala ntchito zambiri zosangalatsa.

Yehova akufuna kuti inunso mudzakhale m’Paradaiso. Tidzadziwa zambiri zokhudza Yehova kuposa zimene tikudziwa panopa. Choncho tiyeni tizilimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova tsiku lililonse mpaka kalekale.

“Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu chifukwa munalenga zinthu zonse ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”​—Chivumbulutso 4:11

Mafunso: Kodi Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso ati? Pa anthu onse otchulidwa m’bukuli, kodi ndi ndani amene mungafune kudzaonana naye m’Paradaiso?

Chivumbulutso 21:3, 4; Yobu 33:25; Miyambo 2:21, 22; Yesaya 11:2-10; 33:24; 65:21; Mateyu 6:9, 10; Yohane 5:28, 29; 17:3

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena