Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/14 tsamba 6
  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Zefaniya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Zefaniya
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Funafunani Yehova Lisanadze Tsiku la Mkwiyo Wake
    Nsanja ya Olonda—2001
  • “Mundilindire”
    Nsanja ya Olonda—1996
  • “Manja Anu Asakhale Olefuka”
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Tsiku la Yehova Lopereka Chiŵeruzo Layandikira!
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
km 7/14 tsamba 6

Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Zefaniya

1. Kodi pa nthawi yomwe Zefaniya anali mneneri zinthu zinali bwanji, nanga tingaphunzire chiyani kwa iye?

1 Cham’katikati mwa zaka za m’ma 600 B.C.E., kulambira Baala kunali ponseponse ku Yuda. Mfumu Amoni, yomwe inali yoipa, inali itaphedwa ndipo Yosiya, yemwe pa nthawiyo anali adakali mwana, anali atayamba kulamulira. (2 Mbiri 33:21–34:1) Pa nthawi imeneyi, Yehova anapatsa Zefaniya ntchito yauneneri kuti alengeze zokhudza chiweruzo cha Yehovayo. Ngakhale kuti mwina mneneri Zefaniya anali wochokera kubanja lachifumu la Yuda, sanafewetse uthenga wa Yehova wodzudzula mafumu a Yuda ndipo anagwira ntchito yake molimba mtima. (Zef. 1:1; 3:1-4) Mofanana ndi Zefaniya, nafenso sitilola kuti chibale chisokoneze kulambira kwathu. (Mat. 10:34-37) Kodi Zefaniya ankalengeza uthenga wotani, nanga zotsatira zake zinali zotani?

2. Kodi tingatani kuti tidzapulumuke pa tsiku la mkwiyo wa Yehova?

2 Bwerani kwa Yehova: Yehova yekha ndi amene angapulumutse anthu pa tsiku la mkwiyo wake. N’chifukwa chake Zefaniya analimbikitsa anthu kuti apite kwa Yehova komanso ayesetse kukhala olungama ndi ofatsa, nthawi isanathe. (Zef. 2:2, 3) N’chimodzimodzinso ndi ife masiku ano. Timalimbikitsa anthu kuti apite kwa Yehova. Koma timaonetsetsanso kuti ifeyo ‘tisasiye kutsatira Yehova.’ (Zef. 1:6) Timapita kwa Yehova pophunzira Mawu ake komanso kumupempha kuti azititsogolera. Timakhala olungama tikamayesetsa kupewa makhalidwe oipa. Komanso tikamagonjera ndi kutsatira zimene gulu la Yehova limatiuza, timasonyeza kuti tikuyesetsa kukhala ofatsa.

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhalabe ndi maganizo oyenera tikamalalikira?

3 Zotsatira Zabwino: Uthenga wa Zefaniya unapangitsa kuti Ayuda ena asinthe. Munthu wina amene uthenga wa Zefaniya unamuthandiza kwambiri anali Yosiya. Iye anayamba kuchita zoyenera pamaso pa Yehova kuyambira ali mwana. Kenako Yosiya anayamba ntchito yolimbikitsa anthu a m’dzikolo kuti asiye kulambira mafano. (2 Mbiri 34:2-5) Masiku anonso ngakhale kuti mbewu zina za Ufumu zimagwera m’mbali mwa msewu, pamiyala kapena paminga, zina zimagwera panthaka yabwino ndipo zimabala zipatso. (Mat. 13:18-23) Tikukhulupirira kuti Yehova azidalitsabe khama lathu tikamapitiriza kufesa mbewu za Ufumu.—Sal. 126:6.

4. N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kupitiriza kuyembekezera Yehova’?

4 Anthu ena a ku Yuda ankaganiza kuti Yehova sangachite chilichonse. Komabe Yehova ananena motsimikiza kuti tsiku lake lalikulu linali pafupi. (Zef. 1:12, 14) Ananenanso kuti adzapulumutsa anthu okhawo amene ankamudalira. (Zef. 3:12, 17) Choncho pamene ‘tikupitiriza kuyembekezera Yehova,’ tiyeni tizitumikira Mulungu wathu mosangalala komanso mogwirizana.—Zef. 3:8, 9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena