Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kulalikira Pogwiritsa Ntchito Intakomu Kapena M’madera a Chitetezo Chokhwima
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Kulalikira pogwiritsa ntchito intakomu kapena kulalikira kudera lomwe nyumba zake ndi za mipanda, kungakhale kovuta. Ndiye kodi tingatani kuti zimenezi zisatilepheretse kugwira ntchito yolalikira modzipereka? Muzikumbukira kuti pali anthu ena amene tingawalalikire uthenga wabwino pogwiritsa ntchito intakomu, foni kapena kalata basi. (Aroma 10:14) Ofalitsa ena agwiritsapo ntchito njirazi ndipo aona kuti ndi zothandiza kwambiri. (Onani Yearbook ya 2011, tsamba 65-66, ndi Yearbook ya 2000, tsamba 54, ndime 3.) Tiyeni tikambirane mmene tingachitire zimenezi.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Pa kulambira kwa pabanja yesererani ulaliki wogwiritsa ntchito foni kapena intakomu ndipo amene akuyesererawo asayang’anizane.