Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 3:
Kugwiritsa Ntchito Malemba Mogwira Mtima
1. N’chifukwa chiyani tifunika kutsindika kwambiri Malemba tikamachititsa maphunziro a Baibulo?
1 Cholinga chathu pochititsa maphunziro a Baibulo ndicho kupanga ophunzira mwa kuthandiza anthu kumvetsa ndi kuvomereza ziphunzitso za Mawu a Mulungu ndi kuzigwiritsa ntchito pa moyo wawo. (Mat. 28:19, 20; 1 Ates. 2:13) Pachifukwa chimenechi, phunziro liyenera kuzikika kwambiri pa Malemba. Choyambirira, kungakhale kothandiza kuonetsa ophunzira mmene angapezere malemba amene akufuna m’Baibulo lawo. Komano, kodi tingagwiritse ntchito motani Malemba kuthandiza anthu ameneŵa kupita patsogolo mwauzimu?
2. Kodi timasankha bwanji malemba m’Baibulo oti tikaŵerenge ndi kukambirana?
2 Sankhani Malemba Oti Mukaŵerenge: Mukamakonzekera, onani mmene lemba lililonse losagwidwa mawu likugwirizanirana ndi nkhani imene mukukakambiranayo, ndipo sankhani malemba oti mukaŵerenge ndi kukambirana pa phunzirolo. Nthaŵi zambiri, ndi bwino kuŵerenga malemba amene amasonyeza kuti zikhulupiriro zathu n’zozikidwa pa Baibulo. Malemba amene amangofotokoza mbiri ya munthu kapena ya nkhani inayake sangafunikire kuwaŵerenga. Ganizirani zosowa ndi moyo wa wophunzira aliyense payekha.
3. Kodi kugwiritsa ntchito mafunso kuli ndi phindu lanji, ndipo kodi tingachite motani zimenezi?
3 Gwiritsani Ntchito Mafunso: M’malo moti inuyo mum’tanthauzire wophunzirayo malemba a m’Baibulowo, muloleni iyeyo kuti atanthauzire. Mungam’limbikitse kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito mafunso mwaluso. Ngati tanthauzo la lembalo lili lodziŵikiratu, mukhoza kungom’funsa kufotokoza mmene lembalo likugwirizanirana ndi zimene zanenedwa m’ndimeyo. Nthaŵi zina, funso lachindunji kapena mafunso angapo angafunike kuti mum’thandize wophunzirayo kuti afike pa mfundo yolondola. Ngati pangafunike kuti mufotokoze zowonjezera, mungatero pambuyo pakuti wophunzirayo wakuyankhani.
4. Kodi tiyenera kufotokoza zochuluka motani pa malemba amene timaŵerenga?
4 Musachulutse Zonena: Munthu waluso lodziŵa kuponya mivi amangofunikira muvi umodzi wokha kuti alase chimene akufuna. N’chimodzimodzinso ndi mphunzitsi waluso. Sachita kufunikira mawu ambirimbiri kuti anene mfundo yofunika. Akhoza kufotokoza nkhani mosavuta, momveka bwino ndi molondola. Nthaŵi zina, mungafunikire kukafufuza m’zofalitsa zina zachikristu kuti muthe kulimvetsa bwino lemba ndi kulifotokoza molondola. (2 Tim. 2:15) Koma pewani kuyesa kufotokoza mbali zonse za lembalo paphunzirolo. Ingofotokozani mbali yokhayo imene ikufunika kuti mumveketse bwino mfundo imene mukukambirana.
5, 6. Kodi tingawathandize motani ophunzira kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pa moyo wawo, koma tifunika kupewa kuchita chiyani?
5 M’thandizeni Kuona Kuti Malembawo Akum’khudza: Pamene kuli koyenera, m’thandizeni wophunzirayo kuona mmene malemba a m’Baibulowo akum’khudzira payekha. Mwachitsanzo, pokambirana lemba la Ahebri 10:24, 25 ndi wophunzira amene sanayambe kupita ku misonkhano yachikristu, mukhoza kukambirana za msonkhano umodzi ndi kum’pempha kuti adzapezekepo. Koma pewani kum’kakamiza. Lolani Mawu a Mulungu kum’thandiza kuchita zimene zili zofunika kuti akondweretse Yehova.—Aheb. 4:12.
6 Pamene tikugwira ntchito yopanga ophunzira, tiyeni tiwalimbikitse ‘kumvera mwa chikhulupiriro’ pogwiritsa ntchito Malemba mogwira mtima.—Aroma 16:26.