Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 12/14 tsamba 2-6
  • Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Matenda a Muubongo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Matenda a Muubongo
  • Galamukani!—2014
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dziwani Zambiri za Matendawa
  • Kumvetsa Zimene Zimachitikira Odwala Matendawa N’kothandiza
  • Mankhwala Ake
  • Kupeza Nthawi Yochita Zinthu Zauzimu N’kothandiza
  • Zimene Mungachite Munthu Amene Mumakonda Akadwala Misala
    Galamukani!—2004
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Matenda Ovutika Maganizo Ndi Vuto la Padziko Lonse
    sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
  • Mulungu Akulonjeza Kuti Kuvutika Maganizo Kudzatheratu
    sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 12/14 tsamba 2-6
Mkazi akumvera chisoni mwamuna wake yemwe akudwala

NKHANI YA PACHIKUTO

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Matenda a Muubongo

Mayi wina wa ku South Africa, dzina lake Claudia yemwe anamupeza ndi matenda a muubongo, anati: “Atangondiuza kuti ndili ndi matendawa, ndinkangoona ngati ndifa basi. Ndinkada nkhawa kwambiri ndikaganizira zoti anthu odwala matendawa amasalidwa.”

Mark, yemwe ndi mwamuna wa Claudia, anati: “Zinanditengera nthawi kuti ndivomereze zoti mkazi wanga wapezeka ndi matenda a muubongo. Koma kenako ndinazindikira kuti chofunika kwambiri ndi kumuthandiza komanso kumusamalira.”

KODI mungamve bwanji inuyo kapena munthu amene mumam’konda atapezeka ndi matenda a muubongo? N’zodziwikiratu kuti zingakhale zowawa kwambiri. Koma ubwino wake ndi woti matendawa ali ndi mankhwala. Tiyeni tione zinthu zingapo zomwe zingakuthandizeni kudziwa zambiri za matendawa.

Dziwani Zambiri za Matendawa

Bungwe loona za umoyo padziko lonse linati: “Matenda a muubongo amagwira anthu ambirimbiri padziko lonse ndipo amene amavutika si wodwala yekhayo. Achibale ndi anzake a wodwalayo amavutikanso. Munthu mmodzi pa anthu 4 alionse amadwala matendawa. Kuvutika maganizo ndi amodzi mwa matenda a muubongo omwe anthu ambiri amadwala padziko lonse. Ena mwa matenda a muubongowa, omwenso ndi oopsa kwambiri, ndi monga kusokonezeka maganizo komanso misala. . . . Ngakhale kuti matenda a muubongo ndi ofala, anthu ambiri odwala matendawa sadziwa, salandira thandizo loyenera ndipo ena amasalidwa.”

Bungwe loona za umoyo padziko lonse linanenanso kuti, anthu ambiri omwe ali ndi matenda a muubongo sapita kuchipatala kukalandira thandizo chifukwa choopa kuti anthu akadziwa kuti ali ndi matendawa, aziwasala.

Ngakhale kuti matenda a muubongo ali ndi mankhwala, bungwe lina loona za matendawa linati, ku United States anthu 60 pa 100 alionse komanso ana 50 pa 100 alionse azaka za pakati pa 8 ndi 15, sanalandire mankhwala a matendawa chaka chatha.

Kumvetsa Zimene Zimachitikira Odwala Matendawa N’kothandiza

Mayi yemwe akudwala matenda a muubongo

Akatswiri odziwa za matenda a muubongo amati, matendawa amapangitsa kuti munthu asamaganize bwino komanso kuti azilankhula kapena kuchita chilichonse chomwe wafuna, popanda kudziletsa. Nthawi zambiri matendawa amalepheretsa munthu kuti azimvana ndi anzake komanso amapangitsa kuti munthu azichita zosalongosoka.

Matenda a muubongo sayamba chifukwa choti munthu ali ndi vuto kapena khalidwe linalake loipa

Zizindikiro za matenda a muubongo zimasiyanasiyana potengera mmene munthu alili, vuto la munthuyo komanso mmene zinthu zilili pa moyo wake. Matendawa saona nkhope. Amagwira aliyense mosatengera zaka, chikhalidwe, mtundu, chipembedzo, maphunziro, kulemera, kusauka kapenanso kuti ndi mwamuna kapena mkazi. Matenda a muubongo sayamba chifukwa choti munthu ali ndi vuto kapena khalidwe linalake loipa. Komatu munthu wodwala matendawa akalandira thandizo akhoza kuchira bwinobwino.

Mankhwala Ake

Madokotala odziwa bwino za matenda a muubongo amatha kuthandiza anthu odwala matendawa, n’kuchira bwinobwino. Koma kuti anthu oterewa akuthandizeni muyenera kupita kuchipatala kuti akakuuzeni zambiri zokhudza matenda anuwo komanso zomwe muyenera kuchita.

Mayi yemwe akudwala matenda a muubongo akulankhula ndi dokotala wodziwa za matendawa

Munthu wodwala matendawa angachire pokhapokha ngati atatsatira malangizo omwe wapatsidwa. Nthawi zina kuti athe kuchita zimenezi ayenera kukhala womasuka kufotokozera ena za matenda akewo. Zimenezi zingathandize kuti athe kufotokozera dokotala mmene akumvera komanso zonse zomwe zikumuchitikira. Izi zingachititse kuti dokotalayo amuthandize kumvetsa bwino zokhudza matendawo. Angamuuzenso zimene ayenera kuchita komanso kumulimbikitsa kuti asasiye kulandira thandizo. Pokaonana ndi dokotalayo ndi bwino kupita ndi mnzake kapena wachibale kuti azimuthandiza komanso kumulimbikitsa.

Anthu ambiri odwala matenda a muubongo akamvetsa bwino zokhudza matendawa komanso akatsatira malangizo onse amene dokotala wawapatsa, amachira. Mark yemwe tamutchula koyamba uja anati: “Mkazi wanga asanamupeze ndi matenda a muubongo, sitinkadziwa zambiri za matendawa. Koma atamupeza nawo, tinamvetsa bwino zokhudza matendawa. Tinazindikiranso kuti tisamadere nkhawa kwambiri za mawa, koma tizingoyesetsa kuthana ndi vuto lomwe lilipo pa nthawiyo. Madokotala, anzathu komanso achibale atithandiza kwambiri.”

Muyenera kupita kuchipatala kukaonana ndi dokotala wodziwa bwino za matenda anuwo kuti akakuuzeni zambiri zokhudza matendawo komanso zomwe muyenera kuchita

Claudia nayenso anati: “Atandiuza kuti andipeza ndi matendawa, ndinangomva ngati ndalandidwa ufulu wonse. Koma patapita nthawi ndinasiya kukhala ndi maganizo amenewa. Ngakhale kuti matendawa amapangitsa kuti tisamakwanitse kuchita zinthu zina, taona kuti n’zotheka kuthetsa mavuto ena omwe poyamba tinkaona ngati ndi osatheka kuwathetsa. Chinanso chomwe chimatithandiza n’choti, timayesetsa kutsatira malangizo omwe madokotala amatipatsa, timayesetsa kumacheza ndi anthu ena komanso kuti tisamangokhalira kudera nkhawa za matendawa.”

Kupeza Nthawi Yochita Zinthu Zauzimu N’kothandiza

Mayi akuwerenga Baibulo

Baibulo silinena kuti kuchita zinthu zauzimu kungapangitse kuti munthu achire matenda ake. Komabe pali anthu ambiri omwe amalimbikitsidwa ndi zimene Baibulo limanena. Mwachitsanzo, limatiuza kuti Mlengi wathu wachikondi amafunitsitsa kuthandiza anthu “a mtima wosweka” komanso ‘a mtima wachisoni.’—Salimo 34:18.

Ngakhale kuti Baibulo si buku la zaumoyo, lili ndi malangizo omwe angatithandize kuchepetsa nkhawa komanso kudziwa zochita tikadwala. Lingatithandizenso kukhala ndi chiyembekezo choti m’tsogolomu padzikoli sipadzakhalanso matenda kapena mavuto alionse. Baibulo limati: “Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.”—Yesaya 35:5, 6.

MAVUTO AMENE AMAKUMANA NAWO

Claudia anati: “Nthawi zina ndimalephera kuchita zinthu zina ndipo ndikamawerenga sindimva zomwe ndikuwerengazo. Matenda angawa amandichititsa kuti ndizikhala ndi nkhawa kwambiri. Izi zimapangitsa kuti ndisamafune kucheza ndi anthu, ngakhale anzanga apamtima. Anthu ena amandiuza kuti mavuto anga si aakulu ngati mmene ndikuganizira ndipo ndisamadandaule kwambiri chifukwa zinthu zisintha n’kuyambanso kuyenda bwino. Ena amandiuza kuti ndisamangoganizira za matenda angawa, koma ndiziganiziranso za zinthu zina zomwe zikuyenda bwino pa moyo wanga. Ndakhala ndikuyesetsa kuchita zimenezi kwa nthawi yaitali koma palibe chasintha. Ndikudziwa kuti anthuwa amandiuza zimenezi chifukwa chondikonda, koma zimangopangitsa kuti ndizidziimba mlandu komanso kuti ndizidziona kuti ndine wolephera.”

ZIMENE MUNGACHITE NGATI MULI NDI MATENDAWA

  1. Muzitsatira malangizo amene dokotala wodziwa bwino za matenda a muubongo wakupatsani.a

  2. Musamadzipanikize kwambiri.

  3. Muzichita masewera olimbitsa thupi.

  4. Muzigona mokwanira.

  5. Tsiku lililonse muzipeza nthawi yokwanira yopuma.

  6. Muzidya zakudya zamagulu onse komanso zopatsa thanzi.

  7. Musamamwe mowa kwambiri komanso musamamwe mankhwala omwe dokotala sanakuuzeni kuti mumwe.

  8. Musamakonde kukhala nokha. Muzicheza ndi anthu amene mumawakhulupirira komanso omwe akudziwa za mavuto anu.

  9. Muzipeza nthawi yochita zinthu zauzimu.b

a Galamukani! sisankhira anthu mankhwala. Mkhristu aliyense ali ndi udindo woonetsetsa kuti chithandizo cha mankhwala chomwe walandira si chotsutsana ndi mfundo za m’Baibulo.

b Malangizo ena othandiza mungawapeze m’nkhani yakuti, “Kodi Mungatani Ngati Mukuvutika Maganizo?” mu Galamukani! ya May 2014.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena