Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 August tsamba 2
  • Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Kudzichepetsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Kudzichepetsa
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amaona Kuti Atumiki Ake Odzichepetsa Ndi Amtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kodi Nkuvaliranji Kudzichepetsa?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • “Ndine . . . Wodzichepetsa”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
  • Khalani Odzichepetsadi
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 August tsamba 2

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Kudzichepetsa

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZICHEPETSA N’KOFUNIKA?

  • Kudzichepetsa kumatithandiza kuti tikhale paubwenzi ndi Yehova.​—Sal. 138:6

  • Kudzichepetsa kumatithandiza kuti tizigwirizana ndi anthu ena.​—Afil. 2:3, 4

  • Kunyada kumabweretsa mavuto.​—Miy. 16:18; Ezek. 28:17

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUDZICHEPETSA?

  • Tizifunsa malangizo kwa ena ndi kuwagwiritsa ntchito.​—Sal. 141:5; Miy. 19:20

  • Tizikhala okonzeka kuthandiza ena pogwira ntchito zooneka ngati zonyozeka.—Mat. 20:25-27

  • Tisalole kuti luso kapena udindo wathu zitipangitse kukhala onyada.​—Aroma 12:3

M’bale akuyeretsa kuchimbudzi pa Nyumba ya Ufumu

Kodi ineyo ndingatani kuti ndizisonyeza kwambiri khalidwe la kudzichepetsa?

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIPEWA ZINTHU ZIMENE ZINGAWONONGE KHALIDWE LANU LA KUKHULUPIRIKA​—KUNYADA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi zimene timachita tikapatsidwa malangizo zimasonyeza kuti tili ndi khalidwe lotani?

  • Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti tikhale odzichepetsa?

  • Kodi ndi njira zinanso ziti zimene tingasonyezere kuti ndife odzichepetsa?

CHITSANZO CHA M’BAIBULO CHOFUNIKA KUCHIGANIZIRA:

Yesu anali munthu wamkulu woposa onse. Koma anali wodzichepetsa ndipo ankatumikira ena.​—Mat. 20:28; Yoh. 13:3-5, 14, 15.

Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani ya kudzichepetsa?’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena