MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo—Kulimba Mtima
N’CHIFUKWA CHIYANI KULIMBA MTIMA N’KOFUNIKA?
Kulalikira kumafuna kulimba mtima.—Mac. 5:27-29, 41, 42
Pa chisautso chachikulu tidzafunika kukhala olimba mtima.—Mat. 24:15-21
Kuopa anthu kumabweretsa mavuto.—Yer. 38:17-20; 39:4-7
KODI TINGASONYEZE BWANJI KULIMBA MTIMA?
Tiziganizira zimene Yehova anachita populumutsa anthu.—Eks. 14:13
Tizipemphera kuti Mulungu atithandize kukhala olimba mtima.—Mac. 4:29, 31
Tizidalira Yehova.—Sal. 118:6
Kodi ndiyenera kulimbana ndi zinthu ziti zimene zimandichititsa mantha ndikamatumikira Mulungu?
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIPEWA ZINTHU ZIMENE ZINGAWONONGE KHALIDWE LANU LA KUKHULUPIRIKA—KUOPA ANTHU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
N’chifukwa chiyani kulimba mtima n’kofunika tikakhala mu utumiki?
Kodi lemba la Miyambo 29:25 likusonyeza bwanji kusiyana pakati pa kuopa anthu ndi kukhulupirira Yehova?
Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala olimba mtima panopa?