Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w05 5/1 tsamba 3
  • Vuto Ladzidzidzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Vuto Ladzidzidzi
  • Nsanja ya Olonda—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mungatani Mutakumana Ndi Vuto Lalikulu?
    Galamukani!—2014
  • Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa N’chosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Mawu Oyamba
    Galamukani!—2020
  • Kodi N’chiyani Chingandithandize Ndikakumana ndi Mavuto?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2005
w05 5/1 tsamba 3

Vuto Ladzidzidzi

OWEN, mwana wa zaka ziwiri ndi theka, ankasewera m’bafa kunyumba kwawo. Kenaka ananyanyamphira kabati ya m’bafamo imene makolo ake ankaona kuti sangaifikire. M’kabatimo munali mankhwala ndipo mwanayo anachita chidwi ndi botolo linalake. Anatsegula botololo n’kugugudiza mankhwala amene analimo. Atatero zinthu zinaipa.

M’botolomo munali mankhwala onyeketsa zinthu a asidi. N’zomvetsa chisoni kuti Owen anafa nawo mankhwalawo. Makolo ake anasokonezeka maganizo mosaneneka. A Percy, omwe ndi bambo ake anayesa kupita kutchalitchi kwawo kuti akalimbikitsidwe. Anapita kwa mbusa n’kumufunsa kuti, “Kodi n’chifukwa chiyani zimenezi zachitika?” Ndiye mbusayo anawayankha kuti, “N’chifukwa choti Mulungu amafuna kamngelo kena kumwamba.” Mawuwa anangowonjezera chisoni cha anamfedwawa chifukwa ankaona kuti ichi sichilungamo ngakhale pang’ono. Koma kodi Mulungu ndiyedi anafuna kuti pachitike tsoka limeneli? A Percy anakhumudwa kwambiri ndi tchalitchicho ndipo anaganiza zolekana nacho.

Poganizira zimene zinachitikazo iwo anadzifunsa kuti: ‘Kodi mwana wanga akuvutikabe? Kodi ndidzamuonanso?’

N’kutheka kuti nanunso munayamba mwadzifunsapo kuti n’chiyani makamaka chimachitika munthu akafa ndiponso ngati zidzatheke kudzaonananso ndi anthu apamtima panu amene anamwalira. Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limayankha mafunso amenewa. Lili ndi mayankho omveka ndiponso olimbikitsa kwa aliyense amene anakumanapo ndi mavuto ngati amenewa. Komanso chachikulu n’chakuti limasonyeza kuti pali chiyembekezo chosangalatsa kwambiri chimene Mulungu analonjeza. Chimenechi n’chiyembekezo cha kuuka kwa akufa.

Werengani nkhani yotsatirayi kuti mudziwe zambiri zokhudza chiyembekezo chosangalatsachi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena