Mawu Oyamba
Nthawi zina tonsefe timakumana ndi mavuto monga matenda, ngozi zam’chilengedwe ndiponso ngozi zina, kapena zachiwawa.
Anthu akufufuza mayankho.
Anthu ena amanena kuti timavutika chifukwa chakuti Mulungu analemberatu kuti tidzakumana ndi mavuto, kapena amati palibe zambiri zomwe tingachite kuti tisamavutike.
Ena amati timavutika chifukwa cha zinthu zoipa zomwe tinachita m’mbuyomu kapena m’moyo wina womwe tinali nawo tisanabadwe m’moyo uno.
Mavuto amachititsa anthu kukhala ndi mafunso ambiri opanda mayankho.