Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 6/14 tsamba 10-11
  • Joseph Priestley

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Joseph Priestley
  • Galamukani!—2014
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE ANAPEZA ZOKHUDZA SAYANSI
  • ZIMENE ANAPEZA ZOKHUDZA CHIPEMBEDZO
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2014
  • Kugwirizanitsa Sayansi ndi Chipembedzo
    Galamukani!—2002
  • Ankasamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Kodi Gasi Amachokera Kuti?
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 6/14 tsamba 10-11
Chithunzi cha Joseph Priestley

ZITHUNZI ZAKALE

Joseph Priestley

Katswiri wina wa nzeru za anthu, dzina lake Frederic Harrison, ananena kuti Joseph Priestley yemwe anali “katswiri pa nkhani zasayansi, zachipembedzo, zandale komanso nzeru za anthu, yemwenso anathandiza kuti zinthu zisinthe ku France ndipo anazunzidwa popanda chifukwa, anachita zinthu zotamandika m’zaka za m’ma 1700.” Frederic Harrison ananenanso kuti, “Joseph Priestley ankachita chidwi ndi zinthu zokhudza makhalidwe abwino komanso kuphunzira zinthu zosiyanasiyana.”

KODI ndi zinthu ziti zimene Joseph Priestley anachita zimene anthu amamukumbukira nazo? Zimene analemba komanso kutulukira zimakhudza mmene anthu amaonera atsogoleri andale, zimene anthu amadziwa pa nkhani ya Mulungu komanso mpweya umene timapumawu.

Priestley akamalemba zasayansi kapena zachipembedzo, ankatsutsa mfundo zabodza ndipo ankayesetsa kupeza zoona pa nkhaniyo. Tiyeni tione mmene anachitira zimenezi.

ZIMENE ANAPEZA ZOKHUDZA SAYANSI

Atakumana ndi wasayansi wina wa ku America, dzina lake Benjamin Franklin mu 1765, Joseph Priestley anayamba kufufuza za magetsi. Pa nthawiyi ankakonda kuchita kafukufuku wa zinthu zosiyanasiyana. Chaka chotsatira, asayansi anzake anachita chidwi ndi zimene iye anapeza ndipo anamusankha kuti akhale membala wa bungwe la zasayansi lotchedwa, Royal Society of London.

Kenako, Priestley anayamba kuchita chidwi ndi sayansi ya mmene zinthu zosiyanasiyana zimapangidwira. Pasanapite nthawi, anatulukira mitundu ingapo ya mpweya monga wa ammonia ndi wa nitrous oxide. Anaphatikizanso madzi ndi mpweya wa carbon dioxide n’kupanga madzi enaake.

Mu 1774, Priestley ali kum’mwera kwa England, anatulukira mpweya wina umene umapangitsa kuti kandulo aziwala kwambiri. Kenako anatenga pang’ono mpweya woterewu n’kuuika m’botolo lagalasi ndipo anaikamonso khoswe. Khosweyo sanafe msanga poyerekeza ndi mmene akanafera zikanakhala kuti anamuika mu mpweya wamba. Priestley anapumanso mpweyawu ndipo ananena kuti “unamuthandiza kuti azipuma mosavuta.”

Apa Joseph Priestley anali atatulikira mpweya wa okosijeni, umene anthufe timapuma.a Koma iye ankaganiza kuti watulukira mpweya wamba umene unalibe zina ndi zina zimene zimapangitsa kuti zinthu ziyake. Zimene ankaganizazi sizinali zoona, chifukwa ambiri amaona kuti “apa Priestley anagwira ntchito yotamandika kwambiri pa moyo wake.”

ZIMENE ANAPEZA ZOKHUDZA CHIPEMBEDZO

Priestley ankaona kuti zinthu zabodza zimene anthu ankanena zokhudza sayansi komanso chipembedzo, zinkalepheretsa anthu kudziwa zoona pa nkhani zimenezi. Komabe zinthu zina zimene Priestley ankakhulupirira pa nthawi imene ankafufuza zokhudza Baibulo, sizinali zogwirizana ndi zomwe Baibulo limanena. Mwachitsanzo, pa nthawi ina iye sankakhulupirira kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu. Ankatsutsanso zimene Baibulo limanena zoti Yesu anali kumwamba asanabwere padziko lapansi.

“Ngati sayansi ingamuthandize munthu kudziwa choonadi, ndiye kuti Priestley anali wasayansi weniweni.”—Katherine Cullen, yemwenso anali wasayansi.

Ngakhale izi zinali choncho, Priestley ankatsutsa zinthu zabodza zimene zipembedzo zinkaphunzitsa zomwe pa nthawiyo zinali zofala ngati mmene zililinso masiku ano. Iye analemba kuti Yesu ndi atumwi ake onse atamwalira, anthu anayamba kuphunzitsa zinthu zabodza monga zakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi komanso zoti mzimu wa munthu sufa. Analembanso kuti anthuwa ankalimbikitsa kugwiritsa ntchito zifaniziro polambira, ngakhale kuti Baibulo limatsutsa zimenezi.

Anthu a m’dziko lakwawo anakwiya kwambiri ndi zimene Priestley analembazi komanso chifukwa choti ankathandiza kuti zinthu zisinthe ku America ndi ku France pa nkhani zandale. Choncho mu 1791, gulu la anthu osagwirizana naye linawotcha nyumba komanso labotale yake ndipo kenako iye anathawira ku United States. Ngakhale kuti anthu amamukumbukira chifukwa cha zimene anatulukira pa nkhani ya sayansi, Joseph Priestley ankakhulupirira kuti kuphunzira za Mulungu komanso cholinga chake, n’kumene kuli “kofunika kuposa chilichonse.”

a Priestley asanatulukire mpweya wa okosijeni, katswiri wina wofufuza mmene zinthu zimapangidwira wa ku Sweden, dzina lake Carl Scheele anatulukirapo mpweyawu koma sanalembe zimene anatulukirazi. Patapita nthawi kuchokera pamene Priestley anatulukira mpweyawu, katswiri winanso wofufuza mmene zinthu zimapangidwira wa ku France, dzina lake Antoine-Laurent Lavoisier, anatchula mpweyawu kuti okosijeni.

DZIWANI IZI

  • Joseph Priestley anabadwa m’chaka cha 1733 pafupi ndi mzinda wa Leeds ku England.

  • Monga wasayansi, anatulukira mitundu yosiyanasiyana ya mpweya.

  • Monga wandale, anathandiza kuti anthu akhale ndi ufulu wolankhula, wopembedza komanso wamaphunziro.

  • Monga m’busa, anatsutsa ziphunzitso zomwe si za m’Malemba monga chiphunzitso chakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi komanso choti mzimu sufa.

  • M’chaka cha 1794, Priestley anathawira ku United States, ndipo anamwalira komweko, pasanathe zaka 10.

KUSIYANA KWA ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA NDI ZOMWE ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA

Anthu achiwawa akuwotcha nyumba ndi labotale ya Priestley

Mu 1791, gulu la anthu osagwirizana ndi Priestley linawotcha nyumba komanso labotale yake

Priestley anapeza kuti zinthu zambiri zimene zipembedzo zimaphunzitsa n’zosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

  • Zimene Ena Amakhulupirira: Yesu ndi wofanana ndi Mulungu.

    Zimene Baibulo Limaphunzitsa: Yesu Khristu ananena kuti: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.”—Yohane 14:28.

  • Zimene Ena Amakhulupirira: Munthu akafa mzimu wake umapita kwinakwake.

    Zimene Baibulo Limaphunzitsa: “Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.”—Ezekieli 18:4.

  • Zimene Ena Amakhulupirira: Si kulakwa kugwiritsa ntchito zifaniziro polambira Mulungu.

    Zimene Baibulo Limaphunzitsa: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli, ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense kapena kupereka ulemerero wanga kwa zifaniziro zogoba.”—Yesaya 42:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena