Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 8/15 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu Wachikondi
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kukonzekera Ukwati Wachipambano
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Nsanja ya Olonda—1999
w99 8/15 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Akristu ayenera kuona motani kufunika kwa kukwaniritsa pangano la ukwati?

Pangano la ukwati ndi losangalatsa, komanso n’lofunika kulisamalira kwambiri. Mkristu aliyense wofikapo sayenera kupepuza pangano la ukwati, akumalingalira kuti angalithetse nthaŵi ina iliyonse mwachibwanabwana. Nthaŵi yonse ya panganolo ilinso nthaŵi yoti aŵiriwo adziŵane bwino asanakwatirane.

Pamene tikukambirana nkhaniyi, tifunikira kudziŵa kuti miyambo yokhudza ukwati, ndi masitepe otsogolera kuukwati, ndi osiyana kwambiri m’malo ndi panthaŵi zosiyanasiyana. Baibulo limasonyeza zimenezi.

Ana aakazi aŵiri a Loti, amene “sanagonepo ndi mwamuna,” anali otomeredwa mwanjira inayake ndi amuna aŵiri akomweko. ‘Akamwini [a Loti] anali pafupi kutenga ana ake aakazi,’ koma Baibulo silitiuza chifukwa chake ndi momwe mapangano aukwatiwo anachitikira. Kodi ana aakaziwo anali akuluakulu? Kodi anali ndi ufulu wosankha amuna odzawakwatira? Kodi anatomeredwa mwa kuchita chinachake poyera? Sitidziŵa. (Genesis 19:8-14, NW) Timadziŵa kuti Yakobo anachita pangano lake ndi bambo wa Rakele, lodzakwatira Rakele pambuyo pakuwagwirira ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri. Ngakhale kuti Yakobo ankatchula Rakele kuti “mkazi wanga,” iwo sanakhalepo malo amodzi m’zakazo. (Genesis 29:18-21) Chitsanzo china ndi cha Davide. Asanakwatire mwana wa Sauli, iye, anayenera kugonjetsa Afilisti m’nkhondo. Atakwaniritsa cholinga cha Sauli, Davide akanatha kukwatira mwana wa Sauli, Mikala. (1 Samueli 18:20-28) “Mapangano aukwati” amenewo sanali ofanana ndiponso n’ngosiyana ndi amene ali ofala m’mayiko ambiri lerolino.

Chilamulo cha Mose chinali ndi malamulo aukwati komanso pangano la ukwati. Mwachitsanzo, mwamuna ankatha kukhala ndi akazi angapo; ankatha kusudzula mkazi pazifukwa zosiyanasiyana, pamene zikuoneka kuti mkazi sankatha kutero. (Eksodo 22:16, 17; Deuteronomo 24:1-4) Munthu akagona ndi namwali wosatomeredwa, amayenera kumukwatira ngati bambo wa mkaziyo avomereza, ndipo samayenera kudzamusudzula mkaziyo. (Deuteronomo 22:28, 29) Malamulo ena amanena za muukwati, monga ngati nthaŵi imene kugonana kumayenera kupeŵedwa. (Levitiko 12:2, 5; 15:24; 18:19) Kodi ndi malamulo ati amene amakhudzana ndi pangano la ukwati?

Mwalamulo, msungwana wotomeredwa mu Israyeli anali mumkhalidwe wosiyana ndi msungwana wosatomeredwa; anali kuonedwa ngati wokwatiwa. (Deuteronomo 22:23-29; Mateyu 1:18, 19) Aisrayeli sankatomerana kapena kukwatirana ndi achibale ena. Kaŵirikaŵiri, aŵa anali achibale a makolo ofanana, koma mapangano aukwati ndi maukwati ena sankaloledwa chifukwa cha ufulu wa choloŵa. (Levitiko 18:6-20; onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya March 15, 1978, masamba 25-8.) N’zoonekeratu kuti atumiki a Mulungu sankafunikira kuona pangano la ukwati mopepuka.

Aisrayeli anali kutsatira malamulo onsewa a Chilamulo, koma Akristu satsatira Chilamulo, kuphatikizapo malamulo ake okhudza pangano la ukwati ndi ukwati. (Aroma 7:4, 6; Aefeso 2:15; Ahebri 8:6, 13) Kwenikweni, Yesu anaphunzitsa kuti chitsanzo cha Chikristu kaamba ka ukwati chinali chosiyana ndi cha m’Chilamulo. (Mateyu 19:3-9) Komabe, sanachepetse kufunika kwa ukwati, ngakhale kwa pangano la ukwati. Motero, nanga bwanji za nkhani imene tikukambiranayi, pangano la ukwati pakati pa Akristu?

M’mayiko ambiri, munthu amadzisankhira yekha munthu amene akufuna kudzakwatirana naye. Pamene mwamuna ndi mkazi alonjezana kudzakwatirana, iwo amaonedwa kuti ali m’pangano la ukwati. Kaŵirikaŵiri palibe lamulo lofuna mwambo winanso wokhazikitsira panganolo. N’zoona, m’madera ena, si chachilendo kuti mwamuna apereke mphete kwa amene adzakhale mkazi wakeyo, monga chisonyezero cha pangano lawo. Kapena, ndi mwambo kulengeza za chitomerocho kwa achibale ndi achinansi, monga pa chakudya kapena pa macheza ena. Zimenezi ndi zosankha zaumwini, osati lingaliro la Malemba. Kwenikweni, pangano la ukwati limachitika pamene aŵiriwo agwirizana.a

Mkristu sayenera kuthamangira kuyamba chibwenzi, kuchita pangano la ukwati, kapena kuloŵa muukwati umene. Timafalitsa ziwiya zozikidwa pa Baibulo zimene zingathandize anthu osakwatira kusankha ngati n’kwanzeru kuyamba chibwenzi kutomera kapena kuloŵa m’pangano la ukwati, ngakhale kuloŵa muukwati weniweniwo.b Mfundo yaikulu m’mauphungu ameneŵa ndiyo yakuti ukwati wachikristu ndi wachikhalire.​—Genesis 2:24; Marko 10:6-9.

Akristu aŵiri ayenera kudziŵana bwino lomwe asanayambe kulingalira za pangano la ukwati. Aliyense wa aŵiriwo angadzifunse kuti, ‘Kodi ndikudziŵadi bwino za m’khalidwe wauzimu wa mnzangayu ndi kudzipereka kwake kwa Mulungu? Kodi n’zoonekera kuti ndidzatumikira Mulungu ndi mnzangayo kwa moyo wonse? Kodi tadziŵana bwino za zofooka zathu? Kodi ndili ndi chikhulupiriro chakuti tidzakhala ogwirizana nthaŵi zonse? Kodi aliyense wa ife tikudziŵana bwino khalidwe lathu la m’mbuyomu ndi mmene zinthu zilili panopa?’

Pamene Akristu aŵiri atomerana, n’choyenera kwa iwo ndi kwa ena kuyembekezera kuti chotsatirapo chake ndi ukwati. Yesu analamula kuti: ‘Manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iyayi, iyayi.’ (Mateyu 5:37) Akristu amene ali m’pangano la ukwati ayenera kukhala otsimikizira kuti adzalikwaniritsa. Komabe, nthaŵi zina, Mkristu amene ali m’pangano la ukwati angazindikire kuti chinachake sichinatchulidwepo kapena mnzakeyo anachibisa asanatomerane. Mwina lingakhale vuto lalikulu lokhudzana ndi khalidwe la m’mbuyomo, ngakhale uchigaŵenga kapena zachiwerewere. Mkristu amene wazindikira zimenezi ayenera kulingalira chochita. Mwina aŵiriwo angakambirane nkhaniyo mozama ndi kugwirizana ngati pangano la ukwatilo lingapitirize. Kapena onse aŵiri angagwirizane kulithetsa. Ngakhale kuti kutero kungakhale nkhani ya aŵiriwo​—popanda wina aliyense kuloŵelerapo, kuyesa kudziŵa zifukwa zimene anathetsera pangano lawo, kapena kupereka chigamulo​—ndi chosankha chachikulu kwambiri. Komanso mwina amene wazindikira za vuto la mnzakeyo angafune kuthetsa panganolo, ngakhale ngati winayo akufuna kuti lipitirirebe.​—Onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya June 15, 1975.

Pali chifukwa chabwino chokambirana nkhani zimenezi munthu asanaloŵe muukwati. Yesu ananena kuti chifukwa chokha chovomerezeka ndi Malemba cha chisudzulo chimene chimaloleza winayo kukwatiranso kapena kukwatiwanso ndi por·nei’a, pamene mmodzi wa okwatiranawo wachita chigololo. (Mateyu 5:32; 19:9) Iye sananene kuti ukwati wolembetsedwa ungathetsedwe mwa chisudzulo ngati wina wazindikira za vuto lina lalikulu limene sanalidziŵe kapena cholakwa chimene mnzakeyo anachita ukwati usanachitike.

Mwachitsanzo, kunali kosavuta kuti munthu agwidwe ndi khate m’masiku a Yesu. Mwamuna wachiyuda atazindikira kuti mkazi wake anali ndi khate (mkaziyo akudziŵa kapena asakudziŵa) pamene amam’kwatira, kodi anali ndi chifukwa chom’sudzulira? Myuda wotsatira Chilamulo akanatha kum’sudzula, koma Yesu sanasonyeze kuti zimenezi n’zoyenera kwa ophunzira ake. Talingalirani zina mwa zochitika za masiku ano. Mwamuna amene ali ndi chindoko, matuza a kumpheto, HIV, kapena matenda ena aliwonse opatsirana, angakwatire osaulula zimenezo. Mwina iye anatenga matendaŵa kwina kudzera m’chiwerewere asanatomerane kapena pambuyo potomerana. Popeza kuti ndi okwatirana tsopano, mkaziyo sangathetse ukwati chifukwa chakuti wazindikira kuti mwamuna wake ali ndi matendaŵa, kapena za khalidwe lake loipa papitapo (ngakhale kusabala kapena kusoŵa mphamvu zakugonana.) Khalidwe loipa lakale limene mmodzi wa aŵiriwo sakukondwera nalo lochitidwa ukwati usanachitike silingakhale chifukwa cha m’Malemba chothetsera ukwati, monga momwe zingakhalire ngati mkaziyo anatenga matenda kapena ankabisa mimba ya mwamuna wina pokwatirana. Tsopano ndi okwatirana ndipo ndi odzipereka kwa wina ndi mnzake.

N’zoona kuti zochitika ngati zimenezi n’zakamodzikamodzi, koma zitsanzo zimenezi zikugogomezera mfundo yaikuluyo yakuti: Pangano la ukwati siliyenera kuonedwa mopepuka. Akristu afunikira kuyesetsa kudziŵana bwino lomwe asanalowe m’pangano la ukwati kapena pambuyo pake. Ayenera kukhala oona mtima pa zimene winayo akufuna kudziŵa kapena zimene ayenera kudziŵa. (M’mayiko ena, aŵiri opalana chibwenzi amayenera kupimitsa kuchipatala. Ena angafune kupimitsa kuti angodziŵa basi.) Motero, kusangalatsa ndi kulemekezeka kwa chitomero kudzathandiza kwambiri pamene aŵiriwo akuyandikira ukwati umene uli wosangalatsa ndi wolemekezeka kwambiri.​—Miyambo 5:18, 19; Aefeso 5:33.

[Mawu a M’munsi]

a M’madera ena, makolo ndiwo amapangabe mapangano a ukwati a ana awo. Zimenezi zingachitike aŵiriwo asanafike pa misinkhu yoti n’kukwatirana. Panthaŵiyi, anawo amaonedwa kukhala otomerana, kapena olonjezedwa kukwatirana, koma sindiko kuti akwatirana.

b Onani buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza, mitu 28-32, ndi buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, mutu 2, ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena