Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 10/1 tsamba 30-31
  • Sunemu—Wodziŵika ndi Chikondi ndi Chiwawa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sunemu—Wodziŵika ndi Chikondi ndi Chiwawa
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhondo Ziŵiri Zofunika
  • Gidiyoni Anagonjetsa Amidiyani
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Gideon ndi Amuna Ake 300
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • “Nyamula Mwana Wako”
    Nsanja ya Olonda—2010
  • “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni”
    Nsanja ya Olonda—2005
Nsanja ya Olonda—1997
w97 10/1 tsamba 30-31

Sunemu​—Wodziŵika ndi Chikondi ndi Chiwawa

KUMMWERA kwa Galileya, kumalire a kummaŵa a dambo la Yezreeli, kunali mzinda wa Sunemu. Ziŵiri mwa nkhondo zazikulu za m’mbiri ya Baibulo zinachitikira mumzinda umenewu, komanso unali kudziŵika monga kumene kunabadwira akazi aŵiri amene anapereka chitsanzo cha chikondi chokhulupirika.

Kuseri kwa Sunemu kunali phiri lomwe amaliganizira kukhala More, pamenenso kudutsa dambo limenelo, makilomita ngati asanu ndi atatu, kunali Phiri la Giliboa. Pakati pa mapiri aŵiri amenewo panali mtunda wa madzi ambiri ndi wa zipatso zambiri​—chimodzi mwa zigawo zotulutsa zakudya zambiri koposa za Israyeli.

Malo obiriŵira ameneŵa ozungulira Sunemu ndi kumene kunachitikira imodzi mwa nkhani zachikondi zochititsa chidwi koposa zomwe zasimbidwapo​—Nyimbo ya Solomo. Nyimbo imeneyi imasimba za msungwana wokongola wapafupi ndi mudzi umenewu amene anakonda kukwatiwa ndi mbusa mnzake kuposa kuvomera Mfumu Solomo kuti akhale mmodzi wa akazi ake. Solomo anagwiritsira ntchito nzeru zake zonse ndi chuma chake chonse kuti amkope mtima. Mobwerezabwereza, anamtamanda kuti: “Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha, wokongola ngati mwezi, woyera ngati dzuŵa?” Ndipo anamlonjeza kumpatsa miyala yonse ya mtengo wapatali imene angaganizire.​—Nyimbo ya Solomo 1:11; 6:10.

Kuti amlaŵitse moyo wachifumu, Solomo anampempha kupita naye ku Yerusalemu monga mmodzi wa omperekeza ake, atatsagana ndi asilikali 60 mwa asilikali ake abwino kwambiri. (Nyimbo ya Solomo 3:6-11) Anamuika m’nyumba yake yachifumu, nyumba yokongola kwabasi moti pamene mfumu yaikazi ya ku Seba anaiona, “anakhululuka malungo.”​—1 Mafumu 10:4, 5.

Koma msungwana wa ku Sunemu anali wokhulupirika kwa mbusa mnyamatayo. “Ngati maula pakati pa mitengo ya m’nkhalango,” iye anatero “momwemo wokondedwa wanga.” (Nyimbo ya Solomo 2:3) Ngakhale kuti Solomo anali ndi minda yake ya mpesa chikwi, munda wa mpesa umodzi​—pamodzi ndi wokondedwa wake​—unamkwanira msungwanayo. Chikondi chake sichinagwedezeke.​—Nyimbo ya Solomo 8:11, 12.

Ku Sunemu kunkakhalanso mkazi wina wokongola. Palibe chimene tidziŵa ponena za kaonekedwe kake kakuthupi, koma ndithudi anali wokongola mumtima. Baibulo limati ‘anadzimana’​—kapena kuti anayesetsa​—kuti nthaŵi zonse azipatsa mneneri Elisa chakudya ndi malo okhala.​—2 Mafumu 4:8-13.

Titha kuona Elisa atayenda ulendo wautali ndi wotopetsa, akubwerera moyamikira ku kachipinda kosanja kamene mkaziyu ndi mwamuna wake anammangira. Ayenera kuti nthaŵi zambiri ankapita kunyumba kwawo, popeza utumiki wake unatha zaka 60. Kodi nchifukwa ninji mkazi wa ku Sunemu ameneyu analimbikira kuti Elisa azikhala panyumba pawo nthaŵi zonse akadzera njira imeneyo? Chifukwa anaona ntchito ya Elisa kukhala yofunika kwambiri. Mneneri wodzichepetsa ndi wodzimana ameneyu anali ngati chikumbumtima cha mtunduwo, namakumbutsa mafumu, ansembe, ndi anthu wamba za udindo wawo wotumikira Yehova.

Mosakayikira mkazi wa ku Sunemu ndi mmodzi wa anthu amene Yesu ankaganizira ponena kuti: “Iye wakulandira mneneri, padzina la mneneri, adzalandira mphotho ya mneneri.” (Mateyu 10:41) Yehova anapatsa mkazi woopa Mulungu ameneyu mphotho yapadera. Ngakhale anali wosabala kwa zaka zambiri, iye anabala mwana wamwamuna. Zaka zambiri pambuyo pake Mulungu anamthandizanso pamene njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri inasakaza dzikolo. Nkhani yokhudza mtima imeneyi imatikumbutsa kuti Atate wathu wakumwamba amaona kukoma mtima konse kumene timasonyeza atumiki a Mulungu.​—2 Mafumu 4:13-37; 8:1-6; Ahebri 6:10.

Nkhondo Ziŵiri Zofunika

Ngakhale kuti Sunemu amakumbukidwa monga kwawo kwa akazi aŵiri okhulupirika ameneŵa, mudziwo unaonanso nkhondo ziŵiri zimene zinasintha mbiri ya Israyeli. Pafupi nawo panali bwalo lankhondo labwino​—chigwa cha pakati pa mapiri a More ndi Giliboa. M’nthaŵi za Baibulo, akazembe ankhondo nthaŵi zonse ankamanga misasa pamalo pamene pali madzi ambiri, chitunda kaamba ka chitetezo, ndipo, ngati nkotheka, malo a pamtunda amene kumunsi kwake kuli chigwa chouma chotakasuka bwino moti magulu a anthu, akavalo, ndi magaleta atha kumayenda bwino. Sunemu ndi Giliboa anali malo otere.

M’nthaŵi ya oweruza, gulu lankhondo la asilikali 135,000 la Amidyani, Aamaleki, ndi ena linamanga misasa m’chigwa cha kutsogolo kwa More. Ngamila zawo zinali “ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” (Oweruza 7:12) Amene anayang’anizana nawo tsidya linalo la chigwacho, pafupi ndi chitsime cha Harodi munsi mwa Phiri la Giliboa, anali Aisrayeli otsogoleredwa ndi Woweruza Gideoni, amene anali ndi asilikali 32,000 okha.

Pamasikuwo nkhondo isanachitike, gulu lililonse linkayesa kuopsa linalo. Magulu a asilikali olankhula mitonzo, ngamila zankhondo, magaleta, ndi akavalo zinali zoopsa kwa asilikali oyenda pansi. Mosakayika konse, Amidyani​—amene anali okonzeka kale pamene Aisrayeli anayamba kusonkhana​—anali oopsa powaona. Pamene Gideoni anafunsa kuti, “Kodi pali amene akuchita mantha ndi kunjenjemera?” zigawo ziŵiri mwa zitatu za gulu lake lankhondo zinayankha mwa kuchoka ku bwalo lankhondolo.​—Oweruza 7:1-3, NW.

Asilikali 10,000 okha achiisrayeli tsopano ndiwo anali kuyang’ana tsidya linalo la chigwacho kuona asilikali 135,000 a adani, ndipo posapita nthaŵi Yehova anachepetsa chiŵerengero cha asilikali achiisrayeli kukhala 300 okha basi. Mwa mwambo wachiisrayeli, gulu laling’ono limeneli linagaŵidwa kukhala magulu atatu. Mumdima, anamwazikana naima kumbali zitatu za misasa ya adani awo. Kenako Gideoni atawalamula, 300 amenewo anaphwanya mbiya zimene zinali zitabisa miunizo, kutukula miuniyo, ndi kukuwa kuti, “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.” Anaomba malipenga awo nawaombabe. Mumdimawo, khamu losokonezeka la asilikali osanganikana linaganiza kuti magulu 300 awathira nkhondo. Yehova anachititsa kuti akanthane, ndipo “anathamanga a m’misasa onse, nafuula, nathaŵa.”​—Oweruza 7:15-22; 8:10.

Nkhondo yachiŵiri inachitika pafupi ndi Sunemu m’nthaŵi ya Mfumu Sauli. Baibulo limasimba kuti “Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Sauli anasonkhanitsa Aisrayeli onse, namanga iwo ku Giliboa,” monga momwe gulu lankhondo la Gideoni linachitira zaka zambiri kumbuyoko. Koma Sauli, mosiyana ndi Gideoni, analibe chikhulupiriro mwa Yehova, nasankha kufunsira kwa wobwebweta ku Endori. Ataona khamu la Afilisti, “anaopa, ndi mtima wake unanjenjemera kwakukulu.” M’nkhondo imene inatsatira, Aisrayeli anathaŵa ndipo anakanthidwa koopsa. Onse aŵiri Sauli ndi Yonatani anataya miyoyo yawo.​—1 Samueli 28:4-7; 31:1-6.

Ndimo mmene zinakhalira kuti mbiri ya Sunemu inadziŵika ndi zonse ziŵiri chikondi ndi chiwawa, kukhulupirira Yehova ndi kudalira ziŵanda. M’chigwa chimenechi, akazi aŵiri anasonyeza chikondi cholimba ndi kuchereza alendo kosatha, ndipo atsogoleri aŵiri a Israyeli anamenya nkhondo zofunika. Zitsanzo zonse zinayi zimasonyeza kufunika kwa kudalira Yehova, amene samalephera kufupa awo omtumikira.

[Chithunzi patsamba 31]

Mudzi wamakono wa Sulam pamalo pamene panali Sunemu wakale, ndipo phiri la More likuoneka kumbuyoko

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena