Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 4/8 tsamba 16-17
  • Kodi Tiyenera Kukwaniritsa Zoŵinda Zathu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tiyenera Kukwaniritsa Zoŵinda Zathu?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zifukwa Zosayenera Nzosafunika
  • Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino
  • Zoŵinda Zolakwa ndi Zotsutsa Malemba
  • Pendani Zoŵinda Zanu Zakale ndi Zamtsogolo
  • Muzikwaniritsa Zimene Mwalonjeza
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Uzikwaniritsa Zinthu Zimene Walonjeza”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Anthu Okhulupirika kwa Yehova Amakwaniritsa Zimene Alonjeza
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 4/8 tsamba 16-17

Lingaliro la Baibulo

Kodi Tiyenera Kukwaniritsa Zoŵinda Zathu?

OKWATIRANA mwachimwemwe aŵiri akuyang’anizana ndi vuto losautsa. Zaka zapitazo, pamene anali ndi chothetsa nzeru chachikulu m’banja, anaŵinda kupereka kwa Mulungu gawo lachikhumi la ndalama zimene anapeza ngati iye akawawonjola m’mavuto awo. Tsopano, pamene akalamba ndipo agwera m’mavuto andalama amene sanayembekezere, akuzizwa, “Kodi tili okakamizika kukwaniritsa choŵinda chimenechi?”

Vuto lawo likugogomezera uphungu wa mwamuna wanzeru wochenjeza za kusafulumira kukamba: “Kusaŵinda kupambana kuŵinda osachita. Usalole m’kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya.”—Mlaliki 5:5, 6.

Zifukwa Zosayenera Nzosafunika

Ngakhale kuti malumbiro osasamala ndi malonjezo achinyengo ndizo mkhalidwe wa chitaganya chamakono cholekerera zinthu, sitiyenera kuganiza kuti Mulungu adzakhulupirira zifukwa zosayenera zodzikhululukira; angakhale amalonda amadziŵa zimenezo bwino lomwe. Nkhani yakuti “Kukhulupirika m’Malonda: Kodi Nkupusitsa Chabe?” ya m’magazini yamalonda ya Industry Week inadandaula kuti: “ Sitimakhulupiriranso kuti anthu anganene zowona, kuti angachite cholondola m’malo mwakufuna phindu chabe, kuti angakwaniritse malonjezo awo.” Ngakhale kuti mabodza olungamitsidwa, monga lakuti “tinakutumizirani kale cheke,” angapulumutse okongoletsa aumunthu, angelo sanganyengedwe konse.

Sitikunena kuti Mulungu amagwiritsira ntchito angelo kuwona kuti zoŵinda zakwaniritsidwa monga momwe amachitira munthu wokongoletsa wofuna kubwezeredwa chiwongola dzanja chopambanitsa amene angagwiritsire ntchito zigaŵenga kukawopseza omkongola ake okhala m’mavutowo kuti alipire ndalama zochuluka. Mmalomwake, Mulungu mwachikondi amachititsa angelo ake kukhala “mizimu yotumikira [kulimbikitsa anthu], yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzaloŵa chipulumutso.” (Ahebri 1:14) Motero, angelo akhoza ndipo amaloŵetsedwamo m’kuyankhidwa kwa mapemphero athu owona mtima.

Komabe, ngati tipitiriza kupanga malonjezo opanda pake m’mapemphero athu, kodi tingakhale oyenera kuyembekezera madalitso a Mulungu? Munthu wanzeru akuti: “Mulungu akwiire mawu ako chifukwa ninji, nawononge [pamlingo winawake] ntchito ya manja ako?”—Mlaliki 5:6b.

Chotero, kuwopa angelo olipsira sikumene kuyenera kutipangitsa kukwaniritsa zoŵinda zathu ndi kupeŵa kupereka zifukwa zodzikhululukira. Mmalomwake, tiyenera kulemekeza unansi wathu ndi Mulungu ndi kukhumba mowona mtima chiyanjo cha Mulungu pa ntchito yathu. Zili monga momwe okwatirana otchulidwa poyambapo ananenera bwino lomwe kuti: “Tifuna kukhala ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu ndi kuchita mogwirizana ndi chifuniro chake.”

Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino

Kuti tikhale ndi chikumbumtima choyera ponena za kukwaniritsa choŵinda, tiyenera kukhala owona mtima kwa ife eni. Nachi chitsanzo: Tinene kuti munthu wina anali nanu ngongole ya ndalama zambiri, koma chifukwa cha tsoka limene lamgwera alephera kukubwezerani. Kodi nchiti chimene mukanakonda—kuti angonyalanyaza zakukulipirani ngongole yonseyo chifukwa awona kuti nkosatheka kapena kuti alinganize kumakulipirani pang’onopang’ono malinga ndi mmene angakhozere?

Mwalingaliro lofananalo, bwanji ngati talephera kukwaniritsa choŵinda chopangidwa mofulumira cha kupereka nthaŵi yonse kapena zinthu zina ku ntchito Zachikristu. Kodi sitiyenera kudzimva kukhala ndi thayo lakuyesayesa kukwaniritsa choŵinda chathu malinga ndi mmene mikhalidwe yapanthaŵiyo ingalolere? “Ngati chivomerezocho chili pomwepo,” analemba motero Paulo, “munthu alandiridwa monga momwe ali nacho” kaya tili ndi zambiri zozipereka kapena zochepa. (2 Akorinto 8:12) Koma bwanji ponena za zoŵinda zopangidwa pamene munthu asanakhale ndi chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi cha Baibulo?

Zoŵinda Zolakwa ndi Zotsutsa Malemba

Ngati tadziŵa kuti choŵinda nchonyansa kapena nchosayenera, tiyenera kuchitaya monga khala lamoto! (2 Akorinto 6:16-18) Nazi zitsanzo za zoŵinda zonyansa:

◻ Zoŵinda zopangidwa kwa milungu yonama kapena milungu yachikazi, monga ngati “mfumu yaikazi yakumwamba” Yachibabulo.—Yeremiya 44:23, 25.

◻ Zoŵinda zotsutsa lamulo, monga lumbiro la amuna 40 amene anakana kulaŵa chakudya kufikira atapha mtumwi Paulo.—Machitidwe 23:13, 14.

◻ Zoŵinda zampatuko zimene zimatsatira “maphunziro a ziŵanda . . . a iwo onena mabodza, . . . akuletsa ukwati, osiitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira chowonadi azilandire ndi chiyamiko.”—1 Timoteo 4:1-4.

Chotero, mwachiwonekere tiyenera kukana zoŵinda zina zakale. Koma ponena za zoŵinda zimene sizimaloŵetsamo chilichonse chotsutsa malemba, nkufuniranji pozembera? Kodi chidziŵitso chathu cholongosoka chimene tili nacho tsopano sichiyenera kutipangitsa kusonyeza ulemu waukulu kuposa ndi kalelonse pa zoŵinda zakale?

Pendani Zoŵinda Zanu Zakale ndi Zamtsogolo

Chotero tiyeneranso kulingalira mwamphamvu tisanawonjezere zoŵinda zamtsogolo zilizonse pa kulambira kwathu. Zoŵinda siziyenera kugwiritsiridwa ntchito monga chabe chosonkhezerera munthu kuchita kapena kupeŵa kuchita kanthu kena, monga ngati kuwonjezera nthaŵi yake m’kulambira Kwachikristu kapena kuleka kudya mopambanitsa. Komabe, Yesu sanatsutse malumbiro onse, monga, mwachitsanzo, pamene tikufunika m’khoti. Koma iye mwachiwonekere anaika malire ponena za malumbiro osasamala, pakuti anachenjeza kuti: “Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama, koma udzapereka kwa [Yehova, NW] zolumbira zako: koma ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse.” (Mateyu 5:33, 34) Kodi nchifukwa ninji iye ananena zimenezi? Kodi zoŵinda zinakhala zosayenera, mosiyana ndi kalelo?

Malumbiro a anthu okhulupirika a m’nthaŵi zakale kaŵirikaŵiri anali odalira pakanthu kena. M’mapemphero ofunika kwambiri iwo anali kumalonjeza Yehova kuti, ‘Ngati mundithandiza m’vuto ili, ndidzakuchitirani chakutichakuti.’ Koma Yesu anati: “Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa.” Mosachilikiza konse zoŵinda zodalira pakanthu kena kwa okhulupirika a m’nthaŵi yake, Yesu anawatsimikiziritsa kuti: “Kufikira tsopano simunapempha kanthu m’dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira.”—Yohane 16:23, 24.

Chidaliro chimenechi m’dzinalo, kapena malo antchito a Yesu, chiyenera kutonthozanso aliyense amene akumvabe kukhala waliwongo chifukwa—ngakhale ngati angayesetse motani—satha kukwaniritsa chimene analonjeza Mulungu “ndi milomo yake osalingilira.” (Levitiko 5:4-6) Chotero, pamene kuli kwakuti sitikupeputsa zoŵinda zathu zakale, sikupemphera mwa dzina la Yesu kokha kumene tingachite komanso tingachonderere kwa Mulungu kugwiritsira ntchito nsembe ya Yesu ya dipo pamachimo athu, ndipo tikhoza kupempha chikhululukiro m’dzina la Yesu. Chotero tikhoza kulandira “chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu [kuyeretsedwa ku] chikumbumtima choipa.”—Ahebri 10:21, 22.

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

Ansembe akuŵinda ku Montmartre

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena