Chisudzulo—Kodi Nchiyani Chimene Baibulo Limanena Kwenikweni?
“CHIMENE Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mateyu 19:6) Kaŵirikaŵiri timamva mawu odziŵika amenewa a Yesu Kristu akugwidwa mawu monga chilengezo chomalizira m’phwando laukwati.
Ndi mawu amenewo, ngakhale kuli tero, kodi Yesu anatanthauza kuti maukwati onse ayenera kukhala okhazikika kotheratu ndipo kuti sipayeneranso kukhala kusudzulana kwa mtundu uliwonse? Mwakumawatenga mawuwo mwa iwo okha, chimenecho chingawonekere kukhala tero. Komabe, nchiyani chimene chinafulumiza Yesu kupanga ndemanga yoteroyo? Kodi iye anali kukhazikitsa chinachake chatsopano?
‘Sinali Nkhani Kuyambira Pachiyambi’
Ganizo la Yesu logwidwa mawu pamwambapa linali mbali ya yankho lake ku funso la Afarisi: “Kodi kuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chirichonse?” (Mateyu 19:3-6) Osakhutiritsidwa ndi yankholo, Afarisiwo anamfunsa iye mowonjezereka mwakufunsa kuti: “Nanga nchifukwa ninji Mose analamulira kupatsa kalata wa chilekaniro ndi kumchotsa?” Pamenepo, Yesu anati: “Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.” Kenaka iye anawonjezera: “Ndipo ine ndinena kwa inu, amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha [dama, NW] nadzakwatira wina, achita chigololo.”—Mateyu 19:7-9.
Tiyenera kudziŵa kuti ndemanga ya Yesu, “koma pachiyambi sikunakhala chomwecho,” linapangidwa m’kulozera ku chisudzulo chomwe chinakwaniritsidwa mwa “kupereka kalata ya chilekaniro.” M’mawu ena, pamene Mulungu anakhazikitsa ukwati woyamba pakati pa Adamu ndi Hava, iye sanapereke kwa iwo “mtundu uliwonse wa maziko” kaamba ka kuthetsa ukwati wawo. Monga okwatirana angwiro, iwo anali ndi chifukwa chirichonse cha kupangira ukwati wawo kukhala wachipambano. Iwo ukakhala wachipambano ngati akapitiriza kukhala mogwirizana ndi lamulo ndi chitsogozo cha Mulungu.
Pamene mtundu wa anthu unagwera m’chimo ndi kupanda ungwiro, kanateronso kakhazikitsidwe ka ukwati. (Aroma 5:12) Popeza kuti anthu sanalinso angwiro, maunansi a anthu anakhala okwinjika ndi kudetsedwa ndi kudzikonda, umbombo, ndi chikondwerero chaumwini. Chimenechi ndi chimene Yesu analozerako monga “kuuma mtima,” chifukwa cha kumene Lamulo la Mose linapanga malo kaamba ka chisudzulo. Komabe, Yesu anawakumbutsa Afarisi kuti: “Koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.” Tsopano, pansi pa mikhalidwe yopanda ungwiro, okwatirana ayenera kuika kuyesetsa kulikonse kofunikira kuthetsa zovuta zirizonse ndi mavuto m’malo mwa kuwagwiritsira ntchito iwo monga maziko kapena chodzikhululukira cha kuthetsera ukwati wawo. Komabe, Yesu analoza kuti pali chopatulidwa chimodzi, chotchedwa kuti, dama. Kusakhulupirika kwa m’banja kungakhale maziko akuthetsera ukwati.
Chiri chosangalatsa kudziŵa mmene kalongosoledwe kosiyanasiyana ka mawu akuti “kokha chifukwa cha [dama, NW]” kaikidwira m’kusungilira kawonedwe kena pa chisudzulo. Maulamuliro a Chikatolika mwachisawawa amachotsa mawu amenewo pamaziko akuti nkhani zofanana nazo mu Marko ndi Luka ziribe mawu amenewo. Komabe, Cyclopedia ya McClintock ndi Strong ikulongosola kuti: “Kugwirizana kowonekeratu kwa ndimezo kuyenera kupezedwa m’lamulo lakuti kusiyana m’kalembedwe kotheratu kuyenera kulongosola kwachidule, ngati ichi chingachitidwe popanda kukakamiza. Tsopano, popeza chisudzulo kaamba ka chifukwa chimodzi chimenecho chinali kuvomerezedwa ndi onse, Marko ndi Luka mwachibadwa angakhale anachitenga ichi kukhala chodziŵikiratu popanda kuchilongosola icho.”
Ena amatsutsa kuti popeza Yesu anagwiritsira ntchito liwu lakuti “dama” (Greek, por·neiʹa) ndipo osati “chigololo” (Greek, moi·kheiʹa), iye ayenera kukhala anatanthauza kachitidwe kosayenera ukwati usanakhale komwe kangapange ukwati kukhala wopanda lamulo ndipo wopanda kanthu. Uku ndi kuika malire kosayenera ku tanthauzo la liwulo. Maulamuliro osiyanasiyana amazindikira kuti por·neiʹa limatanthauza “kupanda chiyero, kuchita chigololo, uhule, dama,” ndipo kuti pa Mateyu 19:9 “limaimira, kapena kuphatikiza, chigololo.” Ena amatsutsa kuti Yesu anali kugwira mawu dama kokha monga chitsanzo chimodzi pakati pa maziko ambiri kaamba ka chisudzulo. Mwachimvekere, uku kuli kukakamiza lingaliro pa lembalo.
Kuchokera ku zokambitsiridwazi, chiri chomvekera kuti Baibulo silimanena kuti maukwati onse ayenera kukhala kwa nthaŵi yosatha ndipo kuti chisudzulo sichiri chovomerezeka kaamba ka chifukwa china chirichonse. Kumbali ina, Baibulo limapereka kokha maziko amodzi ovomerezeka kaamba ka chisudzulo, otchedwa, “maziko a dama.”
“Ukwati Uchitidwe Ulemu”
Mwakulola maziko kaamba ka chisudzulo, kodi Baibulo limalimbikitsa icho? Kodi chivomerezo chimenechi chimachepetsa ukwati kapena kuchilanda icho ulemu wake? Kapena kodi mwakuvomereza maziko amodzi okha kaamba ka chisudzulo, kodi Baibulo likuika thayo losayenerera pa awo omwe akwatira?
Mosiyana kotheratu, Baibulo limalankhula za ukwati monga chimodzi cha zomangira zapafupi kwambiri ndipo zathithithi zimene anthu aŵiri angasangalale nazo. “Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo adzakhala thupi limodzi,” imatero mbiri ya Genesis pa ukwati woyambirira. (Genesis 2:24) Ndipo okwatirana ayenera kuchinjiriza unansi umenewo wa “thupi limodzi” monga chinachake cha mtengo wapatali. “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa,” limachenjeza tero Baibulo.—Ahebri 13:4.
Chanenedwa kaŵirikaŵiri, m’njira imodzi kapena ina, kuti maziko aukwati wokhalitsa ndi wachimwemwe si chikondi cha kuthupi koma kupanda dyera. Chimenecho ndicho chokha chimene Baibulo limasonyeza. Ilo limati: “Koteronso amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha, pakuti munthu sadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu Eklesia . . . ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziwopa mwamuna.” (Aefeso 5:28-33) Ndipo m’chinenero chosabisa mawu, Baibulo likuchenjeza kuti: “Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake, koma chimodzimodzinso mkazi kwa mwamuna. Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye. Musakanizana.”—1 Akorinto 7:3-5.
Pamene okwatirana onse aŵiri ali ofunitsitsa kumamatira ku uphungu wanzeru umenewu, chiri chosalingalirika kuti ukwati wawo udzanyonyotsoka ku nsonga yakuti mmodzi wa iwo adzakhoterera ku mayanjano a kugonana kunja kwa ukwati, chotero, m’chenicheni, kuwononga unansi wa “thupi limodzi.” Ngakhale ngati mmodzi wa okwatiranawo salandira malamulo a Baibulo amenewo, wokwatira wokhulupirirayo angakhale ndi chidaliro chakuti njira ya Mulungu idakali yabwino koposa, ndipo mavuto ambiri a mu ukwati angathetsedwe kapena kupewedwa.
M’malo mwa kuyamikira chisudzulo monga njira ya kuthetsera ukwati wopanda chimwemwe, chotero, Baibulo likufulumiza Akristu kugwira ntchito zolimba kusungilira ukwati wawo pamodzi ndi kupanga iwo kukhala wachimwemwe. “Ukondwere ndi mkazi wokula naye,” umatero mwambo wa Baibulo. “Ukondwe ndi chikondi chake osaleka.”—Miyambo 5:18, 19.
Kodi Kusudzulana kuli Yankho?
Bwanji ngati mnzake wa mu ukwati wa wina akhala wosakhulupirika? Kukhala wotsimikizira, kusakhulupirika kwa mu ukwati kumabweretsa tsoka lalikulu. Wokwatirana wa chigololoyo wabweretsa kupweteka ndi kuvutika kokulira pa mnzake wopanda liwongoyo, yemwe ali ndi kuyenera kwa m’Malemba kwa kusudzula mbali yolakwayo ndi kukwatiranso. Koma kodi iwo ayenera kusudzulana? Kodi imeneyo ndiyo njira yokha yomwe iripo?
Tiyenera kusunga m’maganizo kuti ngakhale kuti Yehova Mulungu wapereka chifukwa cholungama kaamba ka chisudzulo, Baibulo limanenanso za iye: “Adana nako kulekana.” (Malaki 2:16) M’malo mwa kulumphira mwamsanga kumapeto akuti chisudzulo chiri yankho lokha, wina angalingalire kuthekera kwa kusonyeza chifundo ndi chikhululukiro. Nchifukwa ninji?
Chisudzulo moyenerera sichidzachotsa kupwetekedwa ndi kuwaŵidwa, koma chifundo ndi kukhululukira chidzatero, makamaka pamene wolakwayo mowonadi alapa ku cholakwacho. Chikondi chosonyezedwa panthaŵi yovuta imeneyi m’chenicheni chingalimbikitse ukwati. Kuwona nkhaniyo m’chiwunikiro chimenechi kudzathandiza wina wopanda liwongoyo kukulitsa imene ingakhale njira yabwino koposa kuitsatira, akumakumbukira mawu a Yesu: “Wodala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo.”—Mateyu 5:7; yerekezani ndi Hoseya 3:1-5.
Ndiponso ofunika kuyesera pamlingo ali mavuto amene angatulukepo m’chigwirizano ndi ana m’nyumba ya kholo limodzi. Kusungulumwa kwa munthu wosudzulidwayo, nakonso, kumayenera kulingaliridwa. Kwa mkazi, mavutowo amakulitsidwa ndi chenicheni chakuti m’mbali zambiri zadziko lerolino, akazi adakali opanda mwaŵi mwa zachuma. Pambuyo pa kukhala wosunga nyumba kwa unyinji wa zaka, chiri chovuta kwa mayi mmodzi kupitanso ku ntchito ndi kupikisana ndi ena.
Akazi ena amamva kuti pamene iwo ali okwatiwa, iwo ayenera kudzikonzekeretsa iwo eni kaamba ka kuthekera kwa kusudzulana. Iwo angalembetse m’masukulu apadera kapena kusungabe ntchito zawo ndi cholinga chofuna kusungilira kudziimira kwawo pawokha mwa zachuma. Kaya munthu adzafunikira kulondola njira imeneyo kapena ayi chiri chosankha chaumwini. Komabe, m’malo mwa kuwononga nthaŵi ndi mphamvu kukonzekera kaamba ka kuthekera, kodi sichikakhala chanzeru koposa kusunga pakuika nthaŵi ndi nyonga m’kumangilira ukwati wachimwemwe ndi wosatha? Mwakugwirira ntchito molimbika pa kukulitsa chipatso cha mzimu wa Mulungu ndi kusungilira kawonedwe ka umoyo kauzimu, mkazi Wachikristu mwachidziŵikire angasangalale ndi chikondi ndi chitamando cha mwamuna wake. Iye angakhalenso ndi chidaliro m’lonjezo la Mulungu lakuti iye amasamalira kaamba ka zosowa za awo ofunafuna Ufumu choyamba.—Mateyu 6:33; Miyambo 31:28-30; Agalatiya 5:22, 23.
Yankho Lotheratu
Kufikira kuutali umene tikakhalabe m’dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu lopanda ungwiro, tingayembekezere kuti padzakhala mavuto a mu ukwati. Komabe, mwakutsatira uphungu wanzeru wa Baibulo, izi zingachepetsedwe kapena kugwiriridwapo ntchito mokhutiritsa. M’kuwonjezerapo, amuna ndi akazi omwe ali ofunitsitsa kukhala ndi miyezo ya Yehova mu ukwati ndi m’mbali zina za moyo ali odalitsidwa ndi chiyembekezo cha kulowa m’dongosolo latsopano m’limene “chilungamo chidzakhalitsa.”—2 Petro 3:13.
M’dongosolo limenelo, mtundu wa anthu udzakhala womasuka ku kupasuka ndi zotulukapo zonse zomvetsa chisoni za uchimo ndi kupanda ungwiro. Kufikira ku utali umene makonzedwe aukwati akapitirizabe pano pa dziko lapansi, ‘yomwe inali nkhani kuyambira kuchiyambi’ idzakhala muyezo. Ndithudi, chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu sadzachilekanitsa.
[Chithunzi patsamba 5]
Nchiyani chimene Yesu ananena ponena za chisudzulo?
[Chithunzi patsamba 7]
M’dziko latsopano, sikudzakhala mavuto a banja omwe amatsogolera ku chisudzulo