Mutu 20
Kodi Nthaŵi Zonse Umafuna Kukhala Woyamba?
KODI ukudziŵapo wina aliyense amene nthaŵi zonse amafuna kukhala woyamba?— Mwina amakankha anzake pa mzere kuti iye akhale woyamba. Kodi zoterezi unazionapo zikuchitika?— Mphunzitsi Waluso anaona anthu akuluakulu akulimbirana malo oyamba, kapena kuti malo olemekezeka kwambiri. Iye sanasangalale nazo. Tiye tione zimene zinachitikazo.
Kodi unaonapo anthu akufuna kukhala oyamba?
Baibulo limatiuza kuti Yesu anaitanidwa ku phwando kunyumba ya Mfarisi wina yemwe anali mtsogoleri wachipembedzo wofunika kwambiri. Yesu atafika, anayamba kuonerera alendo enanso akubwera ndi kumasankha malo abwino kwambiri. Ndiyeno iye anafotokozera anthu anaitanidwawo nkhani inayake. Kodi ukufuna ndikuuze nkhani yake?—
Yesu ananena kuti: ‘Pamene munthu wina wakuitana ku phwando la ukwati, usakhale pa mpando wabwino kwambiri, kapena kuti wolemekezeka kwambiri.’ Kodi ukudziŵa chifukwa chake Yesu ananena zimenezi?— Iye anafotokoza kuti munthu wina wolemekezeka kuposa iweyo akhoza kukhala ataitanidwanso. Ndiye monga ukuonera pachithunzichi, amene wakonza phwandoyo akubwera ndi kunena kuti: ‘Uyu akhale pamene wakhala iwepa, iweyo kakhale uko.’ Kodi mlendo ameneyu angamve bwanji?— Angachite manyazi chifukwa alendo ena onse angamuone akukakhala pa mpando wosalemekezeka uja.
Yesu anali kusonyeza kuti si bwino kufuna malo apamwamba kwambiri. Motero anati: ‘Pamene waitanidwa ku phwando la ukwati, pita ukakhale kumapeto. Ndiyeno amene anakuitana iwe adzabwera ndi kukuuza kuti, Bwenzi langa, bwera udzakhale pamalo abwino. Choncho iwe udzalemekezeka pamaso pa alendo ena onse pamene ukukakhala pa mpando wabwino.’—Luka 14:1, 7-11.
Kodi ndi mfundo yotani imene Yesu anaphunzitsa pamene analankhula za amene anakhala pa mipando yabwino?
Kodi mfundo yake ya nkhani ya Yesuyi waimvetsa?— Nachi chitsanzo tione ngati waimvetsa. Tayerekeza kuti ukukwera basi yodzaza. Kodi uyenera kuthamangira kupeza mpando m’basimo koma munthu wachikulire ndi kuimirira?— Kodi Yesu zikhoza kumusangalatsa iwe utachita zimenezo?—
Munthu wina anganene kuti Yesu alibe nazo ntchito zimene timachita. Koma kodi iwe umakhulupirira zimenezo?— Pamene Yesu anali pa phwando lija kunyumba ya Mfarisi, anali kuona anthu akusankha malo oti akhale. Kodi sukuganiza kuti zimene timachita masiku ano amachita nazonso chidwi?— Ndiye poti tsopano Yesu ali kumwamba, iyetu ali pamalo abwino kwambiri pamene angathe kuona zimene tikuchita.
Munthu wina akamafuna kukhala woyamba, zingayambitse mavuto. Nthaŵi zambiri anthu amakangana ndipo amakwiya. Zoterezi zikhoza kuchitika pamene munthu wina akufuna kupatsa ana masuwiti. Akangowauza kuti bwerani kuno ndikupatseni masuwiti, aliyense amathamangira kuti akakhale woyamba kulandira. Ndiyeno chingachitike ndi chiyani?— Eya, akhoza kuyamba kukangana.
Kufuna kukhala woyamba kungabweretse mavuto ambiri. Ngakhale atumwi ake a Yesu anapeza nako mavuto. Monga tinaphunzirira m’Mutu 6 wa buku lino, iwo anakangana kuti anali wamkulu ndani. Kodi Yesu anachitapo chiyani?— Inde, anawathandiza. Koma anakangananso. Tiye tione mmene zinayambira.
Atumwiwo, limodzi ndi anthu ena, anali paulendo wopita ku mudzi wa Yerusalemu kwanthaŵi yomaliza ali ndi Yesu. Yesu anali atawafotokozera za Ufumu wake, motero Yakobo ndi Yohane anakhala akuganizaganiza zolamulira limodzi naye monga mafumu. Mpaka iwo anafika pouza amayi awo, Salome, nkhaniyi. (Mateyu 27:56; Marko 15:40) Ndiye pamene anali kupita ku Yerusalemu, Salome anafika kwa Yesu ndi kugwada, kenako ndi kumupempha iye.
Yesu anamufunsa kuti: “Ufuna chiyani?” Iye anati akufuna kuti Yesu akayandikane ndi ana ake mu Ufumu wake, wina akakhale kudzanja lake lamanja ndi wina ku lamanzere. Ndiye pamene atumwi teni ena aja anadziŵa zimene Yakobo ndi Yohane anauza amayi awo kuti apemphe, kodi ukuganiza kuti iwo anamva bwanji?—
Kodi Salome akupempha chiyani kwa Yesu, ndipo kenako ndi chiyani chikuchitika?
Eya, iwo anakwiya kwambiri ndi Yakobo ndi Yohane. Motero Yesu anapatsa atumwi ake onse malangizo anzeru. Yesu anawauza kuti olamulira a dzikoli amasangalala kwambiri akamaoneka amphamvu ndi ofunika. Amafuna kukhala ndi malo apamwamba oti aliyense aziwamvera. Koma Yesu anauza ophunzira ake kuti iwo safunika kukhala otero. M’malo mwake, Yesu ananena kuti: ‘Aliyense amene akufuna kukhala woyamba mwa inu ayenera kukhala kapolo wanu.’ Waona nkhani ija tsopano!—Mateyu 20:20-28.
Kodi umadziŵa zimene kapolo amachita?— Amatumikira anthu ena, ndipo sayembekeza ena kumutumikira. Amakhala pamalo akumapeto, osati pamalo oyamba. Akamachita zinthu amachita mosonyeza kuti ndi munthu wosafunika pa onse, osati monga wofunika kwambiri. Ndipo kumbukira kuti Yesu ananena kuti amene akufuna kukhala woyamba ayenera kuchitira ena zinthu monga mmene kapolo amachitira.
Kodi ukuganiza kuti zimenezi zikutanthauza chiyani kwa ife?— Kodi kapolo akhoza kukangana ndi mbuye wake kuti ndani akhale pa mpando wabwino kwambiri? Kapena kodi akhoza kukangana naye kuti ndani ayambe kudya? Iwe ukuganiza bwanji?— Yesu analongosola kuti nthaŵi zonse kapolo amaona mbuye wake kukhala wofunika kuposa iye.—Luka 17:7-10.
Ndiye m’malo mofuna kukhala woyamba, kodi tiyenera kuchita chiyani?— Eya, tiyenera kukhala monga kapolo wa anthu ena. Zimenezi zikutanthauza kuti tiziika anthu ena patsogolo pathu. Zikutanthauza kuti tiziona anthu ena kukhala ofunika kwambiri kuposa ifeyo. Kodi ungaganizire njira zimene ungaikire anthu ena pamalo oyamba?— Tatsegula pa masamba 40 ndi 41 ndipo onanso njira zina zimene ungaikire ena pamalo oyamba mwa kuwatumikira.
Ndikhulupirira ukukumbukira kuti Mphunzitsi Waluso anaika ena patsogolo mwa kuwatumikira. Ulendo womaliza umene anali ndi atumwi ake madzulo, anagwada ndi kuwasambitsa mapazi. Ngati ifenso tiika anthu ena patsogolo pathu mwa kuwatumikira, tidzasangalatsa Mphunzitsi Waluso komanso Atate ake, Yehova Mulungu.
Tiye tiŵerenge malemba enanso m’Baibulo amene amatilimbikitsa kuti tiziona anthu ena kukhala ofunika kuposa ife: Luka 9:48; Aroma 12:3; ndi Afilipi 2:3, 4.