Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 6/1 tsamba 12-17
  • Chinsinsi Chimene Akristu Sayenera Kusunga!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chinsinsi Chimene Akristu Sayenera Kusunga!
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Chinsinsi Chopatulika” Chidziŵika
  • Ena Ayenera Kuuzidwa Chinsinsi Chomwe Chavumbulidwa!
  • Kumkoŵa Satana m’Chibwano ndi Zokoŵera
  • Koposa ndi Kalelonse!
  • Chinsinsi Chimene Ufunika Kuuzako Ena
    Nsanja ya Olonda—2010
  • ‘Nzeru ya Mulungu Imaonekera mu Chinsinsi Chopatulika’
    Yandikirani Yehova
  • Chinsinsi Chopatulika Chivumbuluka
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Chinsinsi Chimene Tonsefe Timafuna Titachidziwa
    Phunzitsani Ana Anu
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 6/1 tsamba 12-17

Chinsinsi Chimene Akristu Sayenera Kusunga!

“Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi. . . . Mobisika sindinalankhula kanthu.”​—YOHANE 18:20.

1, 2. Kodi tanthauzo la liwu lachigiriki lakuti my·steʹri·on malinga ndi Malemba nlotani?

LIWU lachigiriki lakuti my·steʹri·on latembenuzidwa nthaŵi 25 kuti “chinsinsi chopatulika” ndi nthaŵi zitatu kuti “chinsinsi” mu New World Translation of the Holy Scriptures. Chinsinsi chotchedwa chopatulika chiyeneradi kukhala chofunika kwambiri! Aliyense wopatsidwa mwaŵi wodziŵa chinsinsi chimenecho ayenera kudzimva wolemekezeka kwambiri, pakuti wayesedwa woyenera kudziŵa chinsinsi chimenenso Mulungu Wam’mwambamwamba wa chilengedwe chonse akudziŵa.

2 Buku la Vine lakuti Expository Dictionary of Old and New Testament Words limatsimikiza kuti nthaŵi zambiri mawu akuti “chinsinsi chopatulika” ndiwo kumasulira kwabwino kuposa “chinsinsi.” Limati za my·steʹri·on: “M’[Malemba Achigiriki Achikristu] limatanthauza, osati chinthu chosatheka kumva (monga tanthauzo la liwu lake lachingelezi), koma chinthu chimene, pokhala chosatheka kwa munthu kuchidziŵa payekha popanda womthandiza, chingadziŵike kokha mwa vumbulutso la Mulungu, ndipo chimadziŵika mwanjira ya Mulungu ndi panthaŵi yake yoikika, ndiponso kwa aja okha amene Mzimu Wake umawaunikira. Mwachisawawa chinsinsi chimatanthauza chidziŵitso chobisika; tanthauzo lake la m’Malemba nlakuti choonadi chovumbuluka. Ndiye chifukwa chake mawu amene amagwiritsiridwa ntchito kwambiri pankhaniyi ndiwo ‘chodziŵidwa,’ ‘choonetsedwa,’ ‘chovumbuluka,’ ‘cholalikidwa,’ ‘kumva,’ ‘chofalitsidwa.’”

3. Kodi mpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba unasiyana motani ndi zipembedzo zina zachinsinsi?

3 Kufotokoza kumeneku kukusonyeza kusiyana kwakukulu kwa zipembedzo zachinsinsi zimene zinafala m’zaka za zana loyamba ndi mpingo wachikristu watsopano. Pamene aja omwe analoŵa m’magulu achinsinsi nthaŵi zambiri amatsata lumbiro losunga chinsinsi kuti atetezere ziphunzitso za chipembedzo chawo, Akristu sanauzidwepo kulumbira kusunga chinsinsi chotero. Nzoona kuti mtumwi Paulo analankhula za “nzeru ya Mulungu m’chinsinsi [chopatulika, NW],” naitcha ‘nzeru yobisikayo,’ kutanthauza, yobisika kwa “akulu a nthaŵi ya pansi pano.” Siyobisika kwa Akristu amene inavumbulidwako mwa mzimu wa Mulungu kuti aidziŵikitse kwa anthu.​—1 Akorinto 2:7-12; yerekezerani ndi Miyambo 1:20.

“Chinsinsi Chopatulika” Chidziŵika

4. Kodi “chinsinsi chopatulika” chimanena za yani, ndipo chifukwa ninji?

4 “Chinsinsi chopatulika” cha Yehova chimanena za Yesu Kristu. Paulo analemba kuti: “[Yehova] anatizindikiritsa ife chinsinsi [chopatulika, NW] cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye, kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko. [Inde, mwa iye, NW].” (Aefeso 1:9, 10) Paulo ananena molunjika kwambiri pofotokoza “chinsinsi chopatulika” pamene anatchula kufunika kwake kwa ‘kuzindikira chinsinsi [chopatulika, NW] cha Mulungu, ndiye Kristu.’​—Akolose 2:2.

5. Kodi “chinsinsi chopatulika” chikuphatikizapo chiyani?

5 Koma pali zambiri, pakuti “chinsinsi chopatulika” ndi chinsinsi cha mbali zambiri. Sikungodziŵa chabe kuti Yesu ndiye Mbewu yolonjezedwa kapena Mesiya; chikuphatikizapo udindo umene apatsidwa kuti achite pachifuno cha Mulungu. Chikuphatikizapo boma lakumwamba, Ufumu Waumesiya wa Mulungu, monga momwe Yesu anafotokozera bwino pamene anauza ophunzira ake kuti: ‘Kwapatsidwa kwa inu kudziŵa zinsinsi [zopatulika, NW] za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo.’​—Mateyu 13:11.

6. (a) Kodi nchifukwa ninji ndi zoona kunena kuti “chinsinsi chopatulika” chinali ‘chobisika mwa nthaŵi zonse zosayamba’? (b) Kodi chinavumbulidwa motani pang’onopang’ono?

6 Panafunika kupita nthaŵi yaitali kuchokera pamene Mulungu anatchula nthaŵi yoyamba za chifuno chake chokonza maziko a Ufumu Waumesiya mpaka ‘kutsirizika chinsinsi [chopatulika, NW] cha Mulungu.’ (Chivumbulutso 10:7; Genesis 3:15) Kutsirizika kwake kunali kudzachitika utakhazikitsidwa Ufumuwo, malinga ndi zimene kumasonyeza kuyerekezera Chivumbulutso 10:7 ndi 11:15. Kwenikweni, panapita zaka ngati 4,000 kuchokera pamene lonjezo loyamba la Ufumu linaperekedwa m’Edene kufikira Mfumu Yosankhidwiratu itaonekera mu 29 C.E. Panapitanso zaka zina 1,885 kuti Ufumuwo ukhazikitsidwe kumwamba mu 1914. Umo ndimo mmene “chinsinsi chopatulika” chinavumbulidwira pang’onopang’ono pazaka pafupifupi 6,000. (Onani tsamba 16.) Paulo ananenadi zoona polankhula za “vumbulutso la chinsinsi [chopatulika, NW] chimene chinabisika mwa nthaŵi zonse zosayamba, koma chaonetsedwa tsopano, ndi kudziŵidwa.”​—Aroma 16:25-27; Aefeso 3:4-11.

7. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kumdalira kotheratu kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?

7 Kusiyana ndi anthu, amene moyo wawo ngwaufupi, Yehova samapanikizika ndi nthaŵi kuti avumbule zinsinsi zake nthaŵi isanakwane. Mfundo imeneyi iyenera kutiletsa kutekeseka pamene nkhani zina za Baibulo sizinafotokozedwe motikhutiritsa pakali pano. Kudekha kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene wasankhidwa kukonzera banja lachikristu chakudya panthaŵi yake, kumamletsa kudzikuza ndi kumayesa kulotera zinthu zisanadziŵike bwino. Kapoloyo amayesetsa kupeŵa kuumirira zinthu kosasintha. Iye ngwodzichepetsa moti amavomera kuti pakali pano sangayankhe mafunso onse, pokumbukira bwino Miyambo 4:18. Komatu zimasangalatsa kwambiri kudziŵa kuti Yehova, panthaŵi yake yoikika ndipo mwanjira yake, adzapitiriza kuvumbula zinsinsi zake zokhudza zifuno zake! Tisatekeseketu ndi makonzedwe a Yehova, kuyesa kumtsogolera mopanda nzeru Wovumbula zinsinsiyo. Mmene zilili zolimbikitsa nanga kudziŵa kuti amene Yehova akumgwiritsira ntchito lero samatero ayi! Ali wokhulupirika ndi wanzeru.​—Mateyu 24:45; 1 Akorinto 4:6.

Ena Ayenera Kuuzidwa Chinsinsi Chomwe Chavumbulidwa!

8. Kodi tidziŵa bwanji kuti “chinsinsi chopatulika” chiyenera kudziŵika?

8 Sikuti Yehova wavumbulira Akristu ‘chinsinsi chake chopatulika’ kuti iwo achibise. Ayenera kuchidziŵikitsa, malinga ndi pulinsipulo lomwe Yesu anakhazikitsira otsatira ake onse​—osati atsogoleri achipembedzo angapo okha: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika. Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m’mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m’nyumbamo. Chomwecho muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.”​—Mateyu 5:14-16; 28:19, 20.

9. Kodi nchiyani chisonyeza kuti Yesu sanali woukira boma, monga ena amanenera?

9 Yesu analibe cholinga choukira boma mwa kupanga kagulu kachizembera ka otsatira ake okhala ndi zolinga zachinsinsi. M’buku lakuti Early Christianity and Society, Robert M. Grant analemba za chodzikanira cha Akristu oyambirira chimene Justin Martyr wochirikiza chikhulupiriro ananena m’zaka za zana lachiŵiri kuti: “Ngati Akristu akanakhala oukira boma, akanabisala kuti akwanitse cholinga chawocho.” Koma kodi Akristuwo “akanabisala” bwanji komanso nkukhala ngati “mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri”? Sanayese nkomwe kuvundikira nyali yawo m’mbiya! Chotero, ntchito yawo sinayenere kudetsa nkhaŵa boma. Mlembi ameneyu anapitiriza kuwafotokoza kuti anali “anthu abwino koposa othandizana ndi mfumu kukhazikitsa mtendere ndi bata.”

10. Kodi nchifukwa ninji Akristu sayenera kudzibisa?

10 Yesu sanafune kuti ophunzira ake adzibise ndi kusadziŵika kuti anali m’chipembedzo chonenedwa mpatuko. (Machitidwe 24:14; 28:22) Ngati tilephera kuŵalitsa kuunika kwathu lero, Kristu ndi Atate wake yemwe, Wovumbula zinsinsi, sadzakondwera ayi, ngakhalenso ife sitidzakhala okondwa.

11, 12. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova akufuna kuti Chikristu chidziŵike? (b) Kodi Yesu anapereka motani chitsanzo chabwino?

11 Yehova “safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9; Ezekieli 18:23; 33:11; Machitidwe 17:30) Maziko okhululukirapo machimo a anthu olapa ndiwo chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, amene anadzipereka yekha dipo la onse​—osati oŵerengeka chabe​—kuti “yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Anthu afunika kwambiri kuwathandiza kuti achite zofunika zimene zidzatheketsa kuti aweruzidwe monga nkhosa, osati mbuzi, pachiweruzo chilinkudzacho.​—Mateyu 25:31-46.

12 Chikristu choona sichoyenera kuchibisa ayi; chiyenera kudziŵika mwanjira iliyonse yoyenera ndi yotheka. Yesu mwiniyo anapereka chitsanzo chabwino. Mkulu wa ansembe atamfunsa za ophunzira ake ndi chiphunzitso chake, iye anati: “Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthaŵi zonse m’sunagoge ndi m’Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu.” (Yohane 18:19, 20) Chifukwa cha chitsanzo chimenechi, ndi munthu wanji woopa Mulungu amene angayese nkomwe kusunga chinsinsi zimene Mulungu wanena kuti zilengezedwe poyera? Ndani angayese nkomwe kubisa “chifungulo cha nzeru” chotsogolera kumoyo wamuyaya? Akatero, angakhale ngati onyenga achipembedzo a m’zaka za zana loyamba.​—Luka 11:52; Yohane 17:3.

13. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulalikira nthaŵi iliyonse?

13 Kusapezeketu aliyense wonena kuti ife Mboni za Yehova tasunga chinsinsi uthenga wa Ufumu wa Mulungu! Kaya aulandira uthengawo kapena aukana, anthu ayenera kudziŵa kuti walalikidwa. (Yerekezerani ndi Ezekieli 2:5; 33:33.) Ndiye tiyeni tigwiritsire ntchito nthaŵi iliyonse kulankhula za uthenga wa choonadi kwa onse, kulikonse kumene tingakumane nawo.

Kumkoŵa Satana m’Chibwano ndi Zokoŵera

14. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuzengereza kukhala omasuka pakulambira kwathu?

14 Kumadera ambiri Mboni za Yehova zikukhala nkhani yaikulu m’zofalitsira nkhani zambirimbiri. Monga zinalili kwa Akristu oyambirira, iwo nthaŵi zambiri amawanamizira ndi kuwaika m’gulu limodzi ndi timagulu tachipembedzo tokayikitsa ndi tachinsinsi. (Machitidwe 28:22) Kodi kumasuka kwathu polalikira kungachititse kuti atineneze? Zoona, tingakhale opanda nzeru, ndiponso osatsata uphungu wa Yesu ngati tidziloŵetsa m’mikangano yosafunikira. (Miyambo 26:17; Mateyu 10:16) Komabe, ntchito yaphindu yolalikira Ufumu ndi kuthandiza anthu kuwongolera moyo wawo siiyenera kubisika. Imalemekeza Yehova, kumkweza pamwamba, kusonya kwa iye ndi ku Ufumu wake wokhazikitsidwawo. China chimene chachititsa kuti posachedwapa pakhale chisangalalo chifukwa cha amene akulandira choonadi cha Baibulo ku Eastern Europe ndi mbali zina za Afirika ndiko kumasuka kwakukulu kumene akulalikira nako choonadi tsopano kumeneko.

15, 16. (a) Kodi kumasuka kwathu ndi kulemera kwauzimu kuli ndi ntchito yotani, koma kodi zimenezi ziyenera kutidetsa nkhaŵa? (b) Kodi Yehova akumkoŵeranji Satana m’chibwano ndi zokoŵera?

15 Nzoona kuti anthu amaona kumasuka kumene Mboni za Yehova zimalalikira nako, paradaiso wauzimu amene iwo alimo, ndi kulemera kwawo​—pa anthu ndi chuma chomwe. Pamene zinthu zimenezi zimakopa oona mtima, zingachititsenso otsutsa kuipidwa. (2 Akorinto 2:14-17) Ndipotu mwina zimenezi m’kupita kwa nthaŵi zingakope makamu a Satana kuti aukire anthu a Mulungu.

16 Kodi zimenezi ziyenera kutidetsa nkhaŵa? Osati malinga ndi ulosi wa Yehova wopezeka m’Ezekieli chaputala 38. Umalosera kuti Gogi wa ku Magogi, kutanthauza Satana Mdyerekezi kuyambira pamene anamponyera kudziko lapansi Ufumu utakhazikitsidwa mu 1914, adzatsogolera kuukira anthu a Mulungu. (Chivumbulutso 12:7-9) Yehova akuuza Gogi kuti: “Nudzati, Ndidzakwera kumka ku dziko la midzi yopanda malinga, ndidzamka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mipingiridzo, kapena zitseko; kulanda ndi kufunkha zawo, kubweza dzanja lako liwononge mopasuka muli anthu tsopano, liwononge mtundu wa anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoŵeta ndi chuma, okhala pakati pa dziko.” (Ezekieli 38:11, 12) Komabe, vesi 4 ikusonyeza kuti anthu a Mulungu safunika kuopa kuukirako chifukwa Yehova ndiye adzasonkhezera zimenezo. Koma kodi Mulungu adzaloleranji​—inde, ngakhale kusonkhezera​—kuti anthu ake awaukire koopsa? M’vesi 23 timaŵerenga yankho la Yehova: “Ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.”

17. Kodi kuukira kwa Gogi kumene kwayandikirako tiyenera kukuona motani?

17 Ndiye chifukwa chake, m’malo moopa kuukira kwa Gogi, anthu a Yehova akuyembekeza mwachidwi kukwaniritsika kwina kwa ulosi wa Baibulo umenewo. Nzosangalatsa kudziŵa kuti mwa kulilemeretsa ndi kulidalitsa gulu lake looneka, Yehova akumkoŵa Satana m’chibwano ndi zokoŵera ndi kumkokera iye ndi makamu ake a nkhondo kokawagonjetsa!​—Ezekieli 38:4.

Koposa ndi Kalelonse!

18. (a) Kodi anthu ambiri tsopano ayamba kuzindikira chiyani, ndipo nchifukwa ninji? (b) Kodi kulabadira kwa anthu ulaliki wa Ufumu kukutilimbikitsa kwambiri motani?

18 Masiku ano Mboni za Yehova zakhala zomasuka kwambiri polankhula za zikhulupiriro zawo zochokera m’Baibulo, ngakhale kuti ambiri safuna zimenezi. Pazaka makumi ambiri, zachenjeza za ngozi ya kusuta ndi anamgoneka, kupanda nzeru kwa kulekerera ana osawalanga, zotsatira zake zoipa za zosangulutsa zodzala chisembwere ndi chiwawa, ndi ngozi zake zoika munthu mwazi. Zasonyezanso maumboni owombana a chiphunzitso cha chisinthiko. Anthu ambirimbiri tsopano akunena kuti, “Choncho Mboni za Yehova nzosalakwa nkomwe.” Tikanapanda kukhala omasuka polengeza poyera zikhulupiriro zathu, anthu sakananena zimenezo. Ndipotu musaiŵale kuti mwa kunena zimenezo, iwo akuyamba kumanena kuti, “Choncho iwe Satana, ndiwe wabodza; Yehova ali woona.” Zimenezitu zikutilimbikitsa kwambiri kupitiriza kutsatira chitsanzo cha Yesu, kulankhula poyera mawu a choonadi!​—Miyambo 27:11.

19, 20. (a) Kodi ndi kutsimikiza mtima kotani komwe anthu a Yehova anasonyeza mu 1922, ndipo kodi mawuwo akali kugwira ntchito? (b) Kodi “chinsinsi chopatulika” cha Yehova tiyenera kuchiona motani?

19 Kwa nthaŵi yaitali, anthu a Yehova azindikira ntchito yawo imeneyi. Pamsonkhano wosaiŵalika wa mu 1922, J. F. Rutherford, amene panthaŵiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society, anasonkhezera omvetsera mwa kunena kuti: “Khalani olama maganizo, khalani atcheru, khalani okangalika, khalani olimba mtima. Khalani mboni zokhulupirika ndi zoona za Ambuye. Menyanibe nkhondoyo kufikira zotsala zonse za Babulo zitakhala bwinja. Lengezani uthengawo konsekonse. Dziko liyenera kudziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu ndi kuti Yesu Kristu ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. Lino ndilo tsiku la masiku onse. Taonani, Mfumu ikulamulira! Inu ndinu atumiki ake oilengeza. Chotero, lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi ufumu wake.”

20 Ngakhale kuti mawuwo anali ofunika mu 1922, lero akhalatu ofunika koposa pambuyo pa zaka 75, pamene kuvumbuluka kwa Kristu monga Woweruza ndi Wolipsira kuli pafupi kwambiri! Uthenga wonena za Ufumu wa Yehova wokhazikitsidwa ndi wonena za paradaiso wauzimu amene anthu a Mulungu alimo uli “chinsinsi chopatulika” chaulemerero kwambiri chosatheka kungochisunga! Malinga ndi zimene Yesu mwiniyo anafotokoza bwino, otsatira ake, mothandizidwa ndi mzimu woyera, ayenera kukhala mboni za udindo wake waukulu pachifuno chosatha cha Yehova “kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8; Aefeso 3:8-12) Kunena zoona, monga atumiki a Yehova, Mulungu wovumbula zinsinsi, sitiyenera kusunga chinsinsi chimenechi ayi!

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi “chinsinsi chopatulika” nchiyani?

◻ Tidziŵa bwanji kuti chiyenera kulengezedwa?

◻ Nchiyani chidzasonkhezera Gogi kuukira anthu a Yehova, ndipo tiyenera kuziona motani zimenezo?

◻ Kodi ife, aliyense payekha, tiyenera kutsimikiza kuchitanji?

[Bokosi patsamba 16]

Chinsinsi Chopatulika” Chivumbuluka Pang’onopang’ono

◻ Itapita 4026 B.C.E.: Mulungu alonjeza kuutsa Mbewu yowononga Satana.​—Genesis 3:15

◻ 1943 B.C.E.: Akhazikitsa pangano la Abrahamu, nalonjeza kuti Mbewuyo idzadzera mwa Abrahamu.​—Genesis 12:1-7

◻ 1918 B.C.E.: Isake abadwa nakhala woloŵa panganolo.​—Genesis 17:19; 21:1-5

◻ Cha ku ma 1781 B.C.E.: Yehova atsimikiza kuti Mbewuyo idzadzera mwa mwana wa Isake, Yakobo.​—Genesis 28:10-15

◻ 1711 B.C.E.: Yakobo anena kuti Mbewuyo idzadzera mwa mwana wake Yuda.​—Genesis 49:10

◻ 1070-1038 B.C.E.: Mfumu Davide auzidwa kuti Mbewuyo idzakhala mbadwa yake ndi kuti idzakhala Mfumu, kulamulira kosatha.​—2 Samueli 7:13-16; Salmo 89:35, 36

◻ 29-33 C.E.: Yesu adziŵika kuti ndiye Mbewuyo, Mesiya, woweruza wamtsogolo, ndi Mfumu Yosankhidwiratu.​—Yohane 1:17; 4:25, 26; Machitidwe 10:42, 43; 2 Akorinto 1:20; 1 Timoteo 3:16

◻ Yesu avumbula kuti adzakhala ndi olamulira anzake ndi oweruza, kuti Ufumu wakumwamba udzakhala ndi anthu ake padziko lapansi, ndi kuti otsatira ake ayenera kukhala alaliki a Ufumuwo.​—Mateyu 5:3-5; 6:10; 28:19, 20; Luka 10:1-9; 12:32; 22:29, 30; Yohane 10:16; 14:2, 3

◻ Yesu avumbula kuti Ufumuwo udzakhazikitsidwa panthaŵi yoikika, monga zimachitira umboni zochitika za dziko.​—Mateyu 24:3-22; Luka 21:24

◻ 36 C.E.: Petro auzidwa kuti nawonso osakhala Ayuda adzakhala oloŵa anzake a Ufumu.​—Machitidwe 10:30-48

◻ 55 C.E.: Paulo afotokoza kuti oloŵa nyumba anzake a Ufumu adzauka ndi kukhala ndi moyo wosafa ndi wosavunda mkati mwa kukhalapo kwa Kristu.​—1 Akorinto 15:51-54

◻ 96 C.E.: Yesu, atayamba kale kulamulira otsatira ake odzozedwa, avumbula kuti chiŵerengero chawo chomaliza chidzakhala 144,000.​—Aefeso 5:32; Akolose 1:13-20; Chivumbulutso 1:1; 14:1-3

◻ 1879 C.E.: Zion’s Watch Tower itchula kuti 1914 ndicho chaka chofunika kwambiri pakuvumbuluka kwa “chinsinsi chopatulika” cha Mulungu

◻ 1925 C.E.: Nsanja ya Olonda ifotokoza kuti Ufumu unabadwa mu 1914; “chinsinsi chopatulika” cha Ufumuwo chilengezedwe.​—Chivumbulutso 12:1-5, 10, 17

[Zithunzi patsamba 15]

Monga Yesu Mtsogoleri wawo, Mboni za Yehova zimalengeza poyera Ufumu wa Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena