Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 6/15 tsamba 5-8
  • Kutha kwa Udani Padziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutha kwa Udani Padziko Lonse
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugonjetsa Udani m’Misasa ya Chibalo
  • Mphindi ya Udani
  • Dziko Lopanda Udani
  • Kodi Udani Udzatha Konse?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • N’chifukwa Chiyani Chidani Sichikutha?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Chidani Chikadzatheratu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • N’zotheka Kuthetsa Chidani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 6/15 tsamba 5-8

Kutha kwa Udani Padziko Lonse

PAFUPIFUPI zaka zikwi ziŵiri zapitazo, kagulu kena kanali kodedwa kwambiri. Tertullian akufotokoza mkhalidwe wa maganizo wa Aroma umene unalipo kulinga kwa Akristu oyambirira: “Ngati mvula siigwa, ngati kuchitika chivomezi, ngati kugwa njala kapena mliri, nthaŵi yomweyo anafuula kuti, ‘Ponyerani Akristu ku mkango!’”

Ngakhale kuti anali odedwa, Akristu oyambirira anakaniza mtima wofuna kubwezera chisalungamo. Mu Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, iye anati: “Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: koma ine ndinena kwa inu, Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.”​—Mateyu 5:43, 44.

Unali mwambo wa Ayuda wa pakamwa umene unanena kuti ‘kuda mdani’ kunali chinthu chabwino kuchita. Komabe, Yesu anati tiyenera kukonda mdani wathu, osati bwenzi lathu lokha. Zimenezi nzovuta komanso zotheka. Kukonda mdani sikumatanthauza kukonda njira zake zonse kapena zochita zake. Liwu Lachigiriki lopezeka mu nkhani ya Mateyuyo lachokera ku a·gaʹpe, limene limafotokoza chikondi chimene chimachita mogwirizana ndi lamulo. Munthu amene amasonyeza a·gaʹpe, chikondi chalamulo, amachita zabwino ngakhale kwa munthu amene amamuda ndi kumchitira nkhanza. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ndiko njira yotsanzirira Kristu, ndipo ndiko njira yogonjetsera udani. Katswiri wina Wachigiriki anati: “[A·gaʹpe] amatikhozetsa kugonjetsa chibadwa chathu cha kukwiya ndi kukhumudwa.” Koma kodi zimenezi zingachitike m’dziko lodzala udani lalerolinoli?

Zoonadi, si onse amene amanena kuti ali Akristu amene ali okonzekera kutsatira chitsanzo cha Kristu. Nkhanza zaposachedwapa za ku Rwanda zinachitidwa ndi magulu a mafuko, ambiri amene ziŵalo zake zinanena kuti zinali Akristu. Pilar Díez Espelosín, mvirigo wa Roma Katolika amene wagwira ntchito ku Rwanda kwa zaka 20, anafotokoza za chochitika china chokhudza mtima. Mwamuna wina anafika pa tchalitchi chake atanyamula mkondo umene mwachionekere anali kugwiritsira ntchito. Mvirigoyo anamfunsa kuti: “Kodi uganiza kuti ukuchitanji kumka ukumapha anthu? Suganiza za Kristu kodi?” Mwamunayo anati anatero ndipo anangoloŵabe m’tchalitchicho, nagwada, ndi kupereka pemphero la Rosary mwamphamvu. Koma pamene anamaliza, anachoka kukapitirizabe kupha ena. “Zimenezi zikusonyeza kuti sitikuphunzitsa uthenga wabwino moyenera,” mvirigoyo anavomereza motero. Komabe, kulephera kotero, sikumatanthauza kuti uthenga wa Yesu uli wopereŵera kanthu kena. Udani ungagonjetsedwe ndi awo amene amalondola Chikristu choona.

Kugonjetsa Udani m’Misasa ya Chibalo

Max Liebster ndi Myuda weniweni amene anapulumuka chupululutso cha Holocaust. Ngakhale kuti dzina lake lachiŵirilo limatanthauza kuti “wokondedwa,” anaona udani umene sanaonepo. Akufotokoza zimene anaphunzira ku Germany wa Nazi ponena za chikondi ndi udani.

“Ndinakulira pafupi ndi Mannheim, ku Germany, mkati mwa ma 1930. Hitler ananena kuti Ayuda onse anali opeza phindu olemera amene anali kulima pamsana Ajeremani. Koma choonadi nchakuti atate wanga anali munthu wamba wopanga nsapato. Komabe, chifukwa cha chisonkhezero cha manenanena a Anazi, anansi athu anayamba kutiukira. Pamene ndinali kamnyamata, munthu wina wa m’mudzi wathu anandithira mwazi wa nkhumba pamphumi. Chipongwe chonyazitsa chimenechi chinali chiyambi chabe cha zimene zinalinkudza. Mu 1939 a Gestapo anandimanga ndi kulanda zinthu zanga zonse.

“Kuchokera January 1940 mpaka May 1945, ndinapirira m’misasa ya chibalo isanu yosiyanasiyana: Sachsenhausen, Neuengamme, Auschwitz, Buna, ndi Buchenwald. Atate wanga, amene nawonso anatumizidwa ku Sachsenhausen, anamwalira mkati mwa chisanu chachikulu cha 1940. Ine mwinine ndinanyamula mtembo wawo kumka nawo kumalo owotcherako mitembo, kumene mulu wa mitembo unali kuyembekezera kuwotchedwa. A m’banja langa amene anafera m’misasamo anali asanu ndi atatu, onse pamodzi.

“A kapos anadedwa kwambiri pakati pa akaidi kuposadi alonda a SS. A kapos anali akaidi amene anagwirizana ndi a SS ndipo motero anali kuyanjidwa pa zinthu zina. Anaikidwa kukhala ogaŵira chakudya, ndiponso anali kukwapula akaidi ena. Kaŵirikaŵiri ankachita zinthu mosayenera ndi mopanda nzeru. Ndikhulupirira kuti ndinali ndi chifukwa chachikulu chodera a SS ndi a kapos omwe, koma m’nthaŵi ya kukhala kwanga m’ndende, ndinaphunzira kuti chikondi nchamphamvu kwambiri kuposa udani.

“Kulimbika mtima kwa akaidi amene anali Mboni za Yehova kunandikhutiritsa maganizo kuti chikhulupiriro chawo chinali chozikidwa pa Malemba​—ndipo inenso ndinakhala Mboni. Ernst Wauer, Mboni imene ndinakumana nayo kumsasa wa chibalo wa Neuengamme, anandilimbikitsa kukulitsa mkhalidwe wamaganizo wa Kristu. Baibulo limati “pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zoŵaŵa, sanawopsa, koma anapereka mlandu kwa iye woweruza kolungama.” (1 Petro 2:23) Ndinayesa kuchita mofananamo, kusiyira chilipsiro m’manja mwa Mulungu, amene ali Woweruza wa onse.

“Pa zaka zimene ndinakhala m’misasamo ndinaphunzira kuti kaŵirikaŵiri anthu amachita zinthu zoipa chifukwa cha umbuli. Sikuti alonda onse a SS anali oipa​—panali mmodzi amene anapulumutsa moyo wanga. Pa nthaŵi ina ndinagwidwa ndi matenda a kutseguka m’mimba kwakukulu ndipo ndinali wofooka wosakhoza kuyenda kuchoka pa ntchito panga kumka kumsasa. Ndikanatumizidwa ku mauvuni a gasi a Auschwitz mmaŵa wotsatira, komano mlonda wina wa SS, amene anali wa kuchigawo cha Germany kumene ndinachokera, anandilanditsa. Anandipezera ntchito mu kafiteriya ya SS, mmene ndinakhoza kupeza mpumulo pang’ono kufikira nditachira. Tsiku lina iyeyo anaulula kwa ine kuti: ‘Max, ndikuona ngati kuti ndili pa sitima imene ili paliŵiro lalikulu ndi yopanda mabuleki. Ngati ndidumphamo, ndidzafa. Ngati ndikhalabe momwemo, ndidzafa m’ngozi yake!’

“Anthu ameneŵa anafuna kusonyezedwa chikondi monga momwedi ine ndinafunira. Kwenikweni, chinali chikondi ndi chifundo, limodzi ndi kukhulupirira kwanga Mulungu, zimene zinandikhozetsa kupirira ndi mikhalidwe yoipa yonyazitsayo ndi chiwopsezo cha tsiku ndi tsiku cha kuphedwa. Sindinganene kuti ndinapulumuka wosavulazidwa, koma zipsera zanga za malingaliro zinali zochepa.”

Chikondi ndi kukoma mtima kumene Max akali kusonyezabe zaka 50 pambuyo pake zili umboni wamphamvu wa kuona kwa mawu ake. Nkhani ya Max sindiyo yokha. Iye anali ndi chifukwa champhamvu cha kugonjetsera udani​—anafuna kutsanzira Kristu. Ena amene miyoyo yawo yatsogoleredwa ndi Malemba achita mofananamo. Simone, mmodzi wa Mboni za Yehova wa ku France, akufotokoza mmene anaphunzirira tanthauzo la chikondi chopanda dyera.

“Amayi, a Emma, amene anakhala Mboni nkhondo yadziko yachiŵiri itatsala pang’ono kuyamba, anandiphunzita kuti kaŵirikaŵiri anthu amachita zoipa chifukwa cha kusadziŵa bwino zinthu. Anafotokoza kuti ngati nafenso tiwada, sitili Akristu enieni, popeza kuti Yesu anati tiyenera kukonda adani athu ndi kupempherera otizunza.​—Mateyu 5:44.

“Ndikukumbukira za mkhalidwe wina wovuta kwambiri umene unayesa chikhulupiriro chimenechi. M’nthaŵi imene France analandidwa ndi Anazi, Amayi anavutika kwambiri chifukwa cha mnansi wina wa m’nyumba imene tinali kukhala. Iyeyo anachitira lipoti Amayi kwa a Gestapo, ndipo chotero, amayi anathera zaka ziŵiri m’misasa ya chibalo ya Ajeremani, kumene anatsala pang’ono kufa. Nkhondoyo itatha, apolisi a France anafuna kuti Amayi asayine chipepala chosumira mlandu mkazi ameneyu monga wogwirizana ndi Ajeremani. Koma amayi anakana, akumanena kuti ‘Mulungu ndiye Woweruza ndi Wofupa wa zabwino ndi zoipa.’ Zaka zingapo pambuyo pake, mnansi mmodzimodziyu anadwala kansa yosachiritsika. M’malo mokondwerera tsoka lakelo, amayi anathera maola ambiri akumamthandiza kuchititsa kuti miyezi yotsala ya moyo wake ikhale yabwinopo monga momwe akanathera. Sindidzaiŵala chilakiko cha chikondi chimenechi pa udani.”

Zitsanzo ziŵiri zimenezi zikusonyeza mphamvu ya chikondi chalamulo pa chisalungamo. Komabe, Baibulo lenilenilo limati pali “mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana.” (Mlaliki 3:1, 8) Kodi zimenezi zingakhale bwanji choncho?

Mphindi ya Udani

Mulungu samatsutsa udani wonse. Ponena za Yesu Kristu, Baibulo limati: “Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa.” (Ahebri 1:9) Komabe, pali kusiyana pakati pa kuda choipa ndi kuda munthu wochita choipacho.

Yesu anapereka chitsanzo choyenera pakati pa chikondi ndi udani. Iye anada chinyengo, koma anayesa kuthandiza onyenga kusintha maganizo awo. (Mateyu 23:27, 28; Luka 7:36-50) Anatsutsa nkhondo, koma anapempherera awo amene anamupha. (Mateyu 26:52; Luka 23:34) Ndipo ngakhale kuti dziko linamuda popanda chifukwa, anapereka moyo wake kuti apatse moyo dziko. (Yohane 6:33, 51; 15:18, 25) Anatisiyira chitsanzo changwiro cha chikondi chalamulo ndi udani waumulungu.

Chisalungamo chingadzutse kuipidwa mwa ife, monga momwe chinachitira mwa Yesu. (Luka 19:45, 46) Komabe, Akristu sanalamulidwe kulipsira iwo eni. “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa,” Paulo analangiza motero Akristu a ku Roma. “Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa . . . Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.” (Aroma 12:17-21) Pamene tikana kusunga udani kapena kulipsira pa choipa, chikondi chimapambana.

Dziko Lopanda Udani

Kuti udani uthe padziko lonse, mikhalidwe yoipa yamaganizo yokhomerezeka ya anthu miyandamiyanda iyenera kusintha. Kodi zimenezi zingachitidwe motani? Profesa Ervin Staub akupereka lingaliro lotsatirali: “Sitiŵerengera awo amene timavulaza ndipo timaŵerenga awo amene timathandiza. Pamene tiŵerengera kwambiri anthu amene timathandiza ndi kukhutira ndi kuti tili kuthandiza, timaonanso ife eni kukhala osamala ena ndi othandiza ena kwambiri. Chimodzi cha zonulirapo zathu chiyenera kukhala cha kupanga zitaganya zimene zili zokhoza kuthandiza ena kwambiri.”​—The Roots of Evil.

Mwa mawu ena, kuchotsedwa kwa udani kukufunikira kupangidwa kwa chitaganya chimene anthu angaphunziremo kusonyeza chikondi mwa kuthandizana, chitaganya chimene anthu ake angaiŵale za udani wonse wochititsidwa ndi tsankhu, kukondetsa dziko la munthuwe, ufuko, ndi utundu. Kodi chitaganya chotero chilipo? Talingalirani za chochitika cha mwamuna wina amene anakumana ndi udani mkati mwa chipanduko chotchedwa Cultural Revolution ku China.

“Pamene Cultural Revolution inayamba, tinaphunzitsidwa kuti sitinafunikire kugonja pa ‘nkhondo ya chipani.’ Mkhalidwe wa udani ndiwo umene unali wofala. Ndinakhala wa kagulu ka Red Guard ndi kuyamba kufunafuna ‘adani a chipani’​—ngakhale pakati pa a m’banja langa. Ngakhale kuti ndinali wachichepere panthaŵiyo, ndinakhala ndi phande pa kufufuza m’nyumba za anthu mmene tinkafunafunamo aja amene anasonyeza ‘malingaliro a kuukira boma.’ Ndinachititsanso msonkhano wapoyera umene unatsutsa ‘munthu wosagwirizana ndi chipandukocho.’ Zoonadi, nthaŵi zina milandu imeneyi inazikidwa pa kudana kwa munthu ndi wina m’malo mwa nkhani zandale.

“Ndinaona anthu ambiri​—achichepere ndi achikulire, amuna ndi akazi​—akumakwapulidwa kumene kunakhala kwankhanza mowonjezereka. Mmodzi wa aphunzitsi anga​—munthu wabwino​—anasonyezedwa kwa anthu m’makwalala monga ngati kuti anali mpandu. Miyezi iŵiri pambuyo pake mphunzitsi winanso wolemekezeka wa kusukulu kwanga anapezedwa atafa mu mtsinje wotchedwa Suzhou River, ndipo mphunzitsi wanga wa Chingelezi anaumirizidwa kudzinyonga. Ndinachita kakasi ndi kuzunguzika maganizo. Anthu ameneŵa anali okoma mtima. Kuwachitira motere kunali kolakwa! Chotero ndinadula mayanjano anga onse ndi a Red Guards.

“Sindiganiza kuti nyengo imeneyi ya udani imene inakantha China kwa nyengo yaifupi inali chochitika chokha cha mtundu umenewu. M’zaka za zana lino mwabuka maudani ambiri. Komabe, ndikhulupirira kuti chikondi chingathe kugonjetsa udani. Zimenezi zili kanthu kena kamene ndaona ndekha. Pamene ndinayamba kuyanjana ndi Mboni za Yehova, ndinachita chidwi ndi chikondi chenicheni chimene anasonyeza kwa anthu a mitundu ina ndi a ziyambi zosiyanasiyana. Ndikuyembekezera nthaŵiyo pamene, monga momwe Baibulo limalonjezera, anthu onse adzakhala ataphunzira kusonyezana chikondi.”

Inde, chitaganya cha padziko lonse cha Mboni za Yehova chili umboni weniweni wakuti udani ungathe kuchotsedwa. Kaya akhale amtundu wotani, Mboni zimayesayesa kuchotsa tsankhu ndipo m’malo mwake kusonyeza ulemu weniweni ndi kuthetsa mikhalidwe yotsalira iliyonse ya utundu, ufuko, kapena kukondetsa dziko la munthuwe. Amodzi a maziko a chipambano chawo ndiwo kutsimikizira kwawo kutsanzira Yesu Kristu posonyeza chikondi chalamulo Maziko ena ngakuti amayembekezera Ufumu wa Mulungu kuti udzathetsa chisalungamo chilichonse chimene angakhale akuvutika nacho.

Ufumu wa Mulungu ndiwo yankho lotsimikizirika lobweretsera dziko lopanda udani, dziko limene simudzakhaladi kuipa kapena udani. Polongosoledwa m’Baibulo kukhala “miyamba yatsopano,” boma limeneli lakumwamba lidzatetezera dziko pa chisalungamo. Lidzalamulira pa “dziko latsopano,” kapena pa chitaganya cha anthu chatsopano chimene chidzakhala chitaphunzitsidwa kukondana. (2 Petro 3:13; Yesaya 54:13) Maphunziro ameneŵa akuchitika kale, monga momwe zokumana nazo za Max, Simone, ndi ena ambiri zikuchitira umboni. Kumeneku kwangokhala kuoneratu programu ya padziko lonse ya kuchotsa udani ndi zochititsa zake.

Yehova akufotokoza chotulukapo chake kupyolera mwa mneneri wake Yesaya kuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Mulungu mwiniyo adzalengeza za kutha kwa udani. Idzakhaladi nthaŵi ya kusonyeza chikondi.

[Zithunzi patsamba 7]

Anazi anasindikiza nambala yaukaidi pamkono wakumanzere wa Max Liebster

[Chithunzi patsamba 8]

Posachedwa udani udzakhala chinthu chakale

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena