Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 28 tsamba 70-tsamba 71 ndime 6
  • N’chifukwa Chiyani Ophunzira a Yesu Sankasala Kudya?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Ophunzira a Yesu Sankasala Kudya?
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Afunsidwa za Kusala Chakudya
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kodi Kusala Kudya Kumathandiza Munthu Kuyandikira kwa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kusala Kudya?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Kusala Kudya Nkwachikale?
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 28 tsamba 70-tsamba 71 ndime 6
Ophunzira a Yohane M’batizi akufunsa Yesu zokhudza kusala kudya

MUTU 28

N’chifukwa Chiyani Ophunzira a Yesu Sankasala Kudya?

MATEYU 9:14-17 MALIKO 2:18-22 LUKA 5:33-39

  • OPHUNZIRA A YOHANE ANAFUNSA YESU ZA KUSALA KUDYA

Yohane M’batizi anaponyedwa m’ndende patangopita nthawi yochepa Yesu atakapezeka ku mwambo wa Pasika wa mu 30 C.E. Yohane ankafuna kuti ophunzira ake akhale otsatira a Yesu. Pa miyezi yonse imene Yohane anali kundendeyi si ophunzira ake onse amene anakhala otsatira a Yesu.

Pamene Pasika wa mu 31 C.E. ankayandikira, ena mwa ophunzira a Yohane anapita kwa Yesu n’kukamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?” (Mateyu 9:14) Afarisi ankaona kuti kusala kudya ndi mwambo wachipembedzo. Pa nthawi ina, Yesu anapereka fanizo la Mfarisi yemwe ankadziona kuti ndi wolungama. Popemphera Mfarisiyo ananena kuti: “Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. . . . Ine ndimasala kudya kawiri pa mlungu.” (Luka 18:11, 12) N’kutheka kuti ophunzira a Yohane ankasalanso kudya mwamwambo kapena ankasala kudya chifukwa cha chisoni poganizira kuti Yohane wamangidwa. Anthu ambiri anadabwa kuona kuti ophunzira a Yesu sankasala nawo kudya. Iwo ankaganiza kuti ophunzirawo sakukhudzidwa ndi zimene zamuchitikira Yohane.

Yesu anayankha pogwiritsa ntchito chitsanzo. Iye ananena kuti: “Anzake a mkwati samva chisoni ngati mkwatiyo ali nawo limodzi, si choncho kodi? Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa nthawiyo adzasala kudya.”—Mateyu 9:15.

Yohane anatchula Yesu ngati mkwati. (Yohane 3:28, 29) Pa nthawi imene Yesu anali ndi moyo ophunzira ake sankasala kudya. Koma Yesu ataphedwa, zinali zomveka kuti ophunzira ake akhale ndi chisoni komanso kuti asafune kudya. Komabe zinthu zinasintha Yesu ataukitsidwa. Ophunzirawo analibenso chifukwa chokhalira ndi chisoni kapena kusala kudya.

Kenako Yesu anafotokoza mafanizo awiri awa: “Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Pakuti mphamvu yonse ya chigambacho ingakoke ndi kung’amba malayawo ndipo kung’ambikako kungawonjezeke kwambiri. Ndiponso anthu sathira vinyo watsopano m’matumba achikopa akale. Akachita zimenezo, matumba achikopawo amaphulika ndipo vinyoyo amatayika moti matumbawo amawonongeka. Koma anthu amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa atsopano.” (Mateyu 9:16, 17) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani?

Yesu ankafuna kuti ophunzira a Yohane amvetse chifukwa chimene ophunzira ake sankatsatira miyambo yakale ya Chiyuda monga kusala kudya. Yesu sanabwere kudzawonjezera miyambo yatsopano pa miyambo yakale, kapena kudzalimbikitsa anthu kutsatira miyambo yomwe inali itatsala pang’ono kusiya kugwira ntchito. Kupembedza kumene Yesu ankalimbikitsa kunali kosiyana ndi kumene Ayuda ankatsatira pa nthawiyo chifukwa iwo ankaphatikiza malamulo a Mulungu ndi zikhulupiriro za anthu. Ngati iye akanachita zimenezi, akanakhala ngati akusokerera chigamba chatsopano pamalaya akale kapena kuthira vinyo watsopano m’thumba lachikopa lakale.

MAFANIZO ONENA ZA KUSALA KUDYA

Thumba lachikopa

Yesu anafotokoza fanizo limene anthu ambiri sanavutike kulimvetsa. Iye anafotokoza zimene zimachitika munthu akamasoka malaya. Kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu atasokerera chigamba chatsopano pamalaya akale? Malayawo akachapidwa, chigamba chatsopanocho chimakwinyika n’kuchepa pang’ono zomwe zimachititsa kuti malaya akalewo ang’ambike.

N’zimenenso zinkachitika ndi matumba osungira vinyo opangidwa ndi zikopa za nyama. Pakapita nthawi, chikopacho chinkalimba kwambiri moti sichinkatanuka. Choncho kuthira vinyo mu chikopa choterocho kukanakhala kuwononga chifukwa vinyo watsopano akamawira amafufuma. Zimenezi zikanachititsa kuti matumba akalewo aphulike.

  • Kodi ndani ankasala kudya m’nthawi ya Yesu, nanga ankachitiranji zimenezi?

  • N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu sankasala kudya iye alipo, koma ndi nthawi iti imene akanasala?

  • Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pofotokoza za fanizo la chigamba chatsopano komanso vinyo watsopano?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena