Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 6/1 tsamba 17-19
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi—“Amishonale Enieni!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Omaliza Maphunziro a Gileadi—“Amishonale Enieni!”
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Sukulu ya Gileadi—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Ophunzira Mawu a Mulungu Atsiriza Sukulu Yawo
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Amishonale Owonjezereka Kaamba ka Kututa Kwapadziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kufunitsitsa ndi Mtima Wonse Kumachititsa Anthu Kupita ku Sukulu ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 6/1 tsamba 17-19

Omaliza Maphunziro a Gileadi​—“Amishonale Enieni!”

“KODI mmishonale ngwotani?” Funso limenelo linadzutsidwa m’nkhani ya mkonzi wa nyuzipepala pafupifupi zaka makumi anayi zapitazo. Mlembiyo anati amishonale enieni anali anthu ogwiritsidwa ntchito m’kukonzanso mkhalidwe wa anthu ndi wa zachuma. Komabe, pa Sande, March 5, 1995, pa Jersey City Assembly Hall of Jehovah’s Witnesses, yankho losiyana kwambiri ndi limenelo linaperekedwa mwamphamvu. Chochitika chake? Kumaliza maphunziro kwa kalasi ya 98 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower​—sukulu imene yatumiza amishonale padziko lonse!

Nyimbo ndi pemphero lotsegulira zitatha, Albert D. Schroeder wa Bungwe Lolamulira analonjera mwaubwenzi anthu 6,430 amene anali omvetsera. M’ndemanga zake zotsegulira, Mbale Schroeder anafotokoza bwino lomwe chifukwa chake omaliza maphunziro a Gileadi ali osiyana ndi ena amene adzitcha kuti amishonale. Iye anati: “Baibulo ndilo buku lalikulu lophunziridwa la Gileadi.” Omaliza maphunziro a Gileadi amaphunzitsidwa kukhala, osati antchito othandiza osauka, koma aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Motero iwo ali oyenerera kwambiri kusamalira zosoŵa zauzimu za anthu m’maiko achilendo.

Alankhuli otsatira anafotokozapo mbali zambiri zimene omaliza maphunziro a Gileadi amasonyeza nazo umboni wakuti alidi amishonale “enieni.” Charles Molohan analankhula kwa iwo pa nkhani ya mutu wakuti “Pitirizanibe Kubala Zipatso Zabwino Monga Amishonale.” Pogwira mawu mtumwi Paulo pa Akolose 1:9, 10, Mbale Molohan anakumbutsa omaliza maphunzirowo kuti miyezi yawo isanu yapitayo pa Gileadi inawathandiza kukula “m’chizindikiritso cha Mulungu.” Zimenezi zidzawathandiza kubala zipatso m’njira ziŵiri: mwa kusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu ndi mwa kuuza ena choonadi cha Baibulo.

Daniel Sydlik wa Bungwe Lolamulira anatsatira ndi nkhani ya mutu wothutsa mtima wakuti “Musasinthanitse Moyo Wanu ndi Kanthu Kena.” Iye anatchula za funso la Yesu lakuti: “Munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?” (Mateyu 16:26) Mbale Sydlik anati: “Anthu asinthanitsa miyoyo yawo ndi mkhalidwe wosavuta ndi wofeŵa wa moyo.” Komabe, awo amene ali ndi chikhulupiriro chamoyo samalolera molakwa pa mayesero. Mawu a Yesu amasonyeza kuti munthu ayenera kukhala wofunitsitsa ‘kupereka’ ndiko kuti, kudzimana, kuti apeze moyo wake. Amishonale atsopanowo analimbikitsidwa kupatsa Yehova moyo wawo wonse, zabwino koposa, mu utumiki wake!

Kenako, William Van de Wall wa Dipatimenti ya Komiti Yautumiki analankhula pa mutu wakuti “Mtumwi Paulo​—Chitsanzo Choyenera Kutsanziridwa.” Mbale Van de Wall anafotokoza kuti: “Paulo anapititsa patsogolo ntchito yaumishonale m’zaka za zana loyamba.” Pamenepo, moyenerera, anafotokoza mbali zinayi zimene mtumwi Paulo anaperekeramo chitsanzo chabwino kaamba ka amishonale amakono: (1) Nkhaŵa yeniyeni ya Paulo ndi kukonda kwake anthu, (2) kugwira mtima kwake mu utumiki, (3) modzichepetsa anakana kudzikweza, (4) kudalira kwake Yehova kopanda chikayikiro.

“Lolani Yehova Akusanthuleni m’Gawo Lanu Latsopano” unali mutu wokambidwa ndi Lyman A. Swingle wa Bungwe Lolamulira. Akumagwiritsira ntchito lemba la tsiku, Salmo 139:16, Mbale Swingle anasonyeza kuti, monga amishonale atsopano, iwowo adzakumana ndi mavuto m’magawo awo ndi kuti Yehova amadziŵa njira zowathetsera. “Pitani kwa iye,” iye analimbikitsa motero, “lankhulani naye pamene muli ndi mavuto. Funafunani chimene chili chifuniro chake.”

John E. Barr wa Bungwe Lolamulira analankhula pa mutu wakuti “Chikhulupiriro Chanu Chikula Chikulire.” (2 Atesalonika 1:3) Pa Luka 17:1, timaŵerenga kuti Yesu anati: “Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze.” Ena akhumudwa chifukwa cha maumunthu a amishonale anzawo. Koma Mbale Barr analimbikitsa amishonalewo kukhala ndi chikhulupiriro chofunika kuti akhale okhululukira. Indedi, kunali ponena za nkhaniyi pamene ophunzira a Yesu anapempha kuti: “Mutiwonjezere chikhulupiriro.” (Luka 17:2-5) Chikhulupiriro cha amishonale chingayesedwenso ndi kusintha kwa zinthu kosiyanasiyana m’gulu. “Kodi tili ndi chikhulupiriro chakuti tivomereze zimenezi,” anafunsa motero Mbale Barr, “kapena kodi izo zidzakhala zopinga zonga mapiri?”

Kenako panadza chilangizo choperekedwa ndi alangizi aŵiri a Gileadi. Jack Redford analimbikitsa omaliza maphunzirowo kusunga mkhalidwe wabwino wamaganizo. Anawasimbira za mmishonale wina amene anasiya gawo lake chifukwa cha kusekedwa ndi amishonale anzake. Komabe, Malemba amatichenjeza kusakwiya mosayenera. (Mlaliki 7:9) “Khalani ndi mkhalidwe wabwino wamaganizo,” iye analimbikitsa motero. “Khalani wokhululukira zophophonya ndi kupanda ungwiro kwa ena okuzingani.”

Ndiyeno U. V. Glass, woyang’anira kaundula wa Gileadi, anafunsa kuti: “Kodi muli okonzekera kukalimbana ndi ‘nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika’”? (Maliki 9:11) “Moyo wathu nthaŵi zonse umasintha,” anatero Mbale Glass, “ndipo kusintha kwina kungakhale kovuta kwambiri.” Amishonale ena mosayembekezera akhala ndi thanzi loipa, nthenda, ndi mavuto m’banja, zikumaumiriza ena kusiya magawo awo. “Mulimonse mmene zochitika zosadziŵika zingakhalire,” anatero Mbale Glass, “tidziŵa kuti Yehova amadziŵa zimenezo ndipo amadera nkhaŵa. Ngati timdalira, tidziŵa kuti tidzalakika!”

Nkhani yakuti “Opatulidwa Kaamba ka Utumiki wa Umishonale” inatseka mpambo wa nkhani za mmaŵazo. Theodore Jaracz wa Bungwe Lolamulira anayankha funso lodzutsidwa pachiyambi pa nkhani ino, lakuti, “Kodi mmishonale ngwotani?” Poyankha, iye anafotokoza Machitidwe machaputala 13 ndi 14 ponena za ntchito yaumishonale ya Paulo ndi Barnaba. Mwachionekere, ntchito imeneyo inalunjikitsidwa, osati pa kuthetsa mavuto a m’chitaganya, koma pa ‘kulalikira uthenga wabwino.’ (Machitidwe 13:32) Mbale Jaracz anafunsa kuti: “Kodi simukuvomereza kuti Paulo ndi Barnaba anasonyeza zimene mmishonale weniweni ayenera kukhala?” Ndiyeno mmishonale wina wanthaŵi yaitali Robert Tracy wa ku Mexico anafunsidwa kuti asimbire ena za zokumana nazo zake zina zokondweretsa monga mlaliki.

Programu ya mmaŵayo inafika pachimake pamene Mbale Schroeder anapereka madipuloma kwa omaliza maphunziro 48 amenewo. Omvetsera anakondwera kumvetsera maina a maiko 21 amene amishonalewo anagaŵiridwa: Barbados, Benin, Bolivia, Central African Republic, Costa Rica, Côte d’Ivoire, Ecuador, Equatorial Guinea, Estonia, Guinea-Bissau, Honduras, Latvia, Leeward Islands, Mauritius, Mozambique, Nicaragua, Paraguay, Peru, Senegal, Taiwan, ndi Venezuela.

Pambuyo pa kupuma kaamba ka chakudya chamasana, omvetsera anasonkhananso ndipo anasangalala ndi phunziro la Nsanja ya Olonda laumoyo, lochititsidwa ndi Robert P. Johnson wa Dipatimenti Yautumiki. Ziŵalo za kalasi la 98 zimenezo zinayankha mafunso. Zimenezi zinatsatiridwa ndi mpambo wokondweretsa wa kufunsa kochititsidwa ndi ziŵalo za antchito a Gileadi. Omvetsera analimbikitsidwa kwambiri pamene omaliza maphunzirowo anawasimbira zokumana nazo zawo za kumunda ndi kufotokozanso za maganizo awo ponena za magawo awo akumaiko achilendo.

Kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndi theka, Gileadi inali kumalo a Watchtower Society ku Wallkill, New York. Komabe, mu April 1995, sukuluyo inasamutsidwira ku Watchtower Educational Center yatsopano ku Patterson, New York. Kodi ndimotani mmene banja la Beteli la ku Wallkill linamvera ponena za kusintha kumeneku? Pa kumaliza maphunziro kumeneku ambiri ochokera ku Wallkill anafunsidwa. Mawu awo okhudza mtima anasonyeza bwino kwambiri kuti iwo sadzaiŵala konse ophunzira a Gileadi. Mwachionekere, amuna ndi akazi odzipereka ameneŵa ali amishonale enieni​—odzichepetsa, odzimana, odera nkhaŵa kwambiri pa kufuna kuthandiza ena.

Pamene mwambo wa kumaliza maphunziro unali kufika kumapeto, omvetsera onse anali ndi chidaliro chakuti Sukulu ya Gileadi idzapitiriza mwachipambano kuchita zimene yachita kwa zaka zoposa 50​—kutulutsa amishonale enieni!

[Bokosi patsamba 18]

Ziŵerengero za Kalasi:

Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 8

Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwako: 21

Chiŵerengero cha ophunzira: 48

Avareji ya zaka zakubadwa: 32.72

Avareji ya zaka m’choonadi: 15.48

Avareji ya zaka mu utumiki wa nthaŵi yonse: 10.91

[Chithunzi patsamba 18]

Kalasi la 98 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.

(1) Eszlinger, A.; Mann, T.; Rivera, G.; Baruero, M.; Vaz, M.; Durga, K.; Silweryx H.; Alvarado, D. (2) Toth, B.; Segarra, S.; Hart, R.; Rooryck, I.; Escobar, P.; Ejstrup, J.; Sligh, L.; Rivera, E. (3) Archard, D.; Snaith, S.; Marciel, P.; Koljonen, D.; Waddell, S.; Blackburn, L.; Escobar, M.; Archard, K. (4) Hart, M.; Toth, S.; Koljonen, J.; Bergman, H.; Mann, D.; Blackburn, J.; Park, D.; Vaz, F. (5) Segarra, S.; Sligh, L.; Leslie, L.; Bergman, B.; Baruero, W.; Alvarado, J.; Leslie, D.; Park, D. (6) Silweryx, K.; Eszlinger, R.; Waddell, J.; Snaith, K.; Durga, A.; Rooryck, F.; Ejstrup, C.; Marciel, D.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena