Lingaliro la Baibulo
Kodi Ndani Amapita Kumwamba?
BOMBA lotcheredwa ndi zigaŵenga liphwasula ndege imene ikuuluka, ndi kupha onse okweramo. Achibale ndi mabwenzi a ophedwawo akuuzidwa kuti okondedwa awo tsopano ali kumwamba, monga ngati kuti kunali kulipirira imfa yawo yosayembekezereka yachiwawayo.
Woimba nyimbo wina wotchuka amwalira ndipo akunenedwa kuti ‘akuimba malipenga pamodzi ndi angelo kumwamba.’
Matenda, njala, kapena ngozi zimalanda makanda moyo wawo waphumphu, ndipo atsogoleri achipembedzo amati tsopano makandawo akusangalala ndi mtendere kumwamba, mwinamwake kukhaladi angelo!
Kodi Mulungu amawongolera chisalungamo kwa achichepere ndi achikulire mwa kutengera onse amenewo kwa iyemwini mu mtendere wakumwamba? Kodi kutengeredwa kumwamba kwangokhala njira ya Mulungu yosungira zabwino zonse ndi zotamandika za mwa mtundu wa anthu? Kodi lingaliro la Baibulo nlotani?
Amene Sali Kumwamba
Mawu a Baibulo ali omvekera bwino: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu?” (1 Akorinto 6:9) Komabe, Baibulo limanenanso za olungama ambiri ndi ochitiridwa chisalungamo amene sadzapita kumwamba.
Yesu iyemwini anati za Yohane Mbatizi amene anali pafupi kufera chikhulupiriro: “Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.” (Mateyu 11:11) Ana onse achimuna azaka ziŵiri ndi pansi pake a m’Betelehemu ndi m’mizinda yake anaphedwa mopanda chifundo ndi mfumu yoipa Herode poyesa kuwononga mwanayo Yesu. (Mateyu 2:16) Komabe, Yesu anati: “Ndipo kulibe munthu [mwamuna kapena mkazi kapena mwana] anakwera Kumwamba, koma iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu [Yesu].” (Yohane 3:13) Kodi nchifukwa ninji Yesu sanalankhule za ochitiridwa chisalungamo ameneŵa kuti anali kumwamba?
Yesu Anatsegula Njira
Yesu anadzitcha “njira ndi choonadi ndi moyo” ndipo mtumwi Paulo anamutcha “chipatso choundukula cha iwo akugona.” (Yohane 14:6; 1 Akorinto 15:20) Chotero, palibe amene akanamtsogolera kupita kumwamba. Koma pamene Yesu anapita kumwamba pambuyo pa masiku pafupifupi 40 ataukitsidwa, kodi iye tsopano anatsatiridwa ndi amuna achikhulupiriro omwe anali atamwalira kale? Pambuyo pa masiku khumi, mtumwi Petro anati ponena za Mfumu Davide “adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lerolino. . . . Pakuti Davide sanakwera Kumwamba ayi.”—Machitidwe 2:29, 34.
Motero, kutengeredwa kumwamba kumaphatikizapo zoposa chabe kulipirira chisalungamo chochitidwa kwa munthu kapena zoposa ngakhale kufupidwa kaamba ka kukhulupirika. M’malo mwake, kuli kaamba ka kuumbidwa kwa bungwe la olamulira akumwamba lopangidwa ndi chiŵerengero cha oimira anthu pansi pa chitsogozo cha Kristu, odzozedwa ndi mzimu woyera.—Aroma 8:15-17; Chivumbulutso 14:1-3.
Ufumu Wakumwamba
Yesu anatchula ulamuliro umenewu, kapena boma kukhala “ufumu wa kumwamba” kapena “ufumu wa Mulungu.” (Mateyu 5:3, 20; Luka 7:28) Chifuno sichinali chakuti makamu aakulu a anthu aphatikizidwe m’bungwe la olamulira limeneli. Nchifukwa chake Yesu analitcha “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) M’chinenero choyambirira chogwiritsidwa ntchito m’mbali imeneyi ya Baibulo, liwulo “kagulu” (mi·krosʹ) ndilo losiyana ndi lakuti chigulu (meʹgas), ndipo kugwiritsiridwa ntchito kwake pa Luka 12:32 kumasonyeza kuchuluka kapena kuchepa kwa chiŵerengero. Motero, kukhala chiŵalo cha “ufumu wa kumwamba” sikumalola chiŵerengero chopanda malire. Mwachitsanzo: Mutapemphedwa kuthira madzi pang’ono m’tambula, mudzatsimikizira kuti sanasefukire. Mofananamo, “kagulu ka nkhosa” sikangapangidwe ndi chiŵerengero chosefukira cha anthu. Ufumu wa Mulungu uli ndi chiŵerengero choikika (“kagulu”) cha olamulira pamodzi ndi Kristu.
Chiŵerengero chenicheni cha olamulira ameneŵa, 144,000, chinavumbulidwa kwa mtumwi Yohane. (Chivumbulutso 14:1, 4) Koyambirira kwa Chivumbulutso ameneŵa akunenedwa kukhala ‘ochokera mwa mtundu uliwonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe kukhala ufumu ndi ansembe a Mulungu,’ ndipo adzalamulira dziko lapansi monga mafumu kumwamba. (Chivumbulutso 5:9, 10) Bungwe la olamulira limeneli mogwirizana ndi Yesu Kristu ndilo Ufumu umene anauza otsatira ake kupempherera. Lidzakhalanso bungwe limene adzachotsera ulamuliro woipa wa dziko lino lapansi, likumabwezeretsa chilungamo ndi mtendere pamudzi wa anthu, dziko lapansi, limodzinso ndi umoyo wosatha kwa okhalapo ake.—Salmo 37:29; Mateyu 6:9, 10.
Bungwe la Olamulira Osankhidwa
Popeza kuti maulamuliro aumunthu amene akuloŵedwa m’malo ndi Ufumuwo ali odzala chinyengo, kodi sitingaone chifukwa chake awo ophatikizidwa mu boma lakumwamba limenelo ayenera kukhala osankhidwa mosamalitsa ndi kuyesedwa ndi Mulungu? Mkhalidwe wa mtundu wa anthu pakali pano ungafaniziridwe ndi anthu mazana okwera ndege yowonongeka youluka m’mphepo yoipa. Mumkhalidwe wowopsa woterowo, kodi mungafune kuyenda ndi antchito a m’ndege achichepere, opanda chidziŵitso? Kutalitali! Mkhalidwewo ungafune antchito osankhidwa mosamalitsa malinga ndi ziyeneretso zapamwamba.
Ponena za awo amene adzatumikira kumwamba limodzi ndi Kristu Yesu, timatonthozedwa kudziŵa kuti “Mulungu anaika ziŵalo zonsezo m’thupi, monga anafuna.” (1 Akorinto 12:18) Chikhumbo cha munthu mwini kapena kulakalaka malo mu Ufumu wakumwamba sindiko muyezo wosankhira. (Mateyu 20:20-23) Miyezo yotsimikizirika ya chikhulupiriro ndi khalidwe yaikidwa ndi Mulungu kotero kuti osayenerera asatengedwe. (Yohane 6:44; Aefeso 5:5) Mawu oyamba a Ulaliki wa pa Phiri wa Yesu amasonyeza kuti olamulira anzake a Kristu ayenera kusonyeza kukhala a maganizo auzimu, oleza mtima, okonda chilungamo, achifundo, oyera mtima, ndi amtendere.—Mateyu 5:3-9; onaninso Chivumbulutso 2:10.
Chosangalatsa nchakuti, ochuluka a mtundu wa anthu, ngakhale kuti sanasankhidwe ndi Mulungu kuti akhale pakati pa bungwe loimira limeneli la olamulira lakumwamba sanasiidwe opanda chiyembekezo. Iwo adzalandira dziko lapansi lokongolali ndi kusangalala ndi mapindu a ulamuliro waumulungu umenewu. Amene anafa kalekale chifukwa cha chisalungamo chakale adzabwezeretsedwa ku moyo kudzakhala pamodzi ndi amene adzakhalabe ndi moyo kuona ‘kudza’ kwa Ufumu wa Mulungu m’lingaliro lokwanira. Lonjezo lakuti: “Owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo” lidzakwaniritsidwa.—Mateyu 6:9, 10; Miyambo 2:21; Machitidwe 24:15.