“Kuti Kasataike Kanthu”
Ndi Mtola Nkhani wa Galamukani! ku Ghana
NDINAMPEZA pamalo ake aang’ono ogwirira ntchito mu m’laga wotchedwa Labadi wa ku Accra, akugwira ntchito zolimba kucheka ndi kupala matabwa mwakugwiritsira ntchito zipangizo zakumanja. Dzina lake ndi Adams Akuetteh. Ngwazaka 70 zakubadwa ndipo wakhala wopala matabwa kwa zaka 50.
Pamene ndinamfunsa kundiuza nthaŵi imene anasangalala nayo koposa m’ntchito yake yopala matabwa, mosataya nthaŵi anati zaka zinayi zomwe anagwira ntchito pachimango cha nthambi yatsopano ya Watch Tower Society ku Nungua, Ghana. Kuchokera mu 1984 mpaka 1988.
“Kodi mumagwira ntchito yanji pachimangocho?” ndinafunsa motero.
“Ndinagwira ntchito youmba konkiri ndi kuthandiza okhoma madenga.”
“Ndiganiza kuti amakukumbukirani kwambiri,” ndinatero, “chifukwa cha misomale pachimangocho.”
“Ehede, misomali inde! Mu Ghana muno, misomali njodula kwabasi. Panthaŵiyo [theka la kilogalamu] linkachita ndalama zokwana madola aŵiri kapena atatu a ku United States. Ndiye ndinalingalira kuti, ‘Kodi sitingabwezeretse ina ya misomali imeneyi? Ndidzayesa.’
Choncho ndinayamba pandekha ndipo m’nthaŵi yanga. Pamene woyang’anira chimango anawona zimene ndinkachita, zidamkondweretsa. Basi anandigaŵira imeneyo kukhala ntchito yanga. Chotero, kwazaka zinayi, ndinkapsera pamalopo m’maŵa uliwonse ndikutolera misomali yotaikayo. Ndinasololanso imene ndinapeza m’zithabwa zosweka zoumbiramo konkhiri.”
“Kodi yobuntha ndi yokhota munaitaya?”
“Iyayi. Yobuntha inakhomedwa pa matabwa ofeŵa, kapena choboolera chinagwiritsiridwa ntchito choyamba ndiyeno nkuikhoma pamatabwa a nsita. Yokhotayo ndinaiwongola mosamalitsa ndi nyundo.”
“Kodi ntchito imodzi ndi imodzi imeneyo siinafikire kukhala yogwetsa ulesi?”
“Mwina ikanatero kwa wachichepere, koma sizinatero kwa ine ayi. Woyang’anira chimango anandiuza kuti ntchito yanga inasungitsa ndalama za Sosaite, ndalama za Yehova. Zimenezo zinandikondweretsa zedi. Ndinasangalala kwambiri kuwona mitolo ya misomali yowongoledwa yomwe ndinkakundika ikukula. Ndipo ndinkanena ndeka kuti, ‘Aha, tsopano ndawasiya okhoma denga!’ Komabe, mitoloyo inkatha mwamsanga. Ndiyeno anali kumakuwa ali padengapo kuitanira ina! Basi ndinali kuyambiranso ndi nyundo yanga kuwongola ina.”
“Kodi tsopano mukuchitanji popeza kuti chimango chinatha?”
“Ndinabwereranso muuminisitala wanthaŵi zonse, ndikuyembekezera pamene mubweranso kudzafutukula nthambi ya Ghana. Ndidzakhalako kumeneko, ndikuwongola misomali ndi kusungitsa ndalama—mwachimwemwe.”
Kwazaka zinayi anagwira ntchito imene ena angaiwone kukhala yotsika. Koma Adams Akuetteh, “wowongola misomali wa nthambi ya Ghana,” sanailingalire mwanjira imeneyo. Mwachimwemwe, anabwezeretsa misomali kusungitsa ndalama za Yehova!
Amenewo ndiwo analinso maganizo a Yesu. Ngakhale kuti anali nazo mphamvu zozizwitsa zakuchulukitsa mitanda ya mkate, anati pambuyo pa chakudya: “Sonkhanitsani makombo kuti kasataike kanthu.”—Yohane 6:12.
Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)
[Chithunzi patsamba 32]
Adams Akuetteh, “wowongola misomali wa nthambi ya Ghana”