Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/15 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndani Amene Amapita Kumwanba, ndipo Nchifukwa Ninji?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Akhristu Onse Okhulupirika Amapita Kumwamba?
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/15 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Nchiyani chimene Yesu anachita “kukonza malo” kumwamba kaamba ka atsatiri ake?

Mwamsanga asanakhazikitse Mgonero wa Ambuye, Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti iye akachokapo. Iye anatanthauza, ndithudi, kuti pambuyo pa kufa mochedwerapo tsiku limenelo, iye akayenera kupita kumwamba. Petro anavomereza mwakufunsa kuloledwa kumtsatira iye. Pamenepo Yesu anati: “Mitima yanu isavutike. Sonyezani chikhulupiriro mwa Mulungu sonyezani chikhulupiriro mwa inenso. M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali tero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha; kuti kumene kuli ineko, mukakhale inunso.”​—Yohane 14:1-3, NW.

Kodi ndi “malo” otani amene anafunikira kukonzekeredwa kaamba ka atumwiwo? Otembenuza Baibulo ena alemba Yohane 14:2 m’njira imene imalingiridwa kuti Yesu anali kulankhula ponena za atumwiwo kufuna “malo opumira” panjira yawo yopita kumwamba kapena kupeza kwawo zipinda zosiyanasiyana kumwamba. Komabe, W. E. Vine akunena ponena za liwu la Chigriki lokhudzidwalo: “Palibe chirichonse m’liwulo kusonyeza zipinda zosiyana Kumwamba; ndiponso silikulingalira malo opumulira apakanthaŵi pa msewu.” Liwulo limatanthauza kokha malo okhala. Chotero Yesu anali kulonjeza malo okhala kumwamba kwauzimu kumene iye anali kupita kukakhala ndi Atate wake.​—Aefeso 1:20; 1 Petro 1:4; 3:21, 22.

Koma kodi ndi mwanjira yotani mmene Yesu akakonzekera malo oterowo kaamba ka atsatiri ake okhulupirika? Pambuyo pa kufa imfa ya nsembe, Yesu anapita kumwamba kukapereka pamaso pa Mulungu mtengo wa moyo wa mwazi wake. Ichi poyamba chikapindulira awo omwe akatchedwa olowa m’malo a moyo wakumwamba. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti Kristu sanalowa m’malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza owonawo, komatu m’mwamba momwe, kuwonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.” (Ahebri 9:12, 24-28; Aroma 6:5; 8:17) Chotero pamene Yesu anauza atumwiwo kuti anali kupita “kukakonzekera malo” kaamba ka iwo, iye ndithudi anasunga m’malingaliro ‘kuwonekera kwake pamaso pa Mulungu’ kaamba ka iwo. Kokha pambuyo pa kuchita chimenecho ndi pamene iwo kapena anthu ena akanatha kumtsatira iye kumwamba.​—Afilipi 3:20, 21.

Kodi Yesu anafunikira kuchita zinthu zina kukonzekera malo kaamba ka iwo? Mkupita kwa nthaŵi, iye akatenga mphamvu za ufumu ndipo akamenyana ndi Satana, kumchotsa iye ndi ziwanda zake kuchoka kumwamba. (Chivumbulutso 12:7-9) Ichi chikawoneka kuchiyambi kwa kuyambika kwa chiwukiriro chakumwamba cha atumwi ndi odzozedwa ena ogona mu imfa. (1 Atesalonika 4:14-17) Kaya ndemanga ya Yesu yonena za ‘kukonzekeretsa malo’ kaamba ka atsatira ake inaphatikizapo kuchotsa Satana kumwamba, sitinganene.

M’kuwonjezerapo, sitikudziŵa ngati Yesu anali ndi mathayo ena omwe anayenera kuchita ndi kukonzekera malo kumwamba kaamba ka Akristu odzozedwa. Komabe, mwapang’ono tingakhale otsimikiza kuti Yesu anakonzekeretsa njira kaamba ka atsatiri ake odzozedwa mwakupereka kwa Mulungu mtengo wa “mwazi wake wapadera.” (1 Petro 1:19) Pa maziko a mwazi umenewo, pangano latsopano linakhazikitsidwa pakati pa Yehova Mulungu ndi Akristu odzozedwa ndi mzimu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena