Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lmd phunziro 7
  • Kuchita Khama

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchita Khama
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Paulo Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Paulo
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Paulo
  • Kudzichepetsa
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Kuchita Chidwi ndi Anthu
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Kuleza Mtima
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Kodi Tizichita Ulendo Wobwereza Pakatha Nthawi Yaitali Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd phunziro 7

ULENDO WOBWEREZA

Mtumwi Paulo akulalikira uthenga wabwino kwa anthu omwe asonkhana muholo ya pasukulu.

Machitidwe 19:8-10

PHUNZIRO 7

Kuchita Khama

Mfundo yaikulu: “Anapitiriza kuphunzitsa mwakhama . . . komanso ankalengeza uthenga wabwino.”​—Mac. 5:42.

Zomwe Paulo Anachita

Mtumwi Paulo akulalikira uthenga wabwino kwa anthu omwe asonkhana muholo ya pasukulu.

VIDIYO: Paulo Analalikira Mwakhama ku Efeso

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Machitidwe 19:8-10. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi Paulo anasonyeza bwanji khama pothandiza anthu omwe anasonyeza chidwi m’malo mogwa ulesi ndi anthu omwe ankamutsutsa?

  2. Kodi Paulo anapita maulendo angati kukathandiza anthu achidwiwa, nanga anachita zimenezi kwa nthawi yaitali bwanji?

Zomwe Tikuphunzira kwa Paulo

2. Pamafunika nthawi yokwanira komanso khama kuti tichite maulendo obwereza komanso kuyambitsa maphunziro a Baibulo.

Zomwe Mungachite Potsanzira Paulo

3. Muzibwererakonso pa nthawi yomwe ali ndi mpata. Dzifunseni kuti: Kodi malo komanso nthawi yabwino kwambiri yomwe ndingamupeze ingakhale iti? Kodi iye adzapeza mpata liti? Khalani okonzeka kubwererakonso ngakhale kuti nthawiyo si yabwino kwa inu.

4. Muzipangana nthawi yoti mudzachezenso. Pambuyo pa ulendo uliwonse, kambiranani nthawi yeniyeni yomwe mungadzachezenso naye. Yesetsani kudzakumana naye pa nthawi yomwe mwagwirizanayo.

5. Musamataye mtima msanga. Musamathamangire kuganiza kuti ngati sapezekapezeka pakhomo komanso chifukwa choti amakhala wotanganidwa ndiye kuti basi alibe chidwi. (1 Akor. 13:4, 7) M’malomwake, yesetsanibe kumuyendera. Koma onetsetsani kuti mukugwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru.​—1 Akor. 9:26.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mac. 10:42; 1 Akor. 9:22, 23; 2 Akor. 4:1; Agal. 6:9

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena