Kodi Tizichita Ulendo Wobwereza Pakatha Nthawi Yaitali Bwanji?
1. Kodi kupanga ophunzira kumaphatikizapo kuchita chiyani?
1 Ntchito yopanga ophunzira imaphatikizapo kubwerera kwa aliyense amene wasonyeza kuti akufunitsitsa kuphunzira za Ufumu wa Yehova. (Mat. 28:19, 20) Kawirikawiri nthawi yabwino kupanga ulendo wobwereza imadalira mmene inuyo ndi munthu wachidwiyo mumapezera mpata. N’chifukwa chiyani pa ulendo woyamba tikapeza anthu chidwi tiyenera kubwerera mwansanga?
2, 3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kubwerera mwansanga kwa anthu achidwi?
2 N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kubwerera Mwansanga? Ntchito yolalikira “uthenga wabwino uwu wa ufumu” yatsala pang’ono kutha, ndiponso mapeto a dongosolo lino la zinthu ali pafupi kwambiri. (Mat. 24:14; 1 Pet. 4:7) Choncho pamene tidakali mu “tsiku la chipulumutso,” ndipo anthu achidwi adakalipobe, tiyenera kutsatira malangizo akuti ‘tilalike mawu mwachangu.’ Zimenezi zikuphatikizapo kubwerera mwansanga kwa anthu achidwi, chidwi chawo chisanathe.—2 Akor. 6:1, 2; 2 Tim. 4:2.
3 Satana akufunitsitsa kuononga mbewu ya Ufumu iliyonse imene tingadzale m’mitima ya anthu a chidwi. (Maliko 4:14, 15) Nthawi zambiri anthu amene asonyeza kuti ali ndi chidwi amanyozedwa ndi achibale awo, ogwira nawo ntchito ndi anthu ena. Choncho kubwerera mwansanga kwa anthu amenewa kumathandiza kuti tikapitirize kukambirana nawo zimene tinakambirana nawo paulendo woyamba, anthu ena asanawasokoneze.
4. Kodi n’chiyani chimene tingachite pa ulendo woyamba pofuna kuti tichite ulendo wobwereza?
4 Gwirizanani Zodzakumanso: Musanasiyane pa ulendo woyamba, mungachite bwino kutsimikizirana zoti mudzakumanenso. Funsani funso loti mudzayankhe pa ulendo wotsatira. Kulemba zimene mwagwirizana ndi kuzisunga n’kofunika. Ngati muli ndi mpata, mungathe kupempha kuti mubwerere tsiku lotsatira kapena tsiku lina lapafupi. Ngati mwachita ulendo woyamba kumapeto kwa mlungu ndipo munthu wachidwiyo amagwira ntchito mkati mwa mlungu, mwina angalole kuti mudzamuyenderenso kumapeto kwa mlungu wotsatira. Mukagwirizana zodzakumananso, yesetsani kukwaniritsa lonjezo lanu.—Mat. 5:37.
5. Kodi kubwerera mwansanga kwa anthu achidwi kungatithandize bwanji kukwaniritsa ntchito yopanga ophunzira imene Yesu anatilamula?
5 Tili ndi zifukwa zabwino zotilimbikitsa kubwerera mwansanga kwa anthu achidwi. Choncho, muzigwirizana zodzakumananso ndipo muzibwerera mwansanga, chifukwa “nthawi yotsalayi yafupika.” (1 Akor. 7:29) Tikamabwerera mwansanga kwa anthu amene achita chidwi ndi uthenga wa Ufumu, n’zosakayikitsa kuti khama lathu lidzapindula kwambiri.