Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzisiya Funso Loti Mudzakambirane pa Ulendo Wotsatira
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’Kofunika? Tikapeza munthu wachidwi, tiyenera kupitakonso n’cholinga choti tikathirire mbewu za choonadi zimene tinadzala pa ulendo woyamba. (1 Akor. 3:6) Kuti zimenezi zitheke, timafunika kusiya funso loti tidzakambirane pa ulendo wotsatira komanso kugwirizana tsiku ndi nthawi. Zimenezi zingachititse kuti munthuyo adzakhalenso ndi chidwi pa ulendo wotsatira. Komanso ngati yankho la funso lomwe tamusiyiralo lili m’magazini kapena m’kapepala komwe tamupatsa, zingapangitse kuti awerenge magazini kapena kapepalako. Kusiya funso loti mudzayankhe pa ulendo wotsatira, kumathandizanso kuti inuyo musadzasowe poyambira komanso kuti munthuyo azidziwiratu nkhani yomwe mudzakambirane. Tikam’peza, tingamuuze kuti tabwera kudzayankha funso lomwe tinasiya lija, ndipo kenako tingapitirize.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Mukamakonzekera ulaliki, konzekeraninso funso loti mukafunse munthuyo n’cholinga choti mudzalikambirane pa ulendo wotsatira. Uzani munthu amene mwayenda naye funso lomwe mwakonzekeralo.