Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 November tsamba 3
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Kupanga Ulendo Wobwereza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Kupanga Ulendo Wobwereza
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzisiya Funso Loti Mudzakambirane pa Ulendo Wotsatira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzisiya Mafunso Oti Mudzakambirane Ulendo Wotsatira
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Kukonzekera ndi Chinsinsi cha Maulendo Obwereza Aphindu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 11
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 November tsamba 3

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki Kupanga Ulendo Wobwereza

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Anthu ambiri amene amachita chidwi ndi uthenga wa Ufumu amakhala akufuna kudziwa choonadi chonena za Mulungu. (Yes. 55:6) Choncho, kuti tithe kuwaphunzitsa bwino tiyenera kupitako mobwerezabwereza. Popeza anthu akukumana ndi mavuto osiyanasiyana, njira zimene tingagwiritsire ntchito powathandiza kuti akhalebe ndi chidwi zingakhalenso zosiyanasiyana. Komabe kuti tizipanga maulendo obwereza ogwira mtima, tiyenera kumakonzekera bwino ndiponso tizikhala ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.

Mlongo akukonzekera ulendo wobwereza

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

Alongo awiri akuchita ulendo wobwereza ndipo akuonetsa vidiyo
  • Muziyesetsa kupanga ulendo wobwereza mwansanga, mwina pakangodutsa masiku ochepa.​—Mat. 13:19

  • Muzikhala aubwenzi, aulemu ndiponso muzikhala womasuka

  • Muziyamba n’kupereka moni wansangala ndiponso muzimutchula dzina munthuyo. Muzimukumbutsa zimene mwabwerera. Mwachitsanzo mungamuuze kuti mukudzayankha funso, kudzamupatsa magazini, kudzamusonyeza webusaiti yathu, kudzamuonetsa vidiyo kapena kudzamusonyeza mmene timaphunzirira Baibulo. Muzisintha ulaliki wanu ngati munthuyo wasonyeza kuti pali zina zimene zikumudetsa nkhawa.​—Afil. 2:4

  • Muzimuwerengera lemba, kumupatsa buku kapenanso magazini n’cholinga choti muthirire mbewu ya choonadi imene ikumera mumtima mwake. (1 Akor. 3:6) Muziyesetsanso kuchita zinthu zosonyeza kuti mukufuna akhale mnzanu

  • Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena