‘Lankhulani Mawu a Mulungu Molimbika Mtima’
YEHOVA Mulungu angapatse mphamvu atumiki ake ‘kulankhula Mawu a Mulungu molimbika mtima.’ (Machitidwe 4:31) Ngakhale awo omwe ali achichepere m’njira za chowonadi cha Baibulo ndi osazoloŵera mu ntchito yolengeza safunikira kukhala adwachedwache m’kulankhula mbiri yabwino molimbika mtima. Mu Côte d’Ivoire, ofalitsa aŵiri a mbiri yabwino anali mu utumiki wa kukhomo ndi khomo pamene anakumana ndi profesa wa pa yunivesiti. Mboni yachichepereyo, Seriki, podzimva wosafikapo kulankhula kwa munthu wophunzira woteroyo, analola Mboni inayo kulankhula.
Profesayo anavutitsidwa ndi kunyada kwaufuko ndipo anapatsa Mulungu mlandu wa mavuto aufuko omwe alipo, akumalingalira kuti ndiye amene analenga mafuko osiyanasiyana. Pambuyo pa kukambitsirana kwakutali komwe kunawoneka kukhala kosaphula kanthu, Seriki pomalizira pake analimba mtima kuti alankhule, ndipo mwaulemu anawagwira pakamwa. (1 Atesalonika 2:2) Powona mmene nyumba ya profesayo inakometsedwera ndi mitundu yabwino yokhumbirika, Seriki anafunsa profesayo kuti, “Kodi nchifukwa ninji simunapange nyumba yanu yonseyi kukhala ndi mtundu umodzi?”
“Ukuganiza kuti ndine wopenga eti!” adayankha mwa nchinyulira profesayo. Seriki anayankha nati: “Ayi, koma kodi nchifukwa ninji tingayembekezere Mulungu kupanga chirichonse ndi aliyense mu mtundu wofanana?” Nsongayo inali yomveka. Fanizo lopepuka limenelo linakhala lokhutiritsa, ndipo umboni wabwino unaperekedwa ndi Seriki yemwe poyambapo anali wamantha.