Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • hb tsamba 22-26
  • Mwazi Umene Umapulumutsadi Miyoyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwazi Umene Umapulumutsadi Miyoyo
  • Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MWAZI WOKHA UMENE ULI WOPULUMUTSA MOYO
  • SANGALALANI NDI MOYO WOPULUMUTSIDWA NDI MWAZI
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Mwazi—Wofunika Koposa Kaamba ka Moyo
    Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
Onani Zambiri
Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
hb tsamba 22-26

Mwazi Umene Umapulumutsadi Miyoyo

Mfundo zina nzomvekera bwino kuchokera m’mawu apitawo. Ngakhale kuti anthu ambiri amalingalira kukhala kopulumutsa moyo, kuthirira mwazi nkodzaza maupandu. Chaka chirichonse zikwi zambiri zimafa chifukwa cha kuthiriridwa mwazi; maunyinji ena amadwala kwambiri ndi kuyang’anizana ndi zotulukapo zanthaŵi yaitali. Motero, ngakhale mwalingaliro la kuthupi, pali nzeru kuyambira pakali pano kulabadira lamulo Labaibulo la ‘kusala mwazi.’—Machitidwe 15:28, 29.

Odwala amatetezeredwa kumaupandu ambiri ngati iwo apempha chisamaliro cha mankhwala chopanda mwazi. Madokotala aluso amene avomera kulandira pempho la kugwiritsira ntchito zimenezi pa Mboni za Yehova akulitsa muyezo wa mchitidwe umene uli wopanda upandu ndi wabwino, monga momwe kwatsimikiziridwira m’malipoti osaŵerengeka azamankhwala. Madokotala amene amapereka chisamaliro chabwino popanda mwazi sakulumpha njira zamankhwala zofunika. Mmalo mwake, amalemekeza kuyenera kwa wodwala kwa kudziŵa maupandu ndi mapindu kotero kuti angapange chosankha chanzeru ponena za chimene chidzachitidwa kuthupi lake ndi moyo.

Sitikukhala osadziŵa pankhaniyi, pakuti tikuzindikira kuti sionse amene adzavomerezana ndi njira imeneyi. Anthu amasiyana ponena za chikumbumtima, makhalidwe, ndi lingaliro lamankhwala. Chifukwa cha chimenecho, ena, kuphatikizapo madokotala ena angawone kukhala kovuta kulandira chosankha cha wodwala cha kusala mwazi. Dokotala wina wa opaleshoni wa ku New York analemba kuti: “Sindidzaiŵala zaka 15 zapitazo, monga dokotala wachichepere amene akutsiriza kumene maphunziro pamene ndinaima pambali pabedi wa Mboni ya Yehova ina imene inahcucha mwazi kuchokera m’chironda cha mmimba kufikira imfa. Zifuno za wodwalayo zinachitiridwa ulemu ndipo kuthirira mwazi sikunaperekedwe, koma ndingakumbukirebe kugwiritsidwa mwala kwakukuluko kumene ndinamva monga dokotala.”

Mosakayikira iye anakhulupilira kuti mwazi ukanakhala wopulumutsa moyo. Komabe, chaka chimodzi atalemba zimenezo, The British Journal of Surgery (October 1986) inasimba kuti poyambilira kuchochitika cha kuthiriridwa mwazi, kuchucha m’matumbo kunali ndi “mlingo wa imfa wa 2.5 peresenti chabe.” Chiyambire pamene kuthirira mwazi kunakhala kwachizoloŵezi, ‘mapendedwe aakulu koposa amasimba imfa 10 peresenti.’ Kodi nchifukwa ninji mlingo wa imfa wokwera kuŵirikiza kanayi? Ofufuzawo anapereka lingaliro lakuti: “Kuthiriridwa mwazi koyambilira kukuwonekera kukhala kukusinthitsa mchitidwe wa kuumitsa magazi kumka kukuchucha magazi motero kukumachititsa kuchuchanso.” Pamene Mboni yokhala ndi chironda chochucha mwazi inakana mwazi, chosankha chakecho kwenikweni chingakhale chitakulitsa ziyembekezo zake za kuchira.

Dokotala wa opaleshoni mmodzimodziyu anatinso: “Kupita kwa nthaŵi ndi kusamalira odwala ambiri ziri ndi chikhotelero cha kusintha lingaliro la munthu, ndipo lerolino ndikupeza chidaliro cha pakati pa wodwala ndi dokotala wake, ndi thayo la kulemekeza zifuno za wodwala kukhala zofunika koposa luso lamakhwala latsopano limene likutizinga. . . . Nkokondweretsa kuti kugwiritsidwa mwala kwachoka tsopano ndi kuloŵedwa m’malo ndi lingaliro la kulemekeza kwakukulu ndi ulemu kaamba ka chikhulupiliro cholimba cha wodwala.” Dokotalayo anamaliza ndi kuti: ‘Zimandikumbutsa kuti nthaŵi zonse ndiyenera kulemekeza zofuna zamunthu mwini ndi zachipembedzo mosasamala kanthu za malingaliro anga kapena zotulukapo zake.’

Mungakhale mukudziŵa kale za kanthu kena kamene madokotala ambiri amafika pakuzindikira mwa “kupita kwanthaŵi ndi kusamalira odwala ambiri.” Ngakhale ndi chisamaliro chabwino koposa chamankhwala m’zipatala zabwino kwambiri, pamfundo ina anthu amafa. Othiriridwa mwazi kapena ayi, onse amafa. Tonsefe tikukalamba, ndipo mapeto a moyo akuyandikira. Kumeneko sindiko kufuna imfa. Ndicho chinthu chotsimikizirika. Kufa ndiko chotsimikizirika cha moyo.’

Umboni umasonyeza kuti anthu amene amanyalanyaza lamulo la Mulungu la mwazi kaŵirikaŵiri amawona chivulazo chamwamsanga kapena chochedwerapo; ena amafadi ndi mwazi. Awo amene amachira sanapeza moyo wosatha. Motero kuthiriridwa mwazi sikumapulumutsa miyoyo kwanthaŵi yonse.

Anthu ochuluka amene, kaamba ka zifukwa zachipembedzo ndi/kapena zamankhwala, amakana mwazi koma nalandira mankhwala ena akuchipatala amachira bwino kwambira. Motero iwo angatalikitse moyo wawo kwazaka zingapo. Komaosati kwamuyaya.

Chakuti anthu onse ngopanda ungwiro ndipo amafa mwapang’onopang’ono kumatitsogolera kuchowonadi chachikulu cha zimene Baibulo limanena ponena za mwazi. Ngati timvetsetsa ndi kuzindikira chowonadi chimenechi, tidzawona mmene mwazi ungapulumutsiredi moyo—moyo wathu—kosatha.

MWAZI WOKHA UMENE ULI WOPULUMUTSA MOYO

Monga mmene kwawonedwera pachiyambipo, Mulungu anauza anthu onse kuti sayenera kudya mwazi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mwazi umaimira moyo. (Genesis 9:3-6) Iye anafotokoza zimenezi mowonjezereka mumpambo Wachilamulo woperekedwa kwa Israyeli. Panthaŵi imene mpambo Wachilamulo unayambitsidwa kugwira ntchito, mwazi wa nyama zoperekedwa nsembe ungwiritsiridwa ntchito paguwa la nsembe. (Eksodo 24:3-8) Malamulo a mumpambo umenewo anasonyeza cheni cheni chakuti anthu onse ngopanda ungwiro; ngauchimo, monga mmene Baibulo limanenera. Mulungu anauza Aisrayeli kuti mwanjira ya nsembe zanyama zoperekedwa kwa iye, iwo akatha kuzindikira kufunika kwa kuchititsa machimo awo kuphimbidwa. (Levitiko 4:4-7, 13-18, 22-30) Zowona, zimenezo ndizo zimene Mulungu anawapempha panthaŵiyo kumbuyoko, osati zimene iye akupempha olambira owona lerolino.

Mulungu mwiniyo anafotokoza tanthauzo la kutseri kwa nsembe zimenezo: “Moyo wa nyama [kapena, mphamvu ya moyo] uli m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu paguwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake. Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu.”—Levitiko 17:11, 12.

Paphwando lakale lotchedwa Tsiku Lotetezera, mkulu wa ansembe wa Israyeli anatengera mwazi wa nyama zoperekedwa nsembe mkati mwa chigawo cha kachisi chopatulika koposa, paphata la kulambiridwa kwa Mululngu. Kuchita zimenezo kunali njira yophiphiritsira yopempha Mulungu kuphimba machimo a anthu. (Levitiko 16:3-6, 11-16) Nsembe zimenezo sizinachotse kwenikweni machimo onse, motero zinafunikira kubwerezedwa chaka chirichonse. Chikhalirechobe, kugwiritsiridwa ntchito kumeneku kwa mwazi kunakhazikitsa chitsanzo cha tanthauzo.

Chiphunzitso chachikulu m’Baibulo nchakuti Mulungu akapereka nsembe yangwiro potsirizira pake imene ikachotsa kotheratu machimo a okhulupilira onse. Imeneyi imatchedwa dipo, ndipo imasumika pansembe ya Mesiya wonenedweratuyo, kapena Kristu.

Baibulo limayerekezerea ntchito ya Mesiya ndi zimene zinachitidwa pa Tsiku Lotetezera kuti: “Koma atafika Kristu, Mkulu wansembe wa zokoma zirinkudza, mwa [chihema] chachikulu ndi chagwiro choposa, chosamangika ndi manja, . . . chosati cha chilengedwe ichi, kapena mwa mwazi wambuzi ndi ana a ng’ombe, koma mwa mwazi wa iye yekha, analoŵa kamodzi kumalo opatulika [kumwamba], atalandirapo chiombolo chosatha. Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang’ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.”—Ahebri 9:11, 12, 22.

Motero kukukhala kwachiwonekere chifukwa chake tifunikira kukhala ndi lingaliro la Mulungu la mwazi. Mogwirizana ndi kuyenera kwake monga Mlengi, iye watsimikizira kugwiritsiridwa ntchito kwake kokha. Aisrayeli akale angkhale atapeza mapindu a moyo wabwino mwa kusadya mwazi wa nyama kapena wa munthu, koma zimenezo sizinali mfundo yofunika koposa. (Yesaya 48:17) Iwo anafunikira kupeŵa kuchirikiza miyoyo yawo ndi mwazi, kwakukulukulu sichinali chifukwa chakuti kuchitira mwina kunali koipa, koma chifukwa chakuti kunali chidetso kwa Mulungu. Iwo anafunikira kusala mwazi, osati chifukwa chakuti unali woipitsidwa, koma chifukwa chakuti unali wamtengo wapatali m’kupezea chikhululukiro.

Mtumwi Paulo anafotokoza ponena za dipo kuti: “Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wake [Kristu], chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemelera kwa chisomo chake.” (Aefeso 1:7) Liwu Lachigiriki loyambila lopezedwa pamenepo latembenuzidwa bwino lomwe “mwazi,” koma chiŵerengero cha mamasuliridwe ena a Baibulo chimalakwitsa mwa kuloŵetsa liwulo “imfa” m’malo mwake. Chifukwa cha chimenecho, oŵerenga angaphonye chigogomezero palingaliro la Mlengi wathu la mwazi ndi mtengo wa nsembe umene iye wagwirizana nawo.

Mutu waukulu wa Baibulo umasumika za chenicheni chakuti Kristu anafa monga nsembe ya dipo yangwiro koma iye sanakhalebe wakufa. Motsatira chitsanzo chimene Mulungu anakhazikitsa pa Tsiku Lotetezera, Yesu anaukitsidwira kumwamba “kukawonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.” Kumeneko iye anapereka mtengo wa mwazi wake wa nsembe. (Ahebri 9:24) Baibulo limagogomezera kuti tiyenera kupeŵa njira iriyonse imene ikachititsa ‘kuponderezedwa kwa Mwana wa Mulungu ndi kuyesa mwazi wake monga wa phindu losanunkha kanthu.’ Motero tisungeto kokha unansi wabwino ndi mtendere ndi Mulungu.—Ahebri 10:29; Akolose 1:20.

SANGALALANI NDI MOYO WOPULUMUTSIDWA NDI MWAZI

Pamene tizindikira zimene Mulungu amanena ponena za mwazi, timafika pakukhala ndi ulemu waukulu koposa kaamba ka mtengo wake wopulumutsa moyo. Malemba amafotokoza Kristu monga munthu amene ‘amatikonda ndi amene anatimasula kuuchimo mwanjira ya mwazi wa iye mwini.’ (Chivumbulutso 1:5; Yohane 3:16) Inde, mwanjira ya mwazi wa Yesu, tingapeze chikhululukiro chokwanira ndi chosantha cha machimo athu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Popeza tinayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa iyeyo.” Mmenemo ndimo mmene moyo wosatha ungapulumutsidwire ndi mwazi.—Aroma 5:9; Ahebri 9:14.

Kalekale Yehova Mulungu anapereka chitsimikiziro chakuti kupyolera mwa Kristu ‘mabanja onse a padziko lapansi angathe kudzidalitsa.’ (Genesis 22:18) Dalitso limenelo limaphatikizapo kubwezeretsa dziko lapansi ku paradaiso. Pamenepo anthu okhulupilira sadzakanthidwanso ndi matenda, ukalamba, kapena ngakhale imfa; adzasangalala ndi madalitso amene amapambana kotheratu chithandizo chakanthaŵi chimene ogwira ntchito zamankhwala angatipatse tsopano. Tiri ndi lonjezo lodabwitsa ili: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

Pamenepo, nkwanzeru chotani nanga, kwa ife kulabadira zofunikira zonse za Mulungu! Zimenezo zimaphatikizapo kumvera malamulo ake onena za mwazi, kusaugwiritsira ntchito molakwa ngakhale m’mikhalidwe ya zamankhwala, Motero ife sitidzakhala ndi moyo kwakanthaŵi chabe. Mmalo mwake, tidzasonyeza ulemu wathu waukulu kaamba ka moyo, kuphatikizapo chiyembekzeo chathu chamtsogolo cha moyo wosatha muungwiro waumunthu.

[Bokosi patsamba 25]

Anthu a Mulungu anakana kuchirikiza miyoyo yawo ndi mwazi, osati chifukwa chakuti kuchita zimenezo kunali koipa, koma chifukwa chakuti kunali chidetso, osati chifukwa chakuti mwazi unali woipitsidwa, koma chifukwa chakuti unali wamtengo wapatali.

[Chithunzi patsamba 24]

“Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wake [Yesu], chikhululukiro cha zochimwa.”—Aefeso 1:7

[Chithunzi patsamba 26]

Kupulumutsa moyo ndi mwazi wa Yesu kumatsegula njira ya kumoyo wosatha, wathanzi m’paradaiso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena