Kodi Mulungu Anaikiratu za Mtsogolo Mwathu?
“MAVUTO ambiri ongoganizira akanapeŵedwa ngati liwu lomvedwa molakwa lakuti kuikiratu za mtsogolo silikanatchulidwa nkomwe.” Inu mungadabwe chifukwa chake, ngati mumalitchula liwu lakutilo “kuikiratu za mtsogolo” kapena ngati mwalimvapo likutchulidwa.
Malinga ndi kunena kwa insaikulopediya Yachifrenchi yaposachedwa Yachikatolika yotchedwa Théo, tingachite bwino kwambiri kusagwiritsira ntchito liwu lakuti “kuikiratu za mtsogolo.” Buku lina limati: “Zikuoneka kuti nkhani ya kuikiratu za mtsogolo sindiyonso nkhani yaikulu lerolino m’mikangano ya zaumulungu, ngakhale kwa Aprotesitanti ambiri.”
Komabe, nkhani imeneyi ya kuikiratu za mtsogolo yasokoneza anthu ambiri m’mbiri yonse. Inali mfundo yaikulu ya mkangano umene unayambitsa Nyengo ya Kukonzanso, ndipo ngakhale mkati mwa Tchalitchi cha Katolika, inali nkhani ya mkangano wowopsa wa zaka mazana ambiri. Ngakhale kuti siili ya mkangano kwambiri lerolino, idakali vuto. Kodi ndani amene sangafune kudziŵa kaya ngati za mtsogolo mwake zinaikidwiratu?
Kuikiratu za Mtsogolo —Tanthauzo la Liwuli
Kodi liwulo lakuti “kuikiratu za mtsogolo” limatanthauzanji m’matchalitchi? Dictionnaire de théologie catholique imalifotokoza kukhala “chifuno cha Mulungu cha kupatsa moyo wosatha kwa anthu ena, otchulidwa maina.” Kwakukulukulu zimalingaliridwa kuti osankhidwawo, “otchulidwa maina,” ndiwo akunenedwa ndi mtumwi Paulo m’kalata yake kwa Aroma, m’mawu aŵa: “Mulungu amachita zabwino kwa amene amukonda, amene amaitanidwa mogwirizana ndi chifuno chake. Pakuti amene anawadziŵiratu anawaikiratu za mtsogolo mwawo kuti adzagwirizanitsidwe ndi chithunzi cha Mwana wake . . . Ndipo amene anawaikiratu za mtsogolo mwawo anawaitananso; ndipo amene anawaitana anawalungamitsa; ndipo amene anawalungamitsa anawapatsanso ulemerero.”—Aroma 8:28-30, Revised Standard Version.
Anthu ena amalingaliridwa kuti Mulungu anawasankhiratu asanabadwe nkomwe, kuti akakhale ndi Yesu mu ulemerero wakumwamba. Zimenezi zimabutsa funso limene lachititsa mkangano kwa nthaŵi yaitali: Kodi Mulungu kwenikweni amasankha amene afuna kuwapulumutsa, kapena kodi anthu ali ndi ufulu wa kusankha ndi kufunikira kwa kuchitapo kanthu kuti apeze chiyanjo cha Mulungu ndi kuchisunga?
Augustine, Woyambitsa Chiphunzitso cha Kuikiratu za Mtsogolo
Ngakhale kuti Abambo a Tchalitchi ena anali atalembapo kale za kuikiratu za mtsogolo, Augustine (354-430 C.E.) amalingaliridwa ndi ambiri kuti ndiye anayalira maziko a chiphunzitsocho tchalitchi cha Katolika ndi cha Protesitanti chomwe. Malinga ndi kunena kwa Augustine, olungama anaikidwiratu ndi Mulungu kuyambira kunthaŵi zosayamba kuti akalandire madalitso osatha. Ndiyeno, osalungama, ngakhale kuti sanaikidwiretu ndi Mulungu m’lingaliro lenileni la liwulo, adzalandira chilango chowayenera kaamba ka machimo awo, chiweruzo. Kafotokozedwe ka Augustine kanasiya malo ochepa a ufulu wa kusankha, kakumabutsa mikangano yochuluka.
Oloŵa m’Malo a Augustine
Mkangano wa nkhani ya kuikiratu za mtsogolo ndi ufulu wa kusankha unabukanso nthaŵi ndi nthaŵi m’Nyengo Zapakati, ndipo unafika pachimake mkati mwa Nyengo ya Kukonzanso. Luther anaona kuikiratu za mtsogolo mwa munthu mmodzi ndi mmodzi kukhala chosankha cha Mulungu mwini, popanda Iye kuoneratu zochita kapena ntchito zabwino za mtsogolo za osankhidwawo. Calvin anafika pa ganizo losiyana kwambiri pokhala ndi lingaliro lake la kuikiratu za mtsogolo kwa mbali ziŵiri: Ena amaikidwiratu ku chipulumutso chamuyaya, ndipo ena ku chiweruzo chamuyaya. Komabe, Calvin nayenso anaona chosankha cha Mulungu kukhala chifuniro chake, ngakhale chosazindikirika.
Nkhani ya kuikiratu za mtsogolo ndi yofanana nayo kwambiri ya “chisomo”—liwu logwiritsiridwa ntchito ndi matchalitchi kunena kachitidwe kamene Mulungu amapulumutsira anthu ndi kuwayesa olungama—inakhala yaikulu kwambiri kwakuti mu 1611 ofesi ya Chikatolika ya Holy See inaletsa chilichonse kufalitsidwa ponena za nkhaniyo popanda chilolezo chake. Mkati mwenimwenimo mwa Tchalitchi cha Katolika, ziphunzitso za Augustine zinachirikizidwa mwamphamvu ndi otsatira Jansen Achifrenchi a m’zaka za zana la 17 ndi la 18. Iwo anachirikiza mtundu wa Chikristu chokhwimitsa ndi cha ophunzira ndipo analinso ndi otsatira pakati pa olamulira apamwamba. Komabe, mkangano wa nkhaniyo sunathe. Mfumu Louis XIV analamula kuwonongedwa kwa nyumba yokhalamo achipembedzo ya Port-Royal, kumene kunayambira chiphunzitso cha kutsatira Jansen.
Mkati mwenimwenimo mwa matchalitchi Okonzedwanso Achiprotesitanti, nkhaniyo inali kutali kwambiri ndi kutha. Limodzi ndi ena, Aremonstranti, amene anatsatira Jacobus Arminius, anakhulupirira kuti munthu afunikira kuchitapo kanthu kuti apulumuke. Msonkhano wa atsogoleri a Chiprotesitanti wa ku Dordrecht (1618-19) unathetsa nkhaniyo kwa kanthaŵi pamene unayambitsa mtundu wokhwimitsa wa kusunga mwambo kwa Calvin. Malinga ndi kunena kwa buku lakuti L’Aventure de la Réforme—Le monde de Jean Calvin, mu Germany mkangano umenewu wa nkhani ya kuikiratu za mtsogolo ndi ufulu wa kusankha unadzetsa nyengo yaitali ya “zoyesayesa zosaphula kanthu za kuyanjanitsa, limodzinso ndi nkhanza, kuponyedwa m’ndende, ndi kuletsedwa kwa ophunzitsa zaumulungu.”
Kuikiratu za Mtsogolo Kapena Ufulu wa Kusankha?
Kuyambira pachiyambi, malingaliro aŵiri osiyana kotheratu ameneŵa, kuikiratu za mtsogolo ndi ufulu wa kusankha, abutsa mikangano yowopsa yambiri. Augustine iye mwiniyo analephera kufotokoza kusagwirizana kumeneku. Calvin nayenso anakuona kukhala chosankha cholemekezeka cha Mulungu, motero anakuonanso kukhala kosamvetsetseka.
Koma kodi vumbulutso la Baibulo la mikhalidwe ya Mulungu ndi umunthu wake limatithandiza kumvetsetsa mafunso ameneŵa bwino lomwe? Nkhani yotsatira idzapenda mfundo zimenezi mwatsatanetsatane.
[Zithunzi patsamba 4]
Calvin
Luther
Jansen
[Mawu a Chithunzi]
Zithunzi: Bibliothèque Nationale, Paris