Kodi Kuikiratu za Mtsogolo Kungagwirizanitsidwe ndi Chikondi cha Mulungu?
“TIMATANTHAUZIRA kuikiratu za mtsogolo kukhala makonzedwe amuyaya a Mulungu, a kulinganiziratu zimene akufuna kuchita ndi munthu aliyense. Pakuti iye sanawalenge onse mumkhalidwe umodzimodzi, koma amaikiratu ena ku moyo wamuyaya ndi ena ku chiweruzo chamuyaya.”
Ndi mmene wochirikiza Kukonzanso Wachiprotesitanti John Calvin analongosolera lingaliro lake la kuikiratu za mtsogolo m’buku lakuti Institutes of the Christian Religion. Lingaliro limeneli nlozikidwa pa ganizo lakuti Mulungu amadziŵa zonse ndi kuti zochita za zolengedwa zake sizingachititse zifuno zake kukhala zosayenera kapena kumkakamiza kusintha zinthu.
Koma kodi zimenezi nzimenedi Baibulo limatanthauza ponena za Mulungu? Makamaka, kodi malongosoledwe otero amagwirizana ndi mikhalidwe ya Mulungu, makamaka mkhalidwe wake waukulu koposa—chikondi?
Mulungu Wokhoza Kuneneratu za Mtsogolo
Mulungu akhoza kuneneratu za mtsogolo. Iye amadzilongosola kukhala wokhoza ‘kulalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthaŵi zakale anena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.’ (Yesaya 46:10) M’mbiri yonse ya munthu, Mulungu walembetsa maulosi ake kuti asonyeze kuti iye akhoza kugwiritsira ntchito chidziŵitso chake cha za mtsogolo ndi kuneneratu zochitika.
Chotero, m’masiku a Belisazara, mfumu ya Babulo, pamene mneneri Danieli analota loto la zilombo ziŵiri, china chikumagonjetsa chinzake, Yehova anampatsa mamasuliridwe ake: “Nkhosa yamphongo waiona ya nyanga ziŵiri ndizo mafumu a Mediya ndi Perisiya. Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Helene.” (Danieli 8:20, 21) Mwachionekere, Mulungu anagwiritsira ntchito chidziŵitso chake cha za mtsogolo povumbula kuloŵana m’malo kwa maulamuliro aakulu a dziko. Ufumu wa Babulo wolamulira panthaŵiyo ukaloŵedwa m’malo ndi Amedi ndi Aperisi ndiyeno Girisi.
Maulosi angakhalenso onena za munthu mmodzi. Mwachitsanzo, mneneri Mika analengeza kuti Mesiya akabadwira m’Betelehemu. (Mika 5:2) Ndiponso, m’chochitika chimenechi Mulungu anagwiritsira ntchito chidziŵitso chake cha za mtsogolo. Komabe, chochitika chimenechi chinalengezedwa ndi chifuno chapadera—kudziŵikitsa Mesiya. Chochitika chimenechi sichimavomereza chiphunzitso cha kuikiratu za mtsogolo chophatikizamo munthu aliyense.
Mosiyana ndi zimenezo, Malemba amasonyeza kuti pali mikhalidwe mwa imene Mulungu amasankha kusadziŵiratu zotulukapo. Chiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora chitakhala pafupi, iye analengeza kuti: “Ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziŵa.” (Genesis 18:21) Lembali limatisonyeza bwino lomwe kuti Mulungu sanadziŵiretu ukulu wa mikhalidwe yonyansa m’mizinda imeneyo asanafufuze zinthu.
Zoona, Mulungu akhoza kuoneratu zochitika zina, koma nthaŵi zambiri, iye wasankha kusagwiritsira ntchito chidziŵitso chake cha za mtsogolo. Chifukwa chakuti Mulungu ali wamphamvuyonse, ali ndi ufulu wa kugwiritsira ntchito maluso ake mmene iye angafunire, osati motsatira zofuna za anthu opanda ungwiro.
Mulungu Amene Angawongolere Zinthu
Monga momwe anachitira Calvin, ena amanena kuti Mulungu analinganiziratu kuchimwa kwa munthu asanamulenge ndi kuti anali ataikiratu ‘osankhika’ kuchimwako kusanachitike. Koma ngati kuti zimenezi zinali zoona, kodi sikukakhala chinyengo cha Mulungu kupereka chiyembekezo cha moyo wosatha kwa Adamu ndi Hava, akumadziŵa bwino lomwe kuti iwo sakakhoza kuchifikira? Ndiponso, palibe paliponse pamene Malemba amakana kuti anthu aŵiri oyamba sanapatsidwe chosankha: kaya kutsatira malangizo a Mulungu ndi kukhala ndi moyo kosatha kapena kuwakana ndi kufa.—Genesis, chaputala 2.
Koma kodi tchimo la Adamu ndi Hava linalepheretsadi chifuno cha Mulungu? Iyayi, pakuti iwo atangochimwa, Mulungu analengeza kuti akautsa “mbewu” imene ikawononga Satana ndi atumiki ake ndi kuti akawongoleranso zinthu pa dziko lapansi. Monga momwe tizilombo tating’ono sitingaletsere mlimi kututa mbewu zochuluka, moteronso kusamvera kwa Adamu ndi Hava sikudzaletsa Mulungu kupanga dzikoli paradaiso.—Genesis, chaputala 3.
Pambuyo pake Mulungu anavumbula kuti pakakhala boma la Ufumu loikidwa m’manja mwa mbadwa ya Mfumu Davide ndi kuti ena akagwirizana nayo mu Ufumu umenewu. Enawo akutchedwa “opatulika a Wam’mwambamwamba.”—Danieli 7:18; 2 Samueli 7:12; 1 Mbiri 17:11.a
Kuneneratu za Mtsogolo Sindiko Kuikiratu za Mtsogolo
Pamene Mulungu anasankha kusadziŵa njira imene mtundu wa anthu ukatenga sizinamulepheretse kulosera za zotulukapo za machitidwe a munthu abwino kapena oipa. Makaniki amene achenjeza woyendetsa galimoto za kusakhala bwino kwa galimoto lake sangapatsidwe mlandu wa kuchititsa ngozi ngati ngoziyo ichitika kapena kuimbidwa mlandu wa kuikiratu ngoziyo. Mofananamo, Mulungu sangaimbidwe mlandu wa kuikiratu zotulukapo zoipa za machitidwe a munthu.
Zinalinso motero kwa mbadwa za anthu aŵiri oyamba. Kaini asanaphe mbale wake, Yehova anaika chosankha pamaso pa Kaini. Kodi iye akalilaka tchimo, kapena kodi tchimo likamlaka iye? Palibe chilichonse m’nkhaniyo chimene chimasonyeza kuti Yehova analinganiziratu kuti Kaini akasankhe chinthu choipa ndi kupha mbale wake.—Genesis 4:3-7.
Pambuyo pake, Chilamulo cha Mose chinachenjeza Aisrayeli ponena za chimene chikachitika ngati akafulatira Yehova, mwachitsanzo, mwa kukwatira akazi a mitundu yachikunja. Chimene chinaneneredwa chinachitikadi. Tikhoza kuona zimenezi m’chitsanzo cha Mfumu Solomo, amene m’zaka zapambuyo pake, akazi ake achilendo anamsonkhezera kuyamba kulambira mafano. (1 Mafumu 11:7, 8) Inde, Mulungu anachenjeza anthu ake, koma sanaikiretu machitidwe a mmodzi ndi mmodzi.
Osankhidwa Achikristu akulimbikitsidwa kupirira ngati sakufuna kutaya lonjezo la mphotho ya kulamulira kumwamba pamodzi ndi Kristu. (2 Petro 1:10; Chivumbulutso 2:5, 10, 16; 3:11) Monga momwe ophunzitsa zaumulungu a m’nthaŵi zakale anafunsira, Kodi nchifukwa ninji zikumbutso zoterozo zinaperekedwa ngati kuti chiitano cha osankhidwawo chinaikidwiratu?
Kuikiratu za Mtsogolo ndi Chikondi cha Mulungu
Munthu anapatsidwa ufulu wa kusankha, pakuti analengedwa “m’chifanizo cha Mulungu.” (Genesis 1:27) Ufulu wa kusankha unali wofunika kwambiri kuti anthu alemekeze ndi kutumikira Mulungu mwa chikondi, osati monga maloboti amene kachitidwe kalikonse kamalinganizidwiratu pasadakhale. Chikondi chosonyezedwa ndi zolengedwa zanzeru, zokhala ndi ufulu chikatheketsa Mulungu kutsutsa zinenezo zosalungama. Iye akuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”—Miyambo 27:11.
Ngati kuti atumiki a Mulungu anaikiridwiratu za mtsogolo—kapena kuikidwiratu pa programu, titero kunena kwake—kodi zimenezo sizikakayikitsa chikondi chawo kwa Mlengi wawo? Ndiponso, kodi sizikawombana ndi kupanda tsankhu kwa Mulungu ngati iye akanalinganiziratu zosankha za anthu zokalandira ulemerero ndi chimwemwe popanda kulingalira za mikhalidwe yawo mmodzi ndi mmodzi? Ndiponso, ngati ena achitiridwa mokondera chotero, pamene ena aikidwa ku chilango chosatha, zimenezo sizikapereka konse malingaliro oyamikira mwa “osankhika.”—Genesis 1:27; Yobu 1:8; Machitidwe 10:34, 35.
Chomalizira, Kristu anauza ophunzira ake kulalikira mbiri yabwino kwa mtundu wa anthu. Ngati kuti Mulungu anasankha kale awo odzapulumutsidwa, kodi zimenezi sizikapha changu cholalikira chimene Akristu amasonyeza? Kodi sizikachititsa ntchito yolalikira kukhala yopanda pake?
Chikondi cha Mulungu chopanda tsankhu ndicho mphamvu yaikulu koposa imene ingasonkhezere anthu nawonso kumkonda. Chisonyezero chachikulu koposa cha chikondi cha Mulungu chinali kupereka Mwana wake kaamba ka mtundu wa anthu wochimwa ndi wopanda ungwiro. Chidziŵitso cha Mulungu cha za mtsogolo ponena za Mwana wakeyo chili nkhani yapadera, koma chimatitsimikizira kuti malonjezo akuwongolera zinthu odalira pa Yesu adzakwaniritsidwadi. Chotero tikhale ndi chikhulupiriro mwa Mwanayo ndi kuyandikira kwa Mulungu. Tiyeni tisonyeze chiyamikiro chathu mwa kuvomereza chiitano cha Mulungu cha kuloŵa mu unansi wabwino ndi Mlengi wathu. Lerolino, Mulungu akupereka chiitano chimenechi kwa onse ofuna kugwiritsira ntchito ufulu wawo wa kusankha ndi kusonyeza chikondi chawo kwa iye.
[Mawu a M’munsi]
a Pamene Yesu amalankhula za Ufumu wokonzedwa “pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi” (Mateyu 25:34), ayenera kukhala akusonya nthaŵi ina ya pambuyo pa tchimo loyambalo. Luka 11:50, 51 amagwirizanitsa “kukhazikika kwa dziko lapansi,” kapena kukhazikitsidwa kwa mtundu wa anthu wowomboleka ndi dipo, ndi nthaŵi ya Abele.
[Bokosi patsamba 7]
OIKIDWIRATU ZA MTSOGOLO MWAWO MONGA KAGULU
“Awo amene Mulungu anawadziŵiratu anawaikiratunso za mtsogolo mwawo kuti akafanane ndi Mwana wake, kuti iye akhale wachisamba pakati pa abale ambiri. Ndipo amene anawaikiratu za mtsogolo mwawo, anawaitananso; oitanidwawo, anawalungamitsanso; olungamitsidwawo, anawalemekezanso.” (Aroma 8:29, 30, New International Version) Kodi liwulo ‘kuwaikiratu za mtsogolo’ logwiritsiridwa ntchito ndi Paulo m’mavesiŵa tiyenera kulimva motani?
Paulo pano sanali kupereka chigomeko chosatsutsika chovomereza kuikiratu za mtsogolo mwa munthu mmodzi ndi mmozi. Cha kuchiyambi m’zaka za zana lathu lino, Dictionnaire de théologie catholique inafotokoza zigomeko za Paulo (Aroma, machaputala 9-11) motere: “Ganizo lofala lomakula pakati pa akatswiri Achikatolika nlakuti lingaliro la kuikiratu mtsogolo mwa moyo wosatha silinasonyezedwe.” Ndiyeno buku la maumboni limodzimodzilo likugwira mawu M. Lagrange kukhala akunena kuti: “Nkhani imene kwenikweni inayambitsidwa ndi Paulo siinali konse ya kuikiratu za mtsogolo ndi kuweruziratu koma kokha ya chiitano cha Akunja ku chisomo cha Chikristu, chopinga chake chikumakhala kupanda chikhulupiriro kwa Ayuda. . . . Imanena za magulu, Akunja, Ayuda, ndipo osati anthu mmodzi ndi mmodzi mwachindunji.”—Kanyenye ngwathu.
Osati kale kwambiri, The Jerusalem Bible inanena zofananazo ponena za machaputala ameneŵa (9-11), ikumati: “Motero, nkhani ya machaputala ameneŵa siili vuto la kuikiratu za mtsogolo mwa ulemerero mwa munthu mmodzi ndi mmodzi, kapena ngakhale chikhulupiriro, koma ili ya phande la Israyeli m’kupangitsa mbiri ya chipulumutso cha anthu, vuto lokha lobutsidwa ndi ndemanga za mu OT [Chipangano Chakale].”
Mavesi omalizira a Aroma chaputala 8 ali a nkhani imodzimodziyo. Chifukwa chake, mavesi ameneŵa angatikumbutse bwino lomwe kuti Mulungu anaoneratu kukhalapo kwa kagulu, kapena kabungwe, kochokera pakati pa mtundu wa anthu kamene kakaitanidwa kukalamulira ndi Kristu, limodzinso ndi zofunika zimene akafunikira kuzifitsa—ndipo zinachitika popanda kulinganiziratu pasadakhale anthu mmodzi ndi mmodzi amene akasankhidwa, pakuti zimenezo zikawombana ndi chikondi chake ndi chilungamo.