Kodi Mumakumbukira?
Kodi munalingalirapo mosamalitsa makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati nditero, mwinamwake mudzakhala wokhoza kukumbukira zotsatirazi:
◻ Kodi Akristu odzozedwa ena adzapulumuka ‘chisautso chachikulu’ ndikukhala padziko lapansi kwakanthaŵi asanatengedwe kupita kumwamba?—Chibvumbulutso 7:14.
Baibulo silimanena mwachindunji pankhaniyi. Zolembedwa zina za Baibulo zimawonekera kukhala zikupereka lingaliro lakuti odzozedwa angakhalebe ndimoyo nkudzaloŵa m’dziko latsopano. Komabe, mamiliyoni oyembekezera kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi aphunzitsidwa mofunikira kotero kuti akayambitse dziko latsopano. Chifukwa chake, otsalira ochepawo sangafunikire kaamba ka ntchitoyi, ndipo Mulungu angasankhe kuwatengera kumwamba kaamba ka “ukwati wa Mwanawankhosa” pambuyo pakuphedwa kwa mkazi wachigololo wachipembedzoyo, ‘Babulo Wamkulu.’ (Chibvumbulutso 18:2, 10; 19:2, 7, 8)—8/15, tsamba 31.
◻ Kodi mwamuna ayenera kuika mtima wake pakukhala woyang’anira Wachikristu ndizolinga zotani? (1 Timoteo 3:1)
Mwamuna ayenera kukalamirira ntchito ya woyag’anira, akuchita motero modzichepetsa chifukwa chakuti amafuna kutumikira ena. Chotero pamene asonkhezeredwa ndi zolinga zoyenera, kachitidwe kameneka kumbali yake kangatulukepo madalitso auzimu kwa onse oloŵetsedwamo.—9/1, tsamba 18.
◻ Kodi nchifukwa ninji mtumwi Paulo sanalefulidwe mosasamala kanthu ndizonse zimene anazipirira?
Paulo akufotokoza kuti: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Paulo sanayese konse kusenza mavuto ake payekha. Mmalo mwake, anayang’ana kwa Yehova kuti amchirikize. (Salmo 55:22)—9/1, tsamba 30.
◻ Kodi nchiyani chikutanthauzidwa ndimawu a Paulo pa Aefeso 4:26 akuti: ‘Kwiyani, koma musachimwe’?
Mawu ameneŵa amavomereza kuti munthu angakwiye molungamitsika, koma pamene ichi chichitika, muthuyo sayenera kulola ‘dzuŵa kuloŵa ali chikwiire.’ (Aefeso 4:26) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kuteroko kukapatsa mpata Mdyerekezi kupeza mwaŵi pa munthuyo, mothekera kumnyenga kuchita chinachake choipa, kotero kuti asakhale ndi chivomerezo cha Mulungu. (Salmo 37:8, 9)—9/15, tsamba 21.
◻ Kodi ndikusiyana kwakukulu kotani kumene kulipo pakati pa kaphunzitsidwe ka Mboni za Yehova ndi kaphunzitsidwe ka atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko?
Mboni za Yehova zimaphunzitsa ndiulamuliro wa Mawu a Mulungu, pamene atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko amazika kuphunzitsa kwawo pa mwambo wachipembedzo wachikunja wopatsiridwa kuchokera ku Babulo ndi Igupto.—10/1, tsamba 25.
◻ Kodi nchifukwa chachikulu koposa chiti chimene Mwana wa Mulungu anabwerera padziko lapansi?
Yesu anabwera padziko lapansi kwakukulukulu ndicholinga chodzathetsa nkhani yobutsidwa ndi Satana yokhudza ufumu wa Yehova.—10/15, tsamba 13.
◻ Pamene timatcha maulamuliro akudziko kukhala “aakulu,” kodi timachepetsako ulemu womyenerera Yehova mwanjira iriyonse? (Aroma 13:1)
Ayi, popeza kuti Yehova ali woposa kungokhala ‘wamkulu.’ Iye ndiye “Mfumu Ambuye,” “Wamkulukulu.” (Salmo 73:28, NW; Danieli 7:18, 22, NW) Maulamuliro akudziko ali aakulu kokha kulinga kwa anthu ena ndipo mkati mwachigawo chawo chantchito. Iwo ali ndithayo lakulamulira ndi kuchinjiriza zitaganya.—11/1, tsamba 12.
◻ Kodi nchifukwa ninji chikondi chiri chachikulu koposa pa zipatso zisanu ndi zinayi za mzimu wa Mulungu zotchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23?
Zipatso zisanu ndi zitatu zinazo za mzimu wa Mulungu ziri zisonyezero, kapena mbali zosiyanasiyana, za chikondi, chimene chatchulidwa poyamba. Zipatso zina za mzimu zonsezi ziri mikhalidwe yofunika, koma sizidzatipindulitsa ngati tisoŵeka chikondi. (1 Akorinto 13:3)—11/15, tsamba 14.
◻ Kodi ndimapindu otani omwe alipo pamene tipempherera okhulupirira anzathu?
Pamene nkhaŵa yathu m’pemphero ikhala pa mkhalidwe wabwino wauzimu wa ena, timayandikana nawo mwathithithi m’chikondi chaubale. Timawachitiranso chifundo, tikumagaŵana nawo m’zabwino ndi zipsinjo zawo. Chotero, chiwawo chonse chimazulidwa, kupereka mpata kaamba ka malingaliro omangilira otipangitsa kukhala okondana ndi achimwemwe.—11/15, masamba 21-2.
◻ Kodi nzifukwa zotani zotifunikiritsa kulambira Yehova Mulungu?
Tiyenera kulambira Yehova chifukwa chakuti ndiye Mlengi ndipo mikhalidwe yake imatikokera kwa iye. (Deuteronomo 32:3, 4; 1 Yohane 4:8; Chibvumbulutso 10:6) Baibulo limati: ‘Chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’ (1 Timoteo 4:8) Palibe mulungu aliyense pambali pa Yehova amene angalonjeze chotulukapo choterocho ndiyeno kukwaniritsa lonjezo lake.—12/1, masamba 6-7.