Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g20 No. 3 tsamba 10-11
  • Muzicheza Ndi Anthu Osiyanasiyana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzicheza Ndi Anthu Osiyanasiyana
  • Galamukani!—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Vuto Limene Limakhalapo
  • Mfundo ya M’Baibulo
  • Kodi Kucheza ndi Anthu Osiyanasiyana N’kothandiza Bwanji?
  • Zimene Mungachite
  • Anasiya Tsankho
    Galamukani!—2020
  • Muzisonyeza Chikondi
    Galamukani!—2020
  • Kodi Ndiwonjezere Anzanga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kupeza Anzathu Omwe Timalakalaka
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—2020
g20 No. 3 tsamba 10-11
Azimayi 4 a mitundu yosiyana akucheza komanso kuseka ndipo nawonso ana awo akusewera limodzi mosangalala.

Muzicheza Ndi Anthu Osiyanasiyana

Vuto Limene Limakhalapo

Tikamapewa anthu amene timawaganizira zolakwika, tsankho limakula kwambiri mumtima mwathu. Tikamangocheza ndi anthu amene timaona kuti timafanana nawo, tikhoza kumaganiza kuti zimene ifeyo timaganiza, mmene timamvera mumtima mwathu, komanso mmene timachitira zinthu ndi zokhazo zimene zili zabwino.

Mfundo ya M’Baibulo

“Futukulani mtima wanu.”—2 AKORINTO 6:13.

Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Mawu akuti “mtima” angatanthauze mmene timamvera komanso zimene timakonda. Tikamangokonda anthu okhawo amene timafanana nawo, sitingathe kufutukula mtima wathu. Kuti tipewe vuto limeneli, tiyenera kumachezanso ndi anthu amene timasiyana nawo zinthu zina.

Kodi Kucheza ndi Anthu Osiyanasiyana N’kothandiza Bwanji?

Tikayamba kudziwana ndi anthu ena, timamvetsa chifukwa chake amachita zinthu mosiyana ndi ifeyo. Ndiyeno tikamagwirizana nawo kwambiri, timaiwala kuti ndi ochokera mumtundu wina. Timayamba kuwalemekeza kwambiri ndipo nafenso timayamba kusangalala ndi zimene iwo amasangalala nazo komanso kumva chisoni ndi zimene zikuwamvetsa chisoni.

Taganizirani chitsanzo cha Nazaré. Pa nthawi ina anali ndi maganizo atsankho kwa anthu ochokera m’mayiko ena. Pofotokoza zimene zinamuthandiza kuti asinthe, iye anati: “Ndinkacheza nawo komanso kugwira nawo ntchito. Ndinaona kuti zimene anthu am’dera lathu ankanena zokhudza anthuwa zinali zosiyana kwambiri ndi mmene iwo alili. Ukayamba kugwirizana ndi anthu a zikhalidwe zina, umaphunzira kuti si onse amachita zinthu mofanana ndipo umayamba kuwakonda komanso kuwalemekeza.”

Chenjezo

Anthu ena ali ndi makhalidwe omwe akhoza kubweretsa mavuto kwa iwowo komanso kwa anthu ena. Choncho tiyenera kumasankha bwino anthu ocheza nawo. Si tsankho kupewa kucheza ndi anthu amakhalidwe oipa. N’zoona kuti simuyenera kuchitira zoipa kapena kuphwanya ufulu wa anthu amene satsatira mfundo zimene inuyo mumayendera. Koma ndi nzeru kupewa kucheza nawo.​—Miyambo 13:20.

Zimene Mungachite

Muziyesetsa kupeza mpata wolankhulana ndi anthu ochokera m’mayiko ena, m’mitundu ina kapena omwe amalankhula chinenero china. Mukhoza

  • Kuwafunsa kuti akuuzeni mbiri yawo.

  • Kuwaitana kuti mukadye nawo chakudya.

  • Kumvetsera nkhani zawo zomwe zingakuthandizeni kudziwa zinthu zimene amaona kuti ndi zofunika.

Mukamayesetsa kumvetsa mmene zimene akumana nazo zasinthira moyo wawo mukhoza kuyamba kuona moyenera anthu amtundu umenewo.

Zimene Zinachitikadi: Kandasamy ndi Sookammah (Canada)

“Tinakulira ku South Africa pa nthawi imene anthu ankasankhana mitundu. Anthu osiyana mitundu ankakakamizidwa kuti azikhala m’madera osiyana. Zimenezi zinachititsa kuti anthu azidana kwambiri ndi anthu amitundu ina. Ifeyo tinkadana kwambiri ndi azungu chifukwa ena a iwo ankationa ngati anthu otsika. Pa nthawiyo sitinkaona kuti tinali ndi maganizo a tsankho. M’malomwake, tinkaona kuti ifeyo ndi amene tikusalidwa.

“Tinkafunika kusintha maganizo athu, ndiye tinayamba kucheza ndi anthu azikhalidwe zosiyanasiyana. Titayamba kucheza ndi azungu, tinazindikira kuti anthufe si osiyana kwenikweni. Tonse timakumana ndi mavuto ofanana.

“Pa nthawi ina tinalola kuti banja lina lachizungu libwere kudzakhala nafe kunyumba kwathu kwa nthawi yaitali. Tinadziwana nawo bwino. Kenako tinayamba kugwirizana kwambiri ndipo tinkaona kuti ndife ofanana. Zotsatira zake zinali zakuti tinayamba kuona azungu moyenera.”

Abale enieni

Johny ndi Gideon akupereka moni kwa ana omwe ali panja pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.

Ngakhale kuti poyamba anali osiyana mitundu komanso ankasiyana maganizo pandale, Johny ndi Gideon anayamba kugwirizana kwambiri.

Onererani vidiyo yakuti Johny ndi Gideon: Poyamba Anali Khoswe ndi Mphaka Koma Pano Ndi Ogwirizana. Fufuzani mutu umenewu pa jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena