Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g20 No. 3 tsamba 12-13
  • Muzisonyeza Chikondi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzisonyeza Chikondi
  • Galamukani!—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Vuto Limene Limakhalapo
  • Mfundo ya M’Baibulo
  • Zimene Mungachite
  • Anasiya Tsankho
    Galamukani!—2020
  • Kodi Muli Ndi Mtima Watsankho?
    Galamukani!—2020
  • Kodi Tsankho Lidzatha Liti?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Zimene Zimayambitsa Tsankho
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—2020
g20 No. 3 tsamba 12-13
Mayi wa ku India akuthandiza mayi wachikulire wamtundu wa Caucasia kukwera masitepe ndipo wamunyamulira zinthu zimene amakagula.

Muzisonyeza Chikondi

Vuto Limene Limakhalapo

Maganizo atsankho amakhala ovuta kuwachotsa, ngati mmene zimakhaliranso ndi kachirombo koyambitsa matenda ka vairasi. Pamafunika nthawi komanso khama kuti tichotse tsankho mumtima mwathu. Ndiye kodi mungatani kuti mukwanitse kuchita zimenezi?

Mfundo ya M’Baibulo

Zithunzi: 1. Bambo wa ku Asia wagwira chitseko kuti munthu wakuda yemwe wanyamula makapu a khofi adutse. 2. Munthu wakuda uja akupereka khofi uja kwa anthu omwe amagwira nawo ntchito kuphatikizapo mayi wa ku India uja.

“Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”—AKOLOSE 3:14.

Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Kuchita zinthu zokomera mtima anthu ena kumathandiza kuti anthu azigwirizana. Ndiye mukamasonyeza kwambiri chikondi kwa ena, maganizo atsankho amakuchokerani. Mukaphunzira kukonda ena kwambiri zidzakuthandizani kuti musamawaganizire zolakwika.

Zimene Mungachite

Zithunzi: 1. Mayi wa ku India akuthandiza mayi wachikulire wamtundu wa Caucasia kukwera masitepe ndipo wamunyamulira zinthu zimene amakagula. 2. Mayi wachikulire wamtundu wa Caucasia uja akugawira mabisiketi neba wake yemwe ndi bambo wa ku Asia uja.

Ganizirani zimene mungachite kuti musonyeze chikondi anthu amtundu umene mwakhala mukuuona molakwika. Sikuti mufunika kuwachitira chinachake chachikulu. Mungayese kuchita chimodzi kapena zingapo mwa izi:

Chilichonse chimene mungachite posonyeza ena chikondi, chidzakuthandizani kuchepetsa mtima watsankho

  • Mungawasonyeze kuti ndinu munthu wakhalidwe labwino powatsegulira chitseko kapena powauza kuti akhale pampando umene mwakhala m’basi ngati iwo aimirira.

  • Yesani kukamba nawo tinkhani apa ndi apo ngakhale atakhala kuti sadziwa bwinobwino chilankhulo chanu.

  • Muzikhala oleza mtima akachita zinthu mwa njira imene simukuimvetsa.

  • Muziwamvera chisoni akamafotokoza mavuto awo.

Zimene Zinachitikadi: Nazaré (Guinea-Bissau)

“Nthawi inayake ndinali ndi maganizo atsankho kwa anthu obwera kuchokera mayiko ena. Ndinauzidwa kuti anthu obwera ambiri amanama ku boma n’cholinga choti azipatsidwa thandizo komanso kuti ambiri amakhala zigawenga. Ndiye zinkandivuta kuti ndiziwaona kuti ndi anthu abwinobwino. Komabe sindinkaganiza kuti limeneli ndi tsankho chifukwa ndi mmene anthu ambiri ankaonera anthu obwera.

“Koma kenako ndinazindikira kuti ndinali ndi maganizo atsankho kwa anthu obwera. Nzeru za m’Baibulo zandithandiza kuti ndiziwasonyeza chikondi anthuwa. Panopa sindiwapewa, koma ndimawapatsa moni komanso kucheza nawo. Ndimayesetsa kuti munthu aliyense payekha ndimudziwe bwino. Panopa anthu obwera sindiwaganizira zolakwika komanso sindikhala omangika ndikakhala nawo pafupi.”

“Ndinkafunitsitsa kuthana ndi kupanda chilungamo”

Rafika Morris.

Pofuna kuthana ndi vuto losankhana mitundu, Rafika analowa gulu la anthu ofuna kusintha zinthu. Koma atachita nawo msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova, anaona kuti wapeza mgwirizano womwe ankaufuna.

Onerani vidiyo yakuti Rafika Morris: Ndinkafunitsitsa Kuthana ndi Kupanda Chilungamo. Fufuzani mutu umenewu pa jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena