CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 7-10
Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto
Akhristufe tili ndi utumiki wa mbali ziwiri. Tili ndi “utumiki wokhazikitsanso mtendere” womwe timauchita tikamalalikira komanso kuphunzitsa anthu. Komanso tili ndi ‘utumiki wothandiza anthu’ womwe timachitira Akhristu anzathu. (2 Akor. 5:18-20; 8:4) Choncho tikamathandiza Akhristu anzathu omwe ali pamavuto, timakhala tikuchita utumiki wopatulika. Tikamagwira nawo ntchitoyi:
timathandiza abale ndi alongo athu kupeza zinthu zomwe akusowa.—2 Akor. 9:12a
timathandiza anzathu omwe apanikizika ndi mavuto kuti ayambirenso kuchita zinthu zofunika potumikira Mulungu ndipo amayamba kulalikira mwakhama posonyeza kuyamikira kwawo Yehova.—2 Akor. 9:12b
timathandiza kuti anthu alemekeze Yehova. (2 Akor. 9:13) Ntchito yothandiza anthu pa nthawi yangozi imakhala ngati njira yolalikirira anthu onse, ngakhalenso omwe amadana ndi Mboni za Yehova