Kutsatira Maprinsipulo a Baibulo—Njira Yopambana
“KUNGSHI, kungshi fa tsai!” (Tikuyamikani, lolani kuti mulemere!) Moni wamwambo wa Chaka Chatsopano wa a Chinese umenewu umapereka chigogomezero mukupita patsogolo kwa kuthupi komwe kuli kofala kuzungulira dziko lonse. Kuti alimbikitse kuthekera kwa wina kukhala wolemera, maphunziro angawonedwe kumlingo wachifupifupi kukhala chinthu cholambiridwa. M’maiko ambiri a Kummawa, kawirikawiri chodetsa nkhawa chenicheni cha makolo chimakhala cha kuwapanga ana awo kulowa mu sukuluya nasale yapamwamba kwambiri kotero kuti kenaka akalowe mu sukulu yoyambirira yapamwamba kwambiri ndi kupitirizabe mpaka ku koleji kapena ku yunivesite. Mofananamom’maiko a Kumadzulo ambiri ali otanganitsidwa ndi kulondola kwawo kukhala olemera, ndi njira yokhweka ya moyo.
Kodi ndi motani mmene kutanganitsidwa kwa mwambo umenewo kwa kulondola zinthu zakuthupi kumafananira ndi maprinsipulo a Baibulo? “Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha ndi zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chtayiko,” akuchenjeza motero mtumwi Paulo. Iye akupitiriza kunena kuti: “Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama, chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.” (1 Timoteo 6:9, 10) Kuloza ku chenicheni chomwe kawirikawiri chiri chitsimikiziro pamene anthu apanga kupeza zinthu zakuthupi monga chonulirapo chawo mu zikondwerero za moyo, Mlaliki 5:10 akunena kuti: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva, ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu, ichinso ndi chabe.”
Ha ndi mwa kawirikawiri chotani mmene chimachitikira kuti mwamuna ndi mkazi onse awiri amagwira ntchito molimbika kupeza zosangalatsa moyo, kokha kukhala otanganitsidwa kwambiri kotero kuti sapezeka pa nyumba kusangalala ndi chuma chawo! Mosiyanitsa, asanapereke chenjezo lapamwambalo kwa Timoteo, Paulo ananena kuti: “Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu. Koma, pokhala nazo zakudya ndi zopfunda, zimenezi zitikwanire.” (1 Timoteo 6: 6, 8) Ndipo Miyambo 28:20 amawonjezera lingaliro iri: “Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri, koma wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.” Chiri chomvetsa chisoni motani nanga kuwona anthu omwe amawoneka ozolowereka, ogawira akumapereka maprinsipulo apamwamba akuwona mtima, kudzilemekeza, ndi makhalidwe achibadwa mukuyesayesa kwawo kwakupeza chuma chokulira chowonjezereka!
Mkati mwa Banja
Uli mwambo pakati pa mafuko ena ndi anthu ena kuyembekezera ana awo—makamaka ana awo akazi, omwe kenaka adzachoka pa nyumba ndi kukwatiwa—kupita kukagwira ntchito ndi kutumiza ndalama kunyumba mwezi ndi mwezi kusonyeza chikondi chawo ndi thayo lomwe ayenera kupereka kwa makolo awo ndi kubwezera makolo awo kaamba ka kukhala atawalera iwo. Mwachitsanzo, m’banja limodzi la Mboni za Yehova, mwana wamkazi anauza makolo ake kuti angakonde kupita ku mzinda ndi cholinga chofuna kukakhala mpainiya (mtumiki wa nthawi zonse). Tangolingalirani kukhumudwa kwake pamene makolo ake anamuuza kuti anafuna kuti iye apite kukagwira ntchito kotero kuti adziwatumizira iwo ndalama mwezi ndi mwezi za kuwathandiza iwo! Ayi, iwo sanali okhumba zinthu zakuthupi. Chotero prinsipulo la ana kusamalira okalamba, odwala, kapena makolo amene akufunikira thandizo silinagwire ntchito munjira iyi. (Mateyu 15:4-6; 1 Timoteo 5:8) Unali kokha mkhalidwe wamwambo pakati pa pfuko lawo kuti ana ayenera kuthandiza kukhazikitsa chuma kaamba ka banja. Pamene kawirikawiri chiri choyenerera chifukwa cha kusoweka kwa zoperekedwa za mayanjano, mwambo umenewu unali kutsatiridwa kokha kuti atchuke m’mudzimo kapena chifukwa chokhala atakhudzidwa ndi chikhumbo chofala cha “fa tsai.”
Pamene atate anakambitsirana nkhaniyi ndi mkulu wa Chikristu, iye analimbikitsidwa kulingalira malemba ochuluka ndipo kenaka anapanga chosankha. Pakati pa malemba olozeledwa kwa iye panali 2 Akorinto 12:14 pamene Paulo anakhazikitsa prinsipulo iri: “Pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amayi, koma atate ndi amayi kuunjikira ana.” Pambuyo pakulingalira izi ndi maprinsipulo ena a Baibulo, makolowo anapanga chosankha chawo. Anali wosangalala chotani nanga mwanayo kulandira chilolezo—ndipo angakhale thandizo la za chuma—kukhala mpainiya wokhazikika!
Kugonjera—Kumlingo Wotani?
Mbali ina ku imene miyambo ya kumaloko ndi mikhalidwe yofala kawirikawiri imatsutsana ndi maprinsipulo a Baibulo iri njira yakugonjera. M’maiko ena uli mwambo kufunikira chigonjero chotheratu ku makolo ndi olamulira ena mu mbali zonse za moyo. Sichiri chachilendo mu ena a maiko amenewa kwa amuna a zaka 40 kapena zaka zopitirirapo kukana kuwerenga bukhu liri lonse la chipembedzo chosiyana ndi cha makolo awo kapena kutenga chosankha chokulira chiri chonse popanda kuwafunsa iwo choyamba, kaamba ka mantha a kusawasangalatsa makolo. Komabe, mu maiko amenewo chikukhala chofala kwambiri kupeza achichepere akuukira motsutsana ndi makolo awo. Baibulo limodzi ndi kayang’anidwe kake kolinganizika pa nkhani zoterezi limatithandiza ife kupewa kufika ku milingo iwiri yopambanitsa imeneyi. Prinsipulo la kugonjerako kwa olamulira a anthu linasonyezedwa bwino lomwe pa Machitidwe 4:19 ndi 5: 29. Ndiponso, zindikirani ndi motani mmene Paulo akulimbikitsira ana kukhala omvera kwa makolo, ndipo pa nthawi imodzimodziyo iye akusonyeza kuti sikuli kumvera kopanda malire pamene iye akunena kuti: “Ananu mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino; ‘lemekeza atate wako ndi amako’; ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano.”—Aefeso 6:1-3.
Prinsipulo lina la Baibulo lomwe lingakhudze wina ndi ku ukulu wotani womwe angagonjere ku makolo liri lija la kugonjera kwa mkazi kwa mwamuna wake. “Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi,” analemba motero mtumwi Paulo. Iye kenaka anakulitsa prinsipulo limenelo mwa kukumbukira chimene Yehova ananena pambuyo pa kukhazikitsa ukwati wa munthu woyamba: “Chifukwa cha ichi [mwamuna, NW] adzisiya atate ndi amayi, naphatikizana ndi mkazi wache, ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.”—Aefeso 5:22-31.
Komabe, bwanji ponena za mikhalidwe imene imakhalapo mu maiko ambiri kumene mwana wamwamuna amapitirizabe kukhala mu nyumba ya makolo ake pambuyo pa ukwati wake? Baibulo limasonyeza kuti, mu nthawi ya Chikristu chisanakhale chifupifupi, olambira a Yehova kawirikawiri anali kuchita chimenechi. Pansi pa mikhalidwe imeneyo atate wa nyumbayo anakhalabe kholo la umutu labanja, koma akazi anali kumagonjera kwa amuna awo a iwo eni. Mu maiko ena ngakhale kuli tero, kawirikawiri chimakhala chakuti apongozi amakhala mutu wa mwana wa mkazi wobwera. Ichi chimachipangitsa icho kukhala chovuta kwambiri kaamba ka mwana wamwamuna kugwiritsira ntchito kotheratu maprinsipulo ake a umwamuna aumutu ndinso kwa mkazi wake kukhala wogonjera kotheratu kwa mwamuna wake. Komabe, mwana wamwamuna ayenera kukhala ndi kulinganizika kupereka ulemu kaamba ka makolo ake ndi kuyenerera kwakukhala mutu wa banja lake la iye mwini ngati iye afuna kukhala ndi Yehova monga nkhosi yachitatu muchingwe chophiphiritsira ‘chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.’—Mlaliki 4:12.
Mu maiko ena mkhalidwe wina wovutirapo koposa umadzipeza iwo wokha pamene mwamuna amakwatira m’banja limene mulibe mwamuna wolowa m’malo. Nkhani yotsatirayi ikufanizira mkhalidwe wa ambiri a amuna amenewo pamene pambuyo pake m’moyo iwo aphunzira ndi kuyesa kugwiritsira ntchito maprinsipulo a Baibulo. Mwamuna wachichepere wa Chikatolika anakwatira m’banja la Chikatolika. Kuyambira pachiyambi, iye anapeza kuti anali kudereredwa ndi banjalo ndipo anali wofananako pang’ono ndi wantchito wosalipiridwa yemwe anangoyembekezeredwa kubereka ana kotero kuti dzina labanjalo likhalebe ndi moyo. Popeza uli mwambo m’kakhazikitsidwe kameneka, iye kenaka anayenera kusiya dzina lake la iye mwini, kulola ana ake kumawonedwa monga olowa m’malo a chuma cha banjalo. Pamene iye anaphunzira prinsipulo la umutu wa banja ndi kuyesa kuligwiritsira ntchito, chivomerezo cha mkazi wake chinali chofanana ndi cha ena onse m’banjamo: ‘Sunabweretse kali konse m’banja iri, chotero suyenera kunena kali konse ponena za ndi motani mmene zinthu ziyenera kuchitidwira!’
Pamene sikuli kwakuti makonzedwe amaukwati onse amafika ku mkhalidwe woipa wonga uwu, chingawonedwe mwamsanga kuti kumene mwambo woterowo uli wofala ndi kuti chigonjero ku mbali ya mwamuma chikuyembekezeredwa, mavuto amabukapo m’kugwiritsira ntchito maprinsipulo a Baibulo mogwirizana ndi umutu. Chimakhala chovuta kwambiri kaamba ka mwamuna wa Chikristu kusonyeza umutu wake wachikondi m’banja lake la iye mwini ndipo chimodzimodzinso chimakhala chovuta kwa mkazi kusonyeza kugonjera kwa mwamuna wake ndi “[ulemu wonse, NW]” m’malo mwa makolo ake amene akupitirizabe kukhala nawo.—Aefeso 5:33.
Chitsanzo china cha mmene maprinsipulo a Baibulo angawombanirane ndi mwambo wa kumaloko umakhudza nkhani pamene makolo amakonza maukwati a ana awo. Kwa ana a Chikristu amene ali ndi makolo osakhulupirira, ichi kawirikawiri chimapereka vuto lenileni, popeza makolo amadzimva kukhala atalephera ngati ana awo sanakwatiwe pa msinkhu wakuti wakuti. Mwakutero, chitsenderezo chokulira, kuphatikizapo kumenyedwa kumagwiritsiridwa ntchito kuwakakamiza ana, ndipo makamaka ana a akazi, kuti akwatiwe. Pamene pali kuperewera kwa wokwatirana nawo woyenerera wa Chikristu, makolo osakhulupirira angachite chifupifupi china chiri chonse kukonzekera kaamba ka ukwati, pamene Mkristu adzakumbukira prinsipulo lakukwatira “kokha mwa Ambuye.”—1 Akorinto 7:39; Deuteronomo 7:3, 4.
Pindulani mwa Kutsatira Maprinsipulo a Baibulo
Ubwino wowonekera wa maprinsipulo a Baibulo ndiwo wakuti angapititse patsogolo mwawi wa aliyense amene amafuna kugwiritsa ntchito iwo, mosamala kanthu kuti ndi kuti kumene iye amakhala. Iwo ali okhazikika ndipo amakokera mabanja pamodzi. Amapanga anthu kukhala owona mtima koposa ndi kuwapanga iwo kukhala amuna abwino ndi atate abwino, akazi abwino ndi amayi abwino, ana abwino, olemba ntchito abwino. Iwo angalake mavuto oyambitsidwa mwa kuwombana kwa miyambo ya kumaloko ndi kulinganizitsa kugwiritsidwa ntchito kwa miyambo imeneyi yomwe siiri mwachindunji yowombana ndi chifuno cha Mulungu kaamba ka munthu koma mwina mwake kumachipanga kugwirizana ku chifunocho kukhala kovutirapo. Kodi ndi motani mmene ichi chingachitidwire?
Poyambirira, monga mmene Akristu a mu Tesalonika anachitira, muyenera kuvomereza chenicheni chakuti Baibulo mowonadi liri “mawu a Mulungu.” Ichi chimatanthauza kuzindikira kuti iro liri mowonadi nzeru yochokera ku Magwero apamwamba. Kachiwiri, muyenera kuyesetsa kuphunzira chimene “mawu a Mulungu” amenewa alinacho kaamba kaubwino wanu. Phunzirani kusiyanitsa maprinsipulo ndi malamulo a Mulungu pamene mukuwerenga ndi kuphunzira Baibulo. Kenaka, monga sitepi lachitatu, muyenera kulola mawu amenewo “kugwira ntchito mwa inu.” (1 Atesalonika 2:13) Ichi chimaphatikiza mayanjano athithithi ndi mipingo ya anthu a Mulungu tsopano yokhazikitsidwa mu maiko oposa 200 ndi zisumbu za m’nyanja. Chiri chimenechi vchomwe chapanga ubale wa dziko lonse wa Mboni za Yehova kukhala monga momwe uli—ubale m’chenicheni osati mu dzina lokha.
Choyambirira ndipo chofunika kwambiri, anthu a Yehova ali okondweretsedwa mu umodzi ndi Mulungu mwakulola maprinsipulo a Baibulo kutsogolera miyoyo yawo. Ndi zoturukapo za mtundu wanji? Umodzi wowona ndi wa nthawi zonse ndi anzawo omwenso ali ogwirizana ndi Mulungu, ndiponso mtendere wa maganizo umene umakhutiritsa kupyola mikhalidwe yonse m’dongosolo iri la zinthu. (Afilipi 4: 6, 7) Umodzi umenewo ndi unansi wathithithi ndi Mulungu ndi wina ndi mnzake uli njira imodzi yopititsira patsogolo mkhalidwe wa moyo tsopano ndipo umapereka lonjezo la moyo wosatha mu dongosolo latsopano la zinthu lolungama la Mulungu kumene zinthu zonse potsirizira zidzagonjetseredwa kotheratu ku chifuniro cha Mulungu.—1 Timoteo 4:8; 1 Akorinto 15:28.
[Zithunzi patsamba 7]
Kulilandira Baibulo monga “mawu a Mulungu”
Yesetsani kuphunzira zimene Mawu a Mulungu akunena kaamba ka phindulanu
Lolani Mawu amenewo “kugwira ntchito mwa inu”