Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 1/15 tsamba 23
  • ‘Musaleme pakuchita Zabwino’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Musaleme pakuchita Zabwino’
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Vumbulutso la Kristu ndi Kukhalapo Kwake
  • Kuchita ndi Osalongosoka
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Musafulumire Kugwedezeka pa Maganizo Anu”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Khalani Okonzeka Kaamba ka Tsiku la Yehova!
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Zimene Zili Mʼbuku la 1 Atesalonika
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 1/15 tsamba 23

‘Musaleme pakuchita Zabwino’

Mfundo Zazikulu Zochokera mu Atesalonika Wachiŵiri

NKHAŴA ya mtumwi Paulo kaamba ka Akristu okhala mumzinda wa Tesalonika wa ku Makedoniya inamfulumiza kuwalembera kalata yake yachiŵiri, pafupifupi chaka cha 51 C.E. Ena mumpingomo ankanena molakwa kuti kukhalapo kwa Yesu Kristu kunayandikira. Mwinamwake ngakhale kalata yolingaliridwa molakwa kukhala ya Paulo inamasuliridwa kukhala ikusonyeza kuti “tsiku la Yehova” lidafika.​—2 Atesalonika 2:1, 2, NW.

Chotero kalingaliridwe ka Atesalonika ena kanafunikira kuwongoleredwa. M’kalata yake yachiŵiri, Paulo anawayamikira kaamba ka kukula kwawo m’chikhulupiriro, chikondi chowonjezereka, ndi chipiriro chokhulupirika. Koma anasonyezanso kuti mpatuko ukabwera kukhalapo kwa Yesu kusanafike. Chotero panali nthaŵi zovuta kutsogolo, ndipo kalata ya mtumwiyo ikawathandiza kulabadira chilangizo chake chakuti: ‘Musaleme pakuchita zabwino.’ (2 Atesalonika 3:13) Mawu a Paulo angatithandize mwanjira yofananayo.

Vumbulutso la Kristu ndi Kukhalapo Kwake

Paulo choyamba analankhula za mpumulo ku chisautso. (1:1-12) Ichi chikadza ‘pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu.’ Pamenepo chiwonongeko chosatha chikadza pa osamvera uthenga wabwino. Nkotonthoza maganizo kukumbukira chimenechi pamene tikusautsidwa ndi ozunza.

Chotsatira, Paulo anasonyeza kuti “munthu wosayeruzika” akavumbulidwa kukhalapo kwa Kristu kusanayambe. (2:1-17) Atesalonikawo sanafunikire kukopeka ndi uthenga uliwonse wopereka lingaliro lakuti “tsiku la Yehova” linafika kale pa iwo. Choyamba, mpatuko ukachitika ndipo munthu wosayeruzika akavumbulidwa. Pambuyo pa zimenezo, Yesu akamuwononga, akutero m’kuwonekera kwa kukhalapo Kwake. Panthaŵiyi, Paulo anapemphera kuti Mulungu ndi Kristu atonthoze mitima ya Atesalonika ndi kuwalimbitsa ‘mu ntchito ndi mawu onse abwino.’

Kuchita ndi Osalongosoka

Mawu owonjezereka a Paulo anaphatikizapo malangizo onena zakuchita ndi anthu osalongosoka. (3:1-18) Iye anasonyeza chidaliro chakuti Ambuye akalimbitsa Atesalonika ndikuwachinjiriza kwa woipayo, Satana Mdyerekezi. Koma iwo anafunikira kuchitapo kanthu kaamba ka phindu lawo lauzimu. Iwo anafunikira kudzipatula kwa osalongosoka, aja odziloŵetsa m’nkhani zosawakhudza ndi okana kugwira ntchito. ‘Ngati munthu safuna kugwira ntchito,’ Paulo anatero, ‘asadyenso.’ Anthu oterowo anayenera kuyang’aniridwa, ndipo sipanafunikire kukhala nawo ndi mayanjano, ngakhale kuti anafunikira kulangizidwa monga abale. Akristu okhulupirika a ku Tesalonika sanayenera kulema pakuchita zabwino, ndipo Paulo anakhumba kuti chisomo choposa cha Ambuye Yesu Kristu chikhale nawo onse.

Kalata yachiŵiri ya Paulo kwa Atesalonika imapatsa Mboni za Yehova chitsimikizo chakuti mpumulo wa chisautso chawo udzabwera pamene Kristu ndi angelo ake abwezera chilango awo osamvera mbiri yabwino. Nkolimbikitsanso chikhulupiriro kudziŵa kuti “munthu wosayeruzika” (gulu la atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko) ndi chipembedzo chonyenga chonse adzawonongedwa posachedwapa. Pakali pano, tilabadiretu chilangizo cha Paulo chakusalema pakuchita zabwino.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 23]

Mawu a Yehova Ayende Mofulumira: “Mutipempherere,” analemba motero Paulo, “kuti mawu a Yehova apitirizebe kuyenda mofulumira [kapena, “kuti athamange”] ndikuti alemekezedwe monga momwe kuliri ndi inu.” (2 Atesalonika 3:1, NW; Kingdom Interlinear) Akatswiri ena apereka lingaliro lakuti mtumwiyo ankasonya kwa othamanga okhala paliŵiro lalikulu m’makani. Pamene kuli kwakuti ichi nchosatsimikizirika, Paulo anapempha mapemphero a Akristu a ku Tesalonika kotero kuti iye ndi antchito anzake angafalitse mawu a chowonadi mofulumira ndipopanda chowaletsa. Popeza kuti Mulungu amayankha mapemphero oterowo, mawu ake ‘akuyenda mofulumira’ pamene mbiri yabwino ikulalikidwa mofulumira m’masiku ano otsiriza. Ndiponso mawu a Yehova ‘akulemekezedwa,’ nakwezedwa mwakuya ndi okhulupirira monga ‘mphamvu ya Mulungu ya chipulumutso,’ monga momwe zinaliri pakati pa Atesalonika omwe anawalandira. (Aroma 1:16; 1 Atesalonika 2:13) Ndife okondwa chotani nanga kuti Mulungu akudalitsa alengezi a Ufumu ndikuwonjezera mofulumira mathayo a alambiri ake!​—Yesaya 60:22.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena