Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 8/15 tsamba 17-22
  • “Goli Langa Lili Lofeŵa, ndi Katundu Wanga Ali Wopepuka”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Goli Langa Lili Lofeŵa, ndi Katundu Wanga Ali Wopepuka”
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Goli Lofeŵa
  • Katundu Wopepuka
  • “Mpumulo wa Miyoyo Yanu”
  • ‘Kupeza Mpumulo wa Miyoyo Yanu’
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Yesu Ankatsitsimula Ena
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Mankhwala Omwe Angathandize Kuthetsa Nkhaŵa
    Nsanja ya Olonda—2001
  • “Bwerani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 8/15 tsamba 17-22

“Goli Langa Lili Lofeŵa, ndi Katundu Wanga Ali Wopepuka”

“Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine.”​—MATEYU 11:29.

1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene chimakupatsani mpumulo m’moyo wanu? (b) Kodi munthu ayenera kuchitanji kuti apeze mpumulo umene Yesu analonjeza?

TALINGALIRANI za kusamba madzi ozizirira bwino pambuyo pa tsiku lotentha, kapena kugona tulo tabwino pambuyo pa ulendo wautali wotopetsa​—eya, kumapatsa mpumulo chotani nanga! Ndi mmenenso zimakhalira pamene mtolo wolemera kwambiri uchotsedwa kapena pamene machimo akhululukidwa. (Miyambo 25:25; Machitidwe 3:19) Mpumulo umene timapeza mwa zochitika zotonthoza mtima zimenezi umatilimbikitsa, ndipo umatipatsa nyonga yochitira zowonjezereka.

2 Onse amene akulema ndi kuthodwa angadze kwa Yesu, pakuti anawalonjeza zimenezo​—mpumulo. Komabe, kuti munthu apeze mpumulo wofunika kwambiri umenewo, pali kanthu kena kamene ayenera kukhala wokonzeka kuchita. “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine,” anatero Yesu, “ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” (Mateyu 11:29) Kodi goli limeneli nchiyani? Kodi limadzetsa bwanji mpumulo?

Goli Lofeŵa

3. (a) Kodi ndi magoli otani amene anagwiritsiridwa ntchito m’nthaŵi za Baibulo? (b) Kodi goli limagwiritsiridwa ntchito kuphiphiritsira chiyani?

3 Chifukwa chakuti Yesu anali kukhala pakati pa alimi, iye ndi omvetsera ake anali olidziŵa bwino goli. Kwenikweni, goli ndilo mtengo wautali wopingasa wokhala ndi ndonyo ziŵiri kunsi kwake zokoloŵekamo makosi a nyama ziŵiri, kaŵirikaŵiri zimakhala ng’ombe, kotero kuti zikokere pamodzi chikhasu, ngolo, kapena katundu winawake. (1 Samueli 6:7) Kunalinso magoli a anthu. Ameneŵa anali mtengo umodzi umene munthu anali kupingasa pamapeŵa ake atakoloŵeka katundu uku ndi uku. Antchito anakhoza kunyamulira akatundu olemera pamagolipo. (Yeremiya 27:2; 28:10, 13) Chifukwa cha kugwirizanitsidwa kwake ndi mitolo ndi ntchito, goli kaŵirikaŵiri limagwiritsiridwa ntchito mophiphiritsira m’Baibulo kusonyeza kupondereza ndi ulamuliro.​—Deuteronomo 28:48; 1 Mafumu 12:4; Machitidwe 15:10.

4. Kodi goli limene Yesu amapereka kwa aja obwera kwa iye limaphiphiritsira chiyani?

4 Motero, kodi goli limene Yesu anapempha aja okapeza mpumulo kwa iye kuti alisenze linali lotani? Kumbukirani kuti iye anati: “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine.” (Mateyu 11:29) Munthu amene akuphunzira ali wophunzira. Chotero, kusenza goli la Yesu kumatanthauza kukhala wophunzira wake. (Afilipi 4:3) Komabe, iko kumafuna zochuluka kuposa kudziŵa chabe ziphunzitso zake. Kumafuna machitidwe ogwirizana ndi zimenezo​—kuchita ntchito imene iye anachita ndi kukhala ndi moyo umene anakhala nawo. (1 Akorinto 11:1; 1 Petro 2:21) Kumafuna kugonjera mwaufulu ku ulamuliro wake ndi kwa aja amene iye wapatsa ulamuliro. (Aefeso 5:21; Ahebri 13:17) Kumatanthauza kukhala Mkristu wodzipatulira ndi wobatizidwa, womalandira mautumiki onse ndi mathayo amene kudzipatulira kumeneko kumadza nawo. Limenelo ndilo goli limene Yesu akupereka kwa obwera kwa iye kukapeza chitonthozo ndi mpumulo. Kodi mukufuna kulilandira?​—Yohane 8:31, 32.

5. Kodi nchifukwa ninji kusenza goli la Yesu sikuyenera kukhala koŵaŵitsa?

5 Kupeza mpumulo mwa kusenza goli​—kodi mawu ameneŵa sakuwombana? Kwenikweni sakutero, pakuti Yesu anati goli lake lili “lofeŵa.” Liwu limeneli lili ndi tanthauzo la kufatsa, kukoma, chisomo. (Mateyu 11:30; Luka 5:39; Aroma 2:4; 1 Petro 2:3) Pokhala katswiri wopala matabwa, mwachionekere Yesu anali atapangapo zikhasu ndi magoli, ndipo anayenera kudziŵa kapangidwe ka goli kuti likhazikike bwino kuti ntchito igwirike bwino lomwe ndi mosavuta. Ayenera kuti anaika kunsi kwa magoliwo nsalu kapena chikopa. Magoli ambiri amaikidwa zimenezo kuti asamyule pakhosi, kapena kuperesapo kwambiri. Ndi mmenenso goli lophiphiritsira limene Yesu amapereka kwa ife lilili “lofeŵa.” Ngakhale kuti kukhala wophunzira wake kumaphatikizapo mathayo ena, sikuli kopanikiza koma kopatsa mpumulo. Malamulo a Atate wake Wakumwamba, Yehova, salinso olemetsa.​—Deuteronomo 30:11; 1 Yohane 5:3.

6. Kodi Yesu ayenera kuti anatanthauzanji pamene anati: “Senzani goli langa”?

6 Palinso chinthu china chimene chimachititsa goli la Yesu kukhala “lofeŵa,” kapena losavuta kusenza. Pamene iye anati: “Senzani goli langa,” mwina anatanthauza chimodzi cha zinthu ziŵiri. Ngati anali kunena za goli la nyama ziŵiri zokoka katundu, ndiye kuti anali kutipempha kuti tiloŵe naye m’goli limodzi. Limenelo ndi dalitso lotani nanga​—kukhala ndi Yesu kumbali kwathu akumakoka nafe katundu wathu! Ndiyenonso, ngati Yesu anali kunena za goli logwiritsiridwa ntchito ndi wantchito wamba, pamenepo anali kutipatsa njira yopeputsira katundu aliyense amene tanyamula kapena kuti anyamulike bwino. Mulimonse mmene zingakhalire, goli lake limapatsa mpumulo weniweni chifukwa iye amatitsimikizira kuti: “Chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.”

7, 8. Kodi ndi kuphonya kotani kumene ena amachita pamene amva kupanikizika?

7 Chotero, kodi tiyenera kuchitanji ngati tikumva kuti katundu wa mavuto a moyo amene tanyamula akukhala wosapiririka ndi kuti tatsala pang’ono kutaya mtima? Ena angalingalire molakwa kuti goli la kukhala wophunzira wa Yesu Kristu nlovuta kwambiri kapena kuti limafuna zopambanitsa, ngakhale kuti kwenikweni zimene zikuwathodwetsa ndi zosamalira za moyo. Anthu ena okhala mumkhalidwe umenewo amaleka kupezeka pamisonkhano Yachikristu, kapena amaleka kutenga mbali mu utumiki, akumalingalira kuti adzapezako mpumulo. Komabe, kumeneko kumakhala kuphonya kowopsa.

8 Timazindikira kuti goli limene Yesu amapatsa ndi “lofeŵa.” Ngati sitilikoloŵeka bwino, lingatimyule. Zikatero tiyenera kuyang’anitsitsa goli limene lili papheŵa pathu. Ngati pazifukwa zina, golilo lasekesa kapena silinamangidwe bwino, kuligwiritsira ntchito kudzafuna nyonga yathu yochuluka komanso lidzatipweteka. M’mawu ena, ngati ntchito zateokrase ziyamba kuoneka kukhala mtolo kwa ife, tiyenera kuyang’anitsitsa kuona ngati tikuzichita mwa njira yoyenera. Kodi tili ndi cholinga chotani pochita zimene tikuchita? Kodi timakhala okonzekera bwino pamene tipita kumisonkhano? Kodi timakhala okonzekera kuthupi ndi m’maganizo pamene tiloŵa mu utumiki wakumunda? Kodi tili ndi unansi wabwino ndi ena mumpingo? Ndipo koposa zonse, kodi unansi wathu ndi Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Kristu uli wotani?

9. Kodi nchifukwa ninji goli Lachikristu siliyenera konse kukhala mtolo wosapiririka?

9 Pamene tilandira ndi mtima wonse goli limene Yesu amapatsa ndi kuphunzira molinyamulira bwino, palibe chimene chingalichititse kuoneka kukhala mtolo wosapiririka. Kwenikweni, ngati tingaone m’khalidwewo m’maganizo mwathu​—Yesu pamodzi nafe m’goli​—nkwapafupi kwa ife kuona amene kwenikweni amanyamula mtolo wolemera wa katunduyo. Zikufanana ndi kamwana kamene kayedzamira pa chogwirira cha pulemu, kakumalingalira kuti kakuikankhira kutsogolo, koma kwenikweni, ndi kholo limene likuikankha. Monga Atate wachikondi, Yehova Mulungu amadziŵa bwino lomwe zolephera ndi zofooka zathu, ndipo amathandiza pa zosoŵa zathu mwa Yesu Kristu. “Mulungu . . . adzakwaniritsa chosoŵa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Kristu Yesu,” anatero Paulo.​—Afilipi 4:19; yerekezerani ndi Yesaya 65:24.

10. Kodi zinthu zimamuyendera motani munthu amene amaona nkhani ya kukhala wophunzira kukhala yaikulu?

10 Akristu odzipatulira ambiri azindikira zimenezi mwa kudzionera okha. Mwachitsanzo, pali Jenny, amene amaona kuti kutumikira monga mpainiya wothandiza mwezi uliwonse ndi kugwira ntchito yakuthupi yotanganitsa kwambiri kumamupanikiza kwambiri. Komabe, amalingalira kuti kwenikweni ntchito yaupainiya imamuthandiza kukhala wokhazikika maganizo. Kuthandiza anthu kuphunzira choonadi cha Baibulo ndi kuwaona akumasintha moyo wawo kuti apeze chiyanjo cha Mulungu​—ndi kumene kumampatsa chimwemwe chachikulu koposa m’moyo wake wotanganidwa. Amavomereza ndi mtima wonse mawu a miyambo akuti: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”​—Miyambo 10:22.

Katundu Wopepuka

11, 12. Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anati: “Katundu wanga ali wopepuka”?

11 Kuwonjezera pa kutilonjeza goli “lofeŵa,” Yesu akutitsimikizira kuti: “Katundu wanga ali wopepuka.” Goli “lofeŵa” limakhala litapeputsa kale ntchito; ngati katunduyo apeputsidwanso, ntchitoyo imangokhala yosangalatsa. Komabe, kodi Yesu anatanthauzanji ndi mawu amenewo?

12 Talingalirani zimene mlimi angachite pamene afuna kusintha ntchito za ng’ombe zake, tinene kuti kukoka ngolo m’malo mwa kulima munda. Choyamba adzamasula chikhasu ndi kumangako ngolo. Kungakhale kosayenera kuti iye amange chikhasu pamodzi ndi ngolo ku ng’ombezo. Mofananamo, Yesu sanali kuuza anthu kusanjika katundu wake pamwamba pa amene anali atanyamula kale. Iye anati kwa ophunzira ake: “Palibe mnyamata wa m’nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye aŵiri.” (Luka 16:13) Motero, Yesu anali kupatsa anthu chosankha. Kodi iwo akanangopitiriza kunyamula katundu wolemera amene anali nawo, kapena kodi akanautula ndi kulandira amene iye anali kuwapatsa? Yesu anawapatsa chilimbikitso chachikondi chakuti: “Katundu wanga ali wopepuka.”

13. Kodi anthu a m’tsiku la Yesu anali kusenza katundu wotani, ndipo chotulukapo chinali chiyani?

13 M’tsiku la Yesu, anthu anali kuvutika ndi katundu wolemera amene anawasenzetsa olamulira Achiroma otsenderezawo pamodzi ndi atsogoleri achipembedzo achiphamaso ndi onyenga. (Mateyu 23:23) Poyesetsa kuti atule mtolo wa Aromawo, anthu ena anayesa kusintha zinthu iwo okha. Anadziloŵetsa m’mikangano yandale, koma mapeto awo anakhala atsoka. (Machitidwe 5:36, 37) Ena analimbikira pa kupeza chitukuko cha moyo wawo mwa kudziloŵetsa kwambiri m’ntchito zakuthupi. (Mateyu 19:21, 22; Luka 14:18-20) Pamene Yesu anawasonyeza njira yopezera mpumulo mwa kuwaitana kuti akhale ophunzira ake, si onse amene anali ofunitsitsa kuvomera. Anazengereza kutula katundu amene ananyamula, ngakhale kuti anali wolemera kwambiri, ndi kuti anyamule wake. (Luka 9:59-62) Ha, ndi kuphonya kwatsoka kotani nanga!

14. Kodi nkhaŵa za moyo ndi kukhumba zinthu zakuthupi zingatilemetse motani?

14 Ngati sitisamala, tingachite kuphonya kumodzimodziko lerolino. Kukhala kwathu ophunzira a Yesu kumatimasula pa kumenyera zonulirapo ndi miyezo imene anthu adziko amamenyera kupeza. Ngakhale kuti tiyenerabe kugwira ntchito zolimba kuti tipeze zofunika za tsiku ndi tsiku, sitimapanga zinthu zimenezi kukhala chinthu choyamba m’moyo wathu. Komabe, nkhaŵa za moyo ndi chinyengo cha maubwino a zinthu zakuthupi zingakhale ndi chisonkhezero cha mphamvu pa ife. Ngati tizilola, zikhumbo zoterozo zingatsamwitse choonadi chimene tinachilandira kale. (Mateyu 13:22) Tingakhale otanganitsidwa kwambiri ndi kufuna kukwaniritsa zikhumbo zimenezo kwakuti mathayo athu Achikristu amakhala otopetsa ndiyeno nkumangowachita mofulumira kuti tiwatsirize ndi kuti zitichoke. Kunena zoona, sitingayembekezere kupeza mpumulo uliwonse mu utumiki wathu kwa Mulungu ngati tiuchita ndi mzimu umenewo.

15. Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani ponena za kukhumba zinthu zakuthupi?

15 Yesu anasonyeza kuti moyo wokhutiritsa sumadza ndi kumenyera kukwaniritsa zofuna zathu zonse, koma umadza ndi kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri m’moyo. “Musadere nkhaŵa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala,” anatero iye. “Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?” Ndiyeno anawakumbutsa za mbalame za mumlengalenga nati: “Sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa kumwamba azidyetsa.” Ponena za maluŵa a kuthengo, anati: “Sagwiritsa ntchito, kapena sapota: koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la ameneŵa.”​—Mateyu 6:25-29.

16. Kodi zochitika zasonyezanji ponena za chisonkhezero cha zofuna za kuthupi?

16 Kodi tingaphunzirepo kanthu kena pa maphunziro osavuta a zinthu ameneŵa? Nkodziŵika bwino kuti pamene munthu amenyera zolimba kuti atukuke pa moyo wake, ndi pamenenso amamwerekera kwambiri m’zofuna za dziko ndipo ndi pamenenso mtolo umakhala wolemera kwambiri pamapeŵa ake. Dzikoli lili ndi anthu ambiri amene kufuna kwawo chitukuko kwawasiya ndi mabanja osweka, maukwati osamvana, matenda, ndi mavuto ena. (Luka 9:25; 1 Timoteo 6:9, 10) Wopata mphotho ya Nobel, Albert Einstein anati panthaŵi ina: “Zinthu zokhala nazo, chipambano chakunja, kutchuka, zinthu zabwino​—zonsezi nthaŵi zonse zakhala zondinyansa. Ndimakhulupirira kuti moyo wopepuka ndi wosadzitukumula ndiwo wabwino koposa kwa aliyense.” Mawu ameneŵa amangobwereza uphungu wosavuta wa mtumwi Paulo wakuti: “Chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu.”​—1 Timoteo 6:6.

17. Kodi Baibulo limalangiza kukhala ndi moyo wotani?

17 Pali mbali ina yofunika kwambiri imene sitiyenera kunyalanyaza. Ngakhale kuti “moyo wopepuka ndi wosadzitukumula” uli ndi mapindu ambiri, mwa uwo wokha sumabweretsa chikhutiro. Pali anthu ambiri amene moyo wawo uli wopepuka chifukwa cha mikhalidwe, komabe sali okhutira kapena achimwemwe konse. Baibulo silikutilimbikitsa kuleka kusangalala ndi zinthu zakuthupi ndiyeno nkukhala ndi moyo wodzisautsa. Chigogomezero chili pa kudzipereka kwaumulungu, osati pa kukhala ndi zinthu zokwanira. Timakhala ndi ‘phindu lalikulu’ kokha pamene tigwirizanitsa pamodzi ziŵirizo. Kodi ndi phindu lotani? M’kalata imodzimodziyo, Paulo anapitiriza kusonyeza kuti aja amene ‘sayembekezera chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu’ adzakhala ‘akudzikundikira okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.’​—1 Timoteo 6:17-19.

18. (a) Kodi munthu angapeze motani mpumulo weniweni? (b) Kodi tiyenera kuwaona motani masinthidwe amene tingafunikire kupanga?

18 Tidzapeza mpumulo ngati tiphunzira kutula katundu wathu wolemera amene tingakhale tikunyamula ndi kutenga katundu wopepuka amene Yesu akuupereka. Ambiri amene akonza miyoyo yawo kuti akhale ndi phande lokulirapo mu utumiki wa Ufumu apeza njira ya moyo ya chimwemwe ndi chikhutiro. Inde, kuti munthu achite zimenezo ayenera kukhala ndi chikhulupiriro ndi kulimba, ndipo pangakhalenso zopinga zina panjirayo. Koma Baibulo limatikumbutsa kuti: “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.” (Mlaliki 11:4) Zinthu zambiri sizili zovuta kwenikweni pamene tangotsimikiza mtima kuti tidzazichita. Zikuoneka kuti, mbali yovuta kwambiri ndiyo kutsimikiza m’maganizo. Tingadzitopetse tokha mwa kulimbana ndi lingalirolo kapena ndi kulikaniza. Ngati titsimikiza m’maganizo ndi kufuna kumenyera pa vutolo, tingadabwe mmene ilo limadzakhalira dalitso. Wamasalmo analimbikitsa kuti: “Talaŵani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.”​—Salmo 34:8; 1 Petro 1:13.

“Mpumulo wa Miyoyo Yanu”

19. (a) Kodi tiyenera kuyembekezeranji pamene mikhalidwe ya dziko ikupitiriza kuipa? (b) Kodi timakhala otsimikiza za chiyani pokhala m’goli la Yesu?

19 Mtumwi Paulo anakumbutsa ophunzira a m’zaka za zana loyamba kuti: “Tiyenera kuloŵa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.” (Machitidwe 14:22) Zimenezo nzoona ndi lerolino. Pamene mikhalidwe ya dziko ikupitiriza kuipa, zovuta zimene aja onse ofuna kukhala ndi moyo wolungama ndi wa kudzipereka kwaumulungu amayang’anizana nazo zidzakulirapo kwambiri. (2 Timoteo 3:12; Chivumbulutso 13:16, 17) Komabe, timamva monga momwe Paulo anamvera pamene anati: “Ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osawonongeka.” Chifukwa chake nchakuti tingadalire pa Yesu Kristu kuti adzatipatsa nyonga yoposa yachibadwa. (2 Akorinto 4:7-9) Mwa kulandira ndi mtima wonse goli la kukhala wophunzira, lonjezo la Yesu lidzakwaniritsidwa kwa ife lakuti: “Mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.”​—Mateyu 11:29.

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi goli lofeŵa limene Yesu analonjeza linali chiyani?

◻ Kodi tiyenera kuchitanji ngati timva kuti goli lathu likukhala mtolo wolemetsa?

◻ Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anati: “Katundu wanga ali wopepuka”?

◻ Kodi tingachitenji kuti katundu wathu akhalebe wopepuka?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena