Tidzam’bwezera Motani Yehova?
PAMENE winawake atenga chikondwerero chenicheni, chotentha mwa ife, mwinamwake kuchita chinachake kaamba ka phindu lathu, ndimotani mmene timavomerezera? Kukoma mtima ndi kuwolowa manja nthaŵi zambiri kumabweretsa yankho, kodi sizimatero? Ndi ati, chotero, amene ali malingaliro athu kulinga kwa Mulungu wathu, Yehova, kaamba ka chikondi chake chokoma mtima chokhazikika kwa ife?
Chiri chopepuka, ofulumizidwa monga mmene tiriri ndi zididikizo za tsiku ndi tsiku za moyo, kutenga mapindu a Yehova mosasamala, nthaŵi zina ngakhale kuchita ngati kuti sitiri mowonadi oyamikira. Tingachite bwino, chotero, kuima ndi kuwunikira pa funso la wamasalmo: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zonse anandichitira?” (Salmo 116:12) Ndi m’njira zotani mmene tingavomerezere?
Mapindu Ochokera kwa Yehova
Popanda mphatso ya Yehova ya Mawu ake, Baibulo, tikanakhala otaika chotani nanga! Amuna ndi akazi olimba mtima m’zaka mazana apita anaika m’ngozi miyoyo yawo kuti akhale nalo ndi kuŵerenga bukhuli, ndipo takula m’kumvetsetsa chifukwa chake. Anthu a Mulungu nthaŵi zonse akhala oyamikira kaamba ka Malemba owuziridwa, akumadziŵa mmene liriri lopindulitsa “kaamba ka chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.”—2 Timoteo 3:16.
Tikudziŵa, ngakhale ndi tero, kuti tikhale “okonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino,” tifunikira zoposa kokha chidziŵitso cha m’mutu cha Baibulo. (2 Timoteo 3:17) Chiri kupyolera mu mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu kuti phindu limabweretsedwa ku miyoyo yathu, ndipo nsonga imeneyi ikukokeredwa ku chisamaliro chathu ndi malongosoledwe okoka a Yehova kupyolera mwa mneneri wake Yesaya: “Ndipo tsopano [Mfumu, NW] Ambuye [Yehova, NW] wanditumiza ine ndi mzimu wake. Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israyeli: ‘Ine, ndine Yehova, Mulungu wako, Amene ndikuphunzitsa kupindula, Amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga! Mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.’” (Yesaya 48:16-18) Kupyolera mwa mzimu wake woyera, m’chigwirizano ndi Mawu ake, Yehova akutitsogoza ife kuti tipindule ife eni, ndipo chotulukapo chake chiri mtendere ndi chilungamo.
Kuwonjezerapo, mphamvu yogwira ntchito ya Yehova imagwira ntchito mokhutiritsa kaamba ka phindu lathu chifukwa chakuti dongosolo lapangidwa, gulu la pa dziko lapansi, kupyolera mwa limene mzimu wake woyera umagwira ntchito. Pa 1 Akorinto mutu 12, Paulo akuyerekeza mpingo Wachikristu ku thupi ndi kunena m’versi 7 kuti: “Koma kwa yense kwapatsidwa mawonekedwa a mzimu kuti apindule nawo.” Iye akupitiriza kusonyeza mmene tingapindulire kuchokera ku kukhala mbali ya gulu la pa dziko lapansi la Mulungu.
Zaka zisanu kapena zochulukirapo pambuyo pa kulemba kwake mawu amenewo, iye analemba kalata yake ku mpingo wa mu Efeso mu imene anakulitsa pa mapindu a kukhala wogwirizana ndi makonzedwe a pa dziko lapansi amenewo. Ngakhale kuti chimene ananena chinagwira ntchito choyambirira kwa Akristu odzozedwa, kodi awo a “khamu lalikulu” lerolino nawonso sali ‘okonzedwa kaamba ka ntchito ya utumiki,’ akumakhala ‘amuna achikulire’ mwauzimu, okhazikika m’chikhulupiriro, ‘osakhalanso ana,’ ndi ‘chikondi kumakula mu zinthu zonse mwa iye amene ali mutu, Kristu’? (Chivumbulutso 7:9; Aefeso 4:12-16) Tonsefe tiri ndi chifukwa chabwino cha kukhalira oyamikira.
Wozindikiritsidwa ndi mpingo Wachikristu ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene ntchito yake, ya kutidyetsa ife mwauzimu, irinso umboni wina wakuti Yehova akutipindulitsa ife. (Mateyu 24:45, 46) Tiri pano tsopano m’nthaŵi yonenedweratu ya kukhalapo kwa Ambuye. Kodi “kapolo” akuchita ntchito yake? Mosasamala kanthu za chizimezime cha “masiku otsiriza” amenewa, kodi tadzazidwa ndi chiyembekezo? (2 Timoteo 3:1-5; Aroma 5:5; 1 Timoteo 4:10) Inde! Ndipo chiyembekezo chathu sichiri kokha chokaikira koma chitsimikiziro chotsimikizirika chomangiriridwa pa chikhulupiriro, chimene m’kubwezera chiri chozikidwa pa umboni wolimba.—Ahebri 11:1.
Mowonekera, chotero, Yehova, Wopindulitsa wathu Wamkulu, watipatsa ife zochulukira kaamba ka zimene tiyenera kukhala oyamikira. Funso molingalirika litsatira:
Nchiyani Chomwe Ndidzabwezera kwa Yehova?
Choyamba, tiyenera kuvomereza kuti Yehova samafuna chirichonse kuchokera kwa ife. Iye ali amene akunena kuti, “Siliva ndi wanga, golidi ndi wanga,” mofananamo “ng’ombe za pa mapiri zikwi.” (Hagai 2:8; Salmo 50:10; Yobu 41:11) Ichi chimatanthauza kuti palibe njira ndi imodzi yomwe imene “tingagulire” chiyanjo cha Yehova; komabe tikulimbikitsidwa kupanga zopereka za ufulu kwa iye. (Yerekezani ndi 1 Mbiri 29:14.) Pali mikhalidwe ina yake, ngakhale kuli tero, ku kukhala kwathu ovomerezedwa kupereka mphatso kwa Yehova.
“Ndidzafika kwa Yehova ndi chiyani? Ndi kuwerama kwa Mulungu wam’mwamba? Kodi ndifike kwa iye ndi nsembe zopsyereza, ndi ana a ng’ombe a chaka chimodzi? Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga? Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chiri chokoma. Ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”—Mika 6:6-8.
Tikuphunzira kuchokera ku chimenechi kuti zofuna za Yehova ziri nthaŵi zonse zolingalirika, nthaŵi zonse zopezeka. M’kuwonjezerapo, Yesu analozeratu chofunika choyambirira kuti unansi wathu ponse paŵiri ndi Yehova ndi anthu anzathu uyenera kukhala woyenera kotero kuti zopereka zathu zilandiridwe. (Mateyu 5:23, 24) Pokhala titaika maziko olondola, tsopano tingawone kuti tonsefe tiri ndi chinachake chopatsa Yehova, m’chiyamikiro kaamba ka ubwino wake kwa ife.
Ndimotani Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zimene Tiri Nazo?
Chimatenga nthaŵi, kuyesetsa, ndi ku mlingo winawake ndalama, koma ndi mwaŵi wotani nanga umene iwo uli kuimira Yehova mu ntchito yolalikira! Nsembe imeneyi ya chitamando iri chinachake chimene tonsefe tingampatse Yehova. Pano pali mmene mkulu wachipainiya mmodzi wokhala ndi ana ang’ono atatu akumverera ponena za icho:
“Kugawanamo mu mwaŵi wa utumiki wa nthaŵi zonse kuli koyenerera nsembe yaumwini iriyonse—ndipo moposerapo—chifukwa iri njira yokhutiritsa kwambiri ya kuperekera chitamando kwa Atate wathu wa kumwamba. Ndiponso, imanditheketsa ine ku mlingo winawake kumuyamika iye kaamba ka chifundo chake chokoma mtima chosonyezedwa kwa ine mwaumwini.”
Mkazi wake akuwonjezera kuti: “Ulidi mwaŵi weniweni kuthandiza mwamuna wanga kuchita upainiya. Chimatheketsa banja lonse kukhala ndi kugawanamo kokulira mu utumiki, ndi kuwona dzanja lachikondi la Yehova likupereka kaamba ka ife m’njira yauzimu ndi ya kuthupi kumatipangitsa ife kufuna kutamanda iye mowonjezereka.”
Watch Tower Society yagawira maBaibulo ndi mabukhu a Baibulo pa maziko aufulu kwa zoposa zaka zana limodzi ndi kusindikiza izi pa makina ake chiyambire 1920. Nthaŵi ndi kuyesetsa kwa odzipereka aufulu ogwira ntchito pa Beteli kutulutsa zofalitsidwa zonse zomwe tiri nazo lerolino, limodzi ndi zija za ofalitsa ndi apainiya a mpingo zoti azigawire, kwakhala, m’chenicheni, chopereka chowonjezereka ku ntchito yolalikira yofunika koposa.—Mateyu 24:14.
Ndiponso, Akristu m’maiko okhazikika koposa m’zachuma ali okondweretsedwa kudziŵa kuti mphatso zawo za chifundo za ndalama, zotumizidwa ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society m’dziko lawo, zimatheketsa abale awo ambiri m’mbali zina za dziko kuthera nthaŵi yawo yonse m’kulalikira ndi kupanga ophunzira. Amishonale ochokera ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, oyang’anira adera ndi achigawo, ndi apainiya apadera onsewo amathandizidwa kupitiriza mu utumiki wawo wa nthaŵi zonse ndi zopereka zaufulu zimenezi.
Mwinamwake chiri chosatheka kwa inu kutumikira pa Beteli kapena monga chiwalo cha Wantchito Waufulu wa Programu Yomanga ya Mitundu Yonse. Koma mwinamwake muli ndi ndalama zomwe zingachirikize awo omwe adzilowetsa mu ntchito imeneyi koma omwe akusowa ndalama “zowonjezereka” kudzisungirira iwo eni mu iyo. Kulinganiza kothandiza chotero kungachitike, monga momwe kwalongosoledwera pa 2 Akorinto 8:14. Makalata otsagana ndi zopereka zoterozo aphatikizapo yotsatirayi yochokera kwa mlongo wachikulire yemwe analemba kuti:
“Ndiri woyamikira koposa kaamba ka madalitso onse amene Yehova amandipatsa ine, ndipo ndimapemphera kaamba ka maprojekiti omanga ndi gulu mopitirizabe.”
Mlongo wina ananena kuti: “Ndingakonde kuti ndalama yochepera iyi ichite ubwino wina mwa teokratiki kuposa kukhala mu banki yomwe idzagwa posachedwapa!”
Mbale anadzilongosola iyemwini m’mawu awa: “Kutipatsa uphungu kwa Yehova kwa kugwiritsira ntchito chuma chathu kulemekeza iye iri njira ya chitetezero chenicheni kuchokera ku malonda aumbombo, ‘phiko lachitatu’ la dongosolo loipa la zinthu la Satana. Lolani kuti nditenge mwaŵi uwu kunena mmene ndiriri wachimwemwe kugawirako chinachake ku kufulumiza kwa kuwonjezeka kumene Yehova akutipatsa ife, ndipo ndimamuyamikira iye kaamba ka kuchipangitsa icho kukhala chothekera kwa ine kugwiritsiridwa ntchito.”
Mphatso Zochokera kwa Achikulire ndi Achichepere
Chiri cholimbikitsa kuŵerenga za chigamulo chokhulupirika cha achikulire omwe, ngakhale kuti amayembekezera kupulumuka ku mapeto a dongosolo iri, amatsimikizira, mwa kupanga chikalata chosiyiridwa chuma chamasiye choyenerera, kuti ntchito ya Ufumu ikupindula m’chochitika cha imfa yawo. Malongosoledwe ena olandiridwa kuchokera kwa nduna zotsimikizira chikalata cha kugawa chuma chamasiye, ochitira ndemanga pa mkhalidwe wabwino wa malemuwo, amaphatikizapo:
“Munthu wachifundo koposa kwa aliyense, moyo wake wonse . . . iye anakonda Yehova ndi chilengedwe chake.”
“Nthaŵi zonse, zikondwerero za Ufumu zinali chodera nkhaŵa chake choyambirira.”
“Iye anafikira mphoto yake ya kumwamba pambuyo pa zaka 70 za utumiki wokhulupirika . . . iye nthaŵi zonse anafuna kupititsa patsogolo chowonadi ndi chuma chake.”
Timakondweranso kumva kuchokera kwa achichepere, ofunitsitsa kugwiritsira ntchito zinthu zawo zakuthupi ku ntchito ya Yehova. Kalata imodzi yolandiridwa ku ofesi ya Sosaite mu Britain inachokera kwa wofalitsa wa msinkhu wopita ku sukulu. Iye anasimba kuti iye anapata mphoto yoyambirira mu mpikisano wa kulemba nkhani. Iye anatsekeramo mphoto ya ndalama yonseyo. Zofalitsidwa za Sosaite zinali magwero okulira a nkhani yake yolemba pa “Kudzipereka kwa Chikristu,” chotero iye anadzimva kuti ndalamayo moyenerera inali ya Yehova.
Pambuyo pa kufunsa chimene iye adzamubwezera Yehova, mlembi wa Salmo 116 akupitiriza mu maversi 13 ndi 14 kunena kuti: “Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova. Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse.” Tikumayamikira mphatso yapadera ya chipulumutso kuchokera kwa Yehova kupyolera mwa Mwana wake, timadzimva ofulumizidwa, monga mmene anachitira wamasalmo, kuitanira pa Iye ndi kusunga malonjezo athu kwa Iye.
Yehova watipindulitsa ife mokulira koposa, ndipo chirichonse chomwe tingachite m’kubwezera chimawoneka kukhala chaching’ono m’kuyerekezera. Ndi choyenerera chotani nanga, kenaka, kuti monga kalongosoledwe ka chiyamikiro, tichite zonse zimene tingathe, m’njira iriyonse! “Ndidzapereka kwa inu nsembe ya chiyamiko, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.”—Salmo 116:17.
[Bokosi patsamba 26]
MMENE ENA AMAPEREKERA KU NTCHITO YA UFUMU
◻ MPHATSO: Zopereka zaufulu za ndalama zingatumizidwe mwachindunji ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 21598, Kitwe. Zinthu zonga ngati munda, limodzinso ndi zokometsera kapena zinthu zina za mtengo wapatali, zingaperekedwenso. Kalata yachidule yolongosola kuti zimenezo ziri zopereka zaufulu iyenera kutsagana ndi zopereka zimenezi.l
◻ MAKONZEDWE A CHOPEREKA CHOKHALA NDI MALIRE: Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuti zisungidwe mwa kuikiza, ndi makonzedwe akuti ngati pali chifuno chaumwini, zidzabwezeredwa kwa woperekayo.
◻ INSUWARANSI: Watch Tower Society ingatchulidwe monga mwini wa lamulo wa insuwaransi ya moyo kapena makonzedwe a kuleka ntchito/ndi kupuma ntchito. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa ponena za makonzedwe aliwonse oterowo.
◻ KUIKIZIDWA: Ndalama zosungidwa ku banki zingaikidwe mu kuikizidwa kaamba ka Sosaite. Ngati ichi chachitidwa, chonde dziŵitsani Sosaite. Ndalama, mapangano, ndi katundu zingaperekedwenso pansi pa makonzedwe a kupindulira woperekayo mkati mwa moyo wake wonse. Njira imeneyi imathetsa ndalama zowonongedwa ndi kusatsimikizirika kwa pangano losatsimikiziridwa ndi maulamuliro, pamene mukutsimikizira kuti Sosaite idzalandira katunduyo m’chochitika cha imfa.
◻ MAPANGANO A KUGAWA CHUMA CHA MASIYE: Katundu kapena ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kupyolera mwa pangano la kugawa katundu loikidwa mwa lamulo. Kope liyenera kutumizidwa ku Sosaite.
Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka ndi malangizo onena za nkhani zoterezi, lemberani ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 21598, Kitwe.