Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 12/1 tsamba 24
  • Kusungirira Chikhulupiriro m’Nyumba Yogawanika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusungirira Chikhulupiriro m’Nyumba Yogawanika
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zotulukapo za Kuchitira Umboni ku Banja Lake
  • Kuchokera ku Tondovi Kumka ku Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Mulungu Alibe Tsankhu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Chikondi Chigwirizanitsa Mabanja
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 12/1 tsamba 24

Ripoti la Olengeza Ufumu

Kusungirira Chikhulupiriro m’Nyumba Yogawanika

MTUMWI Paulo anachenjeza Akristu kuti: “Udzipenyerere wekha ndi chiphunzitsocho. Udzikhala mu izi pakuti, pakuchita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) M’dziko lina la Kum’mawa, ‘kukhala’ mwa ziphunzitso za Baibulo kunatulukapo madalitso ozizwitsa kwa Akazi a L​——​ pambuyo pa kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova.

Akazi a L​——​ ndi amuna awo onse aŵiri anachokera ku mabanja a Chihindu. Mkaziyo anachezeredwa ndi Mboni za Yehova mu 1959, ndipo pambuyo pa kuphunzira Baibulo ndi iwo, iye analandira chowonadi cha Mawu a Mulungu. Kenaka iye anachitira umboni kwa mwamuna wake ndi anansi ena. (Yerekezani ndi Yohane 1:40, 41.) Mwamuna wake sanasonyeze chikondwerero, koma mlongo wake wa kuthupi R​——​ anagwirizana m’phunzirolo. Mu 1961 iye ndi mlongo wake anabatizidwa m’chisonyezero cha kudzipereka kwawo kwa Yehova. Pamene ana a Mlongo L​——​ anakula, anaphunzira ndi iwo ndi kuwatenga iwo ku misonkhano. Pamene mwana wamkazi wamkulu koposa, S​——, anamaliza sukulu, iye anapereka moyo wake kwa Yehova, anabatizidwa, ndi kukwatiwa ndi Mboni. M’kupita kwa nthaŵi, ngakhale kuli tero, iye ndi mwamuna wake onse aŵiri anakhala osakangalika. Mwana wamwamuna wamkulu koposa anapita ku maphunziro apamwamba ndi kulowa m’mayanjano oipa. Kenaka iye anakwatira mtsikana wa chikatolika ndi kusiya kuyanjana ndi anthu a Yehova. Ku mbali ina, mwana wamkazi wamng’ono, pambuyo pomaliza sukulu, anapereka moyo wake kwa Yehova ndipo anabatizidwa.

Mlongo L​——​ anapitiriza kuchitira umboni kwa anansi ake. Mlongo wina wa kuthupi anakhala wokondwerera, koma mwamuna wake anamtsutsa iye moipa, kufikira pa kuwononga Baibulo lake ndi mabukhu. Iye sanaloledwe kutenga ana ake atatu ku misonkhano, koma iye anaphunzira ndi iwo kunyumba. M’kupita kwa nthaŵi iye nayenso anapanga kudzipereka ndipo anabatizidwa, m’chiyang’aniro cha chitsutso champhamvu kuchokera kwa mwamuna wake. Potsirizira pake, onse atatu a ana ake anakhala Mboni zodzipereka ndi zobatizidwa.

Pa nthaŵiyo, Mlongo L​——​ anapitiriza kuchitira umboni kwa anansi ake a kuthupi. Pamene analankhula ndi mbale wake ndi mkazi wake, mbaleyo sanasonyeze chikondwerero chirichonse, koma mkazi wake anamvetsera. Pambuyo popeza chidziŵitso chokwanira cha Baibulo, iye anapereka moyo wake kwa Mulungu ndipo anachitira chizindikiro ichi mwa kubatizidwa m’madzi.

Mlongo L​——​ anachitira umboni kwa mbale wina wa kuthupi, yemwe anatsutsa chowonadi. Koma mkazi wake, limodzi ndi mwana wawo wamkazi, anayamba kuphunzira. Mwana wamkaziyo anatumizidwa ku Canada kaamba ka maphunziro a kudziko owonjezereka koma anapitirizabe ndi phunziro lake la Baibulo ndi kuyanjana ndi Mboni kumeneko. Kenaka, nayenso anatenga kaimidwe kake kaamba ka chowonadi ndipo anabatiziddwa. Iye anakwatiwa ndi mbale wachipainiya mu Canada, ndipo atate wake ndi amake anapezekapo pa ukwatiwo. Mayanjano ndi abale ku Canada anali ndi chiyambukiro chabwino pa atatewo.

Zotulukapo za Kuchitira Umboni ku Banja Lake

Zoyesayesa zokhulupirika za Mlongo L​——​ zinadalitsidwa ndi Yehova. M’kupita kwa nthaŵi mwana wake wamkazi wamng’ono koposa anasiya ntchito yake ya malipiro abwino, kutenga ntchito ya pa kanthaŵi, ndi kuyamba kutumikira Yehova monga mtumiki wa nthaŵi zonse. Mwana wamkazi wamkulu kwambiri ndi mwamuna wake anayamba kuphunzira ndi kupezeka pa misonkhano kachiŵirinso ndipo anakhala okangalika mu utumiki. Mwana wake wamwamuna yemwe anakwatira mtsikana wa Chikatolika ndi kupatuka ku chowonadi anayambanso kuphunzira ndipo potsirizira pake anapereka moyo wake kwa Yehova ndipo anabatizidwa. Mwana wamwamuna wamng’ono koposa anakhala wodzipereka ndipo anabatizidwa ndipo kenaka anatenga kaimidwe kake ku nkhani ya uchete. (Yesaya 2:4) Iye analamulidwa kukhala zaka zitatu m’ndende ya nkhondo, koma mkati mwa zonsezi iye anapereka umboni wamphamvu pamaso pa oŵeruza a bwalo lamilandu. Atate wake, mwamuna wa Mlongo L​——, anali wosangalatsidwa koposa ndi kaimidwe kamene mwana wake wamwamuna anatenga kotero kuti iye tsopano anakhala wokondweretsedwa ndi kuyamba kupezeka pa misonkhano.

Ndithudi, ndimotani nanga mmene zinakhalira zokhutiritsa ndi zopatsa mphoto zaka 29 za utumiki wokhulupirika za Mlongo L​——​ m’nyumba yogawanika! Iye tsopano amasangalala kuŵerenga ziwalo 18 za banja ndi anansi a kuthupi omwe akhala obatizidwa. Lolani kuti chokumana nacho chimenechi chikhale magwero a chilimbikitso ndi chitonthozo kwa ambiri a abale ndi alongo athu amene, pansi pa mikhalidwe yofananayo, ayenera kupirira ndi kusungirira chikhulupiriro m’nyumba zogawanika,​—1 Petro 2:19, 20; 1 Akorinto 7:12-16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena