Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 August tsamba 5
  • Achinyamata, Mukhale “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata, Mukhale “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Muzitamanda Yehova Pochita Upainiya
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Kusintha Maola Ofunika kwa Apainiya
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Madalitso a Utumiki wa Upainiya
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 August tsamba 5

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Achinyamata, Mukhale “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”

M’kalata yake youziridwa yopita kwa Tito, mtumwi Paulo ananena kuti achinyamata, kuphatikizapo Tito, ayenera kuyesetsa kuti akhale “chitsanzo pa ntchito zabwino.” (Tito 2:6, 7) Chakumapeto kwa chaputala chomwecho, Paulo anasonyeza kuti Yesu anapereka moyo wake n’kuyeretsa anthu a Yehova kuti akhale “odzipereka pa ntchito zabwino.” (Tito 2:14) Imodzi mwa ntchito zabwino zimenezi ndi kulalikira komanso kuphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu. Ngati ndinu wachinyamata, kodi mungagwiritse ntchito mphamvu zanu pochita upainiya wothandiza kapena wokhazikika?​—Miy. 20:29.

Ngati mukufuna kukhala mpainiya, muyenera kusintha zinthu zina kuti muzipeza mpata woti mukwaniritse cholinga chimenechi. (Luka 14:28-30) Mwachitsanzo mungadzifunse kuti, kodi ndizidzapeza bwanji ndalama zogulira zinthu zofunika ndikamadzachita utumiki wa nthawi zonse? Kodi ndizidzakwanitsa bwanji maola ofunika? Mungachite bwino kumufotokozera Yehova nkhani imeneyi m’pemphero. (Sal. 37:5) Mukhozanso kukambirana nkhaniyi ndi makolo anu komanso abale ndi alongo omwe akhala akuchita utumikiwu kwa nthawi yaitali. Kenako yesetsani kuti mukwaniritse cholinga chanucho. Mukatero Yehova adzakudalitsani kwambiri chifukwa chodzipereka kuti muzimutumikira.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ACHINYAMATA AMENE AKULEMEKEZA YEHOVA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ena analimbana ndi mavuto otani kuti akwanitse kuchita upainiya, nanga anakwanitsa bwanji kuchita zimenezi?

  • Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhale apainiya okhazikika?

  • N’chifukwa chiyani mpainiya ayenera kukhala ndi ndandanda yabwino?

  • Kodi Akhristu ena onse mumpingo angalimbikitse komanso kuthandiza apainiya m’njira zotani?

  • Kodi apainiya amapeza madalitso otani?

Mlongo wachitsikana akuuza bambo ake zoti akufuna kuchita upainiya; m’bale wachinyamata yemwe akuchita upainiya akulemba ndandanda yake; mlongo wachitsikana akulalikira mnzake; mlongo wachitsikana, yemwe ndi mpainiya, akuphunzira Baibulo ndi mayi wina

Kodi ndi zinthu ziti zomwe ndingachite kuti ndikhale mpainiya?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena