MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzitamanda Yehova Pochita Upainiya
Aisiraeli anali ndi zifukwa zomveka zotamandira Yehova. Anawatulutsa m’dziko la Iguputo komanso anawapulumutsa kwa asilikali a Farao. (Eks 15:1, 2) Yehova akupitirizabe kuchitira anthu ake zinthu zabwino. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira zomwe amatichitira?—Sl 116:12.
Njira imodzi ndi kuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Mungapemphe Yehova kuti akupatseni mphamvu komanso mtima wofuna kuchita upainiya. (Afi 2:13) Ambiri amayamba ndi kuchita upainiya wothandiza. Mungasankhe wa maola 30 kapena 50 m’miyezi ya March ndi April kapena pa nthawi imene woyang’anira dera akuchezera mpingo wanu. Pambuyo poona mmene mungasangalalire ndi upainiya wothandiza, mukhoza kukhala ndi mtima wofuna kuyamba upainiya wokhazikika. Ngakhale ena amene amagwira ntchito yolembedwa kapena ena amene amadwaladwala amakwanitsa kuchita upainiya wokhazikika. (mwb16.07 8) Kunena zoona, Yehova ndi woyenera kumutamanda ndipo tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe.—1Mb 16:25.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ALONGO ATATU APACHIBALE A KU MONGOLIA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi alongo atatuwa anafunika kuthana ndi mavuto ati kuti ayambe upainiya?
Kodi anapeza madalitso otani?
Kodi anakhala ndi mwayi wochita mautumiki ena ati chifukwa choti ankachita upainiya wokhazikika?
Kodi chitsanzo chawo chinathandiza bwanji anthu ena?