Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 11/15 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkhani Yofanana
  • “Wansembe Mpaka Muyaya Monga mwa Unsembe wa Melekizedeki”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Mapeto Akudzawo a “Buku la Nkhondo za Yehova”
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Mudzapindula Kuchokera ku Mapangano a Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1989
Nsanja ya Olonda—1993
w93 11/15 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Popeza kuti wansembe wakaleyo wotchedwa Melikizedeke anali munthu weniweni, kodi nchifukwa ninji Baibulo limanena kuti anali “wopanda maŵerengedwe a chibadwidwe chake”?

Mawuwa ali pa Ahebri 7:3. Onani vesilo mogwirizana ndi nkhani yake:

“Pakuti Melikizedeke uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa, amenenso Abrahamu anamgaŵira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali Mfumu ya chilungamo, pameneponso mfumu ya Salemu, ndiko, Mfumu ya mtendere; wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda maŵerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.”​—Ahebri 7:1-3.

Monga momwe kwatchulidwira, Melikizedeke anali munthu weniweni, monga momwe analiri Abrahamu, amene anachita naye zinthu mwachindunji. (Genesis 14:17-20; Ahebri 7:4-10) Pokhala zili motero, Melikizedeke ayenera kukhala anali ndi makolo, atate ndi amayi, ndipo angakhale anali ndi ana. Chifukwa chake, monga munthu iye anayenera kukhala anali nawo maŵerengedwe a chibadwidwe chake, kapena mzera wabanja. Iye analinso ndi mapeto a moyo wake wakuthupi. Panthaŵi ina, Melikizedeke anafa, mogwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo pa Aroma 5:12, 14. Koma popeza kuti sitikudziŵa pamene Melikizedeke anamwalira ndipo motero analeka kutumikira monga wansembe, m’lingaliro limenelo iye anatumikira popanda mapeto odziŵika alionse.

Mu Ahebri, Paulo anapereka ndemanga zonena za Melikizedeke pamene anali kulankhula za ntchito ya Yesu Kristu monga Mkulu Wansembe wopambana. Potchula Melikizedeke monga phiphiritso, kapena chitsanzo, cha Yesu m’ntchito yaunsembe imeneyi, Paulo anati: ‘Yesu . . . wakhala mkulu wa ansembe nthaŵi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.’ (Ahebri 6:20) M’lingaliro lotani?

Paulo ayenera kukhala atazindikira kuti cholembedwa cha Baibulo sichimapereka tsatanetsatane wonena za mzera wobadwira wa Melikizedeke​—makolo ake kapena ana ake othekera alionse. Zili kokha kuti chidziŵitso chimenecho sichikupezeka m’cholembedwa cha Baibulo. Chifukwa chake, malinga ndi zimene Paulo anadziŵa kapena zimene tikudziŵa, Melikizedeke ananenedwa molondola kukhala “wopanda maŵerengedwe a chibadwidwe chake,” “wopanda mpambo wa mzera wobadwira” (W. J. Conybeare), kapena wopanda “mzera wabanja.”​—J. B. Phillips.

Kodi ndimotani mmene Yesu analiri wotero? Zowona, timadziŵa kuti Atate wa Yesu anali Yehova Mulungu ndi kuti amayi wake waumunthu anali Mariya wa fuko la Yuda. Chikhalirechobe, panali kufanana pakati pa Melikizedeke ndi Yesu. Kodi zili choncho motani? Yesu sanabadwire m’fuko la Levi, fuko la ansembe mumtundu wa Israyeli. Ayi, Yesu sanakhale wansembe mwa mawerengedwe achibadwidwe aumunthu. Ngakhale Melikizedeke, amene sanakhale wansembe “monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi,” ndiko kuti, mwa kubadwira m’fuko ndi banja la ansembe. (Ahebri 7:15, 16) M’malo mokhala wansembe kudzera mwa atate waumunthu amene iyemwiniyo anali wansembe, Yesu ‘anatchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melikizedeke.’​—Ahebri 5:10.

Ndiponso, Yesu sanakhale ndi ana alionse kapena oloŵa m’malo unsembe wake. M’lingaliro limenelinso, iye analibe maŵerengedwe a chibadwidwe chake. Iye adzapitirizabe kuchita utumiki wake waunsembe kwamuyaya monga mlangizi wothandiza. Paulo anapereka ndemanga pa utumiki wosalekeza umenewu, akumati:

“Akhala iye [Yesu] nthaŵi yosatha ali nawo unsembe wosasinthika, kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa iye, popeza ali nawo moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.”​—Ahebri 7:24, 25.

Motero, kupenda kwathu mawu a Paulo pa Ahebri 7:3 sikuyenera kukhala chidziŵitso wamba chongosunga m’maganizo mwathu. Kuyenera kukulitsa chiyamikiro chathu cha makonzedwe achikondi amene Yehova Mulungu watikonzera opezera chikhululukiro cha uchimo kwamuyaya ndi cha mmene walinganizira kuti tipeze chithandizo ndi chitsogozo chosalekeza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena