Chitani Zabwino Ndipo Gawanani ndi Ena
1 Dorika “anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo.” (Mac. 9:36, 39) Mtima wake wopatsa unachititsa kuti anthu amene anali kumudziwa ndiponso Yehova Mulungu azimukonda. Lemba la Ahebri 13:16 limati: “Musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” Kodi masiku ano tingachite bwanji zabwino ndi kugawana ndi ena?
2 Njira imodzi imene tingathandizire ena ndiyo kugawana nawo ‘chuma chathu.’ (Miy. 3:9) Zopereka zathu za ntchito ya padziko lonse zimathandiza kumangira Nyumba za Ufumu, Nyumba za Msonkhano, ndi nthambi padziko lonse. Kuwolowa manja kwathu kwathandiza kuti anthu ambiri apindule ndi malangizo ochokera kwa Mulungu ndiponso mayanjano olimbikitsa auzimu.
3 Kuthandizana: Pakagwa tsoka, anthu a Yehova amakhala okonzeka ‘kuchitira chokoma’ okhulupirira anzawo komanso anthu a zikhulupiriro zina. (Agal. 6:10) Fakitale ina ya zamakhwala itaphulika ku France, banja lina limene limakhala pafupi ndi fakitaleyo linafotokoza kuti: “Abale athu achikristu anabwera nthawi yomweyo kudzatithandiza kuyeretsa m’nyumba yathu komanso nyumba za anthu ena mu mdadadawo. Anthu amene tayandikana nawo nyumba anadabwa kwambiri kuona anthu ambiri amene anabwera kudzatithandiza.” Mlongo wina anawonjezera kuti: “Akulu anatithandiza kwambiri. Anabwera kudzatilimbikitsa. Ndipo n’zimenedi tinafunikira kuposa kupatsidwa ndalama kapena katundu.”
4 Ngakhale kuti pali njira zambiri zimene tingachitire zabwino anzathu, njira yabwino koposa imene tingawathandizire ndiyo kugawana nawo choonadi chamtengo wapatali, chimene chimaphatikizapo “chiyembekezo cha moyo wosatha” chimene Yehova walonjeza. (Tito 1:1, 2) Uthenga wa m’Baibulo umatonthozadi anthu amene akulira chifukwa cha zochitika za dzikoli ndiponso chifukwa cha uchimo wawo. (Mat. 5:4) Tiyeni tichite zabwino ndi kugawana ndi ena ngati tingathe kutero.—Miy. 3:27.