Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/05 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira April 11
  • Mlungu Woyambira April 18
  • Mlungu Woyambira April 25
  • Mlungu Woyambira May 2
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 4/05 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira April 11

Nyimbo Na. 4

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kuchita chitsanzo choonetsa mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya April 15 ndi Galamukani! ya May 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. M’chitsanzo chimodzi, onetsani wofalitsa akuchita ulaliki wa mumsewu. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: “Limbikirani Kulalikira.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kupereka ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.

Mph. 15: Zokumana nazo. Pemphani anthu mu mpingomo kufotokoza zokumana nazo zimene zinawasangalatsa pamene munali ndi ntchito yambiri m’mwezi wa March ndi April mogwirizana ndi Chikumbutso ndi nkhani yapadera.

Nyimbo Na. 47 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 18

Nyimbo Na. 76

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Zokumana nazo. Pemphani omvera kufotokoza zokumana nazo zimene zinawasangalatsa pamene amapanga maulendo obwereza kwa anthu amene anawagawira bulosha la Dikirani! Konzeranitu pasadakhale kudzachita zitsanzo za zokumana nazo zosangalatsa zimene zinachitikadi. Yamikirani onse chifukwa chotenga nawo mbali m’ntchito yapadera imeneyi.

Mph. 15: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo​—Gawo 7.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokonzekera nkhani imeneyi, werengani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002, tsamba 27, ndime 5 ndi 6.

Mph. 15: “Chitani Zabwino Ndipo Gawanani ndi Ena.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambeni mogwirizana ndi kwanuko, ndipo tchulani zinthu zothandiza zimene tingachite kuti tithandize ena.

Nyimbo Na. 169 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 25

Nyimbo Na. 111

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi makalata oyamikira zopereka ochokera ku nthambi. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa April. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu), sonyezani chitsanzo cha mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi Galamukani! ya May 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani mmene tingayankhire munthu amene akufuna kuti tisakambirane naye ponena kuti “Sindili wokondwera.” (Onani buku la Kukambitsirana tsamba 16.) Tchulani nkhani zina za m’magaziniwo zomwe zingakhale zosangalatsa kwa anthu a m’gawo lanu. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 10: Zosowa za pampingo.

Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2005 Wakuti ‘Kumvera Mulungu.’” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mlembi wa mpingo. Limbikitsani onse kuyambiratu panopa kukonzekera msonkhano umenewu.

Nyimbo Na. 8 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 2

Nyimbo Na. 148

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Mwachidule kambani mfundo zazikulu kuchokera mu nkhani yakuti “Kuphunzira Bulosha la Dikirani!” pa tsamba 6. Fotokozani kuti nkhani imeneyi ili ndi ndandanda yosonyeza mmene tiziphunzirira buloshali. Limbikitsani onse kuti azikonzekera mokwanira bwino ndi kukatenga nawo mbali mlungu uliwonse paphunziroli, kuyambira mlungu wa May 23.

Mph. 20: Kuyamba Maphunziro a Baibulo ndi Anthu Amene Analandira Bulosha Latsopano. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani mwachidule chitsanzo cha ulendo wobwereza chimene chili pa tsamba 2 la Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2005, makamaka mbali imene aigogomezera kwambiri imene aitchula kumapeto kwa ulendo wobwerezawo. Uzani ofalitsa kuti agwiritse ntchito mfundo zimenezo kusonyezera chitsanzo cha ulendo wobwereza wotsatira. Kenako wofalitsayo agwiritse ntchito tsamba lomalizira la kuchikuto kwa buloshali popempha munthuyo kuti ayambe naye phunziro la Baibulo, ndipo akonze zodzayamba phunziro 1 m’bulosha la Mulungu Amafunanji pa ulendo wotsatira. Limbikitsani onse kukhala ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo ndi amene analandira bulosha la Dikirani!

Mph. 17: “Anthu a Mitundu Yonse Adzapulumuka.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokamba nkhani imeneyi, gwirizanitsani mfundo zake ndi anthu amene amapezeka m’gawo lanu.

Nyimbo Na. 112 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena