Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2005 Wakuti “Kumvera Mulungu”
1 Yehova Mulungu monga Mlangizi wathu Wamkulu, amakonza zoti tizikhala pamodzi kuti azitilangiza njira zake. (Yes. 30:20, 21; 54:13) Amachita zimenezi kudzera mwa gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, limene limakonza misonkhano monga misonkhano yachigawo imene timakhala nayo chaka chilichonse. (Mat. 24:45-47) Maganizo athu ali ngati a wamasalmo Davide, amene anaimba kuti: “M’masonkhano ndidzalemekeza Yehova.” (Sal. 26:12) Davide anazindikira bwino kufunika kolangizidwa ndi Yehova ndipo anali wokonzeka kupezeka pakati pa anthu a Mulungu nthawi zonse pamene asonkhana pamodzi.
2 Kodi mudzakhala nawo pakati pa anthu amene adzapezeke pa Msonkhano Wachigawo wa chaka chino wakuti “Kumvera Mulungu”? Ngati ndi choncho, mfundo zotsatirazi zikuthandizani pamene mukukonzekera kudzapezekapo.
3 Yambiranitu Pano Kukonzekera Zodzapezeka Masiku Onse: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu.” (Miy. 21:5) Kodi mawu amenewa sakutsimikizira kufunika koyambiratu pano kukonzekera kuti mudzapezeke nawo pamsonkhano? Kuti muonetsetse kuti simudzaphonya mbali iliyonse ya pulogalamu yotsitsimula mwauzimu imeneyi, ndi bwino kuyambiratu pano kukonza zilizonse zofunika kuti mudzapezekepo masiku onse atatu. Ngati mukufunika kupempha tchuthi kwa bwana wanu, chitiranitu zimenezo panopa. Ngati mukufunika kukambirana nkhaniyi ndi mkazi kapena mwamuna wanu amene ndi wosakhulupirira, musaganize zodzachita zimenezo kutatsala nthawi yochepa. Mukakumana ndi zovuta zina zilizonse, pempherani kwa Yehova, muli ndi chikhulupiriro chakuti ndi thandizo lake ‘zolinga zanu zidzakhazikika.’ (Miy. 16:3) Kuwonjezeranso pamenepa, mungachite bwino kwambiri kuthandiza ophunzira Baibulo anu kukonzekera kuti azidzapezeka nawo pa chigawo chilichonse.
4 Malo Ogona: Nthaŵi zambiri abale amakonza okha zokakhala ndi achibale kapena mabwenzi awo m’mizinda yomwe mukuchitikira msonkhano. M’midzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’midadada yomwe antchito odzipereka pamsonkhanopo amanga. Pamisonkhano ina, ena amagona m’nyumba zogona ana asukulu. Ngati mukugona kwa abale kapena achibale, si bwino kupezerapo mwayi pa kuchereza kwa abale athu ndi kukhalabe komweko masiku ena n’cholinga choti muthere komweko tchuti msonkhanowo utatha. Malo ogona amenewo ndi anthaŵi ya msonkhano yokha basi. Amene apatsidwa malowo azionetsetsa kuti iwo pamodzi ndi ana awo akuchita ulemu panyumbapo ndi kuti sakuwononga chilichonse kapena kugwiragwira zinthu kapena kulowa malo osayenera iwo kuloŵamo. Ngati pali zina zimene eninyumba zikuwavuta pankhaniyi, aziuza msanga Dipatimenti Yoona za Malo Ogona pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko adzawathandiza.
5 Anthu Amene Ali ndi Zosowa Zapadera: Mtumwi Paulo anafotokoza za abale ena amene anali ngati ‘chitonthozo’ kwa iye. (Akol. 4:7-11) Njira imodzi imene anam’thandizira Paulo inali yom’samalira pa zosowa zake. Kodi mungachite chiyani kuti mukhale ‘chitonthozo’ kwa ena pamsonkhano? Ofalitsa okalamba, odwala, amene ali mu utumiki wa nthawi zonse, ndi ena otero angafunikire zoyendera kapena malo ogona. Achibale ali ndi mbali yaikulu ya udindo wosamala anthu amenewa. (1 Tim. 5:4) Koma ngati achibale awo sangakwanitse kuwathandiza, okhulupirira anzawo angathe kuwathandiza. (Yak. 1:27) Oyang’anira phunziro la buku ayenera kulankhulana ndi anthu a m’magulu awo amene ali ndi zosowa zapadera kuti nthawi ya msonkhano isanafike aonetsetse ngati akonzeka kudzapita ku msonkhano.
6 Antchito Odzipereka Akufunika: Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri podzichepetsa mwa kuganizira zosowa za ena. (Luka 9:12-17; Yoh. 13:5, 14-16) Amene amadzipereka kugwira ntchito pa msonkhano amaonetsanso mzimu wofananawu. Kuti akwaniritse kusamalira zosowa za madipatimenti pamsonkhano, Makomiti a Msonkhano adzayamba kuitana anthu ena posachedwapa kuti agwire nawo ntchito limodzi. M’pofunika kuti makamaka akulu adzipereke ndi kulandira ntchito zosiyanasiyana. Chifukwa cha mzimu wawo wofunitsitsa amapereka chitsanzo chabwino kwa onse mu mpingo.—1 Pet. 5:2, 3.
7 Zimene Ena Amaona: Ku Bwengu pa Msonkhano Wachigawo, pamene anapereka chilengezo chokhudza zinthu zotayika ndi zotoledwa, munthu wina wachidwi amene anaona abale ndi alongo akutenga zinthu zotayika ndi zotoledwa kupita nazo ku dipatimenti yoona za zimenezi anati: “Sindinkadziwa kuti anthu inu ndinu gulu loona mtima chonchi! Kunena zoona Mulungu ali ndi anthu inu. Ichidi ndiye chikondi chenicheni.” Mwamuna wina amene anakhala nawo pa msonkhano kwa masiku atatu, atasirira khalidwe labwino la abale ndi alongo pa msonkhanopo anati: “Kuyambira lero, banja langa lonse tiyamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova.” Mwinamwake ndemanga zimene zili pamwambapazi zinaperekedwa chifukwa cha khalidwe lanu labwino. Tangoganizirani chisangalalo chimene Yehova amakhala nacho akamationa tikuchita zinthu m’njira imene imam’bweretsera matamando ngati amenewa!—1 Pet. 2:12.
8 Kudzera mwa “mdindo wokhulupirika,” Yehova Mulungu wakonza zoti anthu ake adzasonkhane pamodzi kuti adzalandirenso malangizo auzimu. (Luka 12:42) Kukonzekera kuti mudzapezekepo masiku onse atatu n’kofunika khama, koma kudzakhala kopindulitsa kwambiri. Msonkhano Wachigawo wa chaka chino wakuti “Kumvera Mulungu” mosakayikira udzalimbitsa chikhumbo chathu chotumikira Yehova panopa mpaka muyaya. Ndiyetu tiyeni tiyesetse kutsatira mawu a wamasalmo akuti: “Lemekezani Mulungu m’masonkhano.”—Sal. 68:26.
[Bokosi patsamba 4]
Nthawi za Pulogalamu
Lachisanu ndi Loweruka
8:30 a.m. –4:05 p.m.
Lamlungu
8:30 a.m. –3:10 p.m.