Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Popeza kuti Yesu ali mbadwa ya onse aŵiri Jese ndi Davide, nanga nchifukwa ninji amatchedwanso “muzu” wa makolo akewo Jese ndi Davide?
Nthaŵi zonse mumalingalira za muzu wa mtengo kapena chomera kuyamba kukhalapo pasanabwere thunthu lake kapena nthambi zake. Motero kungaoneke kuti Jese (kapena mwana wakeyo Davide) ayenera kutchedwa muzu umene Yesu potsirizira pake anachokerako. Chikhalirechobe, Yesaya 11:10 ananeneratu kuti Mesiya wakudzayo akakhala “muzu wa Jese,” ndipo Aroma 15:12 anagwiritsira ntchito ulosi umenewu kwa Yesu Kristu. Pambuyo pake Chivumbulutso 5:5 chinamutcha “mkango wochokera m’fuko la Yuda, muzu wa Davide.” Pali zifukwa zomutchera ndi maina ameneŵa.
Kaŵirikaŵiri Baibulo limagwiritsira ntchito chomera, monga mtengo, mofanizira. Nthaŵi zina zimenezi zimazikidwa pa mfundo yakuti pamene mbewu imera ndi kukula, mizu imakula pasanakhale mphukira, nthambi zina, kapena chipatso, zimene zimachirikizidwa ndi mizuyo. Mwachitsanzo, Yesaya 37:31 amati: “Otsala amene opulumuka a nyumba ya Yuda adzaphukanso mizu pansi, nadzabala chipatso pamwamba.”—Yobu 14:8, 9; Yesaya 14:29.
Ngati choipa chichitika ku muzu, mtengo wonsewo umayambukiridwa. (Yerekezerani ndi Mateyu 3:10; 13:6.) Mofananamo, Malaki analemba kuti: “Tsiku lirinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.” (Malaki 4:1) Tanthauzo lake nlomvekera bwino—kudulidwa kotheratu. Makolowo (mizu) akadulidwa, limodzinso ndi ana awo (nthambi).a Zimenezi zimagogomezera thayo limene makolo ali nalo kwa ana awo aang’ono; mtsogolo mosatha mwa ana aang’ono mukadalira pa kaimidwe ka makolo awo pamaso pa Mulungu.—1 Akorinto 7:14.
Chilankhulo cha pa Yesaya 37:31 ndi Malaki 4:1 chimasonyeza mfundo yakuti nthambi (ndi zipatso za pa nthambi zachiŵiri) zimapeza moyo wawo ku muzu. Imeneyi ndiyo mfungulo yodziŵira mmene Yesu aliri “muzu wa Jese” ndi “muzu wa Davide.”
M’njira yakuthupi, Jese ndi Davide anali makolo a Yesu; iwo anali mizu, iye akumakhala mphukira kapena nthambi. Yesaya 11:1 anati za Mesiya wakudzayo: “Padzatuluka mphukira pa tsinde la Jese, ndi nthambi yotuluka m’mizu yake idzabala zipatso.” Mofananamo, pa Chivumbulutso 22:16, Yesu akudzitcha “mbadwa ya Davide.” Koma akudzitchanso “muzu wa Davide.” Chifukwa ninji?
Njira imodzi imene Yesu aliri “muzu” wa Jese ndi Davide ndi yakuti mwa iye mbadwo wawo umakhalabe wamoyo. Palibe munthu aliyense lerolino akhoza kupereka umboni wakuti ali wa fuko la Levi, Dani, kapena ngakhale Yuda, koma tingakhale otsimikizira kuti mzera wa Jese ndi Davide ulipobe wamoyo chifukwa chakuti Yesu tsopano ali wamoyo kumwamba.—Mateyu 1:1-16; Aroma 6:9.
Yesu analandiranso malo monga Mfumu yakumwamba. (Luka 1:32, 33; 19:12, 15; 1 Akorinto 15:25) Zimenezi nzoyenerera unansi wake ndi makolo akewo. Mwaulosi, Davide anatcha Yesu Ambuye wake.—Salmo 110:1; Machitidwe 2:34-36.
Chotsirizira, Yesu Kristu wapatsidwa mphamvu monga Woweruza. Mkati mwa Zaka Chikwi zikudzazo, mapindu a dipo la Yesu adzafikanso kwa Jese ndi Davide. Moyo wawo padziko lapansi panthaŵiyo udzadalira pa Yesu, yemwe adzatumikira monga “Atate Wosatha” kwa iwo.—Yesaya 9:6.
Motero, ngakhale kuti Yesu anaphukira kumzera wa Jese ndi Davide, zimene iye wakhala ndi zimene adzakhalanso akuchita zimamuyeneretsa kutchedwa “muzu wa Jese” ndi “muzu wa Davide.”
[Mawu a M’munsi]
a Mawu apamanda m’Phoenicia wamakedzana analembedwa m’chilankhulo chofanancho. Iwo anati za anthu alionse amene anatsegula manda: “Asakhale ndi muzu pansi kapena chipatso pamwamba!”—Vetus Testamentum, April 1961.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.