Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tanthauzo la Dzina la Mulungu Ndiponso Mmene Tingaligwiritsire Ntchito
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
    • angakhale bwanji pa ubwenzi ndi Mulungu ngati sakudziwa dzina lake lenileni lakuti Yehova? Komanso ngati anthu sagwiritsa ntchito dzina la Mulungu, sangadziwenso tanthauzo lake. Kodi dzina la Mulungu limatanthauza chiyani?

      Mulungu anafotokoza yekha tanthauzo la dzina lake kwa mtumiki wake wokhulupirika Mose. Pamene Mose anafunsa za dzina la Mulungu, Yehova anamuyankha kuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.” (Ekisodo 3:14) Choncho Yehova akhoza kukhala chilichonse chimene chingafunikire kuti akwaniritse cholinga chake. Akhozanso kuchititsa kuti chilichonse chokhudza chilengedwe kapena cholinga chake chitheke.

      Tiyerekeze kuti inuyo muli ndi mphamvu zotha kukhala chilichonse chimene mukufuna. Kodi anzanu mungawachitire zotani? Ngati mnzanu wina atadwala kwambiri, mukhoza kukhala dokotala n’kumuchiritsa. Ndipo ngati wina atakhala ndi vuto la zachuma, mukhoza kukhala munthu wolemera n’kumuthandiza. Komabe tikudziwa kuti inuyo simungathe kukhala aliyense amene mukufuna, ndipo ndi mmene tonsefe tilili. Pamene mukupitiriza kuphunzira Baibulo, mudzadabwa kudziwa mmene Yehova amakhalira chilichonse chimene chikufunikira kuti akwaniritse zimene walonjeza. Mudzaonanso kuti amasangalala kugwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza anthu amene amamukonda. (2 Mbiri 16:9) Koma anthu amene sadziwa dzina la Yehova alibe mwayi wothandizidwa mwa njira imeneyi.

      Zimene takambiranazi ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti dzina la Mulungu, lakuti Yehova, ndi loyenera kuti lizipezeka m’Baibulo. Kudziwa tanthauzo lake ndiponso kuligwiritsa ntchito, kudzatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba, Yehova.a

  • Mmene Ulosi wa Danieli Unasonyezera Nthawi Imene Mesiya Adzafike
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
    • ZAKUMAPETO

      Mmene Ulosi wa Danieli Unasonyezera Nthawi Imene Mesiya Adzafike

      MNENERI Danieli anakhala ndi moyo zaka zoposa 500 Yesu asanabadwe. Komabe Yehova anamuululira Danieli zinthu zimene zinathandiza anthu kudziwa nthawi yeniyeni imene Yesu adzadzozedwe, kapena kuti kusankhidwa, kukhala Mesiya, kapena kuti Khristu. Danieli anauzidwa kuti: “Uyenera kudziwa ndi kuzindikira kuti kuchokera pamene mawu adzamveka onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso, kufika pamene Mesiya Mtsogoleri adzaonekere, padzadutsa milungu 7, komanso milungu 62.”—Danieli 9:25.

      Kuti tidziwe nthawi yeniyeni yofikira Mesiya, choyamba tiyenera kudziwa kuti kuwerengera nthawiyi kukuyambira pati. Malinga ndi ulosiwu, nthawiyi ikuyambira “pamene mawu adzamveka onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso.” Kodi mawu amenewa anamveka liti? Malinga ndi zimene Nehemiya ananena, mawu oti mpanda wa Yerusalemu umangidwenso anamveka “m’chaka cha 20 cha mfumu Aritasasita.” (Nehemiya 2:1, 5-8) Olemba mbiri yakale amatsimikizira kuti Aritasasita anayamba kulamulira m’chaka cha 475 B.C.E. Choncho, chaka cha 20 cha ulamuliro wake chinali chaka cha 455 B.C.E. Tsopano tapeza poyambira kuwerengera nthawi yonena za kubwera kwa Mesiya, kuti ndi chaka cha 455 B.C.E.

      Danieli anasonyezanso kutalika kwa nthawi imene idzadutse kuti “Mesiya Mtsogoleri” aonekere. Ulosi wake unanena za “milungu 7, komanso milungu 62,” yomwe ikaphatikizidwa ndi milungu 69. Kodi nthawi imeneyi ndi yaitali bwanji? Mabaibulo ambiri amasonyeza kuti milungu imeneyi si ya masiku 7 okha, koma ndi milungu ya zaka. Choncho mlungu umodzi ukuimira zaka 7. Zomanena kuti zaka 7 ndi mlungu umodzi, sizinali zachilendo kwa Ayuda akale. Mwachitsanzo, chaka cha 7 chilichonse chinali chaka chawo cha Sabata. (Ekisodo 23:10, 11) Choncho mlungu uliwonse unkakhala ndi zaka 7, zomwe zikusonyeza kuti milungu 69 imeneyi ndi zaka zokwanira 483.

      Apatu chatsala n’kuwerengetsera. Kuwerengetsera zaka 483 kuchokera m’chaka cha 455 B.C.E., kukutifikitsa mu 29 C.E. Chaka chimenechi ndi chimene Yesu anabatizidwa n’kukhala Mesiya.a (Luka 3:1, 2, 21, 22) Kumenekutu n’kukwaniritsidwa kochititsa chidwi kwa ulosi wa m’Baibulo.

      Tchati: Ulosi wa m’chaputala 9 cha buku la Danieli wonena za milungu 70 unaneneratu za kubwera kwa Mesiya

      a Kuchokera mu 455 B.C.E. kufika mu 1 B.C.E panadutsa zaka 454. Kuchokera mu 1 B.C.E. kufika 1 C.E. panali chaka chimodzi chokha. Ndipo kuchokera mu 1 C.E. kufika mu 29 C.E. panadutsa zaka 28. Tikaphatikizira, zaka zimenezi zikukwana zaka 483. Yesu ‘anaphedwa’ m’chaka cha 33 C.E., womwe ndi mlungu wa 70. (Danieli 9:24, 26) Onani buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! Mutu 11, ndi Kukambitsirana za m’Malemba, tsamba 231-233. Mabukuwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

  • Yesu Ndi Mesiya Amene Mulungu Ananeneratu Kuti Adzabwera
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
    • ZAKUMAPETO

      Yesu Ndi Mesiya Amene Mulungu Ananeneratu Kuti Adzabwera

      POFUNA kutithandiza kuti tidzathe kuzindikira Mesiya, Yehova Mulungu anauzira aneneri ambiri kuti alembe nkhani zokhudza kubadwa kwa Mpulumutsiyu, utumiki wake, ndiponso imfa yake. Maulosi onsewa anakwaniritsidwa pa Yesu Khristu. N’zochititsa chidwi kuona mmene maulosiwa anafotokozera zinthu motsatirika komanso molondola. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tikambirane maulosi angapo okhudza kubadwa kwa Mesiya ndiponso zinthu zimene zinachitika ali mwana.

      Mneneri Yesaya ananeneratu kuti Mesiya adzabadwira m’banja la Mfumu Davide. (Yesaya 9:7) Yesu anabadwiradi m’banja la Davide.—Mateyu 1:1, 6-17.

      Mneneri winanso wa Mulungu, dzina lake Mika, ananeneratu kuti mwana ameneyu akadzakula adzakhala mfumu komanso kuti adzabadwira ku “Betelehemu Efurata.” (Mika 5:2) Pa nthawi imene Yesu anabadwa, ku Isiraeli kunali mizinda iwiri imene inkadziwika ndi dzina lakuti Betelehemu. Mzinda umodzi unali kufupi ndi ku Nazareti, pomwe wina unali kufupi ndi Yerusalemu ku Yuda. Mzinda wa Betelehemu wakufupi ndi Yerusalemu poyamba unkatchulidwa kuti Efurata ndipo kumeneku ndi komwe Yesu anabadwira mogwirizana ndi mmene ulosi unanenera.—Mateyu 2:1.

      Ulosi wina unaneneratu kuti Mwana wa Mulungu adzaitanidwa kuti “atuluke mu Iguputo.” Yesu ali mwana makolo ake anapita naye ku Iguputo. Iwo anabwerera naye kwawo pambuyo pa imfa ya Herode ndipo kumeneku kunali kukwaniritsidwa kwa ulosiwu.—Hoseya 11:1; Mateyu 2:15.

      Pa tchati chimene chili patsamba 200, malemba amene ali pansi pa mutu wakuti “Ulosi” akufotokoza zinthu zosiyanasiyana zokhudza Mesiya. Yerekezetsani zimene malemba amenewa akunena ndi zomwe zili m’malemba omwe ali pansi pa mutu wakuti “kukwaniritsidwa kwake.” Kuchita zimenezi kungawonjezere zifukwa zina zokuchititsani kukhulupirira kuti Mawu a Mulungu ndi oona.

      Mukamawerenga malembawa muyenera kukumbukira kuti malemba amene ali ndi ulosiwo analembedwa zaka zambirimbiri Yesu asanabadwe. Yesu ananena kuti: “Zonse zokhudza ine zolembedwa m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri ndi m’Masalimo ziyenera kukwaniritsidwa.” (Luka 24:44) Ndipo mukaona m’Baibulo lanu mungatsimikizire kuti maulosi onsewa anakwaniritsidwadi.

      MAULOSI ONENA ZA MESIYA

      CHOCHITIKA

      ULOSI

      KUKWANIRITSIDWA KWAKE

      Adzabadwira m’fuko la Yuda

      Genesis 49:10

      Luka 3:23-33

      Adzabadwa kwa namwali

      Yesaya 7:14

      Mateyu 1:18-25

      Adzabadwira m’banja la Mfumu Davide

      Yesaya 9:7

      Mateyu 1:1, 6-17

      Yehova adzalengeza yekha kuti ndi mwana wake

      Salimo 2:7

      Mateyu 3:17

      Anthu ambiri sadzamukhupirira

      Yesaya 53:1

      Yohane 12:37, 38

      Adzalowa mu Yerusalemu atakwera pa bulu

      Zekariya 9:9

      Mateyu 21:1-9

      Mnzake adzamupereka kwa adani

      Salimo 41:9

      Yohane 13:18, 21-30

      Munthu wom’perekayo adzalandira ndalama 30 zasiliva

      Zekariya 11:12

      Mateyu 26:14-16

      Sadzayankha chilichonse kwa anthu omuimba mlandu

      Yesaya 53:7

      Mateyu 27:11-14

      Adzachita maere pogawana zovala zake

      Salimo 22:18

      Mateyu 27:35

      Adzanyozedwa ali pamtengo wozunzikirapo

      Salimo 22:7, 8

      Mateyu 27:39-43

      Mafupa ake sadzathyoledwa

      Salimo 34:20

      Yohane 19:33, 36

      Adzaikidwa m’manda limodzi ndi anthu olemera

      Yesaya 53:9

      Mateyu 27:57-60

      Adzaukitsidwa thupi lake lisanawonongeke

      Salimo 16:10

      Machitidwe 2:24, 27

      Adzakwezedwa kudzanja lamanja la Mulungu

      Salimo 110:1

      Machitidwe 7:56

  • Kudziwa Zoona Zokhudza Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
    • ZAKUMAPETO

      Kudziwa Zoona Zokhudza Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera

      ANTHU amene amakhulupirira kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyera amanena kuti mwa Mulungu mmodzi muli anthu atatu. Iwo amakhulupirira kuti atatu onsewa ndi ofanana mphamvu komanso onse alibe chiyambi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena